ZAKUMAPETO
Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
KODI lemba la Salimo 83:18 linamasuliridwa bwanji m’Baibulo lanu? M’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lembali analimasulira kuti: “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Mabaibulo ena ambiri amamasuliranso lembali mofanana ndi zimenezi. Komabe m’Mabaibulo ena ambiri, amene ankamasulira Mabaibulowo anachotsa dzina lakuti Yehova, n’kungolemba kuti “Ambuye” kapena “Wamuyaya.” Kodi zolondola ndi ziti? Kodi pavesili panayenera kulembedwa dzina lakuti Yehova, kapena dzina laudindo chabe?
Vesili likufotokoza za dzina la Mulungu. Ndipo m’malemba achiheberi oyambirira, pavesili anatchulapo dzina lenileni la Mulungu. Chinenero cha Chiheberi ndi chimene chinagwiritsidwa ntchito polemba mabuku ambiri a m’Baibulo. M’chinenero chimenechi, dzinali limalembedwa chonchi יהוה (YHWH). M’Chichewa, anthu ambiri dzinali amalitchula kuti “Yehova.” Kodi dzina limeneli limangopezeka pavesi limodzi lokhali? Ayi. M’malemba achiheberi oyambirira, dzinali linkapezeka m’malo pafupifupi 7,000.
Koma kodi dzina la Mulungu ndi lofunika bwanji? Taganizirani za pemphero lachitsanzo limene Yesu Khristu ananena. Pempheroli limayamba ndi mawu akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Nthawi inanso Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Ndipo Mulungu anayankha ali kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.” (Yohane 12:28) Zimenezi zikusonyeza kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri. Koma nanga n’chifukwa chiyani omasulira Mabaibulo ena anachotsa dzinali m’Mabaibulo awo n’kungolembamo mayina audindo?
Zikuoneka kuti anachita zimenezi pa zifukwa ziwiri izi: Choyamba, ambiri amanena kuti si bwino kugwiritsa ntchito dzinali chifukwa panopa palibe amene amadziwa katchulidwe kake kenikeni. Chiheberi chakale chinkalembedwa chopanda zilembo za liwu (mavawelo). Choncho masiku ano palibe munthu amene angadziwe molondola mmene anthu akale ankatchulira zilembo za YHWH zimenezi. Koma kodi chimenechi ndi chifukwa chomveka choti anthu asamagwiritsire ntchito dzina la Mulungu? Mwachitsanzo, n’kutheka kuti kale dzina lakuti Yesu linkatchulidwa kuti Yeshuwa kapena Yehoshuwa, zomwe zikusonyeza kuti panopa palibe amene akudziwa katchulidwe kenikeni ka dzinali komanso mmene Akhristu oyambirira ankalitchulira. Ngakhale zili choncho, anthu a m’mayiko osiyanasiyana amagwiritsabe ntchito dzinali koma amalitchula mogwirizana ndi mmene anthu ambiri achinenero chawocho amalitchulira. N’chimodzimodzinso ndi dzina lanu. Ngati mutapita dziko lina, mungadabwe kuona kuti anthu a m’dzikolo akulitchula mwa njira ina. Choncho, kusadziwa mmene anthu akale ankatchulira dzina la Mulungu, si chifukwa chokwanira chotilepheretsa kuligwiritsa ntchito.
Chifukwa chachiwiri chimene chimachititsa omasulira ambiri kuchotsa dzina la Mulungu m’Baibulo, chikukhudza chikhalidwe chimene Ayuda akhala akuchitsatira kwa zaka zambiri. Ayuda ambiri amakhulupirira kuti dzina la Mulungu siliyenera kutchulidwa n’komwe. Chikhulupiriro chimenechi chiyenera kuti chinayamba chifukwa chosamvetsa lamulo la m’Baibulo limene limati: “Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala, pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.”—Ekisodo 20:7.
Lamulo limeneli limaletsa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu molakwika. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu sakuyenera kugwiritsa ntchito dzinali ngakhale pa zinthu zabwinobwino? Ayi, si choncho. Anthu onse amene analemba nawo Malemba Achiheberi (Chipangano Chakale) anali anthu okhulupirika amene ankatsatira Chilamulo cha Mulungu chimene anapereka kwa Aisiraeli akale. Komabe ankagwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu pafupipafupi. Mwachitsanzo, dzinali ankaligwiritsa ntchito m’masalimo amene ankaimbidwa ndi anthu ambirimbiri. Ndipotu Yehova Mulungu anauza anthu amene amamulambira kuti aziitana pa dzina lake ndipo anthu okhulupirika amatsatira malangizo amenewa. (Yoweli 2:32; Machitidwe 2:21) Choncho Akhristu oona masiku ano saopa kugwiritsa ntchito moyenera dzina lenileni la Mulungu ndipo zikuoneka kuti Yesu ankaligwiritsanso ntchito.—Yohane 17:26.
Zimene anthu omasulira Mabaibulo ena anachita pochotsa dzina lenileni la Mulungu n’kungogwiritsa ntchito mayina audindo, ndi kulakwitsa kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti Mulungu azioneka ngati wosatheka kulankhula naye komanso kukhala naye pa ubwenzi. Komatu Baibulo limalimbikitsa anthu kuti akhale pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova.” (Salimo 25:14) Taganizirani za mnzanu wapamtima. Kodi zingatheke kuti muzigwirizana naye kwambiri koma musakumudziwa dzina lake? Mofanana ndi zimenezi, kodi anthu angakhale bwanji pa ubwenzi ndi Mulungu ngati sakudziwa dzina lake lenileni lakuti Yehova? Komanso ngati anthu sagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, sangadziwenso tanthauzo lake. Kodi dzina la Mulungu limatanthauza chiyani?
Mulungu anafotokoza yekha tanthauzo la dzina lake kwa mtumiki wake wokhulupirika Mose. Pamene Mose anafunsa za dzina la Mulungu, Yehova anamuyankha kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (Ekisodo 3:14) Choncho Yehova akhoza kukhala chilichonse chimene chingafunikire kuti akwaniritse cholinga chake. Akhozanso kuchititsa kuti chilichonse chokhudza chilengedwe kapena cholinga chake chitheke.
Tiyerekeze kuti inuyo muli ndi mphamvu zotha kukhala chilichonse chimene mukufuna. Kodi anzanu mungawachitire zotani? Ngati mnzanu wina atadwala kwambiri, mukhoza kukhala dokotala n’kumuchiritsa. Ndipo ngati wina atakhala ndi vuto la zachuma, mukhoza kukhala munthu wolemera n’kumuthandiza. Komabe tikudziwa kuti inuyo simungathe kukhala aliyense amene mukufuna, ndipo ndi mmene tonsefe tilili. Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadabwa kudziwa mmene Yehova amakhalira chilichonse chimene chikufunikira kuti akwaniritse zimene walonjeza. Mudzaonanso kuti amasangalala kugwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu amene amamukonda. (2 Mbiri 16:9) Koma anthu amene sadziwa dzina la Yehova alibe mwayi wothandizidwa mwa njira imeneyi.
Zimene takambiranazi ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti dzina la Mulungu, lakuti Yehova, ndi loyenera kuti lizipezeka m’Baibulo. Kudziwa tanthauzo lake ndiponso kuligwiritsa ntchito, kudzatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova.a
a Kuti mumve zambiri zokhudza dzina la Mulungu, tanthauzo lake komanso zifukwa zotichititsa kuligwiritsa ntchito polambira, onani kabuku kakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, ndiponso mutu woyamba m’Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu. Timabukuti ndi tofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.