Dziŵani Mlengi Wanu
“Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako.”—EKSODO 33:19.
1. N’chifukwa chiyani Mlengi ayenera kulandira ulemu?
MTUMWI Yohane, yemwe analemba buku lomaliza la m’Baibulo, analemba mawu ofunika kwambiri onena za Mlengi aŵa: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Monga momwe nkhani yoyambayo inafotokozera, zambiri zimene sayansi yamakono yapeza zimawonjezera zifukwa zokhulupirira mwa Mlengi wa zinthu zonse.
2, 3. (a) Kodi anthu ayenera kuphunziranji ponena za Mlengi? (b) N’chifukwa chiyani kuonana ndi Mlengi mwachindunji sikofunikira?
2 Monga momwe kulili kofunika kuvomereza kuti Mlengi aliko, n’kofunikanso kum’dziŵa kuti ndi wotani—kuti ali ndi umunthu wake weniweni, ndi njira zimene anthu amakopeka nazo. Kaya mwaphunzira zochuluka motani, kodi sikungakhale kopindulitsa kum’dziŵabe bwino? Zimenezo si zochita kufuna kuonana naye mwachindunji, monga momwe timaonanirana ndi anthu anzathu.
3 Yehova ndiye Gwero ngakhale la nyenyezi, ndipotu dzuŵali ndi nyenyezi yocheperapo poiyerekeza ndi nyenyezi zina. Kodi mungaganize zofuna kufika kufupi ndi dzuŵa lenilenilo? Kutalitali! Anthu ambiri safuna n’kuliyang’ana kapena kukhala padzuŵa lamphamvulo alibe zovala kwa nthaŵi yaitali. Pakati pake, kutentha kwake kumafika 15,000,000 degrees Celsius (27,000,000°F.). Sekondi iliyonse, ng’anjo yotentha koopsa imeneyi imaotcha matani ake mamiliyoni anayi kukhala mphamvu. Kachigawo kakang’ono chabe ka kutentha ndi kuunika kwake n’kamene kamafika padziko lapansi, koma kachigawoko kamatha kuchirikiza moyo wa zamoyo zonse pansi pano. Mfundo zazikulu zimenezo ziyenera kutisonyeza bwino kwambiri mphamvu zoopsa za Mlengi. Ndiye chifukwa chake Yesaya analemba za “mphamvu . . . [za Mlengi] zazikulu, . . . popeza ali wolimba mphamvu.”—Yesaya 40:26.
4. Kodi Mose anapempha chiyani, ndipo Yehova anayankha motani?
4 Komano kodi mukudziŵa kuti miyezi ingapo Aisrayeli atatuluka mu Igupto mu 1513 B.C.E., Mose anapempha Mlengi kuti: “Ndionetsenitu ulemerero wanu.” (Eksodo 33:18) Pokumbukira kuti Mulungu ndiyenso Gwero la dzuŵa, mutha kumvetsa chifukwa chimene anauzira Mose kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.” Mlengi analola Mose kubisala penapake m’Phiri la Sinai pamene Iye ‘anapitirira.’ Ndiyeno Mose anaona “m’mbuyo” mwa Mulungu, titero kunena kwake, kuwala kotsatira ulemerero wa Mlengi, kapena kukhalapo kwake.—Eksodo 33:20-23; Yohane 1:18.
5. Kodi Mlengi analiyankha motani pempho la Mose, kupereka umboni woti chiyani?
5 Chikhumbo cha Mose chofuna kum’dziŵa bwino Mlengi chinakhutiritsidwa. Polankhulira mwa mngelo, Mulungu anadutsa pafupi ndi Mose ndi kulengeza kuti: “Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34:6, 7) Zimenezi zikusonyeza kuti kum’dziŵa bwino Mlengi sikumaphatikizapo kuona thupi lake lenilenilo, koma kudziŵa bwino mmene alili, umunthu wake ndi mikhalidwe yake.
6. Kodi chitetezo cha thupi n’chodabwitsa motani?
6 Njira imodzi imene tingachitire zimenezo ndiyo mwa kuzindikira mikhalidwe ya Mulungu m’zinthu zimene analenga. Talingalirani za mphamvu yoteteza thupi lanu ku matenda. M’kope lofotokoza za chitetezo cha thupi, magazini ya Scientific American inati: “Kuyambira pamene munthu asanabadwe mpaka imfa yake, chitetezo cha thupi chimenechi chimakhalabe chili chire. Mamolekyu ndi maselo ambiri osiyanasiyana . . . amatiteteza ku tizilombo tomwe timaloŵa m’thupi ndi kuyambitsa matenda. Popanda chitetezo chimenechi, anthu sangakhale ndi moyo.” Kodi chitetezo chimenecho chimachokera kuti? Nkhani ina m’magazini imeneyo inati: “Mitundumitundu yochuluka zedi imeneyo ya maselo othandizana m’njira yozizwitsa komanso yaluso amene amateteza thupi ku tizilombo toyambitsa matenda imachokera ku maselo angapo oyambirira amene amapangika mwa mluza patapita milungu isanu ndi inayi kuchokera pamene mimba inakhala.” Mayi woyembekezera amapatsira chitetezo cha thupi kwa mwana wake wosabadwayo. Pambuyo pake, mwa kumuyamwitsa, amapatsiranso maselo oteteza thupi ku matenda ndi zinthu zina zofunika kwa khanda lake.
7. Kodi tinganenenji za chitetezo chamatupi athu, zimene zikutifikitsa pa mfundo yoti chiyani?
7 Muli ndi zifukwa zomveka zonenera kuti chitetezo cha thupi lanu chimaposa mankhwala ena alionse amakono. Chotero, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zikusonyezanji ponena za Wokonza ndi Wopereka chitetezocho?’ Chitetezo chimenechi chimene ‘chimayamba mwa mluza patapita milungu isanu ndi inayi kuchokera pamene mimba inakhala’ chimenenso chimakhala chokonzeka kuteteza khanda longobadwa kumene, chimasonyezadi nzeru ndi kukonzekera. Komano kodi palinso zina zimene tingaone m’chitetezo chimenechi ponena za Mlengi? Kodi ambiri a ife timati chiyani ponena za Albert Schweitzer ndi ena amene anapereka moyo wawo wonse pa ntchito yopereka chithandizo chamankhwala kwa anthu osauka? Nthaŵi zambiri timawathokoza anthu achifundo ngati ameneŵa. Choteronso, kodi tinganenenji za Mlengi wathu, amene amapereka chitetezo cha thupi kwa olemera ndi osauka omwe? Ndithudi, iye ndi wachikondi, wosakondera, wachifundo, ndi wolungama. Kodi zimenezi sizikugwirizana ndi zimene Mose anamva ponena za Mlengi?
Amavumbula Mmene Alili
8. Kodi Yehova amadzivumbula kwa ife m’njira yapadera iti?
8 Komano palinso njira ina yom’dziŵira bwino Mlengi wathu—Baibulo. Zimenezi n’zofunika kwambiri chifukwa chakuti pali zinthu zina ponena za iye zimene sayansi ndi chilengedwe chonse sizingasonyeze m’pang’ono pomwe ndi zinthu zina zimene zimafotokozedwa bwino lomwe m’Baibulo. Chitsanzo cha zinthu zofotokozedwa bwino lomwe m’Baibulo ndicho dzina laumwini la Mlengi. Ndi Baibulo lokha limene limavumbula dzina la Mlengi ndi tanthauzo lake. Mu mipukutu yachihebri ya Baibulo, dzina lakeli lilimo nthawi ngati 7,000 lolembedwa m’makonsonanti anayi amene angatembenuzidwe kukhala YHWH kapena JHVH, amene nthaŵi zambiri m’Chichewa amaŵerengedwa kuti Yehova.—Eksodo 3:15; 6:3.
9. Kodi dzina laumwini la Mlengi limatanthauza chiyani, ndipo tinganenepo kuti bwanji?
9 Kuti tim’dziŵe bwino Mlengi, tiyenera kuzindikira kuti sali chabe mphamvu ina yake imene inalenga zonse kapena wotchedwa kuti “Ine Ndine,” wosadziŵika bwino. Dzina lake limasonyeza kuti sali chabe zimenezo. Dzinalo ndi mtundu wina wa mneni wachihebri wotanthauza “kukhala.”a (Yerekezani ndi Genesis 27:29; Mlaliki 11:3.) Dzina la Mulungu limasonyeza kuti “Amachititsa Kukhalako” ndipo limagogomezera mfundo yakuti amakhala ndi zolinga ndiponso amazichita. Mwa kudziŵa dzina lakelo ndi kuligwiritsa ntchito, tingakhale otsimikiza kwambiri kuti amakwaniritsa malonjezo ake ndi kuchititsa chifuno chake.
10. Kodi tingapezemo nzeru zofunika zotani mu mbiri ya Genesis?
10 M’Baibulo ndimo mmene zolinga za Mulungu ndi umunthu wake zafotokozedwa. Mbiri ya Genesis imasonyeza kuti panthaŵi inayake anthu anali pamtendere ndi Mulungu, ndipo ankayembekeza kukhala ndi moyo wautali komanso watanthauzo. (Genesis 1:28; 2:7-9) Mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, tingakhale otsimikizira kuti Yehova adzathetsa mavuto ndi zokhumudwitsa zimene zasautsa anthu kwa nthaŵi yaitali. Timaŵerenga za kukwaniritsidwa kwa chifuno chake kuti: “Dzikoli linagwiritsidwa mwala, osati mwa kufuna kwake, koma mwa kufuna kwa Mlengi, amene mwakutero, analipatsa chiyembekezo chakuti tsiku lina . . . lidzakhale ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:20, 21, The New Testament Letters, yotembenuzidwa ndi J. W. C. Wand.
11. N’chifukwa chiyani tingaphunzire nkhani zosimbidwa m’Baibulo, ndipo kodi nkhani ina yotero ndi yotani?
11 Baibulo lingatithandizenso kum’dziŵa bwino Mlengi wathu chifukwa limasimba zochita zake ndi Israyeli wakale. Talingalirani chitsanzo chokhudza Elisa ndi Namani, kazembe wankhondo wa Aaramu okonda nkhondowo. Pamene muŵerenga nkhani imeneyi pa 2 Mafumu chaputala 5, mudzaona kuti mtsikana wachiisrayeli yemwe anali mu ukapolo anayankhula molimbika kuti Namani atha kuchiritsidwa khate lake mothandizidwa ndi Elisa ku Israyeli. Namani anapitako akuyembekeza kuti Elisa adzachita mwambo wochiritsa. M’malo mwake, Elisa anauza Mwaramuyo kuti akasambe mu Mtsinje wa Yordano. Ngakhale kuti anyamata a Namani ndiwo anam’limbikitsa kuti achite zimene wauzidwa, atakasamba, anachira. Namani anapereka mphatso zamtengo wapatali, zimene Elisa anakana. Kenako wogwira naye ntchito anazemba kupita kwa Namani, kuyankhula bodza, ndi kulandira mphatso zina zamtengozo. Kusaona mtima kwakeko kunapangitsa kuti akanthidwe ndi khate. Imeneyi ndi nkhani yochititsa chidwi, yosonyeza zofooka za munthu—nkhani imene tingatengepo phunziro.
12. Kodi tikupezapo maganizo otani ponena za Mlengi pankhani ya Elisa ndi Namani?
12 M’njira yosangalatsa kwambiri nkhaniyo ikusonyeza kuti Mlengi Wamkulu wa chilengedwe chonse atha kusonyeza chiyanjo kwa mtsikana wamng’ono ngakhale kuti Iye ndi wokwezeka kwambiri, mosiyana kwambiri ndi malingaliro a anthu ambiri lerolino. Zimasonyezanso kuti Mlengi samangoyanja fuko kapena mtundu umodzi wokha. (Machitidwe 10:34, 35) Chosangalatsa n’chakuti m’malo moyembekezera anthu kugwiritsa ntchito njira zachinyengo—zofala kwa “asing’anga” ena akale ndi amakono—Mlengi anasonyeza nzeru zodabwitsa. Anadziŵa kuchiritsa khate. Anasonyezanso nzeru ndi chilungamo posalola zakatangalezo kuchitika. Kodi zimenezinso sizogwirizana ndi zimene Mose anamva ponena za umunthu wa Yehova? Ngakhale kuti nkhani ya m’Baibulo imeneyo ndi yaifupi, tikuphunzirapo zinthu zambiri bwanji ponena za mmene Mlengi alili!—Salmo 33:5; 37:28.
13. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene tingatengerepo maphunziro ofunika pa nkhani za m’Baibulo.
13 Nkhani zina zonena za kusayamikira kwa Aisrayeli ndi zimene Mulungu anachita zimapereka umboni wakuti Yehova amasamaladi. Baibulo limanena kuti kaŵirikaŵiri Aisrayeli anapikisana naye, kum’pweteketsa mtima. (Salmo 78:40, 41) Chotero, Mlengi amakhudzidwa mtima, ndipo amasamala zimene anthu amachita. Palinso zambiri zimene tingaphunzire pa nkhani za anthu odziŵika kwambiri. Davide atasankhidwa kukhala mfumu ya Israyeli, Mulungu anauza Samueli kuti: “Munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Inde, Mlengi amayang’ana zimene tili mkati mwathu, osati maonekedwe wamba akunja. N’zosangalatsa bwanji!
14. Pamene tiŵerenga Malemba Achihebri, kodi tingachitenji kuti tipindule?
14 Mabuku 39 a m’Baibulo analembedwa nthaŵi ya Yesu isanafike, ndipo tifunikira kuwaŵerenga. Tiyenera kutero osati chabe kuti tiphunzire nkhani za m’Baibulo kapena mbiri yakale ayi. Ngati tikufunadi kuphunzira mmene Mlengi alili, tiyenera kusinkhasinkha pa nkhani zimenezo, mwinanso tikuganiza kuti, ‘Kodi chochitika chimenechi chikutisonyezanji ponena za umunthu wake? Ndi mikhalidwe yake iti imene ikuonekera panopo?’b Kuchita zimenezo kungapangitsenso ngakhale okayikira kuti aone kuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndipo chimenecho chidzakhala chiyambi chawo cha kudziŵa bwino lomwe Wolilemba wake.
Mphunzitsi Wamkulu Atithandiza Kudziŵa Mlengi
15. Chifukwa chiyani zochita ndi ziphunzitso za Yesu ziyenera kukhala zolangiza?
15 Inde, anthu amene amakayikira zonena kuti kuli Mlengi kapena amene sam’dziŵa bwino Mulungu sadziŵa zambiri ponena za Baibulo. Mwinanso munakumanapo ndi anthu amene sadziŵa kuti anayamba kukhalapo ndani, Mose kapena Mateyu ndiponso amene sadziŵa kalikonse ponena za zochita kapena ziphunzitso za Yesu. Zimenezo n’zomvetsa chisoni kwambiri chifukwa munthu angaphunzire zambiri ponena za Mlengi kwa Mphunzitsi Wamkulu, Yesu. Pokhala anali woyandikana kwambiri ndi Mulungu, anali wokhoza kusonyeza mmene Mlengi alili. (Yohane 1:18; 2 Akorinto 4:6; Ahebri 1:3) Ndipo anaterodi. Kwenikweni, panthaŵi ina yake anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.”—Yohane 14:9.
16. Kodi kuyankhulana kwa Yesu ndi mkazi wachisamariya kumasonyeza chiyani?
16 Tiyeni titenge chitsanzo ichi. Nthaŵi ina yake Yesu atatopa ndi ulendo wake, anayankhula ndi mkazi wina Msamariya pafupi ndi mzinda wa Sukari. Anam’fotokozera mfundo zofunika kwambiri za choonadi, makamaka zokhudza kufunika kwa ‘kulambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.’ Ayuda a m’nthaŵi zimenezo sanali kufuna kuyandikana ndi Asamariya. Koma Yesu anasonyeza kuti Yehova amafuna kulandira amuna ndi akazi oona mtima a m’mitundu yonse, monganso taonera m’nkhani yokhudza Elisa ndi Namani. Ziyenera kutitsimikizira kuti Yehova sali ngati anthu achipembedzo achidani ndiponso osalolera amene adzaza dziko lerolino. Tingalingalirenso mfundo yakuti Yesu analolera kuphunzitsa mkazi, ndipotu mkazi wokhala ndi mwamuna yemwe sanali wake mwalamulo. M’malo mom’dzudzula, Yesu anayankhula naye mwaulemu, m’njira yom’thandiza kwambiri. Kenako, Asamariya enanso anamvetsera Yesu nanena: “Tidziŵa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.”—Yohane 4:2-30, 39-42; 1 Mafumu 8:41-43; Mateyu 9:10-13.
17. Kodi nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro imapereka lingaliro lotani?
17 Tiyeni tione chitsanzo china chosonyeza mmene tingaphunzirire za Mlengi mwa kudziŵa bwino zochita ndi ziphunzitso za Yesu. Kumbukirani zimene zinachitika pamene Lazaro bwenzi la Yesu anamwalira. Nthaŵi ina Yesu anali atasonyeza kuti ali ndi mphamvu youkitsa akufa. (Luka 7:11-17; 8:40-56) Koma kodi anamva bwanji ataona Mariya mlongo wa Lazaro akulira? Yesu “anadzuma mumzimu, navutika mwini.” Sanali wosamva chisoni kapena wosatha kukhudzika mtima; iye “analira.” (Yohane 11:33-35) Ndipo kumeneku sikunali kungofuna kusonyeza chisoni. Yesu anasonkhezereka kuthandiza—anaukitsa Lazaro. Mutha kuona mmene zimenezi zinathandizira atumwi kuzindikira mmene Mlengi amamvera ndi zimene amachita. Ziyeneranso kutithandiza ifeyo ndi ena kumvetsa umunthu ndi njira za Mlengi.
18. Kodi ndi motani mmene anthu ayenera kuonera kuphunzira Baibulo?
18 Palibe chifukwa chochitira manyazi ndi kuphunzira Baibulo ndi zinthu zowonjezera ponena za Mlengi wathu. Baibulo si buku loti linatha ntchito. Winawake amene analiphunzira ndi kukhala wantchito mnzake wa Yesu anali Yohane. Pambuyo pake anadzalemba kuti: “Tidziŵa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziŵitso [“nzeru,” NW], kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.” (1 Yohane 5:20) Onanitu kuti kugwiritsa ntchito “nzeru” kuti tidziŵe “Woonayo,” Mlengi, kungatitsogolere ku “moyo wosatha.”
Kodi Ena Mungawathandize Motani Kuphunzira za Iye?
19. Kodi n’chiyani chachitidwa kuti tithandize anthu okayikira?
19 Anthu ena amafuna zambiri kuti akhulupirire kuti kuli Mlengi wachifundo amene amasamala za ife ndi kuti azindikire kuti ndi wotani. Padakali anthu mamiliyoni ambiri amene akukayikabe za Mlengi kapena amene sam’ganizira monga momwe Baibulo limanenera. Kodi mungawathandize motani? Pamisonkhano yachigawo ndi yamitundu yonse ya Mboni za Yehova ya mu 1998/99, chida chothandiza kwambiri chinatulutsidwa m’zinenero zambiri—buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? (Kodi Kuli Mlengi Amene Amasamala za Inu?)
20, 21. (a) Kodi buku la Creator tingaligwiritse ntchito bwino motani? (b) Simbani mmene buku la Creator lathandizira kale anthu.
20 Ndi buku limene lidzawonjezera chikhulupiriro chanu mwa Mlengi wathu ndi kumvetsa kwanu umunthu wake ndi njira zake. N’chifukwa chiyani sitingakayikire zimenezi? Chifukwa buku la Is There a Creator Who Cares About You? lakonzedwera zolinga zimenezo. Nkhani yaikulu m’mitu yonse m’bukulo ndi yakuti “Kodi n’chiyani chingawonjezere tanthauzo la moyo wanu?” Nkhani zake zakonzedwa m’njira yoti ngakhale anthu amaphunziro apamwamba adzachita nazo chidwi. Komanso limalongosola zosoŵa zathu tonsefe. Muli mfundo zosangalatsa komanso zokopa maganizo kwa anthu amene amakayikira kuti kuli Mlengi. Bukuli silifotokoza nkhani ngati kuti woŵerenga amakhulupirira mwa Mlengi. Okayikira adzakopedwa ndi mmene likufotokozera zinthu zimene sayansi yatulukira posachedwa ndi malingaliro amene akhalapo. Mfundo ngati zimenezo zidzalimbitsanso chikhulupiriro cha anthu amene amakhulupirira mwa Mulungu.
21 Pophunzira buku latsopanoli, mudzaona kuti zigawo zina zimalongosola mbiri ya Baibulo mwachidule m’njira yosonyezanso mbali zina za umunthu wa Mulungu, kuthandiza oŵerenga kum’dziŵa bwino Mulungu. Ambiri amene aliŵerenga kale asimba mmene zimenezo zachitikiradi kwa iwo. (Onani nkhani yotsatira, masamba 25-6.) Zikhalenso momwemo ndi inu pamene mulizoloŵera bukulo ndi kuligwiritsa ntchito pothandiza ena kufika pom’dziŵa bwino Mlengi wawo.
[Mawu a M’munsi]
a M. J. Gruenthaner, Mjezwiti yemwe ndi katswiri wamaphunziro, pamene anali mkonzi wamkulu wa magazini yotchedwa The Catholic Biblical Quarterly, anafotokoza mneni ameneyu malinga ndi mmene anafotokozera mneni wina wofanana naye, kuti “sanena za chinthu chosadziŵika bwino chimene munthu amangoyerekeza kuti chilipo koma nthaŵi zonse amanena za chinthu chenicheni chokhalako, kutanthauza kuti choonekera m’njira yozindikirika bwino kuti chilipodi.”
b Pamene makolo asimbira ana awo nkhani za m’Baibulo, angathandize ana awo mwa kufunsa mafunso ngati ameneŵa. Chotero achinyamatawo angam’dziŵe Mulungu, ndiponso angaphunzire kusinkhasinkha pa Mawu ake.
Kodi Munazindikira?
◻ Ndi motani mmene Mose anam’dziŵira bwino Yehova pa Phiri la Sinai?
◻ N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo kuli kothandiza pofuna kudziŵa mmene Mulungu alili?
◻ Pamene tikuŵerenga Baibulo, kodi tingachitenji kuti tiyandikire kwambiri kwa Mlengi wathu?
◻ Kodi mwakonzeka kuligwiritsa ntchito motani buku la Creator?
[Chithunzi patsamba 20]
Kodi mphamvu yathu yodziteteza ku matenda imasonyezanji ponena za Mlengi wathu?
[Chithunzi patsamba 21]
Chigawo cha mipukutu yotchedwa “Dead Sea Scrolls,” ndi Tetiragalamatoni (dzina la Mulungu m’Chihebri) yomwe yasonyezedwayo
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Shrine of the Book, Israel Museum, Jerusalem
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi tingaphunzirenji pa zimene Yesu anachita ataona chisoni cha Mariya?