Yakobo Anaona Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
MOYO wa Yakobo unali wa mavuto okhaokha. Iye anakakamizika kuthaŵa kuti apulumutse moyo wake chifukwa choti mchimwene wake amene anabadwa naye mapasa anali atakwiya koopsa ndipo anali kufuna kumupha. M’malo mokwatira mtsikana amene maso ake anadyerera, anam’pusitsa n’kuyamba wakwatira wina, mapeto ake n’kukhala ndi akazi anayi ndipo izi zinam’dzetsera mavuto ankhaninkhani. (Genesis 30:1-13) Anagwirira ntchito zaka 20 mkulu wina amene ankam’dyera masuku pamutu. Analimbana ndi mngelo ndipo analumala. Mwana wake wamkazi anagwiriridwa, ana ake aamuna n’kupulula miyandamiyanda ya anthu, ndipo analira chifukwa cha kusoŵa komvetsa chisoni kwa mwana wake amene ankam’konda kwambiri ndiponso imfa ya mkazi wake wapamtima. Atakakamizika kusamuka ali wokalamba pothaŵa njala, iye anati masiku ake anali “oŵerengeka ndi oipa.” (Genesis 47:9) Ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, Yakobo anali munthu wokonda zinthu zauzimu, amene ankakhulupirira Mulungu. Kodi anaika chikhulupiriro chake pachabe? Kodi tingaphunzirenji mwa kupenda zinthu zochepa za moyo wa Yakobo?
Anali Wosiyana Kwambiri ndi Mchimwene Wake
Pamene panagona vuto kuti Yakobo asagwirizane ndi mchimwene wake panali pakuti iye ankaona chuma chauzimu kukhala chofunika pamene Esau ankachiona monga chopanda ntchito. Mtima wa Yakobo unali pa lonjezo limene Mulungu anapanga kwa Abrahamu ndipo anadzipereka kusamalira banja limene Mulungu anasankha kulandira lonjezolo. Motero, Yehova ‘anam’konda.’ Yakobo anali “wofatsa,” mawu osonyeza kuti anali wakhalidwe labwino kwambiri. Mosiyana ndi zimenezi, Esau analibe chidwi ndi choloŵa chake chauzimu moti anachigulitsa kwa Yakobo pamtengo wotsika kwambiri. Movomerezedwa ndi Mulungu, Yakobo atanena kuti iye ndiye woyamba kubadwa ndi kulandira madalitso omwe poyamba mchimwene wake ndiye anayenera kulandira, Esau anakalipa koopsa. Motero Yakobo anathaŵa n’kusiya zonse zomwe ankazikonda, koma n’zosakayikitsa kuti zomwe zinadzachitika zinam’limbitsanso mtima.—Malaki 1:2, 3; Genesis 25:27-34; 27:1-45.
M’maloto, Mulungu anaonetsa Yakobo angelo akukwera ndi kutsika makwerero kapena miyala yosanja kuchoka pansi mpaka kumwamba ndipo anafotokoza kuti adzateteza Yakobo ndi mbewu yake. “Mwa iwe ndi mu mbewu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.”—Genesis 28:10-15.
Koma ndiye ndi zolimbikitsatu zimenezi! Yehova anam’tsimikizira kuti malonjezo amene anapanga kwa Abrahamu ndi Isake adzalemeretsa mwauzimu banja la Yakobo. Yakobo anadziŵitsidwa kuti angelo angathe kutumikira anthu amene Mulungu akuwayanja, ndipo anam’tsimikizira kuti Mulungu adzam’teteza. Poyamikira, Yakobo analumbira kuti adzakhala wokhulupirika kwa Yehova.—Genesis 28:16-22.
Yakobo sanalande choloŵa cha Esau. Anyamataŵa asanabadwe, Yehova ananena kuti “wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.” (Genesis 25:23) Wina angafunse kuti, ‘Kodi sizikanakhala zosavuta ngati Mulungu akanapangitsa kuti Yakobo ayambirire kubadwa?’ Zomwe zinadzachitika pambuyo pake zimatiphunzitsa mfundo zofunika kwambiri. Mulungu sasungira madalitso anthu amene akuganiza kuti ndiwo ayenera kulandira madalitsowo, koma amachitira chisomo anthu amene iye wafuna. Motero, ukulu unapita kwa Yakobo, osati kwa mchimwene wake, amene analibe nawo ntchito. Mofanana ndi zimenezi, chifukwa chakuti mtundu wa Ayuda unasonyeza mtima wonga wa Esau, iwo unaloŵedwa m’malo ndi Israyeli wauzimu. (Aroma 9:6-16, 24) Kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova masiku ano sicholoŵa chosachigwirira ntchito, ngakhale munthu atabadwira m’banja kapena pamalo a anthu oopa Mulungu. Onse ofuna madalitso a Mulungu ayenera kuyesetsa kukhala oopa Mulungu, kumaonadi zinthu zauzimu kukhala zofunika.
Analandiridwa ndi Labani
Pofika ku Padanaramu kuti akayang’ane mkazi pakati pa abale ake, Yakobo anakumana ndi msuweni wake Rakele, mwana wa Labani, pachitsime ndipo anagubuduza mwala wolemera kwambiri wotsekera chitsimecho kuti ziŵeto zomwe Rakele ankadyetsa zimwe madzi.a Rakele analiutsa liwiro la kumudzi kukanena za kufika kwake, ndipo Labani anathamangira komweko kukakumana ndi Yakobo. Labani ayenera kuti anakhumudwa ngati ankakumbukira za chuma chomwe banja lake linalandira kwa mtumiki wa Abrahamu, chifukwa Yakobo anali chimanjamanja. Koma Labani mwachionekere anaona kenakake komwe angapindule nako mwa Yakobo, anapeza munthu wolimbikira ntchito.—Genesis 28:1-5; 29:1-14.
Yakobo anawasimbira nkhani yake. Sizikudziŵika bwinobwino ngati anafotokoza chinyengo chimene anachita kuti alandire choloŵa cha ukulu, koma atamva “zinthu zonsezo,” Labani anati: “Etu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa.” Katswiri wina wa maphunziro ananena kuti n’kutheka kuti mawuŵa anaonedwa monga kum’pempha Yakobo kuti azikhala naye kapena kuti Labani akuvomera kuteteza Yakobo monga mbale wake. Mulimonse mmene zinalili, Labani mwamsangamsanga anayamba kuganizira mmene angapindulire ndi mphwakeyu.
Labani anayambitsa nkhani yomwe inawakanganitsa zaka 20 zotsatira. “Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe?” anafunsa motero. “Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?” Ngakhale kuti Labani ankafuna kuoneka ngati malume wabwino kwambiri, iye anathetsa ubale wake ndi Yakobo, n’kuyamba kumuona ngati wantchito. Poti Yakobo anali atakonda Rakele, iye anayankha kuti: “Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng’ono.”—Genesis 29:15-20.
Anthu anali kutomerana mwa kupereka malowolo ku banja la mkazi. Pambuyo pake Chilamulo cha Mose chinadzaika masekeli 50 monga mtengo wa anamwali amene agwiriridwa. Katswiri wina wamaphunziro, Gordon Wenham, ananena kuti “chuma cha malowolo sichinali kuposa pamenepa,” koma nthaŵi zambiri ankapereka malowolo “ochepa kwambiri.” (Deuteronomo 22:28, 29) Yakobo sakanatha kupereka malowolowo. Anadzipereka kuti am’gwirire ntchito Labani zaka zisanu ndi ziŵiri. Wenham anapitiriza kuti: ‘Popeza kuti kale m’masiku a Ababulo malipiro a anthu aganyu anali pakati pa sekeli latheka ndi sekeli limodzi pamwezi, (pakati pa masekeli 42 ndi 84 m’zaka zisanu ndi ziŵiri zathunthu), Yakobo anali kulonjeza Labani malowolo ochuluka kwambiri kuti atenge Rakele.’ Labani sanalimbelimbe, anavomera.—Genesis 29:19.
Kwa Yakobo, zaka zisanu ndi ziŵiri zinali ngati “masiku oŵerengeka,” poti anam’konda kwambiri Rakele. Kenako, iye anaitanitsa mkazi wake wophimbidwa bwinobwino, osadziŵa n’komwe za chinyengo cha Labani. Taganizirani mmene anakhumudwira m’maŵa mwake ataona kuti sanagone ndi Rakele, koma wagona ndi Leya, mkulu wake! Yakobo anafunsa kuti: “Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?” Labani anayankha kuti: “Satero kwathu kuno, kupatsa wamng’ono asanapatse wamkulu. Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuwonjezera zaka zina zisanu ndi ziŵiri.” (Genesis 29:20-27) Poti sakanatha kudziteteza ndiponso anali atamunyenga kale, Yakobo sakanachitira mwina koma kuvomera zimenezi ngati ankafuna Rakele.
Mosiyana ndi nthaŵi yoyamba ija, zaka zina zisanu ndi ziŵiri zotsatirazi zinali zowawa kwambiri. Kodi Yakobo akanaiŵala bwanji chinyengo choipa cha Labani? Nanga bwanji za Leya, amene anagwirizana ndi zachinyengozo? Inde, Labani sankaganizira n’komwe za tsogolo lopweteka lomwe anali kukonzera Leya ndi Rakele. Ankangofuna kuti zake ziyende basi. Rakele amene anali wokhumudwa kale n’kale anavutikanso ndi nsanje Leya atabereka ana aamuna anayi motsatizana, pamene iye anali wosabala. Kenako chifukwa chofunitsitsa ana, Rakele anangopereka mtsikana wake wantchito kuti am’berekere ana, ndipo mwampikisano, Leya nayenso anachita chimodzimodzi. Mapeto ake Yakobo anakhala ndi akazi anayi, ana 12, ndipo m’banja lake munalibe mtendere ngakhale pang’ono. Komabe, Yehova anali kupanga Yakobo kukhala mtundu waukulu.—Genesis 29:28–30:24.
Anadalitsidwa ndi Yehova
Ngakhale kuti anali m’mavuto, Yakobo anaona kuti Mulungu anali naye monga momwe analonjezera. Nayenso Labani anaona zimenezi, chifukwa chakuti ziŵeto zochepa zomwe anali nazo pamene Yakobo ankafika zinaswana kwambiri pamene zinkasamalidwa ndi mphwakeyu. Posafuna kuti Yakobo azipita, Labani anam’pempha kuti atchule malipiro omwe akufuna kuti am’gwirire ntchito inanso, ndipo apa Yakobo anasankha ziŵeto zamawangamawanga zomwe zibadwe pa ziŵeto za Labani. Akuti m’dera limeneli, nkhosa kaŵirikaŵiri zinkakhala zoyera ndipo mbuzi zinkakhala zakuda kapena zofiirira; ziŵeto zochepa chabe n’zomwe zinkakhala zamawangamawanga. Motero poganiza kuti uwu unali mwayi wake, Labani sanalimbelimbe, anangovomera ndipo mwamsangamsanga anapatula ziŵeto zamawangamawanga n’kuziika kutali kuti zisamayenderane ndi ziŵeto zomwe ankasamalira Yakobo. Mwachidziŵikire iye ankaganiza kuti Yakobo sapindula nalo kwambiri panganolo, moti malipiro ake sadzakwana n’komwe malipiro a mwana mmodzi pa ana asanu alionse a mbuzi ndi nkhosa omwe abusa ambiri akale ankalandira. Koma Labani analemba m’madzi, chifukwa chakuti Yehova anali ndi Yakobo.—Genesis 30:25-36.
Motsogozedwa ndi Mulungu, Yakobo anabereketsa ziŵeto zokula bwino ndiponso zamphamvu zomwe iye ankafunazo. (Genesis 30:37-42) Njira yake yobereketsera ziŵeto sinali yolondola. Ndipo, Nahum Sarna, katswiri wa maphunziro, anati, “tikatengera pa sayansi, ziŵeto zomwe iye ankafunazo zikanabadwa mwa kukweretsa ziŵeto zamtundu umodzi zomwe zingathe kubereka ana amawangamawanga, [ndipo] ziŵeto zoterozo zimadziŵika ndi . . . mphamvu za ana omwe zabereka.”
Ataona zotsatira zake, Labani anayesa kusintha pangano lija lakuti ziŵeto zamizeramizera, madonthomadontho, ndiponso zamawangamawanga ndi za mphwake. Ankangofuna kuti zake ziyende, koma zinalibe kanthu kuti Labani analisintha motani panganoli, Yehova anaonetsetsa kuti Yakobo zikumuyendera bwino nthaŵi zonse. Labani, kwake kunali kumangokukuta mano basi. M’nthaŵi yochepa, Yakobo analemera kwambiri, anali ndi ziŵeto zambiri, antchito, ngamila, ndiponso abulu, osati chifukwa cha nzeru zake, koma chifukwa chakuti Yehova anali kum’thandiza. Kenako anauza Rakele ndi Leya kuti: “Atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanam’lole iye andichitire ine choipa. . . . Mulungu anazichotsa zoŵeta za atate wanu, nandipatsa ine.” Yehova anatsimikiziranso Yakobo kuti Iye waona zonse zomwe Labani anali kuchita ndipo Yakobo asade nkhaŵa. Mulungu anati: “Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako ndipo ndidzakuchitira iwe bwino.”—Genesis 31:1-13; 32:9.
Ndiyeno, atam’chokera Labani wachinyengoyu, Yakobo ananyamuka ulendo wakwawo. Ngakhale kuti panali patatha za 20, iye ankamuopabe Esau, ndipo anachita mantha kwambri atamva kuti Esau akubwera ndi amuna mazana anayi. Kodi Yakobo akanatani? Popeza anali munthu wokonda zauzimu wokhulupirira Mulungu nthaŵi zonse, iye anachita zinthu mwachikhulupiriro. Anapemphera, n’kuvomera kuti iye sanali woyenerera kuti Yehova amuchitire zabwino ndipo anapempha Mulungu chifukwa cha malonjezo Ake kuti apulumutse iye ndi banja lake m’dzanja la Esau.—Genesis 32:2-12.
Kenako panachitika zinthu zosayembekezeka. Munthu wina wachilendo, amene anali mngelo, analimbana ndi Yakobo usiku, ndipo atam’gwira kamodzi kokha anabzungunula ntchafu ya Yakobo. Iye anakana kum’siya mngeloyo pokhapokha atayamba wam’dalitsa. Kenako mneneri Hoseya ananena kuti Yakobo “analira, nam’pembedza [kuti am’dalitse, NW].” (Hoseya 12:2-4; Genesis 32:24-29) Yakobo ankadziŵa kuti kuoneka kwa angelo m’mbuyomo kunali kogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwa pangano la Abrahamu mwa mbewu yake. Motero anayesetsa kulimbana naye zolimba ndipo anadalitsidwa. Panthaŵiyi, Mulungu anam’sintha dzina n’kukhala Israyeli, kutanthauza kuti “Woyesana (Wolimbana) ndi Mulungu,” kapena kuti “Mulungu Amayesa.”
Kodi Ndinu Wofunitsitsa Kulimbana?
Kulimbana ndi mngelo ndiponso kukumananso ndi Esau sanali mavuto okhawo omwe Yakobo anafunika kuthana nawo. Komabe, zochitika zomwe taonazi zikusonyeza umunthu wake. Pamene Esau anali woti sakanatha kupirira njala yochepa chabe imene anali nayo kuti ateteze ukulu wake, Yakobo anayesetsa pamoyo wake wonse kuti alandire madalitso, ngakhale kulimbana ndi mngelo kumene. Monga momwe Mulungu analonjezera, Yakobo anatsogoleredwa ndiponso kutetezedwa ndi Mulungu, anakhala kholo la mtundu waukulu ndiponso kholo la Mesiya.—Mateyu 1:2, 16.
Kodi ndinu wofunitsitsa kuchita khama kuti muyanjidwe ndi Yehova, ndiye ngati kuti mukuchita kulimbira kuti muyanjidwe? Masiku ano, moyo ndi wamavuto ndiponso zopinga zambiri kwa anthu omwe akufuna kuchita zofuna za Mulungu, ndipo nthaŵi zina sintchito yamaseŵera kuti asankhe zochita zoyenerera. Komabe chitsanzo chabwino cha Yakobo chimatilimbikitsa kwambiri kuti tipitirize kuyembekezera mphoto yomwe Yehova akutilonjeza.
[Mawu a M’munsi]
a Zinachitikazi zikufanana ndi nthaŵi imene mayi wa Yakobo, Rebeka, anamwetsa madzi ngamila za Eliezere. Kenako Rebeka anathamangira kumudzi kukafotokoza za kufika kwa mlendoyo. Ataona zinthu zagolide zomwe mlongo wake analandira monga mphatso, Labani anathamanga kukalandira Eliezere.—Genesis 24:28-31, 53.
[Zithunzi patsamba 31]
Yakobo anayesetsa pamoyo wake wonse kuti alandire madalitso