Kulimbikitsidwa ndi “Zazikulu za Mulungu”
“Tiwamva iwo ali kulankhula m’malilime athu zazikulu za Mulungu.”—MACHITIDWE 2:11.
1, 2. Kodi n’chinthu chodabwitsa chiti chimene chinachitika ku Yerusalemu pa Pentekoste mu 33 C.E.?
TSIKU lina m’maŵa kumapeto kwa chilimwe m’chaka cha 33 C.E., chinthu china chodabwitsa chinachitikira gulu la amuna ndi akazi, ophunzira a Yesu Kristu amene anasonkhana m’nyumba ya munthu wina ku Yerusalemu. “Mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene anali kukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogaŵanikana, onga amoto . . . Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena.”—Machitidwe 2:2-4, 15.
2 Khamu la anthu linasonkhana kumaso kwa nyumbayo. Ena mwa iwo anali Ayuda amene anabadwira ku mayiko ena, “amuna opembedza” amene anabwera ku Yerusalemu kuti akondwerere phwando la Pentekoste. Iwo anadabwa kwambiri chifukwa chakuti aliyense anamva ophunzirawo akulankhula “zazikulu za Mulungu” m’chinenero cha kwawo. Kodi zimenezo zinatheka bwanji popeza onse amene anali kulankhulawo anali a ku Galileya?—Machitidwe 2:5-8, 11.
3. Kodi ndi uthenga wotani umene mtumwi Petro anauza khamu la anthu pa Pentekoste?
3 Mmodzi mwa anthu a ku Galileya amenewo anali mtumwi Petro. Iye anafotokoza kuti milungu ingapo izi zisanachitike, anthu opanda chilungamo anapha Yesu Kristu. Komabe, Mulungu anaukitsa Mwana wake. Kenako, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake ambiri, kuphatikizapo Petro ndi ena amene analipo panthaŵiyi. Masiku khumi okha mmbuyomo, Yesu anakwera kumwamba. Ndi iyeyo amene anatsanulira mzimu woyera kwa ophunzira ake. Kodi zimenezi zinali ndi tanthauzo lililonse kwa anthu amene anali kukondwerera Pentekostewo? Inde. Imfa ya Yesu inawatsegulira njira yoti akhululukidwe machimo awo ndi kulandira “mphatso ya Mzimu Woyera” ngati akanamukhulupirira. (Machitidwe 2:22-24, 32, 33, 38) Kodi anthu amene anali kuonererawo anachita chiyani atamva “zazikulu za Mulungu” zimenezi? Ndipo kodi nkhani imeneyi ingatithandize bwanji kupenda utumiki wathu kwa Yehova?
Analimbikitsidwa Kuchitapo Kanthu!
4. Kodi ndi ulosi uti wa Yoweli umene unakwaniritsidwa pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E.?
4 Atalandira mzimu woyera, ophunzira ku Yerusalemu nthaŵi yomweyo anayamba kuuza ena uthenga wabwino wachipulumutso, ndipo anayambira ndi khamu la anthu limene linasonkhana m’maŵa umenewo. Kulalikira kwawo kunakwaniritsa ulosi wosangalatsa umene Yoweli, mwana wa Petueli, analemba zaka mazana asanu ndi atatu zimenezi zisanachitike. Iye anati: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya; ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo . . . lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.”—Yoweli 1:1; 2:28, 29, 31; Machitidwe 2:17, 18, 20.
5. Kodi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anali kulosera mulingaliro lotani? (Onani mawu a m’munsi.)
5 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Mulungu adzapanga aneneri, amuna ndi akazi, monga mmene analili Davide, Yoweli, ndi Debora, ndi kuwagwiritsa ntchito kuti azilosera za m’tsogolo? Ayi. ‘Ana aamuna ndi aakazi, akapolo ndi adzakazi’ achikristu adzanenera mulingaliro lakuti mzimu wa Yehova udzawalimbikitsa kulalikira “zazikulu” zimene Yehova wachita ndiponso zimene adzachita. Motero, iwo adzakhala olankhulira a Wam’mwambamwamba.a Koma kodi khamu la anthulo linachitapo chiyani?—Ahebri 1:1, 2.
6. Kodi anthu ambiri m’khamulo analimbikitsidwa kuchita chiyani atamva nkhani ya Petro?
6 Khamu la anthulo litamva zimene Petro anafotokoza, ambiri mwa iwo analimbikitsidwa kuchitapo kanthu. Iwo “analandira mawu ake” ndipo “anabatizidwa; ndipo anawonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.” (Machitidwe 2:41) Popeza anali Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda, iwo ankadziŵa ziphunzitso zoyambirira za m’Malemba. Zimene anali kudziŵazo pamodzi ndi kukhulupirira zimene anaphunzira kwa Petro, zinali maziko oti abatizidwe “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19) Atabatizidwa, iwo “anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi.” Ndiponso, iwo anayamba kuuza ena chikhulupiriro chawo chimene anangochipeza kumenecho. Inde, “tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m’kachisi, . . . ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse.” Chifukwa cha ntchito yochitira umboni imeneyi, “[Yehova] anawawonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.” (Machitidwe 2:42, 46, 47) Mipingo yachikristu inayambika mwamsanga m’madera amene okhulupirira atsopanoŵa anali kukhala. N’zosakayikitsa kuti mwa zina, kuwonjezeka kumeneku kunachitika chifukwa cha changu chawo polalikira “uthenga wabwino” atabwerera kwawo.—Akolose 1:23.
Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu
7. (a) Kodi n’chiyani chimakopera anthu a mitundu yonse ku gulu la Yehova masiku ano? (b) Kodi mukuona kuti pangakhale kuwonjezeka kotani m’munda wa padziko lonse ndiponso kwanuko? (Onani mawu a m’munsi.)
7 Bwanji nanga za amene akufuna kukhala atumiki a Mulungu lerolino? Iwonso afunika kuphunzira Mawu a Mulungu mosamala. Pamene akutero, iwo amam’dziŵa Yehova kukhala Mulungu “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6; Machitidwe 13:48) Amaphunzira za makonzedwe achikondi a Yehova a dipo limene anapereka kudzera mwa Yesu Kristu, yemwe mwazi wake umene anakhetsa ungawayeretse ku machimo onse. (1 Yohane 1:7) Iwo amayamikiranso kudziŵa cholinga cha Mulungu chakuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Kukonda Gwero la “zazikulu” zimenezi kumadzaza m’mitima yawo, ndipo amalimbikitsidwa kulalikira choonadi cha mtengo wapatali chimenechi. Ndiyeno amakhala atumiki a Mulungu odzipatulira ndi obatizidwa ndipo amapitiriza “kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.”b—Akolose 1:10b; 2 Akorinto 5:14.
8-10. (a) Kodi zimene zinachitikira mkazi wina wachikristu zinasonyeza bwanji kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu? (b) Kodi nkhani imeneyi yakuphunzitsani chiyani za Yehova ndi mmene amachitira ndi atumiki ake? (Eksodo 4:12)
8 Zimene atumiki a Mulungu amadziŵa mwa kuphunzira Baibulo n’zozama. Zimenezi zimalimbikitsa mitima yawo, kusintha maganizo awo, ndiponso amakhala nazobe. (Ahebri 4:12) Mwachitsanzo, mkazi wina dzina lake Camille analembedwa ntchito yosamalira anthu okalamba. Mmodzi mwa anthu amene anali kuwasamalira anali a Martha, omwe anali a Mboni za Yehova. Popeza a Martha anali kudwala kwambiri matenda a maganizo, iwo ankafunikira kuwayang’anira nthaŵi zonse. Ankafunika kuwakumbutsa kudya, ngakhale kumeza chakudya kumene. Komabe, panali chinthu chimodzi chimene sanali kuiwala, monga momwe tionere.
9 Tsiku lina, a Martha anaona Camille akusisima chifukwa cha nkhaŵa imene anali nayo chifukwa cha mavuto ake. A Martha anam’kupatira Camille ndipo anam’pempha kuti aziphunzira naye Baibulo. Koma kodi mmene a Martha anali kudwalira akanatha kuphunzitsa Baibulo? Inde, akanatha kutero! Ngakhale kuti sankatha kukumbukira zinthu, a Martha sanaiwale Mulungu wawo wamkulu ndiponso choonadi cha mtengo wapatali chimene anaphunzira m’Baibulo. Pa phunzirolo, a Martha anali kuuza Camille kuti aŵerenge ndime iliyonse, kuŵerenga Malemba amene awasonyeza pa ndimeyo, kuŵerenga funso m’munsi mwa tsambalo, ndiyeno n’kuliyankha. Zimenezi zinachitika kwanthaŵi yaitali ndithu ndipo ngakhale kuti a Martha sankatha kuchita zambiri, Camille anapita patsogolo kudziŵa Baibulo. A Martha anazindikira kuti Camille anafunika kusonkhana ndi ena amene anali ndi chidwi chotumikira Mulungu. Poganizira zimenezi, iwo anapatsa wophunzira wawoyo diresi ndi nsapato, kuti akhale ndi zovala zabwino pokasonkhana koyamba ku Nyumba ya Ufumu.
10 Camille analimbikitsidwa ndi chikondi ndi chitsanzo cha a Martha ndiponso chikhulupiriro chawo. Iye anaona kuti zimene a Martha anali kum’phunzitsa m’Baibulo zinali zofunika kwambiri, popeza a Martha anaiŵala pafupifupi chilichonse kupatulapo zimene anaphunzira m’Malemba. Kenako, Camille atamutumiza ku malo ena osamalira okalamba, anazindikira kuti inali nthaŵi yoti achitepo kanthu. Kwanthaŵi yoyamba, iye analoŵa m’Nyumba ya Ufumu, atavala diresi ndi nsapato zimene a Martha anam’patsa, ndipo anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Camille anapita patsogolo ndipo anabatizidwa.
Kulimbikitsidwa Kutsatira Miyezo ya Yehova
11. Kuwonjezera pa kukhala achangu pa ntchito yolalikira, kodi tingasonyeze bwanji kuti talimbikitsidwa ndi uthenga wa Ufumu?
11 Masiku ano, pali Mboni za Yehova zoposa sikisi miliyoni zimene zikulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ padziko lonse monga anachitira a Martha ndiponso mmene akuchitira Camille tsopano. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mofanana ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, iwo alimbikitsidwa kwambiri ndi “zazikulu za Mulungu.” Amayamikira kuti ali ndi mwayi wokhala ndi dzina la Yehova ndi kuti iye wawatsanulira mzimu wake. Chifukwa cha zimenezi, iwo amayesetsa ‘kuyenda koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo,’ kutsatira miyezo yake m’mbali zonse za moyo wawo. Mwa zina, iwo amalemekeza miyezo ya Mulungu ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa.—Akolose 1:10; Tito 2:10.
12. Kodi ndi malangizo osapita m’mbali ati okhudza kavalidwe ndi kudzikongoletsa amene ali pa 1 Timoteo 2:9, 10?
12 Inde, Yehova waika miyezo pankhani ya kaonekedwe kathu. Mtumwi Paulo anafotokoza ina mwa miyezo ya Mulungu pankhani imeneyi. Anati: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.”c Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu ameneŵa?—1 Timoteo 2:9, 10.
13. (a) Kodi “chovala choyenera” chimatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti miyezo ya Yehova ndi yotheka kuitsatira?
13 Mawu a Paulo akufotokoza kuti Akristu ayenera ‘kudziveka okha ndi chovala choyenera.’ Sayenera kukhala auve m’kaonekedwe kawo. Aliyense, ngakhale osauka angakwanitse muyezo umenewu mwa kuonetsetsa kuti zovala zawo n’zaukhondo ndiponso zooneka bwino. Mwachitsanzo, chaka chilichonse Mboni za m’dziko lina la ku South America zimayenda makilomita ambiri kudutsa m’nkhalango ndiyeno zimayendanso maola ambiri pa bwato kuti zikapezeke pa msonkhano wawo wachigawo. Si zachilendo kuti munthu agwere mumtsinje kapena kuti zovala zikoledwe ndi timitengo pamene akuyenda. Motero, anthu ameneŵa pofika ku malo a msonkhanowo, amakhala asakuoneka bwino. Zikatero, amapeza nthaŵi n’kusoka mabatani, kukonza zipi, ndiponso kuchapa ndi kusita zovala zimene avale pa msonkhanowo. Amanyadira kuitanidwa kwawo kudzadya pa gome la Yehova, ndipo amafuna kuvala moyenera.
14. (a) Kodi kuvala ndi “manyazi ndi chidziletso” kumatanthauza chiyani? (b) Kodi tifunika kutani kuti tivale ‘monga anthu ovomereza kulemekeza Mulungu’?
14 Paulo ananenanso kuti tiyenera kuvala ndi “manyazi ndi chidziletso.” Zimenezi zikutanthauza kuti kaonekedwe kathu sikayenera kukhala kosadziletsa, kuvala masitayelo osayenera, kuvala modzutsa chilakolako cha kugonana, zovala zoonetsa m’kati, kapena zosonyeza kutengeka kwambiri ndi mafashoni. Ndiponso, tiyenera kuvala mosonyeza kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ Kodi zimenezi sizikutichititsa kuiganizira bwino nkhaniyi? Imeneyi si nkhani yongovala moyenerera popita ku misonkhano ya mpingo ndiyeno n’kutairira ngati si nthaŵi ya misonkhano. Kaonekedwe kathu nthaŵi zonse kayenera kusonyeza ulemu chifukwa ndife Akristu ndiponso atumiki tsiku lonse lathunthu. N’zachidziŵikire kuti zovala zathu zogwirira ntchito ndiponso zakusukulu zidzagwirizana ndi ntchito imene tikuchita. Komabe, tiyenera kuvala moyenera ndiponso mwaulemu. Ngati kavalidwe kathu nthaŵi zonse kamasonyeza kuti timakhulupirira Mulungu, sitidzapeŵa kulalikira mwamwayi chifukwa chochita manyazi ndi kaonekedwe kathu.—1 Petro 3:15.
“Musakonde Dziko Lapansi”
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kupeŵa kutsanzira dziko pankhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa? (1 Yohane 5:19) (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kutengekatengeka pa kavalidwe ndi kudzikongoletsa?
15 Uphungu umene uli pa 1 Yohane 2:15, 16 umatipatsanso malangizo a mmene tingasankhire zovala ndiponso mmene tingadzikongoletsere. Timaŵerenga kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.”
16 Uphungu umenewutu ndi wa panthaŵi yake. M’nthaŵi ino pamene anzathu amatisonkhezera kwambiri kuchita zosayenera, sitiyenera kulola kuti dziko litilamulire mmene tingasankhire zovala. Masitayelo a kavalidwe ndi kudzikongoletsa sali bwino zaka zino. Ngakhale kavalidwe ka anthu a m’maofesi ndi akatswiri ena sikali muyezo wodalirika wa kavalidwe koyenera Akristu. Ichi n’chifukwa china chimene tiyenera nthaŵi zonse kuona kufunika koti ‘tisafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano’ ngati tikufuna kutsatira miyezo ya Mulungu ndi ‘kukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’—Aroma 12:2; Tito 2:10.
17. (a) Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kuwaganizira tikamagula chovala kapena kusankha sitayelo yake? (b) N’chifukwa chiyani mitu ya mabanja iyenera kuonetsetsa mmene anthu a m’banja mwawo akuonekera?
17 Musanagule chovala chilichonse, n’kwanzeru kudzifunsa kuti: ‘Kodi sitayelo imeneyi yandisangalatsa chifukwa chiyani? Kodi pali dzina la msangalatsi wotchuka, amene ndimamukonda? Kodi chovalacho n’cha sitayelo ya gulu la achifwamba kapena gulu limene limalimbikitsa mzimu wodziimira ndi wopanduka?’ Tiyeneranso kuyang’anitsitsa chovalacho. Ngati lili diresi kapena siketi, kodi ndi yaitali bwanji? Aisoka bwanji? Kodi chovalacho n’choyenera ndiponso chopereka ulemu, kapena n’chothina, chodzutsa chilakolako cha kugonana, kapena chosonyeza kutayirira? Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikavala chovala chimenechi sindikhumudwitsa ena?’ (2 Akorinto 6:3, 4) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira bwino mbali imeneyi? Chifukwa chakuti Baibulo limati: “Kristunso sanadzikondweretsa yekha.” (Aroma 15:3) Mitu ya mabanja iyenera kuonetsetsa mmene anthu a m’banja mwawo akuonekera. Pofuna kulemekeza Mulungu wamkulu amene amamulambira, mitu ya mabanja isazengereze kupereka uphungu wolimba koma wachikondi pakafunika kutero.—Yakobo 3:13.
18. N’chiyani chimakuchititsani kusamala kwambiri kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwanu?
18 Uthenga umene timalengeza umachokera kwa Yehova yemwe ndi chitsanzo chachikulu cha ulemu ndi chiyero. (Yesaya 6:3) Baibulo limatilimbikitsa kumutsanzira “monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Kavalidwe kathu ndiponso kudzikongoletsa kwathu zingachititse ena kulemekeza kapena kunyoza Atate wathu wakumwamba. Mosakayika, timafuna kusangalatsa mtima wake!—Miyambo 27:11.
19. Kodi ndi phindu lotani limene limapezeka mwa kulengeza kwa ena “zazikulu za Mulungu”?
19 Kodi mukuganiza bwanji za zinthu “zazikulu za Mulungu” zimene mwaphunzira? Kunena zoona, ndife amwayi kuti taphunzira choonadi. Popeza timakhulupirira m’mwazi umene Yesu Kristu anakhetsa, timakhululukidwa machimo athu. (Machitidwe 2:38) Chifukwa cha zimenezi, timakhala aufulu kulankhula ndi Mulungu. Sitiopa imfa monga mmene amachitira anthu ena amene alibe chiyembekezo. M’malo mwake, Yesu amatitsimikizira kuti tsiku lina “onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Yehova watikomera mtima potiululira zinthu zonsezi. Ndiponso watitsanulira mzimu wake. Motero, kuyamikira mphatso zabwino zonsezi kuyenera kutilimbikitsa kulemekeza miyezo yake yapamwamba ndi kum’tamanda mwachangu, kulengeza “zazikulu za Mulungu” zimenezi kwa ena.
[Mawu a M’munsi]
a Yehova atasankha Mose ndi Aroni kuti akalankhule ndi Farao m’malo mwa anthu ake, Iye anauza Mose kuti: ‘Ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.’ (Eksodo 7:1) Aroni anali mneneri mulingaliro lakuti anali wom’lankhulira Mose osati wolosera za m’tsogolo.
b Mwa khamu lalikulu limene linapezeka pa chikumbutso chapachaka cha Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chimene chinachitika pa March 28, 2002, anthu miyandamiyanda sakutumikira Yehova pakalipano. Tikupemphera kuti mitima ya ambiri mwa anthu achidwi ameneŵa idzalimbikitsidwa posachedwa kuti adzipereke kulandira mwayi wokhala ofalitsa uthenga wabwino.
c Ngakhale kuti Paulo anali kulankhula kwa akazi achikristu, mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa amuna ndi achinyamata achikristu.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ndi “zazikulu” ziti zimene anthu anamva pa Pentekoste mu 33 C.E., ndipo anachita chiyani atamva zimenezo?
• Kodi munthu amachita chiyani kuti akhale wophunzira wa Yesu Kristu, ndipo kukhala wophunzira kumaphatikizapo chiyani?
• N’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tizisamala kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu?
• Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuziganizira pofuna kuona ngati chovala kapena sitayelo ingakhale yoyenera?
[Chithunzi patsamba 15]
Petro analengeza kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa
[Zithunzi patsamba 17]
Kodi kaonekedwe kanu kamachititsa ena kulemekeza Mulungu amene mumamulambira?
[Zithunzi patsamba 18]
Makolo achikristu ayenera kuonetsetsa mmene anthu a m’banja mwawo akuonekera