Yehova Ali Wololera!
“Nzeru yochokera kumwamba ili . . . yololera.”—YAKOBO 3:17, NW.
1. Kodi ndimotani mmene ena asonyezera Mulungu kukhala wosalolera, ndipo mumaliona motani lingaliro loterolo ponena za Mulungu?
KODI mumalambira Mulungu wa mtundu wotani? Kodi mumamkhulupirira kukhala Mulungu woumirira, wa chilungamo chokhwimitsa, wouma mtima ndi wosasunthika palingaliro lake? Kwa mtsogoleri Wachiprotestanti John Calvin, Mulungu ayenera kukhala ataonekera mwa njira imeneyo. Calvin ananena kuti Mulungu ali ndi “makonzedwe amuyaya ndi osasinthika” ponena za munthu aliyense payekha, akumaikiratu kwa munthu aliyense kuti adzakhala kosatha mwachimwemwe kapena kuzunzidwa kosatha m’moto wa helo. Tangolingalirani: Ngati zimenezi zikanakhala zoona, palibe chimene mukanachita, mosasamala kanthu ndi mmene mukanayesayesera, kuti musinthe makonzedwe a Mulungu osasinthika okhalapo kwa nthaŵi yaitali, ponena za mtsogolo mwanu. Kodi mungakopeke ndi Mulungu wosalolera woteroyo?—Yerekezerani ndi Yakobo 4:8.
2, 3. (a) Kodi tingachitire fanizo ndi chiyani kusalolera kwa mabungwe ndi magulu aumunthu? (b) Kodi ndimotani mmene masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba la Yehova amasonyezera kukhoza Kwake kusintha?
2 Tili otonthonzedwa chotani nanga podziŵa kuti Mulungu wa Baibulo ali wololera kwambiri! Ali anthu osati Mulungu amene amayedzamira pa kukhala oumirira ndi osasinthika, chifukwa cha kupanda ungwiro kwawo. Mabungwe a anthu akhoza kukhala osasinthika mofanana ndi sitima ya katundu. Pamene sitima yaitali ya katundu ikuthamanga ndipo yapeza chinthu panjanji, kutembenuka kumakhala kosalingalirika nkomwe, ndipo kuima kumakhala kovuta kwambiri. Sitima zina zili ndi mphamvu yokankhira kutsogolo yaikulu kwambiri kwakuti zimapitirira mtunda woposa kilomita imodzi zitagwira mabuleki! Mofananamo, chombo cha mafuta chachikulu kwambiri chingapitirire mtunda wa makilomita asanu ndi atatu mainjini ake atazimitsidwa. Ngakhale atasinthidwa kubwerera kumbuyo, chingapitirirebe kutsogolo kwa makilomita atatu! Koma tsopano talingalira za galimoto lochititsa mantha kwambiri koposa ziŵiri zimenezi, limene limaimira gulu la Yehova.
3 Zaka zoposa 2,600 zapitazo, Yehova anapatsa mneneri wake Ezekieli masomphenya omwe anachitira chithunzi gulu Lake lakumwamba la zolengedwa zauzimu. Linali galeta la ukulu wochititsa mantha, “galimoto” lake la Yehova lolamuliridwa ndi iye nthaŵi zonse. Chochititsa chidwi koposa ndicho mmene linayendera. Njinga zake zazikuluzo zinali ndi mbali zinayi zonse zodzaza ndi maso, motero zinali zokhoza kuona kulikonse ndi zokhoza kukhweta panthaŵi yomweyo, popanda kuima kapena kutembenuka. Ndipo galimoto lalikulukulu limeneli silinali kuyamba lapitirira mofanana ndi chombo cha mafuta chapamadzi chachikulu kwambiri kapena sitima ya katundu. Linali kuyenda pa liŵiro la mphezi, ndi kukhoza kukhotera uku ndi uku! (Ezekieli 1:1, 14-28) Yehova ali wosiyana kwambiri ndi Mulungu amene Calvin anamlalikira monga momwe galeta Lake liliri losiyana kwambiri ndi makina wambawo opangidwa ndi munthu. Iye ali wokhoza kusintha moyenerera. Kuzindikira mkhalidwe umenewu wa umunthu wa Yehova kuyenera kutithandiza kukhala okhoza kusintha ndi kupeŵa msampha wa kukhala osalolera.
Yehova—Munthu Wokhoza Kusintha Koposa Onse m’Chilengedwe Chonse
4. (a) Kodi ndimotani mmene dzina la Yehova lenilenilo limamsonyezera kukhala Mulungu wokhoza kusintha? (b) Kodi ndi maina aulemu ena ati amene amagwira ntchito kwa Yehova Mulungu, ndipo kodi nchifukwa ninji ali oyenerera?
4 Dzina la Yehova lenilenilo limasonyeza kukhoza kwake kusintha. “Yehova,” m’lingaliro lenileni limatanthauza kuti “Wochititsa Kukhalako.” Zimenezi mwachionekere zimatanthauza kuti Yehova amadzichititsa kukhala Wokwaniritsa wa malonjezo ake onse. Pamene Mose anafunsa Mulungu ponena za dzina lake, Yehova analongosola za tanthauzo lake mwa njirayi: “Ndidzatsimikizira kukhala amene ndidzatsimikizira kukhala.” (Eksodo 3:14, NW) Matembenuzidwe a Rotherham amanena mwachindunji kuti: “Ndidzakhala aliyense amene ndifuna.” Yehova amatsimikizira kukhala, kapena amasankha kukhala, aliyense amene ali wofunikira kotero kuti akwaniritse zifuno zake zolungama ndi malonjezo ake. Chotero, iye ali ndi mndandanda wokhumbirika wa maina aulemu, onga Mlengi, Atate, Ambuye Mfumu, Mbusa, Yehova wa makamu, Wakumva pemphero, Woweruza, Mlangizi Wamkulu, Mombolo. Iye wadzichititsa kukhala onsewa ndi enanso kotero kuti achite zifuno zake zachikondi.—Yesaya 8:13; 30:20; 40:28; 41:14; Salmo 23:1; 65:2; 73:28; 89:26; Oweruza 11:27; onaninso New World Translation, Appendix 1J.
5. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti kukhoza kusintha kwa Yehova kumatanthauza kuti mkhalidwe wake kapena miyezo imasintha?
5 Pamenepa, kodi zimenezi zimatanthauza kuti mkhalidwe wa Mulungu kapena miyezo yake imasintha? Iyayi; monga momwe Yakobo 1:17 amanenera kuti, “amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” Kodi pali kuwombana kulikonse pamenepa? Kutalitali. Mwachitsanzo, kodi ndi kholo lachikodi lotani limene silimasinthasintha mbali zake kaamba ka phindu la ana ake? Mkati mwa tsiku limodzi chabe, kholo lingakhale phungu, wophika, woyeretsa m’nyumba, mphunzitsi, wopereka chilango, bwenzi, makanika, nesi—mndandandawo ukupitirizabe. Khololo silimasintha umunthu pamene lisintha mbali zimenezi; ilo limangosinthira ku zosoŵa zapanthaŵiyo. Zilinso motero kwa Yehova koma pamlingo waukulu koposa. Palibe malire pazimene iye angadzichititse kukhala kotero kuti apindulitse zolengedwa zake. Kuya kwa nzeru zake kulidi kodabwitsa!—Aroma 11:33.
Kulolera, Chizindikiro cha Nzeru Yaumulungu
6. Kodi ndi tanthauzo lenileni lotani ndi malingaliro ena a liwu Lachigiriki limene Yakobo anagwiritsira ntchito polongosola nzeru yaumulungu?
6 Wophunzira Yakobo anagwiritsira ntchito liwu lokondweretsa polongosola nzeru ya Mulungu ameneyu wokhoza kusintha kwambiri. Iye analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba ili . . . yololera.” (Yakobo 3:17, NW) Liwu Lachigiriki limene anagwiritsira ntchito pano lakuti (e·pi·ei·kesʹ) nlovuta kutembenuza. Otembenuza agwiritsira ntchito mawu onga “kufatsa,” “kuchitira chifundo,” “kudziletsa,” ndi “kulingalira ena.” New World Translation imalimasulira kuti “kulolera,” ndi mawu amtsinde osonyeza kuti tanthauzo lenileni ndilo “kugonja.”a Liwulo limaperekanso lingaliro la kusaumirira pa mawu a lamulo, kusakhala wokhwima mosayenerera kapena kuuma khosi. Katswiri wotchedwa William Barclay akunena kuti mu New Testament Words: “Chinthu chachikulu ndi chofunikira ponena za epieikeia nchakuti lili ndi magwero ake kwa Mulungu. Ngati Mulungu akadaumirira pa miyezo yake, ngati Mulungu akadagwiritsira ntchito pa ife miyezo yokhwima ya lamulo, kodi zikanatikhalira motani? Mulungu ali chitsanzo chopambana cha munthu amene ali wa epieikēs ndi amenenso amachitira ena mwa epieikeia.”
7. Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera kulolera m’munda wa Edene?
7 Talingalirani za nthaŵi pamene mtundu wa anthu unapandukira uchifumu wa Yehova. Kukanakhala kosavuta chotani nanga kwa Mulungu kupha apandu osayamikira atatuwo, Adamu, Hava, ndi Satana! Ndi kupwetekedwa mtima kwakukulu kotani nanga kwamtsogolo kumene iye akanakupeŵa! Ndipo kodi ndani yemwe akadatsutsa kuti iye analibe kuyenera kwa kuweruza ndi chilungamo chokhwima choterocho? Komabe, Yehova samapanikizira gulu lake longa galeta lakumwambalo kuyenda pa muyezo wokhwima, wosasinthika wa chilungamo. Motero galeta limenelo silinangopitirira ndi kukagunda banja la anthu ndi ziyembekezo zonse za mtsogolo mwa chimwemwe mwa mtundu wa anthu. Mmalomwake, Yehova anayendetsa galeta lakelo pa liŵiro la mphezi. Mwamsanga pambuyo pa chipandukocho, Yehova Mulungu analinganiza chifuno chofika patali chimene chinapereka chifundo ndi chiyembekezo ku mbadwa zonse za Adamu.—Genesis 3:15.
8. (a) Kodi ndimotani mmene lingaliro lolakwa la Dziko Lachikristu limasiyanira ndi kulolera kolungama kwa Yehova? (b) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kulolera kwa Yehova sikumatanthauza kuti iye angalolere molakwa miyezo yake yaumulungu?
8 Komabe, kulolera kwa Yehova sikumatanthauza kuti iye angalolere molakwa malamulo a mkhalidwe aumulungu. Matchalitchi a lerolino a Dziko Lachikristu angalingalire kuti akukhala ololera pamene akunyalanyaza makhalidwe oipa kaamba kofuna kupeza chiyanjo kwa nkhosa zawo zopanduka. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 4:3.) Yehova samaswa malamulo a iye mwini, ndiponso samalolera molakwa malamulo ake a mkhalidwe. Mmalomwake, amasonyeza kufunitsitsa kwa kugonja, kusinthira ku mikhalidwe, kotero kuti malamulo a mkhalidwe amenewo angagwiritsiridwe ntchito ponse paŵiri mwachilungamo ndi mwachifundo. Iye nthaŵi zonse amakumbukira kuchita chilungamo ndi mphamvu molinganiza ndi chikondi ndi nzeru yake yololera. Tiyeni tipende njira zitatu zimene Yehova amasonyezera kulolera.
“Wofunitsitsa Kukhululukira”
9, 10. (a) Kodi kukhala “wofunitsitsa kukhululukira” nkogwirizana motani ndi kulolera? (b) Kodi ndimotani mmene Davide anapindulira ndi kufunitsitsa kukhululukira kwa Yehova, ndipo chifukwa ninji?
9 Davide analemba kuti: “Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi [wofunitsitsa kukhululukira, NW], ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.” (Salmo 86:5) Pamene Malemba Achihebri ankatembenuzidwa m’Chigiriki, liwu lotanthauza “wofunitsitsa kukhululukira” linatembenuzidwa kukhala e·pi·ei·kesʹ, kapena “kulolera.” Ndithudi, kukhala wofunitsitsa kukhululukira ndi kusonyeza chifundo ndiko mwinamwake njira yofunika koposa yosonyezera kulolera.
10 Davide mwiniyo anadziŵa bwino lomwe za kulolera kwa Yehova m’nkhani imeneyi. Pamene Davide anachita chigololo ndi Bateseba ndi kulinganiza kuti mwamuna wake aphedwe, onse aŵiri iye ndi Bateseba anayenera chilango cha imfa. (Deuteronomo 22:22; 2 Samueli 11:2-27) Ngati kuti oweruza aumunthu ouma khosi ndiwo akanaweruza mlanduwo, onse aŵiriwo akadataya miyoyo yawo. Koma Yehova anasonyeza kulolera (e·pi·ei·kes), kumene, malinga ndi kunena kwa Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words, “kumasonyeza kulingalira ena kumene kumayang’ana ‘mwachifundo ndi mololera pa zifukwa za mlanduwo.’” Zifukwa zimene zinasonkhezera chiweruzo chachifundo cha Yehova mwachionekere zinaphatikizapo kulapa koona mtima kwa olakwawo ndi chifundo chimene Davide iye mwini anali atasonyeza kwa ena. (1 Samueli 24:4-6; 25:32-35; 26:7-11; Mateyu 5:7; Yakobo 2:13) Komabe, molingana ndi kudzilongosola kwa Yehova pa Eksodo 34:4-7, kunali kulolera pamene Yehova anawongolera Davide. Iye anatumiza mneneri Natani kwa Davide ndi uthenga wamphamvu, akumagogomezera kwa Davide mfundo yakuti iye anali atanyoza mawu a Yehova. Davide analapa ndipo motero sanafe pa tchimo lakelo.—2 Samueli 12:1-14.
11. Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera kufunitsitsa kukhululukira pamlandu wa Manase?
11 Chitsanzo cha Mfumu Manase wa Yuda nchapadera kwambiri pankhaniyi, popeza kuti Manase, mosiyana ndi Davide, anali woipa kwambiri kwa nthaŵi yaitali. Manase anachirikiza machitachita onyansa akulambira m’dzikomo, kuphatikizapo kupereka nsembe anthu. Iye angakhale atachititsa kuti mneneri wokhulupirika Yesaya ‘achekedwe pakati.’ (Ahebri 11:37) Kuti alange Manase, Yehova adalola kuti iye atengedwe ukapolo ku Babulo. Komabe, Manase analapa m’ndendemo nachonderera chifundo. Monga yankho pa kulapa koona mtima kumeneku, Yehova anali “wofunitsitsa kukhululukira”—ngakhale pa mlandu woipitsitsa umenewu.—2 Mbiri 33:9-13.
Kusintha Njira ya Kachitidwe Patabuka Mikhalidwe Yatsopano
12, 13. (a) M’nkhani ya Nineve, kodi ndi kusintha kwa mikhalidwe kotani kumene kunasonkhezera Yehova kusintha kachitidwe kake? (b) Kodi ndimotani mmene Yona anadzisonyezera kukhala wosalolera mosiyana ndi Yehova Mulungu?
12 Kulolera kwa Yehova kumasonyezanso kufunitsitsa kwake kusintha njira yake ya kachitidwe pamene mikhalidwe yatsopano ibuka. Mwachitsanzo, pamene mneneri Yona anayenda m’makwalala a Nineve wakaleyo, uthenga wake wouziridwa unali wosavuta: Mzinda waukuluwo ukawonongedwa atapita masiku 40. Komabe, mikhalidwe inasintha—kusintha kwakukulu! Aninevewo adalapa.—Yona, chaputala 3.
13 Kuli kothandiza kupenda kusiyana kwa mmene Yehova ndi Yona anachitira pamene mikhalidwe inasintha. Yehova kwenikweni anasintha njira ya galeta lake lakumwamba. M’chochitikachi iye anasintha, akumakhala wokhululukira machimo mmalo mwa kukhala “wankhondo.” (Eksodo 15:3) Kumbali inayo, Yona anali wosasinthika konse. Mmalo moyendera limodzi ndi galeta la Yehova, iye anachita mofanana kwambiri ndi sitima ya katundu kapena chombo cha mafuta chachikulu kwambiri zotchulidwa poyambapo. Iye anali atalengeza chiwonongeko, motero chiyenera kukhala chiwonongeko basi! Mwinamwake analingalira kuti kusintha kulikonse m’kachitidweko kukamnyazitsa pamaso pa Anineve. Komabe, moleza mtima, Yehova anaphunzitsa mneneri wake wouma khosiyo phunziro losaiŵalika la kulolera ndi chifundo.—Yona, chaputala 4.
14. Kodi nchifukwa ninji Yehova anasintha njira yake ya kachitidwe ponena za mneneri wake Ezekieli?
14 Yehova wasintha njira yake ya kachitidwe pazochitika zinanso—ngakhale pankhani zina zazing’ono. Mwachitsanzo, nthaŵi ina pamene anatuma mneneri Ezekieli kuchita seŵero laulosi, malangizo a Yehova anaphatikizapo lakuti Ezekieli aphike chakudya chake pamoto wa ndowe za munthu. Zimenezi zinali zonkitsa kwa mneneriyo, yemwe anadandaula kuti, “Ha, Ambuye Yehova!” napempha kuti asachititsidwe chonyansa choterocho kwa iye. Yehova sananyalanyaze malingaliro a mneneriyo monga osayenera; mmalo mwake, iye analola Ezekieli kugwiritsira ntchito ndowe za ng’ombe, nkhuni zofala m’maiko ambiri kufikira lerolino.—Ezekieli 4:12-15.
15. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti Yehova wakhala wofunitsitsa kumvetsera ndi kuyankha anthu? (b) Kodi ndi phunziro lotani limene zimenezi zingatiphunzitse?
15 Kodi sikuli kothuzitsa mtima kulingalira za kudzichepetsa kwa Mulungu wathu Yehova? (Salmo 18:35) Iye ali wam’mwambamwamba kwambiri kuposa ife; komabe amamvetsera moleza mtima kwa anthu opanda ungwiro ndipo ngakhale kusintha kachitidwe kake moyenerera panthaŵi zina. Iye analola Abrahamu kuchonderera kwa iye kwa nthaŵi yaitali ponena za kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora. (Genesis 18:23-33) Ndipo analola Mose kunena mawu otsutsa ganizo Lake la kuwononga Aisrayeli opandukawo ndipo mmalo mwake kupanga mtundu wamphamvu kuchokera mwa Mose. (Eksodo 32:7-14; Deuteronomo 9:14, 19; yerekezerani ndi Amosi 7:1-6.) Mwakutero iye anapereka chitsanzo chabwino koposa kwa atumiki ake aumunthu, amene afunikira kusonyeza kufunitsitsa kofananako kwa kumvetsera kwa ena pamene kukhala kololereka ndi kotheka kutero.—Yerekezerani ndi Yakobo 1:19.
Kulolera Pochita Ulamuliro
16. Kodi Yehova ali wosiyana motani ndi anthu ambiri m’njira imene amachitira ulamuliro?
16 Kodi mwaona kuti pamene anthu apeza ulamuliro wowonjezereka, ambiri amaonekera kuti kulolera kwawo anthu ena kumacheperachepera? Mosiyana ndi zimenezo, Yehova ali ndi malo apamwamba koposa aulamuliro m’chilengedwe chonse, komabe ali chitsanzo chopambana cha kulolera. Iye amachita ulamuliro wake mwa njira yololera yosalephera. Mosiyana ndi anthu ambiri, Yehova sali wotekeseka pa ulamuliro wake, motero samadzimva wokakamizika kuutetezera mwansanje—monga kuti kugaŵira ena mlingo winawake wa ulamuliro kungawopseze wakewo. Kwenikweni, pamene kunali munthu wina mmodzi yekha m’chilengedwe chonse, Yehova anapereka ulamuliro waukulu kwa iyeyo. Iye anapanga Logosi kukhala “mmisiri” wake, kuyambira pamenepo akumapanga zinthu zonse kupyolera mwa Mwana wake wokondedwa ameneyu. (Miyambo 8:22, 29-31; Yohane 1:1-3, 14; Akolose 1:15-17) Iye pambuyo pake anampatsa “mphamvu zonse . . . kumwamba ndi pa dziko lapansi.”—Mateyu 28:18; Yohane 5:22.
17, 18. (a) Kodi Yehova anatumiziranji angelo ku Sodomu ndi Gomora? (b) Kodi Yehova anapempheranji angelo kupereka malingaliro a mmene akanyengera Ahabu?
17 Mofananamo, Yehova amapatsa zolengedwa zake zambiri mathayo amene akanawachita bwinopo iye mwini. Mwachitsanzo, pamene anauza Abrahamu kuti, “ndidzatsikatu [ku Sodomu ndi Gomora] ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira,” sanatanthauze kuti akapita kumeneko iye mwiniyo. Mmalomwake, Yehova anasankha kugaŵira ulamuliro ndipo anasankha angelo kukampezera chidziŵitso chimenecho. Anawapatsa ulamuliro wa kutsogoza ntchito imeneyi ya kupeza maumboni ndi kubwezera lipoti kwa iye.—Genesis 18:1-3, 20-22.
18 Panthaŵi ina, pamene Yehova anasankha kupereka chiweruzo pa Mfumu Ahabu yoipayo, Iye anaitana angelo kumsonkhano wakumwamba kuti apereke malingaliro a mmene ‘akanyengera’ mfumu yopandukayo kuti ikamenye nkhondo imene ikathetsa moyo wake. Ndithudi, Yehova, Magwero a nzeru zonse, sanafunikire thandizo pakusankha njira yabwino koposa ya kachitidwe! Komabe, iye analemekeza angelo mwa kuwapatsa mwaŵi wa kupereka malingaliro nawapatsa ulamuliro wa kuchitapo kanthu pa uyo amene iye anamsankha.—1 Mafumu 22:19-22.
19. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova amachepetsa unyinji wa malamulo ake amene amapanga? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova amadzisonyezera yekha kukhala wololera pa zimene amayembekezera kwa ife?
19 Yehova samagwiritsira ntchito ulamuliro wake mwa kutsendereza ena. M’zimenezinso amasonyeza kulolera kosayerekezereka. Iye amachepetsa mosamalitsa unyinji wa malamulo amene amapanga ndi kuletsa atumiki ake ‘kupitirira zolembedwa’ mwa kuwonjezera malamulo otopetsa odzipangira okha. (1 Akorinto 4:6; Machitidwe 15:28; siyanitsani ndi Mateyu 23:4.) Iye samafuna kumvera kosalingalira kwa zolengedwa zake, koma mwanthaŵi zonse amapereka chidziŵitso chokwanira kuwatsogolera ndipo amawaikira chosankha, akumawalola kudziŵa phindu la kumvera ndi zotulukapo za kusamvera. (Deuteronomo 30:19, 20) Mmalo mwa kuchititsa anthu kudzimva aliwongo, amanyazi, kapena amantha, iye amafuna kufikira mitima yawo; amafuna kuti anthu amtumikire mwa chikondi chenicheni mmalo mokakamizidwa. (2 Akorinto 9:7) Utumiki wa mtima wonse woterowo umakondweretsa mtima wa Mulungu, motero iye sali “wovuta kukondweretsa” wosalolera.—1 Petro 2:18, NW; Miyambo 27:11; yerekezerani ndi Mika 6:8.
20. Kodi kulolera kwa Yehova kumakuyambukirani motani?
20 Kodi sikodabwitsa kuti Yehova Mulungu, amene ali ndi mphamvu yaikulu kuposa aliyense m’chilengedwe, samaigwiritsira ntchito mphamvuyo mwanjira yosalolera, ndi kuwopsezera ena? Komabe, anthu, pokhala opanda pake powayerekezera ndi iye, ali ndi mbiri ya kutsenderezana wina ndi mnzake. (Mlaliki 8:9) Mwachionekere, kulolera kuli mkhalidwe wamtengo wapatali, umene umatisonkhezera kukonda Yehova koposerapo. Chimenecho, chingatisonkhezerenso kukulitsa mkhalidwe umenewu. Kodi tingachite motani zimenezo? Nkhani yotsatira idzayankha funso limenelo.
[Mawu a M’munsi]
a Kalelo mu 1769, wolemba dikishonale John Parkhurst anatanthauzira liwulo kukhala “kugonja, maganizo ogonja, kufatsa, kudekha, kuleza mtima.” Akatswiri ena aperekanso “kugonja” kukhala tanthauzo lake.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi dzina la Yehova ndi masomphenya a galeta lake lakumwamba zimasonyeza motani kukhoza kwake kusintha?
◻ Kodi kulolera nchiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji kuli chizindikiro cha nzeru yaumulungu?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene Yehova wasonyezera kuti ali “wofunitsitsa kukhululukira”?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova wasankha kusintha njira yake ya kachitidwe m’zochitika zina?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova amasonyezera kulolera kwake m’njira imene amachitira ulamuliro wake?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi nchifukwa ninji Yehova anakhululukira Mfumu yoipayo Manase?