Kodi Ndani Angakhale Bwenzi la Mulungu?
INU mungakhale bwenzi la Mulungu. Zaka 4,000 zapitazo, mwamunayo Abrahamu anakhulupirira Yehova Mulungu. Chimenechi chinaŵerengeredwa kwa iye monga chilungamo, ndipo kholo limenelo linadzatchedwa “bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23) Chotero ngati inu muli ndi chikhulupiriro mwa Yehova, mungakhalenso bwenzi la Mulungu.
Mosakaikira mabwenzi amaitaniridwa ku chakudya monga alendo. M’chenicheni, mbali ya Salmo lodziŵika bwino lomwe la 23 limalongosola Mulungu monga wolandira alendo wokoma mtima. Linati: “[Yehova] mundiyalikira gome pamaso panga m’kuwona kwa adani anga. . . . Chikho changa chisefuka.”—Salmo 23:5.
Pa nthaŵi inanso, wamasalmo mmodzimodziyo—Mfumu Davide wa Israyeli wakale—anafunsa kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?” (Salmo 15:1) Mophiphiritsira, zimenezi zimatanthauza kuyandikira Yehova m’pemphero lovomerezeka ndi kumlambira. Ndimwaŵi waukulu chotani nanga! Kodi kungatheke motani kwa anthu opanda kuyeneretsedwa kukhala mabwenzi ndi alendo a Mulungu?
Salmo la 15 limayankha funso limeneli. Limatchula ziyeneretso zotsimikizirika khumi za okhumba kukhala mabwenzi ndi alendo a Mulungu. Tiyeni tilingalire ziyeneretso zimenezi chimodzi pa nthaŵi imodzi, kuyamba ndi vesi 2.
“Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo”
Mbadwa za Abrahamu zinachuluka kwambiri chifukwa chakuti Abrahamu anali wamakhalidwe osalakwika poyenda pamaso pa Yehova. (Genesis 17:1, 2) “Kuyenda” nthaŵi zina kumatanthauza kulondola njira yakutiyakuti m’moyo. (Salmo 1:1; 3 Yohane 3, 4) Kwa mabwenzi a Mulungu ndi alendo, sikuli kokwanira kukhala mbali yachipembedzo, kukondwera ndi zimango zake zokometseredwa, ndi kugawanamo m’mapwando ozoloŵereka. Si onse onena “Ambuye, Ambuye” kapena kulengeza kuti amadziŵa Mulungu adzalandira madalitso a Ufumu wake. (Mateyu 7:21-23; Tito 1:16) Mabwenzi a Yehova ‘amayenda mosalakwa’ pamaso pake ndipo ‘amachita chilungamo’ mogwirizana ndi miyezo yake.—Mika 6:8.
Zimenezi sizimasiya mpata wa kusawona mtima kwa mtundu uliwonse, chisembwere chakugonana, ndi chinyengo. Mulungu mwiniyo amatiuza chifukwa chake, akumati: “Mudzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:16) Kodi chipembedzo chanu chimamamatira ku miyezo yapamwamba ya Mulungu, ngakhale kuchotsa okana kugwirizana ndi ziyeneretso zake? Kodi mumaumirira pa mkhalidwe wolungama kaamba ka inumwini ndi banja lanu? Ngati ziri choncho, mudzayenerera chiyeneretso chotsatira cha mabwenzi ndi alendo a Mulungu.
“Nanena zowonadi mumtima mwake”
Ngati tifuna ubwenzi wa Mulungu, sitinganame kapena kutembenukira ku kulankhula mawu osyasyalika ndi a mitima iŵiri. (Salmo 12:2) Tiyenera ‘kulankhula chowonadi mumtima mwathu,’ osangokhala nacho pa milomo yathu. Inde, tifunikira kukhala owona mtima chamkati ndipo tiyenera kupereka umboni wa “chikhulupiriro chosanyenga.” (1 Timoteo 1:5) Anthu ena amanama kapena kulankhula chowona chosakwanira kupeŵa kuchita manyazi. Ena amanyenga pamayeso a kusukulu kapena kunyenga pa zimene angalipirire misonkho. Machitachita otero amasonyeza kusoŵeka kwa chikondi kaamba ka chimene chiri chowona. Komatu chowonadi ndi ntchito zolungama zimachokera m’mitima yeniyeniyo ya mabwenzi a Mulungu. (Mateyu 15:18-20) Iwo sali aphyuta kapena achinyengo.—Miyambo 3:32; 6:16-19.
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo munavala watsopano.” (Akolose 3:9, 10) Inde, awo olankhuladi chowonadi mumtima mwawo amadziveka iwo eni ndi “munthu watsopano.” Kodi ndinu wowona mtima kotheratu kwa inu mwini ndi kwa ena, kulankhula chowonadi mumtima mwanu? Ngati mukutero, zimenezo ziyenera kuyambukira zimene mumalankhula ponena za ena.
“Amene sasinjirira ndi lilime lake”
Kufikira chiyeneretso chimenechi cha alendo a Mulungu, sitiyenera konse kulankhula mwakaduka ponena za ena. (Salmo 15:3) Mneni Wachihebri womasulidwa ‘kusinjirira’ watengedwa kuchokera ku liwu lotanthauza “phazi” ndipo limatanthauza “kuponda” ndiko kuti “kuderukaderuka.” Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.” (Levitiko 19:16; 1 Timoteo 5:13) Ngati tisinjirira munthu wina, kumuipitsira mbiri yake yabwino, sitingakhale mabwenzi a Mulungu.
Davide analengeza kuti: “Wakuneneza mnzake mtseri, [ndidzamkhalitsa chete, NW.]” (Salmo 101:5) Ifenso tingakhalitse chete oneneza ngati tikana kumvetsera kwa iwo. Ndipo mchitidwe wabwino ndiwo kusanena zirizonse ponena za munthu amene palibe zimene sitikananena ngati iye analipo. Kuli bwino ngati tilamulira lilime lathu mwanjirayo. Komabe, kuli kofunika chotani nanga kulamulira zochita zathunso!
“Sachitira mnzake choipa”
Panopa oyenerera ndiwo mawu a Yesu akuti: “Zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Kuti tikhale ndi chiyanjo cha Mulungu, tiyenera kupeŵa kuchita choipa. Wamasalmo ananena kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; Awalanditsa m’manja mwa oipa.” (Salmo 97:10) Chotero ngati tifuna ubwenzi ndi Mulungu ndi thandizo, tifunikira kuvomereza miyezo yake.
Kukaniza chimene chiri choipa kumaphatikizapo kusalakwira aliyense pochita malonda kapena m’njira zina. Sitiyenera kuchita chirichonse kupweteka mnzathu, mwa mawu ndi kachitidwe, koma tiyenera kumchitira zinthu zabwino. Zimenezi zingakhudze mbali iriyonse ya moyo. Mwachitsanzo, pamene tiyendetsa galimoto, mwaulemu tingalole oyenda pansi kudutsa. Tingathandize okalamba, kulimbikitsa ochita tondovi, kutonthoza achisoni. Pa mfundo ino, Yehova amakhazikitsa chitsanzo chabwino kwambiri. Monga momwe ananenera Yesu kuti, Mulungu “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, navumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:43-48) Chogwirizana ndi kuchitira ena zabwino ndicho kupeŵa chimene wamasalmo akutchula motsatira.
“Ndipo satola mseche pa mnansi wake”
Tonsefe timalakwa, ndipo timakhala oyamikira chotani nanga pamene mabwenziwo asankha kunyalanyaza zolakwa zazing’ono zimenezi! Tikanamva chisoni ngati bwenzi lathu la ponda apo mpondepo linavumbula zofooka zathu zazing’ono koma zochititsa manyazi kwa ena. Anthu ena amachita zimenezi kuti anthu asawone zolakwa zawo kapena kudzipangitsa iwo eni kuwonekera kukhala oposa ena. Koma machitidwe amenewo samayenerera awo okhumba kukhala mabwenzi a Mulungu.
“Wobisa cholakwa afunitsa chikondano; koma wobwerezabwereza mawu afetsa ubwenzi,” imatero Miyambo 17:9. Ndithudi, sitiyenera kuyesa kubisa machimo aakulu. (Levitiko 5:1; Miyambo 28:13) Koma ngati tifuna kukhala mabwenzi a Mulungu, ‘sitidzamvetsera,’ kapena kuvomereza, nkhani zoneneza mabwenzi abwino kukhala zowona. (1 Timoteo 5:19) Mabwenzi a Yehova amalankhula zabwino ponena za atumiki a Mulungu m’malo mofalitsa mphekesera ponena za iwo, kuwonjezera zimene iwo akupirira nazo kale kuchokera ku zitonzo zochitidwa ndi anthu osapembedza. Mabwenzi ndi alendo a Mulungu amachenjeranso ndi mabwenzi awo, popeza Davide akuwonjezera mu vesi 4 kuti:
“M’maso mwake munthu wowonongeka anyozeka”
Pofunafuna mapindu adyera, anthu ena amachita ubwenzi ndi anthu okhupuka kapena otchuka ngakhale ngati ali a makhalidwe oipa. (Yerekezani ndi Yuda 16.) Komatu ife sitingakhale mabwenzi a Yehova ngati tiyanjana ndi oipa. Tiyenera kuda choipa kwambiri kotero kuti sitimafuna kuyanjana ndi anthu ozoloŵera kuchichita. (Aroma 12:9) Mfumu ya Israyeli Yoramu inali yoipa kwambiri kotero kuti mneneri Elisa anaiwuza kuti: “Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang’anitsani, kapena kukuwonani.” (2 Mafumu 3:14) Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera kulabadira chenjezo la mtumwi Paulo lakuti: “Mayanjano oipa aipsya makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.
Pamenepa, ngati tilemekeza ubwenzi wathu ndi Yehova, tidzakana kuyanjana ndi ochita zoipa. Tidzachita nawo kokha zinthu zofunikira. Mabwenzi athu adzasankhidwa kaamba ka unansi wawo wabwino ndi Mulungu, osati kaamba ka mkhalidwe wawo m’dziko. Tidzasankha mabwenzi mwanzeru ngati tiri ndi mantha aulemu kwa Mulungu. Pa mfundoyi, tamverani chiyeneretso chachisanu ndi chiŵiri chofunikira kufikiridwa ndi alendo a Yehova.
“Koma awachitira ulemu akuwopa Yehova”
Kuti tikhale mabwenzi ndi alendo a Mulungu, tiyenera kumuwopa. Ikutero Miyambo 1:7: “Kuwopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziŵa.” Kodi “kuwopa Yehova” nchiyani? Iko kuli mantha aulemu kaamba ka Mulungu ndi chinthentha choyenera cha kusamkondweretsa. Zimenezi zimatulukira m’chidziŵitso chowona, chilango chopulumutsa moyo, ndi nzeru yakumwamba imene iri chitsogozo chotsimikizirika.
Owopa Yehova amamamatira ku miyezo yake yolungama ngakhale ngati kutero kungachititse kusekedwa. Mwachitsanzo, ambiri amaseka pamene owopa Mulungu amagwira ntchito mwamphamvu, ali owona mtima pa ntchito, kapena kufuna kuthandiza ena mwauzimu. Koma kodi ndimotani mmene munthu waumulungu amawonera anthu olungama oterowo? ‘Iye amalemekeza akuwopa Yehova,’ nawalemekeza kwambiri, ngakhale ngati zimenezi zingatanthauze kupirira mtonzo. Kodi inu muli ndi ulemu woterowo kwa owopa Mulungu? Potchula chiyeneretso china chopezera chiyanjo cha Mulungu, wamasalmo akuwonjezera kuti:
“Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ayi”
Panopa lamulo la makhalidwe abwino ndilo kukwaniritsa malonjezo athu, monga momwe Mulungu amachitira. (1 Mafumu 8:56; 2 Akorinto 1:20) Ngakhale ngati pambuyo pake tipeza kuti kuchita zimene tinalonjeza kuli kovuta kwambiri, sitiyenera kusintha maganizo athu ndi kukana lonjezo lathu. Panopa Malemba a Septuagint Yachigriki, Peshitta Yachisiriya, ndi Vulgate Yachilatin amanena kuti, “kulumbira kwa mnansi wake.” Ngati tilumbira kuchita chinachake kapena kupanga chiwindo choyenerera, tiyenera kuchichita. (Mlaliki 5:4) Ndithudi, ngati tamva kuti chimene tinalonjeza sichiri chogwirizana ndi malemba, sitiyenera kuchichita.
Yoswa sanaswe pangano ndi Agibeoni ngakhale kuti pambuyo pake anadziŵa kuti iwo anamnyenga popangana. (Yoswa 9:16-19) Chotero tiyenera kukhala amuna, akazi, ndi ana osunga mawu athu. Tisalonjeze anthu ena ndiyeno kuwagwiritsa mwala pamene mwaŵi wokondweretsa kwambiri utitsegukira. Yesu ananena kuti: “Koma manenedwe anu akhale, Inde, Inde; Ayi, Ayi.” (Mateyu 5:37) Makamaka odzipereka kwa Yehova ayenera kukhala otsimikiza kusunga lonjezo lawo la kumtumikira kosatha monga Mboni zake. Kuwonjezera pa kusunga malonjezo, tiyenera kukhala achifundo m’nkhani za ndalama, monga momwe Davide akusonyezera mu Salmo la 15, vesi 5.
“Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu”
Ndalama zokongoletsedwa kaamba ka zifuno za bizinesi moyenerera zingabwezeredwe ndi chiwongola dzanja. Koma panopa Davide anatanthauza ‘kukongoletsa ndalama’ kwa aumphaŵi. Lamulo la Mose linanena molunjika kuti: “Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamŵerengere phindu.” (Eksodo 22:25; Levitiko 25:35, 36) Pamene Nehemiya anapeza osauka ovutika monga minkhole ya okongoletsa mofuna phindu lalikulu, anathetsa kulimana pamsana kotero.—Nehemiya 5:1-13.
Pa liwu lakuti “phindu,” Davide anagwiritsira ntchito mawu Achihebri otengedwa ku mawu ena otanthauza “kuluma.” Zimenezi zimapereka lingaliro lakuti okongoletsa mofuna phindu lalikulu aumbombowo anali kudyera osaukawo zochepera zimene anali nazo. Mwachiwonekere, kuli bwino kwambiri kuthandiza okanthidwa ndi umphaŵi popanda kuyembekezera chobwezera chirichonse. Yesu ananena zimenezo mwa kunena kuti: “Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena chamadzulo, . . . uitane aumphaŵi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.” (Luka 14:12-14) Munthu wokhumba kukhala bwenzi ndi mlendo wa Mulungu sakalima pamsana konse umphaŵi wa mnansi wake kapena kuchita chimene wamasalmo akupitirizabe kutchula.
“Ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa”
Chiphuphu chiri ndi chisonkhezero choipitsa. Aisrayeli analamulidwa kuti: “Musamasamalira . . . kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, nichiipsa mawu a olungama.” (Deuteronomo 16:19) Iridi mphulupulu kutenga chiphuphu kuvulaza “wosachimwa,” mwinamwake mwa kusintha umboni wa m’khoti. Ngwonyansa chotani nanga mmene Yudase Iskariyote analiri kulandira chiphuphu kupereka Yesu wosalakwa!—Mateyu 26:14-16.
Tingadzilingalire kukhala osalakwa m’mbali imeneyi. Koma kodi tinayamba tayesedwapo kulipira ndalama kuti tionjoke mu mkhalidwe wochititsa manyazi? Mneneri Samueli sanalandire konse “chokometsera mlandu,” kapena chiphuphu. (1 Samueli 12:3, 4) Tonsefe tiyenera kudzisungira mwanjira imeneyo ngati titi tikhale mabwenzi ndi alendo a Mulungu.
“Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka ku nthaŵi zonse”
Pambuyo pa kulongosola kwake mfundo khumi za munthu wolungama, Salmo la 15 limamaliza ndi mawu apamwambawo. Iwo angatichititsedi ife kupenda chipembedzo chathu. Ngati chiri chipembedzo chowona, chiyenera kutiphunzitsa (1) kuyenda mosalakwa ndi kuchita chilungamo, (2) kulankhula chowonadi mumtimamo, (3) kupeŵa kusinjirira ena, ndi (4) kuleka kuchita choipa chirichonse. Chipembedzo chovomerezeka kwa Mulungu (5) chidzatitetezera kutonza anzathu olungama olongosoka ndipo (6) chidzatipangitsa kupeŵa kuyanjana ndi anthu a mayendedwe oluluzika. Chipembedzo chowona chidzatisonkhezera (7) kulemekeza owopa Yehova, (8) kuchita zimene talonjeza ngati ziri zoyenerera, (9) kupatsa osauka mosalipiritsa chiwongola dzanja, ndi (10) kusalandira konse chiphuphu motsutsana ndi munthu wosalakwa.
Davide sakunena kuti aliyense woŵerenga, wakumva, wakulankhula, kapena ngakhale kukhulupirira zinthu zimenezi “sadzagwedezeka ku nthaŵi zonse.” Zimenezi zidzakhala kokha zochitikira munthu “wakuchita izi.” Chikhulupiriro chopanda ntchito zochichirikiza chiri chakufa ndipo sichimabweretsa chiyanjo cha Mulungu. (Yakobo 2:26) Ochita zinthu zabwino zotchulidwa mu Salmo la 15 sadzagwedezeka, popeza Yehova adzawatetezera ndi kuwachirikiza.—Salmo 55:22.
Ndithudi, pali zofunikira zambiri pa kulambira koyera koposa mfundo khumi zotchulidwa mu Salmo 15. Pambuyo pake ophunzira a Yesu anaphunzira zinthu zina ponena za kulambira Mulungu “mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23, 24) Chotero inunso mungatero, popeza kuti anthu ochita zinthu zimenezi alipo lerolino. Kuyanjana mokhazikika ndi Mboni za Yehova zimenezi ndi kuphunzira Baibulo kudzapanga chiyembekezo cha moyo m’paradaiso wa pa dziko lapansi kumene mungakhale mlendo ndi bwenzi la Mulungu kosatha.