Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mu Israyeli wakale, kodi muuni wozizwitsa umene nthawi zina unali kutchedwa Shekina, umene unaonekera m’Chipinda Chopatulikitsa m’chihema kapena m’kachisi unali kutanthauza chiyani?
Yehova, Atate wachikondi ndi Mtetezi wa anthu ake, anapereka zizindikiro zosonyeza Aisrayeli kuti panthawiyo Iye anali pakati pawo. Chimodzi mwa zizindikirozo chinali mtambo wowala mochititsa chidwi umene unali kukhalapo pamalo om’lambirira.
Muuni wowala mochititsa chidwi umenewo unali kusonyeza kuti Yehova anali pakati pawo. Muuniwo unkaonekera m’Chipinda Chopatulikitsa cha m’chihema chokumanira ndiponso cha m’kachisi amene Solomo anamanga. Muuni wozizwitsawo sunatanthauze kuti Yehova weniweniyo anali pakati pawo ayi. Mulungu sangakhale m’nyumba yomangidwa ndi anthu. (2 Mbiri 6:18; Machitidwe 17:24) Kuwala kodabwitsako komwe kunaonekera m’malo opatulika a Mulungu kunapatsa chidaliro mkulu wa ansembe. Ndiponso kupyolera mwa mkulu wa ansembeyo, Aisrayeli onse anadziwa kuti anali otetezeka, komanso kuti zosowa zawo zidzasamalidwa chifukwa chakuti Yehova anali pakati pawo.
Pambuyo pa nyengo ya kulembedwa kwa Baibulo, muuni umenewu unatchedwa Shekina (shekhi·nahʹ) m’Chiaramu. Liwu limeneli limatanthauza “chimene chimakhazikika” kapena kuti “malo okhazikikapo.” Liwu limeneli silipezeka m’Baibulo, koma limapezeka m’malemba Achiaramu omasuliridwa kuchokera ku Malemba Achihebri otchedwanso kuti Tagamu.
Popereka malangizo omangira chihema chokumanira, Yehova anauza Mose kuti: “Uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m’likasamo. Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa.” (Eksodo 25:21, 22) Likasa lotchulidwalo linali bokosi lokutidwa ndi golide limene linali m’Chipinda Chopatulikitsa. Pa chivundikiro cha Likasalo panali akerubi awiri agolide.
Kodi Yehova anali kulankhula kuchokera pati? Yehova mwiniyo anapereka yankho pamene anauza Mose kuti: “Ndioneka mumtambo pachotetezerapo.” (Levitiko 16:2) Mtambo umenewu unali kulenjekeka pamwamba pa Likasa lopatulikalo pakati pa akerubi awiriwo. Baibulo silinena kuti mtambowo unali kulenjekeka pamtunda wotani pamwamba pa akerubiwo.
Mtambo wowala umenewu unaunikira m’Chipinda Chopatulikitsa. Kwenikweni, kuwala konse kwa m’chipindamo kunali kwa muuni umenewu. Muuniwo ndi umene unaunikiranso mkulu wa ansembe pamene analowa m’chipinda cham’katikati chimenecho pa Tsiku la Chitetezo. Mkulu wa ansembeyo anali kuimirira pamaso pa Yehova.
Kodi muuni wozizwitsa umenewu uli ndi tanthauzo lililonse kwa Akristu? Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya mzinda umene “sikudzakhala usiku.” Mzindawo ndi Yerusalemu Watsopano, amene ndi Akristu odzozedwa oukitsidwa kuti akalamulire limodzi ndi Yesu. Kuwala kwa mumzinda wophiphiritsa umenewu si kochokera ku dzuwa kapena ku mwezi ayi. Ulemerero wa Yehova Mulungu ndi umene mwachindunji umaunikira gululi, ngati mmene muuni wa Shekina unaunikira m’Chipinda Chopatulikitsa. Komanso Mwanawankhosayo, Yesu Kristu, ndiye “nyali” ya mzindawo. Nawonso ‘mzindawo’ umaunikira ndi kuchirikiza mwauzimu anthu owomboledwa m’mitundu yonse, kuti aone njira yoyendamo.—Chivumbulutso 21:22-25.
Chifukwa chakuti amalandira madalitso ochuluka kuchokera kumwamba, olambira Yehova amakhala otsimikiza kuti Yehova ndiye Mbusa wawo wowateteza ndi Atate wawo wachikondi.