-
“Yehova Amadziwa Anthu Ake”Nsanja ya Olonda—2014 | July 15
-
-
4. (a) Kodi Paulo sankakayikira za chiyani? (b) Nanga anasonyeza bwanji zimenezi m’kalata yake yopita kwa Timoteyo?
4 Paulo sankakayikira zoti Yehova amadziwa anthu amene akumulambira mwachinyengo komanso anthu amene amamumvera ndi mtima wonse. Mawu amene anauziridwa kulemba m’kalata yake yopita kwa Timoteyo amasonyeza zimenezi. Atafotokoza mmene ampatuko ankasokonezera anthu ena mumpingo, Paulo analemba kuti: “Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire, ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: ‘Yehova amadziwa anthu ake,’ ndiponso akuti: ‘Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.’”—2 Tim. 2:18, 19.
-
-
“Yehova Amadziwa Anthu Ake”Nsanja ya Olonda—2014 | July 15
-
-
6 Mu vesi limene ananena za “maziko olimba a Mulungu,” Paulo anagwiranso mawu amene Mose anauza Kora ndi anzake opezeka pa Numeri 16:5. Iye anagwiritsa ntchito zimene zinachitika m’nthawi ya Mose pofuna kulimbikitsa Timoteyo komanso kumutsimikizira kuti Yehova amadziwa ngati anthu ayamba mpatuko ndipo sawalekerera. Yehova sanalole kuti Kora asokoneze cholinga chake ndipo sakanalolanso kuti ampatuko amene anali mumpingo wachikhristu achite zimenezi. Paulo sanafotokoze kwenikweni tanthauzo la “maziko olimba a Mulungu.” Koma mawu amene anagwiritsa ntchitowa ayenera kuti anathandiza Timoteyo kukhulupirira kwambiri njira za Yehova.
-
-
“Yehova Amadziwa Anthu Ake”Nsanja ya Olonda—2014 | July 15
-
-
8, 9. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo za pa “chidindo” chimene Paulo anatchula?
8 Mawu ophiphiritsa a Paulo pa 2 Timoteyo 2:19 akunena za maziko okhala ndi chidindo. Kale, anthu ankakonda kudinda chidindo pa maziko a nyumba. Chidindocho chinkasonyeza dzina la munthu amene anamanga kapena mwiniwake wa nyumbayo. Paulo anali woyamba kugwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa amenewa m’Baibulo.a Chidindo cha pa “maziko olimba a Mulungu” chimanena mfundo ziwiri. Yoyamba ndi yakuti: “Yehova amadziwa anthu ake.” Yachiwiri ndi yakuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.” Mfundozi zimatikumbutsa zomwe zili pa Numeri 16:5.—Werengani.
-