-
Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
16. Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti imene imakhudza kuchotsa mimba? (Onaninso mawu a m’munsi.)
16 Ngakhalenso moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu. Kale ku Isiraeli, munthu akavulaza mayi woyembekezera ndipo ngati mayiyo kapena mwana wosabadwayo wamwalira, Mulungu ankaona kuti wolakwayo ndi wakupha munthu, ndipo ankafunika kuphedwa kuti ‘alipire moyo.’c (Werengani Ekisodo 21:22, 23.) Ndiye kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akamaona ana ambirimbiri osabadwa akuphedwa chaka chilichonse pochotsa mimba? Ndipotu ana ambiri amaphedwa mwanjira imeneyi chifukwa makolo awo ndi odzikonda ndipo amakonda chiwerewere.
-
-
Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
c Mabaibulo ena amamasulira lembali m’njira yosonyeza kuti munthu angalandire chilango ngati amene wafa ndi mayi yekha. Komabe, olemba mabuku otanthauzira mawu a m’Baibulo amanena kuti mmene mawuwa analembedwera m’Chiheberi, “zikusonyezeratu kuti sankanena za imfa ya mayi yokha.” Onaninso kuti Baibulo silinena kuti chilango cha Yehova chimenechi chinkaperekedwa potengera kukula kwa mwana wosabadwayo.
-