Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimawonera kugula katundu wakuba?
Akristu amapeŵa kukhala ndi mbali iriyonse m’kugula katundu kapena zinthu zakuba.
Kuba nkulakwa mosakaikira konse. Lamulo la Mulungu kwa Israyeli linanena motsimikiza kuti: “Usabe.” (Eksodo 20:15; Levitiko 19:11) Ngati mbala inagwidwa, inayenera kulipa chobedwacho kaŵiri, kanayi, kapena kasanu, kudalira pamikhalidweyo.
Chiyambire m’nthaŵi zakale, mbala zimagulitsa zinthu zobedwazo mmangumangu kuti zipeze phindu lamwamsanga ndi kuti zisapezedwe ndi umboni wa mlanduwo. Chifukwa chake, kaŵirikaŵiri zimagulitsa katundu wobedwayo pamtengo wotsika umene umakhala wovuta kwa ogula kukana. Kachitidwe koteroko kayenera kuti kanaphatikizidwa m’zolembedwa pa Eksodo 22:1 kuti: “Munthu akaba ng’ombe, kapena nkhosa, nakaipha, kapena kuigulitsa, adzilipa ng’ombe zisanu pa ngo’mbeyo, ndi nkhosa zisanu pa nkhosayo.”
Polingalira tanthauzo la malamulo ameneŵa, Rabi wotchedwa Abraham Chill analemba kuti: “Nkulakwa kugula kapena kulandira chinthu chakuba, ngakhale ngati chinthucho sichinadziŵike kukhala chakuba. Chotero, munthu sayenera kugula mbuzi kwa mbusa, chifukwa chakuti mwina mbusayo akuchita malondawo osadziŵa womlemba ntchito ndipo afuna kutenga ndalamayo.”—The Mitzvot—The Commandments and Their Rationale.
Kwenikweni lamulo la Mulungu silimaletsa ‘kugula mbuzi kwa mbusa,’ chabe chifukwa cholingalira kuti mwina angabere womlemba ntchito ndalamayo, kumene kulidi kugulitsa mbuzi yakuba. Koma kumbali ina, atumiki a Yehova sayenera kukhala ndi mbali m’malonda (a mbuzi kapena chinthu chirichonse) pamene kuli kodziŵikiratu kuti sichake wogulitsayo kapena kuti nchakuba. Lamulo la Mulungu limasonyeza kuti Iye amalemekeza katundu wa mwiniwake, koma mbala imalanda katundu wa mwiniwake. Munthu amene agula chinthu chodziŵika kukhala chakuba sangakhale mbala kwenikweni, koma kugula kwake chinthucho kumachepetsa mpata wakuti mwiniwake akachipezenso.—Miyambo 16:19; yerekezerani ndi 1 Atesalonika 4:6.
Tonsefe timadziŵa bwino lomwe kuti ogula amafuna kugula zinthu pamtengo wabwino kwambiri. Akazi kuzungulira padziko lapansi amafuna kugula zinthu pa selo, amayesa kusagula zinthu mwamsanga kufikira nyengo pamene mitengo itsika, kapena kugula ku maholoselo ndi masitolo amene mitengo imakhalako bwino. (Miyambo 31:14) Komabe, chifuno chotero chakugula zinthu pamtengo wotsika chiyenera kukhala ndi malire amakhalidwe abwino. Okhulupirika m’nthaŵi ya Nehemiya anakana kugula zinthu pa Sabata, ngakhale ngati akanagula zinthu zabwino pamtengo wotsika patsikulo. (Nehemiya 10:31; yerekezerani ndi Amosi 8:4-6.) Zirinso motero kwa Akristu. Kukana kwawo kuba kumawathandiza kulamulira chikhumbo chakugula katundu wotsika mtengo wodziŵikiratu kukhala wakuba.
Aliyense angakhale akudziŵa kuti a uje ndi a uje amagulitsa katundu wakuba. Kapena mtengo wa chinthu wotchulidwa mwamtseri ungakhale wotsika modabwitsa kwakuti munthu aliyense wolingalira bwino akhoza kudziŵa kuti katunduyo ayenera kukhala wakuba. Ngakhale lamulo la dziko lingasonyeze kufunika kwa kulingalira koteroko. Chigawo china cha bukhu linalake lamalamulo chimanena kuti:
“Sikofunikira kwenikweni kuti woimbidwa mlanduyo adziŵe tsatanetsatane wa mlanduwo, kudziŵa kuti chinthucho chinabedwa kwa yani kapena ndi yani, liti, kuti, kapena mikhalidwe pamene chinabedwa, koma chofunika ndikungodziŵa basi kuti katunduyo ngwakuba. . . . Makhoti ena amatenga lingaliro lakuti upanduwo umatsimikiziridwa ndi chenicheni chakuti woimbidwa mlanduyo anagula chinthucho pansi pa mikhalidwe yokhoza kukhutiritsa munthu aliyense wolingalira bwino kuti chinali chakuba.”
Izi zimaperekanso chifukwa chabwino kwa Mkristu chopeŵera kugula katundu wakuba. Kugula kwake katundu woteroyo kumampanga kukhala woswa lamulo. Kwenikweni, m’maiko ena munthu amene wagula zinthu zakuba pansi pamikhalidwe iriyonse amalingaliridwa kukhala waliwongo kapena wakuswa lamulo. Anthu ambiri samazengereza kuswa lamulo ngati awona kuti sadzadziŵidwa. Akristu, amene amafuna ‘kumvera maulamuliro aakulu’ samachita zimenezo. Kumvera kwawo malamulo kumawapangitsa kusagwidwa monga apandu, ndipo kumawathandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova.—Aroma 13:1, 4, 5.
Abrahamu bwenzi la Mulungu anapereka chitsanzo chabwino ponena za chikumbumtima. M’masiku ake olamulira a kum’maŵa anayi anagonjetsa mafumu a dziko lokhalamo Loti, nafunkha chuma chambiri. Abrahamu analondola, kugonjetsa adaniwo, nabweza katundu wobedwayo. Mfumu ya Sodomu inati kwa Abrahamu: “Utenge chuma iwe wekha” monga mphotho. Mmalomwake, Abrahamu anabweza katunduyo kwa mwiniwake, naati: “Sindidzatenga . . . ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu.”—Genesis 14:1-24.
Akristu samafuna phindu landalama lirilonse lopezedwa ndi katundu wakuba. Yeremiya analemba kuti: “Monga nkhwali iumatira pa mazira amene siinaikira, motero iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama.” (Yeremiya 17:11) Chotero, pambali pa kusonyeza nzeru yawo mwakusaswa malamulo a Kaisara pakatundu wakuba, Akristu amafuna kulemekeza chiŵeruzo chachilungamo cha Mulungu mwakupeŵa kuphatikizidwa mwanjira iriyonse m’chisalungamo cha kuba. Davide analemba mfundo yabwino kuti: “Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwawo kwa oipa ambiri.”—Salmo 37:16.