Kodi Mukufuna Yehova Mwakhama?
MWAMUNA wina wachikristu anali kufunitsitsa kuuza mapasinjala anzake uthenga wabwino wa m’Baibulo popita kuntchito m’sitima. (Marko 13:10) Koma, anali kuchita mantha. Kodi anangosiyira pomwepo? Ayi, anapempherera nkhaniyo ndi mtima wonse ndipo anayesetsa kuphunzira zimene angachite kuti ayambitse kukambirana. Yehova Mulungu anayankha pempho lake ndipo anamupatsa mphamvu kuti alalikire.
Khama limeneli n’lofunika pamene tikufuna Yehova ndiponso madalitso ake. Mtumwi Paulo anati: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye [mwakhama, NW].” (Ahebri 11:6) Kungofuna Yehova sikokwanira. Verebu lachigiriki limene alimasulira kuti “kufuna mwakhama” limatanthauza kuyesetsa kwambiri ndiponso kulimbikira. Zimenezi zimafunika kuzichita ndi mtima wonse, nzeru zonse, moyo wonse, ndi mphamvu zonse. Ngati tikufuna Yehova mwakhama, sitichita zinthu mwamphwayi, mosaikirapo mtima, kapena mwaulesi. M’malo mwake, timam’funa mwachangu.—Machitidwe 15:17.
Anthu Amene Anafuna Yehova Mwakhama
M’Malemba muli zitsanzo zambiri za anthu amene anayesetsa kwambiri pofuna Yehova. Mmodzi wa iwo anali Yakobo, amene analimbana mwamphamvu ndi mngelo wa Mulungu mpaka mbandakucha. Mngelo ameneyu anali ndi thupi la munthu. Pachifukwa chimenechi, Yakobo anapatsidwa dzina lakuti Israyeli (Woyesana ndi Mulungu) chifukwa ‘anayesana,’ kapena kuti anapirira, anayesetsa, analimbana, ndi Mulungu. Mngeloyo anamudalitsa chifukwa cha khama lake.—Genesis 32:24-30.
Ndiye panali mayi wina wa ku Galileya amene sanatchulidwe dzina, amene anadwala nthenda yokha mwazi kwa zaka 12, ndipo anamva “zowawa zambiri.” Ndi matendaŵa sanafunike kukhudza anthu ena. Komabe, analimba mtima kupita kukakumana ndi Yesu. Iye ankati: “Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.” Tamuganizirani akuvutika kuti adutse ‘khamu lalikulu limene limam’tsata [Yesu], ndi kum’kanikiza Iye.’ Mkaziyu atangokhudza chovala cha Yesu, anazindikira kuti “kasupe wa nthenda yake adaphwa”—nthenda yake yosachiritsikayo inachiritsika! Yesu atafunsa kuti, “Ndani anakhudza zovala zanga?” mkaziyo anachita mantha. Koma Yesu anamuuza mwachifundo kuti: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.” Khama lake linapindula.—Marko 5:24-34; Levitiko 15:25-27.
Nthaŵi ina, mkazi wa ku Foinike anam’pempha Yesu ndi mtima wonse kuchiritsa mwana wake wamkazi. Yesu anayankha kuti sikunali koyenera kupereka chakudya cha ana kwa tiagalu. Iye anatanthauza kuti sangasamalire amene sanali Aisrayeli kusiya Ayuda oyenerera. Atazindikira mfundo ya fanizo lakelo, mkaziyo anapemphabe kuti: “Etu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye awo.” Yesu ataona kuti mkaziyo anali ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso woona mtima anati: “Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira.”—Mateyu 15:22-28.
Kodi n’chiyani chikanachitika anthu ameneŵa akanapanda kulimbikira pa zimene amafuna? Kodi akanalandira madalitso akanakhala kuti anafooka atangokumana ndi zopinga kapena atangokanidwa koyamba? Ayi. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza bwino zedi mfundo imene Yesu anaphunzitsa, yakuti kulimbikira, kapena kuti “liuma,” n’loyenera, ngakhale lofunika, pofuna Yehova.—Luka 11:5-13.
Mogwirizana ndi Chifuno Chake
M’nkhani zimene takambiranazi, za anthu amene anachiritsidwa mozizwitsa, kodi ndi khama lokha limene linali kufunika kuti achiritsidwe? Ayi, zopempha zawo zinafunika kugwirizana ndi chifuno cha Mulungu. Yesu anapatsidwa mphamvu zochitira zinthu zozizwitsa kuti apereke umboni wapadera wakuti anali Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwayo. (Yohane 6:14; 9:33; Machitidwe 2:22) Ndiponso, zozizwitsa zimene Yesu anachita zinali zitsanzo za madalitso aakulu a padziko lapansi amene Yehova adzapatse anthu mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1000.—Chivumbulutso 21:4; 22:2.
Chifuno cha Mulungu sichakutinso anthu amene ali m’chipembedzo choona akhale ndi mphamvu yochitira zozizwitsa, monga kuchiritsa ndiponso kulankhula malilime. (1 Akorinto 13:8, 13) M’malo mwake, chifuno chake masiku athu ano ndi zinthu monga kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse kuti ‘anthu onse afike pozindikira choonadi.’ (1 Timoteo 2:4; Mateyu 24:14; 28:19, 20) Atumiki a Mulungu angayembekezere Mulungu kumva mapemphero awo ochokera pansi pa mtima ngati ayesetsa ndi mtima wonse ndiponso mogwirizana ndi chifuno chake.
Ena angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani tifunika kuyesetsa pamene cholinga cha Mulungu chidzachitikabe basi?’ Ngakhale kuti n’zoona kuti Yehova adzachita cholinga chake kaya anthu achite zotani, iye amasangalala kukhala ndi anthu amene akuchita chifuno chake. Yehova tingamuyerekezere ndi munthu womanga nyumba. Womangayo ali ndi pulani yonse ya nyumbayo, koma amasankha zinthu zomangira zopezeka kumaloko. Mofananamo, Yehova ali ndi ntchito yoti achite masiku ano ndipo amasangalala kugwiritsa ntchito atumiki ake odzipereka.—Salmo 110:3; 1 Akorinto 9:16, 17.
Lingalirani nkhani ya mnyamata wina dzina lake Toshio. Atafika kusukulu ya sekondale, anafuna kulalikira mmene angathere m’gawo lake lapadera limeneli. Nthaŵi zonse ankakhala ndi Baibulo ndipo ankayesetsa kwambiri kukhala Mkristu wamakhalidwe abwino. Chakumapeto kwa chaka chake choyamba pasukulupo, panapezeka mpata wolankhula kwa anzake m’kalasi. Toshio anapempha Yehova kuti amuthandize ndipo anasangalala kuona kalasi yonse ikumvetsera kwambiri nkhani yake yakuti “Ndimafuna Kuti Upainiya Udzakhale Ntchito Yanga.” Anafotokoza kuti akufuna kukhala mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Mmodzi mwa anzakewo anavomera kuphunzira naye Baibulo ndipo anapita patsogolo mpaka kubatizidwa. Toshio anapindula kwambiri chifukwa cha khama lake pochita zinthu mogwirizana ndi mapemphero ake.
Kodi Ndinu Wakhama Bwanji?
Mungasonyeze m’njira zambiri kuti mukufuna Yehova ndi madalitso ake mwakhama. Choyamba, pali zinthu zofunika kwambiri zimene mungachite, monga kukonzekera bwino misonkhano yachikristu. Mumasonyeza khama limene mukuchita pofuna Yehova mwa kupereka mayankho okonzedwa bwino, nkhani zolimbikitsa, ndiponso zitsanzo zogwira mtima. Mungasonyezenso khama lanu mwa kuwongolera utumiki wanu. Bwanji osayesa kukhala waubwenzi mukafika pakhomo la munthu ndi kugwiritsa ntchito mawu oyamba ogwira mtima oyenerana ndi gawo lanu? (Akolose 3:23) Mwa kudzipereka ndi mtima wonse, mwamuna wachikristu angathe kulandira maudindo mu mpingo, monga kukhala mtumiki wotumikira kapena mkulu. (1 Timoteo 3:1, 2, 12, 13) Mwa kudzipereka, mungapeze chimwemwe chifukwa cha mzimu wanu wopatsa. Mungathe kufunsira kuti mukagwire ntchito yomanga nthambi kapena kukatumikira ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Ngati muli mbale woyenera ndiponso wosakwatira, mwina mungafune kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, imene imathandiza abale auzimu kukhala abusa abwino. Ngati muli pabanja, mwina utumiki wa umishonale ungakhale njira yosonyezera kuti mumafunitsitsa kutumikira kwambiri Yehova. Mwinanso mungathe kusamukira kumene kukufunika anthu ambiri olalikira Ufumu.—1 Akorinto 16:9.
Chofunika kwambiri ndi mtima umene mumachita nawo utumiki wanu. Kaya mwapatsidwa udindo wotani, usamalireni mwakhama, mwamphamvu, ndiponso ndi “mtima woona.” (Machitidwe 2:46; Aroma 12:8) Muyenera kuona utumiki uliwonse monga mpata wosonyeza kuti mumafunitsitsa kutamanda Yehova. Nthaŵi zonse pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni, ndipo chitani zonse zimene mungathe. Mukatero mudzapindula kwambiri.
Khama Lipindula
Kodi mukum’kumbukira mwamuna uja wachikristu amene anapemphera kuti athe mantha n’cholinga choti azilalikira kwa mapasinjala anzake? Yehova anadalitsa zimene iye anali kufunitsitsa ndi mtima wonse. Mbale uja anayesetsa kugwiritsa ntchito mawu oyamba osangalatsa, ndipo anasankha nkhani zimene angayambitsire kukambirana. Iye anatha kugwiritsa ntchito Baibulo mogwira mtima kulalikira kwa bambo amene anali kuda nkhawa ndi kusokonezeka kwa maubale a anthu. Atapanga maulendo obwereza angapo kwa mwamuna ameneyo m’sitimamo, anayamba naye phunziro la Baibulo lapanyumba. Inde, Yehova anam’dalitsa chifukwa cha khama lake.
Inunso mungapeze zoterezi ngati mupitiriza kufuna Yehova mwakhama. Ngati mulimbikira modzichepetsa ndi kuika mtima wanu wonse pa ntchito ya Mulungu iliyonse imene mukuchita, Yehova adzakugwiritsani ntchito mogwirizana ndi zolinga zake ndipo adzakudalitsani kwambiri.
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi n’chiyani chikanachitika mkazi ameneyu akadapanda kulimbikira?
[Chithunzi patsamba 27]
Kodi mumalimbikira popempha Yehova kuti akudalitseni?
[Zithunzi patsamba 28]
Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukufuna Yehova mwakhama?