Ufulu Waulemerero Posachedwapa kwa Ana a Mulungu
“Cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru . . . ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wachivundi, ndi kuloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—AROMA 8:20, 21.
1. Kodi nsembe ya Yesu inaphiphiritsiridwa motani pa Tsiku Lachitetezo?
YEHOVA anapereka Mwana wake wobadwa yekha monga nsembe ya dipo imene inatsegula njira ya anthu 144,000 yopezera moyo wakumwamba ndiponso inatheketsa anthu ena onse kukhala ndi ziyembekezo zosatha zapadziko lapansi. (1 Yohane 2:1, 2) Monga momwe inanenera nkhani yapita, nsembe ya Yesu yoperekedwa kaamba ka Akristu odzozedwa ndi mzimu inali kuphiphiritsiridwa pa Tsiku Lachitetezo limene linali kuchitika chaka ndi chaka pamene mkulu wa ansembe wa Israyeli anali kupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yauchimo kaamba ka iye mwini, banja lake, ndiponso fuko la Levi. Patsiku lomwelo, iye anali kupereka mbuzi kuti ikhale nsembe yauchimo kaamba ka Aisrayeli onse, monga momwe nsembe ya Kristu idzapindulitsira mtundu wonse wa anthu. Mophiphiritsira, mbuzi yamoyo inali kutenga machimo a anthu onse a chaka chapita, ndipo kenaka inali kuloŵerera m’chipululu.a—Levitiko 16:7-15, 20-22, 26.
2, 3. Kodi mawu a Paulo olembedwa pa Aroma 8:20, 21 amatanthauzanji?
2 Atamaliza kufotokoza za chiyembekezo cha anthu amene adzakhala “ana a Mulungu” akumwamba, mtumwi Paulo anati: “Chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wachivundi, ndi kuloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:14, 17, 19-21) Kodi mawu ameneŵa amatanthauzanji?
3 Pamene kholo lathu Adamu analengedwa monga munthu wangwiro, iye anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Chifukwa chakuti anachimwa, iye analoŵa mu “ukapolo wachivundi” ndipo mtundu wonse wa anthu unayambukiridwa ndi mkhalidwe umenewu. (Aroma 5:12) Mulungu analola anthu kubadwa ndi chiyembekezo choyang’anizana ndi “utsiru” chifukwa cha choloŵa chawo cha kupanda ungwiro, koma iye anapereka chiyembekezo kudzera mwa “mbewu,” Yesu Kristu. (Genesis 3:15; 22:18; Agalatiya 3:16) Chivumbulutso 21:1-4 chimafotokoza za nthaŵi imene ‘imfa, maliro, kulira, ndi choŵaŵitsa sizidzakhalaponso.’ Popeza kuti limeneli ndi lonjezo loperekedwa kwa “anthu,” likutitsimikizira kuti gulu la anthu a m’dziko lapansi latsopano okhala mu ulamuliro wa Ufumu adzaona maganizo ndi thupi zikubwezeretsedwa kukhala ndi thanzi lenileni ndiponso adzalandira moyo wosatha monga “ana a Mulungu” apadziko lapansi. Mu Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Kristu, anthu omvera ‘adzamasulidwa ku ukapolo wachivundi.’ Akadzapezeka kuti ali okhulupirikabe kwa Yehova pachiyeso chomaliza, iwo adzamasulidwa kwamuyaya ku uchimo wacholoŵa ndi imfa. (Chivumbulutso 20:7-10) Anthu okhala padziko lapansi panthaŵiyo ‘adzaloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’
Iwo Akunena Kuti “Idzani”
4. Kodi ‘kutenga madzi a moyo kwaulere’ kumatanthauzanji?
4 Ndi chiyembekezo chosangalatsa chotani nanga chimene mtundu wonse wa anthu uli nacho! Nzosadabwitsa konse kuti Akristu odzozedwa ndi mzimu amene adakali padziko lapansi akutsogolera mokangalika pa kuuza ena za chimenechi! Monga anthu amene adzakhale mbali ya “mkwatibwi” wa Mwanawankhosa waulemereroyo, Yesu Kristu, otsalira odzozedwa akuchita nawo ntchito yokwaniritsa mawu otsatirawa aulosi: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 21:2, 9; 22:1, 2, 17) Ayi ndithu, mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu sakukhudza anthu odzozedwa a 144,000 okha. Mzimu wa Mulungu ukupitirizabe kugwira ntchito mwa otsalira padziko lapansi a gulu la mkwatibwi mwa kunena kuti “Idzani.” Aliyense wakumva ndiponso amene ali ndi ludzu la chilungamo akupemphedwa kunena kuti “Idzani,” kudzipindulitsa ndi makonzedwe abwino kwambiri a Yehova kaamba ka chipulumutso.
5. Kodi Mboni za Yehova zili zosangalala kukhala ndi ayani pakati pawo?
5 Mboni za Yehova zimakhulupirira makonzedwe a Mulungu a kupereka moyo kudzera mwa Yesu Kristu. (Machitidwe 4:12) Iwo ali osangalala kukhala ndi anthu oona mtima pakati pawo amene amafuna kuphunzira za zifuno za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake. Anthu onse amene akufuna ‘kudza ndi kutenga madzi amoyo kwaulere’ mu “nthaŵi yachimaliziro” ino ali ndi ufulu wopita ku Nyumba za Ufumu za Mbonizo.—Danieli 12:4.
Masinthidwe Malinga Nkupita kwa Nthaŵi
6. Kodi mzimu wa Mulungu wagwira ntchito motani kwa atumiki a Yehova panthaŵi zosiyanasiyana?
6 Mulungu ali ndi nthaŵi yokwaniritsira zifuno zake, ndipo zimenezi zimakhudza zimene iye amachita kwa anthu. (Mlaliki 3:1; Machitidwe 1:7) Ngakhale kuti mzimu wa Mulungu unadza pa atumiki ake amene anakhalako Chikristu chisanadze, iwo sanadzozedwe monga ana ake auzimu. Komabe, kuyambira pa Yesu, nthaŵi inali itakwana yakuti Yehova ayambe kugwiritsira ntchito mzimu woyera podzoza amuna ndi akazi odzipatulira kuti adzalandire choloŵa chakumwamba. Nanga kodi zinthu zili bwanji m’tsiku lathu? Mzimu womwewo ukugwira ntchito pa “nkhosa zina” za Yesu, koma sukudzutsa mwa iwo chiyembekezo ndi chikhumbo cha moyo wakumwamba. (Yohane 10:16) Pokhala ndi chiyembekezo chopatsidwa ndi Mulungu cha kukhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso, iwo amathandiza otsalira odzozedwa mosangalala pantchito yochitira umboni m’nthaŵi ino ya kusintha kwa zinthu kuchoka m’dziko lakale kupita m’dziko latsopano la Mulungu lolungama.—2 Petro 3:5-13.
7. Kodi Ophunzira Baibulo anali kuchita ntchito iti yotuta, koma kodi iwo anadziŵa chiyani ponena za paradaiso?
7 Mulungu anayamba ‘kuloŵetsa ana ambiri mu ulemerero’ mwa kutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E., ndipo mwachionekere iye anakhazikitsa nthaŵi imene adzamaliza kusonkhanitsa “Israyeli [wauzimu] wa Mulungu” wokhala ndi chiŵerengero cha 144,000. (Ahebri 2:10; Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 7:1-8) Kuyambira mu 1879, ntchito yotuta yokhudza Akristu odzozedwa inali kutchulidwa kaŵirikaŵiri m’magazini ino. Koma Ophunzira Baibulo (amene tsopano akutchedwa Mboni za Yehova) anadziŵanso kuti Malemba amanenanso za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda yachingelezi ya m’July 1883 inati: “Pamene Yesu adzakhazikitsa ufumu wake, kuthetsa kuipa konse, ndi zina zotero, dziko lino lapansi lidzakhala paradaiso, . . . ndipo onse amene ali m’manda awo adzaloŵamo. Ndipo mwa kumvera malamulo ake iwo angadzakhale ndi moyo wosatha mmenemo.” M’kupita kwa nthaŵi, ntchito yosonkhanitsa odzozedwa inayamba kuchepa, ndipo pang’ono ndi pang’ono anthu amene analibe chiyembekezo chakumwamba anayamba kusonkhanitsidwira m’gulu la Yehova. Panthaŵiyo, Mulungu anapereka chidziŵitso chachikulu kwa atumiki ake odzozedwa, Akristu obadwanso.—Danieli 12:3; Afilipi 2:15; Chivumbulutso 14:15, 16.
8. Kodi kumvetsetsa za chiyembekezo chapadziko lapansi kunachitika motani zaka zoyambirira za m’ma 1930?
8 Anthu amene ali ndi ziyembekezo zapadziko lapansi akhala akuyanjana ndi mpingo wachikristu makamaka kuyambira mu 1931. M’chaka chimenecho, Yehova anaunikira otsalira a Akristu odzozedwa ndi mzimu kuti azindikire kuti Ezekieli chaputala 9 amanena za gulu limeneli la padziko lapansi, amene akusindikizidwa chizindikiro kuti adzapulumuke ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Mu 1932 anapeza kuti anthu onga nkhosa ameneŵa a m’tsiku lathu anachitiridwa chithunzi ndi Yonadabu (Yehonadabu), mnzake wa Yehu. (2 Mafumu 10:15-17) Mu 1934 zinadziŵika bwino kuti “Ayonadabu” amayenera “kudzipereka,” kapena kuti kudzipatulira, kwa Mulungu. Mu 1935 “unyinji,” kapena kuti “khamu lalikulu”—limene kale ankalilingalira kuti ndilo gulu lauzimu lachiŵiri limene lidzakhala “anzawo” a mkwatibwi wa Kristu kumwamba—linadziŵika kuti ndi nkhosa zina zokhala ndi ziyembekezo zapadziko lapansi. (Chivumbulutso 7:4-15; 21:2, 9; Salmo 45:14, 15) Ndipo makamaka kuyambira mu 1935, odzozedwa akhala akutsogolera pantchito yosonkhanitsa anthu oona mtima amene akufunitsitsa kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso.
9. Chitapita chaka cha 1935, nchifukwa ninji Akristu ena anasiya kudya zizindikiro za pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye?
9 Chitapita chaka cha 1935, Akristu ena amene anali kudya mkate ndi vinyo pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye anasiya kudya. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anazindikira kuti chiyembekezo chawo chinali chapadziko lapansi, osati chakumwamba. Mkazi wina amene anabatizidwa mu 1930 anati: “Ngakhale kuti [kudya] kunali kulingaliridwa kukhala chinthu choyenera kuchichita, makamaka kwa atumiki a nthaŵi zonse okangalika, sindinadzimvepo kuti ndinali ndi chiyembekezo chakumwamba. Kenaka, mu 1935, tinauzidwa momveka bwino kuti khamu lalikulu lokhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi lili kusonkhanitsidwa. Ambiri a ife tinasangalala pamene tinazindikira kuti tinali mbali ya khamu lalikulu limenelo, ndipo tinasiya kudya zizindikiro.” Ngakhale nkhani za m’zofalitsa zachikristu zinasinthanso. Pamene kuli kwakuti kwenikweni zofalitsa za m’zaka zapita zinalembedwera otsatira a Yesu odzozedwa ndi mzimu, kuyambira mu 1935 Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena a ‘kapolo wokhulupirika’ anali kupereka chakudya chauzimu chothandiza magulu onse aŵiri odzozedwa ndi anzawo okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi.—Mateyu 24:45-47.
10. Kodi ndi motani mmene wodzozedwa wosakhulupirika angaloŵedwere m’malo?
10 Tiyeni tinene kuti wodzozedwa wina wakhala wosakhulupirika. Kodi pangakhale woloŵa m’malo mwake? Paulo anasonyeza zambiri m’nkhani yake yonena za mtengo wa azitona wophiphiritsira. (Aroma 11:11-32) Ngati pangafunikire kuti wina wodzozedwa ndi mzimu aloŵedwe m’malo ndi wina, mofananamo Mulungu angapereke chiitano chakumwamba kwa munthu wina amene chikhulupiriro chake chakhala chopereka chitsanzo mwa kupereka utumiki wopatulika kwa iye kwa zaka zambiri.—Yerekezerani ndi Luka 22:28, 29; 1 Petro 1:6, 7.
Zifukwa Zambiri Zoyamikirira
11. Mosasamala kanthu zakuti kaya chiyembekezo chathu nchotani, kodi Yakobo 1:17 akutitsimikizira chiyani?
11 Mosasamala kanthu za malo kumene tingatumikirire Yehova mokhulupirika, iye adzakwaniritsa zosoŵa zathu ndi zokhumba zathu zabwino. (Salmo 145:16; Luka 1:67-74) Kaya tili ndi chiyembekezo chenicheni chakumwamba kapena chiyembekezo chathu nchapadziko lapansi, tili ndi zifukwa zabwino zambiri zoyamikirira Mulungu. Iye nthaŵi zonse amachita zinthu zokomera anthu amene amamkonda. Wophunzira Yakobo ananena kuti “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wamauniko,” Yehova Mulungu. (Yakobo 1:17) Tiyeni tilingalirepo za zingapo mwa mphatso ndi madalitso ameneŵa.
12. Nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova wapereka chiyembekezo chosangalatsa kwa aliyense wa atumiki ake okhulupirika?
12 Yehova wapereka chiyembekezo chosangalatsa kwambiri kwa aliyense wa atumiki ake okhulupirika. Iye waitanira ena ku moyo wakumwamba. Kwa mboni zimene zinakhalako Chikristu chisanadze, Yehova anapereka chiyembekezo chabwino kwambiri cha kuukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Mwachitsanzo, Abrahamu anali kukhulupirira chiukiriro ndipo anayembekezera “mudzi wokhala nawo maziko”—Ufumu wakumwamba umene udzampangitsa kuti aukitsidwire ku moyo wapadziko lapansi. (Ahebri 11:10, 17-19) Mofananamo, m’nthaŵi ino yamapeto, Mulungu akupereka chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso kwa anthu mamiliyoni ambiri. (Luka 23:43; Yohane 17:3) Zoonadi, aliyense amene Yehova wampatsa chiyembekezo chachikulu chimenecho ayenera kuchiyamikira kwambiri.
13. Kodi mzimu woyera wa Mulungu wagwira ntchito motani kwa anthu ake?
13 Yehova amapereka mzimu wake woyera monga mphatso kwa anthu ake. Akristu amene anapatsidwa chiyembekezo chakumwamba ali odzozedwa ndi mzimu woyera. (1 Yohane 2:20; 5:1-4, 18) Komabe, atumiki a Mulungu amene ali ndi ziyembekezo zapadziko lapansi amathandizidwa ndi kutsogozedwa ndi mzimuwo. Munthu amene anali pakati pa ameneŵa ndiye Mose, amene anali ndi mzimu wa Yehova, monganso amuna 70 amene anasankhidwa kuti amthandize. (Numeri 11:24, 25) Mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera, Bezaleli anatumikira monga munthu waluso mogwirizana ndi ntchito yomanga chihema cha Israyeli. (Eksodo 31:1-11) Mzimu wa Mulungu unadza pa Gideoni, Yefita, Samsoni, Davide, Eliya, Elisa, ndi ena. Ngakhale kuti anthu ameneŵa a m’nthaŵi zakale sadzaloŵetsedwa konse mu ulemerero wakumwamba, iwo anatsogozedwa ndi kuthandizidwa ndi mzimu woyera, monga momwe zikuchitikira kwa nkhosa zina za Yesu lerolino. Choncho, kukhala ndi mzimu wa Mulungu kwenikweni sikutanthauza kuti tili ndi maitanidwe akumwamba. Komabe, mzimu wa Yehova umatitsogoza, umatithandiza pantchito yolalikira ndi kuchita ntchito zina zopatsidwa ndi Mulungu, umatipatsa ukulu woposa wamphamvu, ndipo umabala mwa ife zipatso zake za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Yohane 16:13; Machitidwe 1:8; 2 Akorinto 4:7-10; Agalatiya 5:22, 23) Kodi sitingayamikire mphatso yosangalatsa yochokera kwa Mulungu imeneyi?
14. Kodi timapindula motani ndi mphatso za Mulungu za chidziŵitso ndi nzeru?
14 Chidziŵitso ndi nzeru zili mphatso zochokera kwa Mulungu zimene tiyenera kuyamikira, kaya chiyembekezo chathu chikhale chakumwamba kapena chapadziko lapansi. Chidziŵitso cholongosoka cha Yehova chimatithandiza ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri’ ndiponso ‘kuyenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo.’ (Afilipi 1:9-11, NW; Akolose 1:9, 10) Nzeru yaumulungu imagwira ntchito monga chotitetezera ndi chotitsogolera pamoyo wathu. (Miyambo 4:5-7; Mlaliki 7:12) Chidziŵitso choona ndi nzeru zimachokera m’Mawu a Mulungu, ndipo odzozedwa ochepa amene adakali padziko lapansi kwenikweni amakopeka ndi zimene mawuwo amanena mogwirizana ndi chiyembekezo chawo chakumwamba. Komabe, kukonda Mawu a Mulungu ndi kuwamvetsetsa bwino sizisonyeza kuti ndiyo njira imene Mulungu amatiuzira kuti tinaitanidwira ku moyo wakumwamba. Ndipotu amuna ena monga Mose ndi Danieli analemba mabuku ena a m’Baibulo, koma iwo adzaukitsidwira ku moyo wapadziko lapansi. Kaya chiyembekezo chathu chikhale chakumwamba kapena chapadziko lapansi, tonsefe timalandira chakudya chauzimu kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wovomerezedwa ndi Yehova. (Mateyu 24:45-47) Tonsefe tili oyamikira chotani nanga pokhala ndi chidziŵitso chimenechi!
15. Kodi imodzi mwa mphatso za Mulungu zazikulu kwambiri nchiyani, ndipo kodi inu mumaiona motani?
15 Imodzi mwa mphatso zazikulu kwambiri za Mulungu ndiyo makonzedwe achikondi a nsembe ya dipo ya Yesu, imene imatipindulitsa kaya tili ndi chiyembekezo chakumwamba kapena chiyembekezo chapadziko lapansi. Mulungu anakonda dziko la anthu “kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ndipo chikondi cha Yesu chinamsonkhezera “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Monga momwe anafotokozera mtumwi Yohane, Yesu Kristu “ndiye chiombolo cha machimo athu [a odzozedwa]; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Choncho, tonsefe tiyenera kuwayamikira kwambiri makonzedwe achikondi ameneŵa akuti tipulumuke ndi kukhala ndi moyo kosatha.b
Kodi Mudzapezekapo?
16. Kodi ndi chochitika chosaiŵalika chiti chimene chidzakumbukiridwa pa April 11, 1998 dzuŵa litaloŵa, ndipo kodi ndani amene ayenera kudzapezekapo?
16 Chiyamikiro chathu kaamba ka nsembe ya dipo yoperekedwa ndi Mulungu mwa Mwana wake chiyenera kutisonkhezera kuti tidzapezeke pa Nyumba za Ufumu kapena pamalo ena alionse pamene Mboni za Yehova zidzasonkhana dzuŵa litaloŵa pa April 11, 1998, pokumbukira imfa ya Kristu. Pamene anayambitsa chochitikachi pamodzi ndi atumwi ake okhulupirika usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi, Yesu anati: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19, 20; Mateyu 26:26-30) Odzozedwa ochepa amene adakali padziko lapansi ndiwo amene adzadya mkate wopanda chotupitsa, woimira thupi laumunthu la Yesu losachimwa, ndi kumwa vinyo wofiira wosaledzeretsa, woimira mwazi wake wokhetsedwa pansembeyo. Akristu odzozedwa ndi mzimu okha ndiwo amene ayenera kudya ndi kumwa chifukwa chakuti ndiwo amene ali m’pangano latsopano ndi pangano la Ufumu ndiponso ali ndi umboni wosatsutsika wakuti ali ndi mzimu woyera wa Mulungu kotero kuti chiyembekezo chawo nchakumwamba. Anthu ena mamiliyoni ambiri adzapezekapo monga oonerera aulemu amene amayamikira chikondi chimene chinasonyezedwa ndi Mulungu ndiponso Kristu mogwirizana ndi nsembe ya Yesu imene imapangitsa kuti pakhale chiyembekezo cha moyo wosatha.—Aroma 6:23.
17. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ponena za kudzozedwa ndi mzimu?
17 Zikhulupiriro zakale zachipembedzo, kukhudzidwa mtima kwambiri chifukwa cha imfa ya wokondedwa, mavuto a pamoyo wapansi pano, kapena malingaliro akuti alandira madalitso ena ake ochokera kwa Yehova zingapangitse anthu ena kuganiza molakwa kuti iwo ngoitanidwira ku moyo wakumwamba. Koma tonsefe tiyenera kukumbukira kuti Malemba satilamulira kuti tizidya zizindikiro za pa Chikumbutso posonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka nsembe ya dipo ya Kristu. Ndiponso, kudzozedwa ndi mzimu ‘sikufuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu,’ Amene anadzoza Yesu monga Mwana wake wauzimu ndi kuloŵetsa anthu ena 144,000 okha mu ulemerero.—Aroma 9:16; Yesaya 64:8.
18. Kwa ambiri amene akutumikira Yehova lerolino, kodi ndi madalitso otani amene ali mtsogolo mwawo?
18 Anthu miyandamiyanda amene akutumikira Yehova m’masiku ano otsiriza ali ndi chiyembekezo chopatsidwa ndi Mulungu cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (2 Timoteo 3:1-5) Posachedwapa, iwo adzasangalala ndi paradaiso wokongola kwambiri ameneyu. Panthaŵiyo akalonga adzayang’anira zinthu zonse zapadziko lapansi pansi pa ulamuliro wakumwamba. (Salmo 45:16) Kudzakhala mtendere popeza kuti anthu amene adzakhala padziko lapansi panthaŵiyo adzatsatira malamulo a Mulungu ndi kuphunzira zambiri ponena za njira za Yehova. (Yesaya 9:6, 7; Chivumbulutso 20:12) Padzakhala ntchito yambiri yochita, kumanga nyumba ndi kugonjetsa dziko lapansi. (Yesaya 65:17-25) Ndipo tangolingalirani za kukumananso kwachimwemwe kwa mabanja pamene akufa adzakhalanso ndi moyo! (Yohane 5:28, 29) Chikadzatha chiyeso chomaliza, kuipa konse kudzachotsedwa. (Chivumbulutso 20:7-10) Zikadzachitika zimenezi, dziko lapansi lidzadzazidwa kosatha ndi anthu angwiro amene ‘adzamasulidwa ku ukapolo wachivundi ndi kuloŵetsedwa mu ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 225-6.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ‘kutenga madzi a moyo kwaulere’ kumatanthauzanji?
◻ Kaya chiyembekezo chathu chikhale chakumwamba kapena chapadziko lapansi, kodi tiyenera kuyamika Mulungu pazifukwa ziti?
◻ Kodi ndi chochitika chiti cha chaka ndi chaka chimene tonsefe tiyenera kupezekapo?
◻ Kodi anthu ambiri a Yehova akuyembekezanji mtsogolomu?
[Chithunzi patsamba 18]
Anthu mamiliyoni ambiri ayamba ‘kutenga madzi a moyo kwaulere.’ Kodi muli pakati pawo?