Khalani ‘m’Mudzi Wopulumukirako’ Nimukhale ndi Moyo!
“[Ayenera kukhala, NW] m’mudzi wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe.”—NUMERI 35:28.
1. Kodi Wolipsa mwazi ndani, ndipo adzachita chiyani posachedwapa?
YESU KRISTU, Wolipsa mwazi m’malo mwa Yehova, ali pafupi kuukira. Wolipsa ameneyu pamodzi ndi makamu ake a angelo, posachedwapa adzakantha onse amene mosalapa ali ndi liwongo la mwazi. Inde, Yesu adzakhala Wakupha wa Mulungu mkati mwa “chisautso chachikulu” chimene chikuyandikira mofulumira. (Mateyu 24:21, 22, NW; Yesaya 26:21) Nthaŵiyo anthu sadzazemba liwongo lawo la mwazi.
2. Kodi malo enieni okha opulumukirako ndi ati, ndipo ndi mafunso otani amene afunikira mayankho?
2 Njira yachisungiko ndiyo kuloŵa pamsewu wa ku mudzi wophiphiritsira wopulumukirako ndi kuthaŵa kupulumutsa moyo wako! Ataloŵa m’mudzi, wothaŵayo afunika kukhala mmenemo, pakuti ndiwo malo enieni okha opulumukirako. Koma mungadabwe kuti, ‘Popeza ambiri a ife sitinaphepo munthu, kodi tilidi ndi liwongo la mwazi? Kodi nchifukwa ninji Yesu ali Wolipsa mwazi? Kodi mudzi wamakono wopulumukirako nchiyani? Kodi aliyense angachokemo nakhaladi wotetezereka?’
Kodi Tilidi ndi Liwongo la Mwazi?
3. Kodi ndi mbali iti ya Chilamulo cha Mose imene idzatithandiza kuona kuti anthu mamiliyoni zikwi zambiri ali ndi liwongo la mwazi?
3 Mbali ya Chilamulo cha Mose idzatithandiza kuona kuti mamiliyoni zikwi zambiri pa dziko lapansi ali ndi liwongo la mwazi. Mulungu anaika pa Aisrayeli mlandu wokhudza onse wa kukhetsa mwazi. Ngati wina anapeza munthu wina ataphedwa ndipo amene anamupha sanadziŵike, oweruza anali kuyesa mtunda kufikira kumidzi yozinga malowo kuti adziŵe mudzi umene unali pafupi kwambiri. Kuti achotse liwongolo, akulu a mudzi umene unaganiziridwa kukhala ndi liwongo la mwazi anali kutenga ng’ombe yamsoti yosagwirapo ntchito naidula khosi m’chigwa chosalima. Anachita zimenezi pamaso pa ansembe Achilevi ‘pakuti Yehova anasankha iwo akonze kupanda konse.’ Akulu a mudziwo anasamba manja awo pamsotiwo nati: “Manja athu sanakhetsa mwazi uwu, ndi maso athu sanauona. Yehova, [musauŵerengere kwa anthu anu Israyeli, NW], amene munawawombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israyeli.” (Deuteronomo 21:1-9) Yehova Mulungu sanafune kuti dziko la Israyeli liipitsidwe ndi mwazi ngakhale anthu ake onse kukhala ndi liwongo la mwazi lokhudza onse.
4. Kodi Babulo Wamkulu ali ndi mbiri yotani ya liwongo la mwazi?
4 Inde, pali chinthu chimene tingatche liwongo la mwazi lokhudza onse. Talingalirani liwongo lalikulu la mwazi limene Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ali nalo. Aha, iye ngwoledzera ndi mwazi wa atumiki a Yehova! (Chivumbulutso 17:5, 6; 18:24) Zipembedzo za Dziko Lachikristu zimati zimatsatira Kalonga wa Mtendere, koma nkhondo, zilango zankhanza zachipembedzo, ndi nkhondo za mtanda zakupha zamchititsa kukhala ndi liwongo la mwazi kwa Mulungu. (Yesaya 9:6; Yeremiya 2:34) Kunena zoona, ayenera kukhala ndi liwongo lalikulu kaamba ka anthu mamiliyoni ambiri omwe anafa m’nkhondo ziŵiri zadziko m’zaka za zana lino. Chotero, otsatira chipembedzo chonyenga limodzi ndi ochirikiza nkhondo za anthu ndi otengamo mbali ali ndi liwongo la mwazi kwa Mulungu.
5. Kodi anthu ena akhala motani ngati wakupha munthu mwangozi mu Israyeli?
5 Anthu ena apha dala anzawo kapena chifukwa chosasamala. Ena atenga mbali m’magulu opha anzawo, mwinamwake mosonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo omwe amati kuchita zimenezo ndi chifuniro cha Mulungu. Ndipo ena azunza ndi kupha atumiki a Mulungu. Komabe, ngakhale kuti sitinachite zimenezo, tili ndi mlandu wokhudza tonsefe kaamba ka kutayika kwa miyoyo ya anthu chifukwa chakuti sitinadziŵe malamulo a Mulungu ndi chifuniro chake. Tili ngati munthu wopha mnzake mwangozi ‘amene anapha mnzake osati mwadala.’ (Deuteronomo 19:4) Anthu otero afunikira kuchonderera chifundo cha Mulungu ndipo ayenera kuthaŵira m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo. Ngati satero, tsoka la Wolipsa mwazi lidzawagwera.
Malo a Yesu Ofunika Kwambiri
6. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yesu ndiye wachibale wa anthu wapafupi kwambiri?
6 Mu Israyeli wolipsa mwazi anali wachibale wapafupi kwambiri wa wophedwayo. Kuti alipsire onse ophedwa pa dziko lapansi ndipo makamaka atumiki a Yehova ophedwa, Wolipsa mwazi wamakono ayenera kukhala wachibale wa anthu onse. Amene wakwaniritsa malowo ndi Yesu Kristu. Iye anabadwa ali munthu wangwiro. Yesu anapereka moyo wake wosachimwa mu imfa kukhala nsembe ya dipo, ndipo ataukitsidwa kupita kumwamba, anapereka mtengo wake kwa Mulungu m’malo mwa mbadwa za Adamu zomafa. Motero Kristu anakhala Momboli wa anthu, wachibale wathu wapafupi kwambiri—woyenerera monga Wolipsa mwazi. (Aroma 5:12; 6:23; Ahebri 10:12) Yesu amatchedwa mbale wa otsatira ake odzozedwa oyenda m’mapazi ake. (Mateyu 25:40, 45; Ahebri 2:11-17) Pokhala Mfumu yakumwamba iye amakhala “Atate Wosatha” kwa aja amene adzapindula ndi nsembe yake monga nzika zake za pa dziko lapansi. Ameneŵa adzakhala ndi moyo kosatha. (Yesaya 9:6, 7) Chotero Yehova moyenerera waika Wachibale wa anthu ameneyu kukhala Wolipsa mwazi.
7. Pokhala Mkulu wa Ansembe wamkulu, kodi Yesu amawachitira chiyani anthu?
7 Yesu alinso Mkulu wa Ansembe wosachimwa, woyesedwa, ndi wachifundo. (Ahebri 4:15) Pamalo amenewo iye amagwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yake yotetezera machimo kwa anthu. Midzi yopulumukirako inakhazikitsidwa kaamba ka “ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pawo.” (Numeri 35:15) Chotero Mkulu wa Ansembe wamkulu choyamba anagwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yake kwa otsatira ake odzozedwa, “ana a Israyeli.” Tsopano akuugwiritsira ntchito kwa ‘alendo’ ndi ‘okhala pakati pawo’ m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo. “Nkhosa zina” zimenezi za Ambuye Yesu Kristu zikuyembekezera kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi.—Yohane 10:16; Salmo 37:29, 34.
Mudzi Wopulumukirako Wamakono
8. Kodi mudzi wophiphiritsira wopulumukirako nchiyani?
8 Kodi mudzi wophiphiritsira wopulumukirako nchiyani? Suuli malo onga Hebroni, wina wa midzi isanu ndi umodzi ya Alevi yopulumukirako ndi kwawo kwa mkulu wa ansembe wa Israyeli. Mudzi wopulumukirako wamakono ndiwo makonzedwe a Mulungu otichinjiriza ku imfa chifukwa cha kuswa kwathu lamulo lake la kupatulika kwa mwazi. (Genesis 9:6) Aliyense wakuswa lamulolo, kaya mwadala kapena mwangozi, ayenera kupempha Mulungu kumkhululukira ndi kumfafanizira tchimo lake mwa chikhulupiriro m’mwazi wa Mkulu wa Ansembe, Yesu Kristu. Akristu odzozedwa oyembekezera kupita kumwamba ndi “khamu lalikulu” loyembekezera kukhala pa dziko lapansi alandira iwo eni mapindu a nsembe ya Yesu yotetezera machimo ndipo ali m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo.—Chivumbulutso 7:9, 14; 1 Yohane 1:7; 2:1, 2.
9. Kodi Saulo wa ku Tariso anaswa motani lamulo la Mulungu la mwazi, koma anasonyeza motani kusintha kwa khalidwe lake?
9 Asanakhale Mkristu, mtumwi Paulo anaswa lamulo la mwazi. Monga Saulo wa ku Tariso, iye anazunza otsatira a Yesu ndipo anavomerezadi kuphedwa kwawo. “Komatu,” anatero Paulo, “anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.” (1 Timoteo 1:13; Machitidwe 9:1-19) Saulo anasonyeza mzimu wakulapa, umene pambuyo pake unatsimikizidwa ndi ntchito zambiri za chikhulupiriro. Koma pamafunika zambiri osati chikhulupiriro chokha m’dipo kuti munthu aloŵe m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo.
10. Kodi zimatheka bwanji kupeza chikumbumtima chokoma, ndipo tiyenera kuchita chiyani kuti tichisunge?
10 Munthu wopha mnzake mwangozi akanatha kukhala mu wina wa midzi yopulumukirako ya Israyeli kokha ngati anasonyeza kuti anali ndi chikumbumtima chokoma kulinga kwa Mulungu pankhani yokhetsa mwazi. Kuti tikhale ndi chikumbumtima chokoma, tiyenera kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu, kulapa machimo athu, ndi kusintha moyo wathu. Tifunika kupempha chikumbumtima chokoma pakudzipatulira kwathu kwa Mulungu m’pemphero kupyolera mwa Kristu, tikumasonyeza zimenezi mwa ubatizo wa m’madzi. (1 Petro 3:20, 21) Chikumbumtima chokoma chimenechi chimatilola kukhala ndi unansi woyera ndi Yehova. Njira yokha yosungira chikumbumtima chokoma ndiyo kukwaniritsa zofunika za Mulungu ndi kuchita ntchito yopatsidwa kwa ife m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo, monga momwedi othaŵira m’midzi yopulumukirako yakale anafunikira kumvera Chilamulo ndi kuchita ntchito imene anapatsidwa. Ntchito yaikulu kwa anthu a Yehova lerolino ndi ija ya kulengeza uthenga wa Ufumu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kuchita ntchito imeneyo kudzatithandiza kukhala nzika zothandiza m’mudzi wopulumukiramo wamakono.
11. Kodi tiyenera kupeŵa chiyani ngati titi tikhale otetezereka m’mudzi wopulumukiramo wamakono?
11 Kuchoka m’mudzi wopulumukiramo wamakono ndiko kudzipereka ife eni ku chiwonongeko, pakuti Wolipsa mwazi posachedwapa adzakantha onse amene ali ndi liwongo la mwazi. Ino si nthaŵi yopezeka kunja kwa mudzi wotetezereka umenewu kapena kumalo angozi pafupi ndi malire a mabusa ake. Tingapezeke kunja kwa mudzi wophiphiritsira wopulumukirako ngati titaya chikhulupiriro m’nsembe yotetezera machimo ya Mkulu wa Ansembe. (Ahebri 2:1; 6:4-6) Ndiponso sitingakhale otetezereka ngati titengera njira za dziko, kuima m’malire a gulu la Yehova, kapena kupatuka pa miyezo yolungama ya Atate wathu wakumwamba.—1 Akorinto 4:4.
Kumasuka ku Mudzi Wopulumukirako
12. Kodi omwe kale anali ndi liwongo la mwazi ayenera kukhala nthaŵi yotani m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo?
12 Munthu wopha mnzake mwangozi mu Israyeli anafunikira kukhala m’mudzi wopulumukiramo “kufikira atafa mkulu wa ansembe.” (Numeri 35:28) Chotero kodi omwe kale anali ndi liwongo la mwazi ayenera kukhala nthaŵi yotani m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo? Kufikira pamene sadzafunikiranso mautumiki a Mkulu wa Ansembe, Yesu Kristu. “Akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye,” anatero Paulo. (Ahebri 7:25) Malinga ngati uchimo uliwonse ndi liwongo la mwazi lakale zipitiriza kukhalapo, mautumiki a Mkulu wa Ansembe ngofunika kuti anthu opanda ungwiro akhale ndi kaimidwe kabwino kwa Mulungu.
13. Kodi “ana a Israyeli” amakono ndani, ndipo ayenera kukhala nthaŵi yotani ‘m’mudzi wopulumukirako’?
13 Kumbukirani kuti midzi yopulumukirako yakale inakhazikitsidwa kaamba ka “ana a Israyeli,” alendo, ndi okhala pakati pawo. “Ana a Israyeli” ndiwo Aisrayeli auzimu. (Agalatiya 6:16) Iwo ayenera kukhala m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo kwa nthaŵi yonse imene akhala ndi moyo pa dziko lapansi. Chifukwa? Chifukwa chakuti akali ndi thupi lopanda ungwiro choncho afunikira mtengo wotetezera machimo wa Mkulu wa Ansembe wawo wakumwamba. Koma Akristu odzozedwa ameneŵa atafa ndi kuukitsidwira ku moyo wauzimu kumwamba, samafunikiranso mautumiki otetezera machimo a Mkulu wa Ansembe; amakhala atasiya kosatha thupi lawo ndi liwongo lake la mwazi. Kwa odzozedwa oukitsidwa amenewo, Mkulu wa Ansembe amakhala atafa pamalo ake otetezera machimo ndi owachinjiriza.
14. Kodi nchiyaninso chimene chimafuna kuti aja amene akuyembekezera kupita kumwamba akhale m’mudzi wopulumukiramo wamakono?
14 Kukhala kwawo ndi chibadwa cha umunthu kumafuna kuti aja amene adzakhala “oloŵa anzake a Kristu” akumwamba akhale m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo kufikira atamaliza mokhulupirika moyo wawo wa pa dziko lapansi mu imfa. Akafa, amapereka nsembe chibadwa cha umunthu kosatha. (Aroma 8:17; Chivumbulutso 2:10) Nsembe ya Yesu imangogwira ntchito kwa aja amene ali ndi chibadwa cha umunthu. Nchifukwa chake, Mkulu wa Ansembe amafa kwa aja a Israyeli wauzimu pamene aukitsidwa monga zolengedwa zauzimu amene adzakhala kumwamba kwamuyaya monga “oyanjana nawo umulungu.”—2 Petro 1:4.
15. Kodi ‘alendo’ ndi ‘okhala pakati pawo’ amakono ndani, ndipo Mkulu wa Ansembe wamkulu adzawachitira chiyani?
15 Kodi ndi liti pamene Mkulu wa Ansembe “adzafa” kwa ‘alendo’ ndi ‘okhala pakati pawo’ amakono, kuwalola kuchoka m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo? Akhamu lalikulu ameneŵa sadzachoka m’mudzi wopulumukiramo umenewu chitangopita chisautso chachikulu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti adzakhalabe ndi matupi awo ochimwa ndi opanda ungwiro ndipo adzafunikira kukhala pansi pa chitetezo cha Mkulu wa Ansembe. Mwa kulandira iwo eni mautumiki otetezera machimo mkati mwa ufumu wake wa zaka chikwi ndi unsembe wake, adzapeza ungwiro wa umunthu. Ndiyeno Yesu adzawapereka kwa Mulungu kuti chiyeso chomaliza ndi chogamuliratu kosatha chiperekedwe pa umphumphu wawo mwa kumasula Satana ndi ziŵanda zake kwa kanthaŵi. Chifukwa chakuti adzapambana chiyeso chimenechi ndi chivomerezo cha Mulungu, Yehova adzawayesa olungama. Motero adzapeza ungwiro wonse wa umunthu.—1 Akorinto 15:28; Chivumbulutso 20:7-10.a
16. Kodi ndi liti pamene opulumuka chisautso chachikulu sadzafunikiranso mautumiki otetezera machimo a Mkulu wa Ansembe?
16 Chotero, opulumuka chisautso chachikulu adzafunikira kusunga chikumbumtima chokoma mwa kukhala m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo kufikira mapeto a Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. Monga anthu opeza ungwiro, iwo sadzafunikiranso mautumiki otetezera machimo a Mkulu wa Ansembe ndipo adzachoka pansi pa chitetezo chake. Pamenepo Yesu adzafa kwa iwo monga Mkulu wa Ansembe, pakuti sadzafunikiranso kuwatumikira ndi mwazi woyeretsa wa nsembe yake. Nthaŵiyo iwo adzachoka m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo.
17. Kodi nchifukwa ninji aja ouka mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi sadzafunikira kuloŵa m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo ndi kukhala mmenemo?
17 Kodi aja amene adzauka mkati mwa Ulamuliro wa Yesu wa Zaka Chikwi adzafunikira kuloŵa m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo ndi kukhala mmenemo kufikira atafa mkulu wa ansembe? Ayi, chifukwa chakuti mwa imfa yawo, analipirira chilango cha machimo awo. (Aroma 6:7; Ahebri 9:27) Komatu, Mkulu wa Ansembe adzawathandiza kupeza ungwiro. Ngati adzapambana chiyeso chomaliza pambuyo pa Zaka Chikwi, Mulungu adzawayesanso olungama ndi kuwapatsa chitsimikizo cha moyo wamuyaya pa dziko lapansi. Zoonadi, kulephera kukwaniritsa zofunika za Mulungu kudzadzetsa chiweruzo chotsutsa ndi chiwonongeko kwa anthu onse amene sadzapambana chiyeso chomaliza monga osunga umphumphu.
18. Ponena za ufumu ndi unsembe wa Yesu, kodi nchiyani chimene chidzakhala ndi anthu kosatha?
18 Akulu a ansembe Achiisrayeli anamwalira potsiriza pake. Koma Yesu “akhala mkulu wa ansembe nthaŵi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.” (Ahebri 6:19, 20; 7:3) Chotero kutha kwa udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe wochita unkhoswe kwa anthu sikudzathetsa moyo wake. Zotulukapo zabwino za utumiki wake monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe zidzakhala ndi anthu kosatha, ndipo anthu adzamuyamika iye kwamuyaya pokhala atawatumikira pamalo ameneŵa. Ndiponso, ku umuyaya wonse Yesu adzatsogolera pa kulambira Yehova koyera.—Afilipi 2:5-11.
Maphunziro Ofunika Kwambiri kwa Ife
19. Kodi ndi phunziro lotani lonena za udani ndi chikondi limene tingatengepo pa makonzedwe a midzi yopulumukirako?
19 Tingaphunzire maphunziro osiyanasiyana pa makonzedwe a midzi yopulumukirako. Mwachitsanzo, munthu aliyense wakupha mnzake chifukwa cha udani wukulu sanaloledwe konse kukhala m’mudzi wopulumukiramo. (Numeri 35:20, 21) Chotero kodi munthu amene ali m’mudzi wopulumukiramo angalole motani kuda mbale wake kukula mumtima mwake? “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu,” analemba motero mtumwi Yohane, “ndipo mudziŵa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.” Choncho tiyeni “tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu.”—1 Yohane 3:15; 4:7.
20. Kuti atetezereke kwa Wolipsa mwazi, kodi aja okhala m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo ayenera kuchita chiyani?
20 Kuti atetezereke kwa wolipsa mwazi, anthu opha anzawo mwangozi anafunikira kukhala m’mudzi wopulumukiramo ndi kusadutsa malire a mabusa ake. Bwanji nanga za awo amene ali m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo? Kuti apulumuke kwa Wolipsa mwazi wamkulu, iwo ayenera kusatuluka m’mudziwo. Inde, afunikira kupeŵa zinthu zokopa zimene zingawapititse kumalire a mabusa, titero kunena kwake. Ayenera kusamala kuti sakulola chikondi cha dziko la Satana kukhala mumtima mwawo. Zimenezi zingafune pemphero ndi khama, koma mpamene miyoyo yawo imadalira.—1 Yohane 2:15-17; 5:19.
21. Kodi aja okhala m’mudzi wamakono wopulumukiramo akuchita ntchito yotani yofupa?
21 Anthu opha anzawo mwangozi okhala m’midzi yopulumukirako yakale anafunikira kukhala ogwira ntchito opindulitsa. Momwemonso, “ana a Israyeli” odzozedwa apereka chitsanzo chabwino monga ogwira ntchito yakututa ndi olengeza Ufumu. (Mateyu 9:37, 38; Marko 13:10) Pokhala ‘alendo’ ndi ‘okhala pakati pawo’ m’mudzi wopulumukiramo wamakono, Akristu oyembekezera kukhala pa dziko lapansi ali ndi mwaŵi wa kugwira ntchito imeneyi yopulumutsa moyo limodzi ndi odzozedwa omwe adakali pa dziko lapansi. Ndipo ntchito imeneyo njofupa chotani nanga! Awo amene akugwira ntchito mokhulupirika m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo adzapulumuka imfa yamuyaya pamanja a Wolipsa mwazi. M’malo mwake, adzapeza mapindu amuyaya m’mautumiki ake monga Mkulu wa Ansembe wamkulu wa Mulungu. Kodi inu mudzakhala m’mudzi wopulumukiramo ndi kukhala ndi moyo kosatha?
[Footnote]
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti anthu mamiliyoni zikwi zambiri pa dziko lapansi ali ndi liwongo la mwazi?
◻ Kodi ndi malo otani amene Yesu Kristu akukwaniritsa kulinga kwa anthu?
◻ Kodi mudzi wophiphiritsira wopulumukirako nchiyani, ndipo munthu amaloŵamo motani?
◻ Kodi anthu adzamasuka liti ku mudzi wophiphiritsira wopulumukirako?
◻ Kodi ndi maphunziro otani amene tingaphunzirepo pa makonzedwe a midzi yopulumukirako?
[Chithunzi patsamba 16]
Kodi mukudziŵa malo ofunika kwambiri amene Yesu Kristu akukwaniritsa?