Yandikirani Mulungu
“Ndidziwa Zowawitsa Zawo”
“WOYERA, Woyera, Woyera, Yehova.” (Yesaya 6:3) Mawu ouziridwa amenewo akusonyeza kuti Yehova Mulungu ndi woyera ndi waukhondo kufika pamapeto penipeni. Koma mwina mungafunse kuti: ‘Kodi kuyera kumeneku kumam’pangitsa kuti asamafune kuchita zinthu ndi anthu?’ ‘Kodi Mulungu wotereyu angaganizire za munthu wochimwa ngati ine?’ Tiyeni tikambirane mawu olimbikitsa opezeka pa Eksodo 3:1-10, amene Mulungu anauza Mose.
Tsiku lina Mose akuweta nkhosa anaona zinthu zodabwitsa kwambiri. Anaona chitsamba chikuyaka moto koma ‘osanyeka.’ (Vesi 2) Podabwa ndi zimenezi anayandikira kuti aonetsetse. Ndiyeno pogwiritsa ntchito mngelo, Yehova analankhula ndi Mose kuchokera m’chitsamba choyaka motocho. Iye anati: “Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, m’popatulika.” (Vesi 5) Tangoganizirani mfundo imeneyi. Malo onsewo anakhala oyera chifukwa choti panafika nthumwi ya Mulungu.
Panali chifukwa chimene chinapangitsa Mulungu kufuna kulankhulana ndi Mose. Iye anati: “Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m’Aigupto, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zawo.” (Vesi 7) Mulungu ankadziwa mavuto onse amene anthu ake ankakumana nawo komanso ankamva kulira kwawo. Moti nayenso zinkamupweteka. Taonani kuti Mulungu anati: “Ndidziwa zowawitsa zawo.” Ponena za mawu akuti “ndidziwa,” buku lina linati: “Mawuwa akusonyeza kukhudzidwa mtima, kukoma mtima ndi chifundo.” Mawu amene Yehova anauza Mose anasonyeza kuti iye ndi Mulungu wachifundo komanso woganizira anthu kwambiri.
Nanga kodi Mulunguyo anachita chiyani? Sikuti anangoyang’ana n’kumva chisoni kapena kungomvetsera chabe ayi. Chisoni komanso chifundo zinamulimbikitsa kuchitapo kanthu. Iye anakonza zoti apulumutse anthu ake ku Iguputo n’kuwalowetsa “m’dziko moyenda mkaka ndi uchi.” (Vesi 8) Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Utulutse anthu anga . . . m’Aigupto.” (Vesi 10) Mwamphamvu ya Mulungu, zimenezi zinachitikadi ndipo mu 1513 B.C.E., Mose anatsogolera Aisiraeli potuluka mu Iguputo.
Mpaka pano, Yehova sanasinthe. Anthu amene amamulambira ayenera kudziwa kuti iye amaona mavuto awo ndipo amamva kulira kwawo. Iye amadziwa bwino zowawitsa zawo. Komatu sikuti Yehova amangomva chisoni akaona atumiki ake okhulupirika. Mulungu wachifundo amachitapo kanthu kuti awathandize “pakuti amasamala” za iwo.—1 Petulo 5:7.
Chifundo cha Mulungu chimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo. Iye amathandiza anthu opanda ungwirofe kuti tikhale oyera komanso ovomerezeka kwa iye. (1 Petulo 1:15, 16) Mayi wina wachikhristu yemwe anavutika maganizo komanso kukhumudwa analimbikitsidwa ndi nkhani ya Mose pachitsamba paja. Iye anati: “Ngati Yehova anachititsa kuti nthaka ikhale yoyera kuli bwanji ineyo. Mfundo imeneyi yandithandiza kwambiri.”
Kodi mukufuna kudziwa zambiri za Mulungu woyera, Yehova? N’zotheka kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa iye ‘amadziwa mapangidwe athu; amakumbukira kuti ife ndife fumbi.’—Salmo 103:14.