-
Mose ndi Aroni—Alengezi Olimba Mtima a Mawu a MulunguNsanja ya Olonda—1996 | January 15
-
-
Monga momwe Yehova anawalangizira, Aroni anachita chozizwitsa chimene chinasonyezadi ukulu wa Yehova pa milungu ya Igupto. Anaponya ndodo yake pansi pamaso pa Farao, ndipo pamenepo inakhala chinjoka chachikulu! Atadabwa ndi chozizwitsa chimenechi, Farao anaitana amatsenga ake.a Mothandizidwa ndi mphamvu ya ziŵanda, amuna ameneŵa anachita zofananazo ndi ndodo zawo.
-
-
Mose ndi Aroni—Alengezi Olimba Mtima a Mawu a MulunguNsanja ya Olonda—1996 | January 15
-
-
a Liwu lachihebri lotembenuzidwa “amatsenga” limasonya ku kagulu ka amatsenga amene anali kunena kuti anali ndi mphamvu kuposa ziŵanda. Anthu anali kukhulupirira kuti amuna ameneŵa ankalamula ziŵanda ndipo izo zinkamva ndi kuti ziŵanda zinalibe mphamvu pa amatsenga ameneŵa.
-