N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka kwa Yehova?
“Usiku mngelo wa Mulungu wanga, amene ndikum’chitira utumiki wopatulika, anaima pafupi nane.”—MAC. 27:23.
1. Kodi anthu amene akukabatizidwa amakhala atachita kale chiyani, motero tingafunse mafunso ati?
“PAMAZIKO a nsembe ya Yesu Khristu, kodi mwalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?” Ili ndi limodzi mwa mafunso awiri omwe anthu amene akukabatizidwa amayankha pamapeto pa nkhani ya ubatizo. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kudzipereka kwa Yehova? Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatithandiza motani? N’chifukwa chiyani n’zosatheka kulambira Mulungu movomerezeka popanda kudzipereka kwa iye? Kuti timvetse mayankho a mafunso amenewa, choyamba tiyeni tione kaye tanthauzo la kudzipereka.
2. Kodi kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani?
2 Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione kaye zimene mtumwi Paulo ananena pofotokoza ubwenzi wake ndi Mulungu. Polankhula ndi gulu la anthu amene anali nawo limodzi m’sitima imene inakumana ndi mkuntho, iye anati, Yehova ndi “Mulungu wanga” [“Mulungu amene ndili wake,” Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu]. (Werengani Machitidwe 27:22-24.) Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu onse ndi anthu a Yehova. Koma dziko lonse “lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Akhristu amakhala a Yehova, pamene adzipereka moyenerera m’pemphero. Kudzipereka kumeneku, ndi lumbiro limene Mkhristu amalipanga yekha ndipo kenako amabatizidwa m’madzi.
3. Kodi ubatizo wa Yesu unaimira chiyani ndipo kodi otsatira ake amam’tsanzira bwanji?
3 Yesu anatipatsa chitsanzo posankha yekha kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anabadwa ali wodzipereka kale kwa Mulungu chifukwa anabadwira mumtundu wa Isiraeli womwe unali wodzipereka kwa Mulungu malinga ndi Chilamulo. Komabe mwa kubatizidwa, Yesu anafuna kuchitanso zinthu zina zowonjezera pamenepo. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti iye anati: “Taonani! Ndabwera . . . kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” (Aheb. 10:7; Luka 3:21) Motero, ubatizo wa Yesu unaimira kuti iye waonekera kwa Mulungu Atate wake kuti achite chifuniro Chake. Otsatira ake amam’tsanzira pochitanso chimodzimodzi. Komabe kwa iwo, ubatizo wa m’madzi umasonyeza kwa anthu kuti anadzipereka okha kwa Mulungu m’pemphero.
Mmene Kudzipereka Kumatithandizira
4. Kodi ubwenzi wa Davide ndi Jonatani umatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kufunika kwa pangano?
4 Kudzipereka kwa Mulungu si nkhani yamasewera ayi. Limeneli si lonjezo wamba. Koma kodi kudzipereka kumatithandiza motani? Tiyeni tiyerekezere zimenezi ndi zimene zimachititsa kuti anthu akhale ndi ubwenzi wolimba. Kuti munthu ukhale ndi mnzako wa ponda apa m’pondepo, pamafunika kuti nawenso uzichitapo kanthu. Paubwenzi wotero mumakhulupirirana kwambiri ndipo mumakhala okonzeka kuthandizana m’njira zosiyanasiyana. M’Baibulo muli zitsanzo za mabwenzi amene ankagwirizana kwambiri. Mwachitsanzo, Davide ndi Jonatani anafika pochita pangano la ubwenzi wawo. (Werengani 1 Samueli 17:57; 18:1, 3.) Ngakhale kuti zoterezi sizichitikachitika, munthu ukamadziwa kuti mnzakoyo angasunge malonjezo amene mungapangane, ubwenzi wanu umakhala wolimba.—Miy. 17:17; 18:24.
5. Kodi kapolo ankatani kuti azikhalabe ndi mbuye wake wabwino mpaka kalekale?
5 Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chinafotokozanso njira ina imene pangano linkathandizira anthu. Ngati kapolo amene mbuye wake anali wabwino akufuna kuti azikhalabe naye, ankatha kuchita pangano ndi mbuye wakeyo kuti adzam’gwirira ntchito mpaka kalekale. Chilamulochi chinati: “Mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am’boole khutu lake ndi lisungulu; ndipo iye azim’gwirira ntchito masiku onse.”—Eks. 21:5, 6.
6, 7.(a) Kodi mapangano amathandiza bwanji anthu? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani pa nkhani ya ubwenzi wathu ndi Yehova?
6 Okwatirana amafunika kuti azikhulupirika kwambiri ku malonjezo amene anapanga. Pangano la mu ukwati silili ngati pangano la bizinesi, chifukwa nkhani yaikulu imakhala pa munthuyo. Anthu awiri amene amakhala limodzi popanda pangano la ukwati, ubwenzi wawo sukhala wolimba ndipo ana awo sakhala otetezeka. Koma amene anakwatirana ndipo amakhulupirika m’banja, amakhala ndi zifukwa za m’Malemba zowachititsa kuti aziyesetsa kuthetsa mavuto awo mwachikondi.—Mat. 19:5, 6; 1 Akor. 13:7, 8; Aheb. 13:4.
7 M’nthawi za m’Baibulo anthu ankachita mapangano pankhani za malonda kapena polembana ntchito ndipo zimenezi zinali zothandiza. (Mat. 20:1, 2, 8) Kuchita zimenezi n’kothandizanso masiku ano. Mwachitsanzo, zimakhala bwino kulemberana pangano tisanayambe kupanga bizinesi ndi munthu wina kapena tisanayambe ntchito pakampani. Ndiyeno ngati pangano limathandiza pa ubwenzi, ukwati, ndiponso pa ntchito, kuli bwanji ndi ubwenzi wanu ndi Yehova? Tsopano tiyeni tione mmene anthu anapindulira chifukwa chodzipereka kwa Yehova Mulungu komanso mmene kudzipereka kumeneku kumasiyanirana kwambiri ndi malonjezo ena.
Aisiraeli Anapindula Chifukwa Chodzipereka kwa Mulungu
8. Kodi kudzipereka kwa Aisiraeli kunali ndi tanthauzo lotani?
8 Mtundu wa Isiraeli wonse unadzipereka kwa Yehova pamene unalumbira kwa iye. Yehova anasonkhanitsa mtunduwo pafupi ndi phiri la Sinai ndipo anati: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu.” Anthuwo anavomereza kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eks. 19:4-8) Kudzipereka kwa Aisiraeli kunali ndi tanthauzo lina lalikulu kuposa lonjezo loti adzakhala okhulupirika kwa iye. Kunatanthauza kuti iwo anali anthu a Yehova ndipo Yehovayo ankawaona kuti ndi ‘chuma chake chapadera.’
9. Kodi Aisiraeli anapindula motani chifukwa chodzipereka kwa Mulungu?
9 Aisiraeli anapindula chifukwa chokhala anthu a Yehova. Iye anali wokhulupirika kwa iwo ndipo ankawasamalira ngati mmene kholo limasamalira mwana wake. Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wom’bala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” (Yes. 49:15) Yehova ankawalangiza kudzera m’Chilamulo, kuwalimbikitsa pogwiritsa ntchito aneneri, ndi kuwateteza pogwiritsa ntchito angelo. Wamasalmo wina analemba kuti: “Aonetsa mawu ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israyeli. Sanatero nawo anthu a mtundu wina.” (Sal. 147:19, 20; Werengani Salmo 34:7, 19; 48:14.) Yehova amasamaliranso anthu amene amadzipereka kwa iye masiku ano ngati mmene ankachitira ndi mtundu wake kalelo.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudzipereka kwa Mulungu?
10, 11. Kodi anthufe timabadwira m’banja la Mulungu? Fotokozani.
10 Anthu ena akamaganizira za kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa amadzifunsa kuti, ‘Kodi sindingathe kumalambira Mulungu popanda kudzipereka kwa iye?’ Zimenezi n’zosatheka. Kuti timvetse chifukwa chake, tiyeni tiganizire mmene Mulungu amationera panopo. Tisaiwale kuti tchimo la Adamu linachititsa kuti tonse tibadwire kunja kwa banja la Mulungu. (Aroma 3:23; 5:12) Choncho, kudzipereka n’kofunika kwambiri kuti Mulungu atilandire m’banja lake la zolengedwa za kumwamba ndi dziko lapansi. Tiyeni tione chifukwa chake tikutero.
11 Palibe bambo aliyense amene angabereke mwana wangwiro monga mmene Mulungu anafunira pachiyambi. (1 Tim. 6:19) Sitibadwa tili ana a Mulungu chifukwa choti kuchimwa kwa anthu oyambirira kunachititsa kuti anthu onse asakhalenso ana a Mulungu, yemwe ndi Tate wachikondi ndiponso Mlengi. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 32:5.) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu onse akhala ali kunja kwa banja la Yehova la zolengedwa za kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo ndi otalikirana ndi Mulungu.
12. (a) Kodi anthu opanda ungwiro ayenera kutani kuti akhale m’banja la Mulungu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuchita tisanabatizidwe?
12 Komabe, tingathe kupempha Mulungu patokha kuti tikhale m’banja la atumiki ake.a Kodi zimenezi zingatheke bwanji popeza ndife anthu ochimwa? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Tikamabatizidwa, timapempha Mulungu kuti atipatse chikumbumtima chabwino kuti tikhale ovomerezeka kwa iye. (1 Pet. 3:21) Koma pali zinthu zina zimene tiyenera kuchita tisanabatizidwe. Tiyenera kudziwa Mulungu, kuyamba kum’khulupirira, kulapa machimo athu ndiponso kusintha njira zathu. (Yoh. 17:3; Mac. 3:19; Aheb. 11:6) Palinso chinthu china chimene tiyenera kuchita tisanalandiridwe m’banja la Mulungu. Kodi chinthu chake n’chiyani?
13. N’chifukwa chiyani m’pomveka kuti munthu amene akufuna kulandiridwa m’banja la atumiki a Mulungu ayenera kulonjeza kaye kuti akudzipereka kwa iye?
13 Kuti munthu ayandikire kwa Mulungu n’kulandiridwa m’banja la atumiki ake, ayenera kuchita pangano ndi Yehova. Kuti timvetse mfundoyi, tayerekezani kuti bambo wina wachifundo akufuna kutenga mwana wamasiye kuti azimulera m’banja lake. Bamboyo ndi waulemu wake ndipo amadziwika kuti ndi munthu wabwino. Komabe asanamutenge, bamboyo akufuna kuti mwanayo alonjeze chinthu chimodzi. Bamboyo akuti: “Ndisanakutenge ndikufuna ulonjeze kuti uzindikonda ndi kundimvera ngati bambo ako.” M’pomveka kuti bamboyo sangalole kutenga mwanayo ngati salonjeza zimenezi. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye amalola anthu kuti akhale m’banja lake ngati anthuwo akulonjeza ndi mtima wonse kuti akudzipereka kwa iye. Baibulo limati: “Perekani matupi anu kwa iye: nsembe ya moyo, odzipereka ndi oyenera kulandiridwa ndi iye.”—Aroma 12:1, The New English Bible.
Kudzipereka Kumasonyeza Chikondi Ndiponso Chikhulupiriro
14. N’chifukwa chiyani kudzipereka kwa Mulungu kumasonyeza chikondi?
14 Tikadzipereka kwa Mulungu, timasonyeza kuti timam’konda kwambiri. Lonjezo limeneli, limafananako ndi lonjezo la ukwati. Mwamuna wachikhristu amasonyeza kuti amakonda mkazi wake mwa kulonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa iye zivute zitani. N’zoona kuti munthu amene wadzipereka mwa njira imeneyi mtima wake umakhala pa mnzakeyo osati pa malonjezowo ayi. Komabe mwamuna wachikhristu amadziwa kuti n’zosatheka kukhala ndi mkazi wakeyo popanda malumbiro a ukwati. Nafenso sitingakhale m’banja la Yehova popanda kulonjeza kuti tikudzipereka kwa iye. Choncho timadzipereka kwa Mulungu chifukwa chakuti timafunitsitsa kukhala anthu ake ndipo tatsimikiza kukhala okhulupirika kwa iye zivute zitani. Timachita zimenezi ngakhale kuti ndife opanda ungwiro.—Mat. 22:37.
15. N’chifukwa chiyani tingati kudzipereka kwa Mulungu kumasonyeza chikhulupiriro?
15 Tikadzipereka kwa Mulungu timasonyeza kuti timamukhulupirira. N’chifukwa chiyani tikutero? Kukhulupirira Yehova kumatichititsa kukhulupirira kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kwa ife. (Sal. 73:28) Timadziwa kuti kuyenda ndi Mulungu pakati pa “m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota” si chinthu chapafupi. Koma timakhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti atithandiza tikamayesetsa kuchita zimenezi. (Afil. 2:15; 4:13) Timadziwa kuti ndife opanda ungwiro, koma timakhulupirira kuti ngati titalakwitsa chinachake, Yehova angatichitire chifundo. (Werengani Salmo 103:13, 14; Aroma 7:21-25.) Timakhulupirira kuti Yehova adzatidalitsa chifukwa chokhala ndi mtima wofunitsitsa kumutumikira zivute zitani.—Yobu 27:5.
Kudzipereka kwa Mulungu Kumabweretsa Chimwemwe
16, 17. N’chifukwa chiyani kudzipereka kwa Yehova kumabweretsa chimwemwe?
16 Yesu anafotokoza mfundo ya choonadi yakuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) N’chifukwa chake kudzipereka kwa Yehova kumabweretsa chimwemwe popeza kuti timapereka moyo wathu wonse kwa iye. Yesu anapeza chimwemwe chochuluka mu utumiki wake wapadziko lapansi chifukwa chakuti anali wopatsa. Nthawi zina ankalephera kupuma, kudya ndiponso kuchita zinthu zina momasuka, n’cholinga chakuti athandize ena kupeza njira yakumoyo. (Yoh. 4:34) Yesu ankasangalala kuchita zinthu zokondweretsa mtima wa Atate wake. Iye anati: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.”—Yoh. 8:29; Miy. 27:11.
17 Motero, mawu amene Yesu anauza ophunzira ake, ndi othandiza kuti anthu akhale ndi moyo wabwino. Iye anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Kuchita zimenezi kumatithandiza kukhala paubwenzi ndi Yehova. Kodi pali munthu winanso amene angatisamalire mwachikondi kuposa Yehova?
18. N’chifukwa chiyani kudzipereka kwa Yehova n’kumachita chifuniro chake kumatichititsa kukhala achimwemwe kwambiri kuposa kudzipereka ku chinachake kapena kwa munthu wina aliyense?
18 Kudzipereka kwa Yehova, n’kumachita chifuniro chake, kumabweretsa chimwemwe. Chimwemwe chimenechi chimaposa chimene timapeza tikadzipereka kuchita chinthu china chilichonse kapena tikadzipereka kwa munthu aliyense. Mwachitsanzo, anthu ambiri amadzipereka kwambiri kuti apeze chuma, komabe sakhala osangalala ndipo sakhutira ndi zimene akuchitazo. Koma anthu amene amadzipereka kwa Yehova, amapeza chimwemwe chosatha. (Mat. 6:24) Iwo amakhala osangalala chifukwa chodziwa kuti ndi mwayi kukhala “antchito anzake a Mulungu.” Koma iwo amadzipereka kwa Mulungu osati ku ntchitoyo. (1 Akor. 3:9) Ndipo palibe amene amayamikira kwambiri kudzipereka kwawo koposa Yehova. Ndipotu ngakhale iwo atakalamba,Yehova adzachititsa kuti akhalenso anyamata n’cholinga chakuti asangalale ndi chikondi chake kwamuyaya.—Yobu 33:25; werengani Aheberi 6:10.
19. Kodi anthu amene adzipereka kwa Yehova amakhala ndi mwayi wotani?
19 Mukapereka moyo wanu kwa Yehova, mumakhala naye paubwenzi wa ponda apa m’pondepo. Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8; Sal. 25:14) M’nkhani yotsatira, tiona chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti ndi chinthu chanzeru kusankha kukhala anthu a Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a “Nkhosa zina” za Yesu zidzakhala ana a Mulungu pamapeto pa zaka 1,000. Komabe, chifukwa choti iwowa anadzipereka kwa Mulungu, angathe kutchula Mulungu kuti “Atate” ndipo amaonedwa kuti ali m’banja la olambira Yehova.—Yoh. 10:16; Yes. 64:8; Mat. 6:9; Chiv. 20:5.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani?
• Kodi timapindula bwanji tikadzipereka kwa Mulungu?
• N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kudzipereka kwa Yehova?
[Chithunzi patsamba 6]
Kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwathu, kumabweretsa chimwemwe chosatha