Yandikirani Mulungu
Atate wa Ana Amasiye
BAIBULO limati: “Mulungu mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye.” (Salmo 68:5) Mawu ouziridwa amenewa akutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza Yehova Mulungu, yakuti iye ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu osowa. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, chikusonyeza kuti iye amamvera chisoni ana amene makolo awo anamwalira. Tiyeni tione lemba loyamba m’Baibulo limene lili ndi mawu akuti “mwana wamasiye,” lomwe ndi Eksodo 22:22-24.
Mulungu anachenjeza Aisiraeli kuti: “Musazunza . . . mwana wamasiye aliyense.” (Vesi 22) Pamenepa, sikuti Mulungu ankangowadandaulira anthuwa kuti azithandiza ana amasiye, koma ankawapatsa lamulo. Mwana amene bambo ake anamwalira, ankasowa munthu womusamalira komanso womuteteza, choncho zinali zosavuta kuti anthu ena azimuzunza. Koma vesili likusonyeza kuti palibe amene ankaloledwa “kuzunza” mwana wamasiye mwa njira ina iliyonse. Mawu akuti “kuzunza” amatanthauzanso “kuvutitsa,” “kupondereza,” ndiponso “kuchitira ena nkhanza.” Mulungu ankaona kuti kuzunza mwana wa masiye linali tchimo lalikulu. N’chifukwa chiyani linali tchimo lalikulu?
Chilamulo chinanenanso kuti: “Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo.” (Vesi 23) Pa vesi 22 pali mawu akuti “musazunza,” ndipo zimenezi zikusonyeza kuti mtundu wonse wa Isiraeli unafunika kutsatira lamulo la Mulungu limeneli. Koma pa vesi 23 pali mawu akuti “ukawazunza,” ndipo zimenezi zikusonyeza kuti munthu aliyense payekha anafunika kutsatira lamulo limeneli. Yehova ankaona zonse ndiponso ankamvetsera kulira kwa ana amasiye ndipo iwo akam’pempha, iye anali wokonzeka kuwathandiza.—Salmo 10:14; Miyambo 23:10, 11.
Kodi n’chiyani chinkachitikira munthu amene wazunza mwana wamasiye, moti mwanayo n’kufika polirira Mulungu? Yehova anati, “mkwiyo wanga udzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga.” (Vesi 24) Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limanena kuti mawuwa “angalembedwenso kuti ‘mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno,’ zimene zikutanthauza kukwiya kwambiri.” Taonani kuti Yehova sanasiyire oweruza a ku Isiraeli nkhani zoterezi. Iye ankapereka yekha chilango kwa munthu aliyense wopondereza ana amasiye.—Deuteronomo 10:17, 18.
Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) Iye amamverabe chisoni ana amasiye. (Yakobe 1:27) Dziwani kuti Atate wa ana amasiye amakwiya kwambiri anthu ena akamazunza ana osalakwawa. Ndipo anthu omwe amapondereza ana amasiye sadzapulumuka “mkwiyo waukali wa Yehova.” (Zefaniya 2:2) Anthu oipa amenewa adzadziwa kuti “ndi chinthu choopsa kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo.”—Aheberi 10:31.