Chilungamo Kaamba ka Onse ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu
“Pakuti Atate akonda Mwana . . . anapereka kuweruza konse kwa Mwana.”—YOHANE 5:20, 22.
1. Ndimotani mmene inu mukuyang’anizirana ndi mafunso ofanana ndi awo oyang’anizana ndi anthu ena m’zana loyambirira?
KODI chilungamo chiri chofunika motani kwa inu? Ndi kuyesayesa kochulukira kotani komwe inu mukaika kuti mutsimikiziridwe za kulandira chilungamo chowona ndipo ngakhale cha kukhala ndi moyo pamene icho chifalikira dziko lonse lapansi? Inu muli oyenera kulingalira ponena za mafunso amenewo, monga momwe anachitira amuna ndi akazi ena otchuka mu Atene, Grisi.
2, 3. (a) Nchiyani chomwe chinapangitsa kuitana kwa Paulo kaamba ka kulapa kwa omvetsera ake a ku Atene? (b) Nchifukwa ninji kulapa kungamveke kwachilendo kwa omvetsera amenewo?
2 Iwo anamva nkhani yokumbukirika yoperekedwa ndi mtumwi Wachikristu Paulo ku bwalo lamilandu lotchuka la Areopagi. Iye choyamba analingalira pa kukhalako kwa Mulungu mmodzi, Mlengi, kwa amene tonsefe timaŵerengera moyo wathu. Ichi chinatsogolera ku mathedwe enieni akuti tiri oŵerengera kwa Mulungu ameneyu. Pa nsonga imeneyi Paulo analengeza kuti: “Nthaŵi za kusadziŵako tsono [monga za kulambira mafano kwa anthu] Mulungu analekerera, koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima.”—Machitidwe 17:30.
3 Mowona, kulapa kukakhala chikhulupiriro chozizwitsa kwa gulu limenelo. Chifukwa ninji tero? Agriki akale anadziŵa za kulapa mlingaliro la kudzimva moipidwa pa zochitika zinazake kapena ndemanga. Monga mmene dikishonale ina imalozera ku icho, ngakhale kuli tero, liwulo “sili[na]lingalire nkomwe masinthidwe mu makhalidwe abwino onse, kasinthidwe kotheratu m’njira ya moyo, kutembenuka komwe kumayambukira mkhalidwe wonse.”
4. Ndemanga ya Paulo ponena za kulapa inachirikizidwa ndi kutsimikizira kotani?
4 Komabe, inu mosakaikira mungawone chifukwa chimene kulapa kotheratu kumeneko kuli koyenerera. Tsatirani nzeru yeniyeni ya Paulo. Anthu onse amaŵerengera moyo wawo kwa Mulungu, chotero onse ali oŵerengera kwa iye. Chiri, kenaka, kokha cholondola ndi cholungama kaamba ka Mulungu kuyembekezera iwo kumfunafuna iye, kupeza chidziŵitso cha iye. Ngati anthu a ku Atene amenewo sanadziŵe maprinsipulo ake ndi chifuno, iwo anafunikira kuphunzira zinthu zimenezi ndipo kenaka kulapa ndi cholinga chofuna kubweretsa miyoyo yawo m’chigwirizano ndi iwo. Ichi sichikadalira pa kokha mmene chinaliri choyenerera kuchita tero. Tingawone chifukwa chake kuchokera ku mawu amphamvu otsirizira a Paulo akuti: “Chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu [m’chilunjiko, NW] ndi munthu amene anamuikiratu, napatsa anthu onse chitsimikizo pamene anamuukitsa iye kwa akufa.”—Machitidwe 17:31.
5. Ndimotani mmene opezekapo anachitira ku kukamba kwa Paulo, ndipo nchifukwa ninji?
5 Versi limenelo, lodzala ndi tanthauzo, lokhutiritsa chotero, limayenerera kusanthula kwathu kosamalitsa, popeza kuti limabweretsa chiyembekezo kaamba ka chilungamo changwiro m’nthaŵi yathu. Onani malongosoledwe akuti: “kupangiratu tsiku,” “kuweruza dziko lokhalamo anthu,” “[m’chilunjiko, NW],” “ndi munthu amene anamuikiratu,” “napatsa chitsimikizo,” “namuukitsa iye.” Mawu amenewo “namuukitsa iye” anabweretsa kuvomereza kwamphamvu kuchokera ku gulu la Paulo. Monga momwe maversi 32-34 amasonyezera, ena anaseka. Ena anangochokapo pa kukambitsiranako. Komabe, oŵerengeka anakhala okhulupirira olapa. Ngakhale kuli tero, lolani kuti, tikhale anzeru kwambiri kuposa unyinji wa gulu la anthu a ku Atene, popeza kuti ichi chiri chofunika koposa ngati timakhumba chilungamo chowona. Kuti tipeze tanthauzo lenileni mu versi 31, choyamba onani pa kalongosoledwe kakuti: “[Iye, NW] anapangira tsiku limene adzaŵeruza dziko lokhalamo anthu.” Kodi ndani “iye” ameneyo, ndipo kodi ndi iti yomwe iri miyezo yake, makamaka ponena za chilungamo?
6. Ndimotani mmene tingaphunzirire ponena za Uyo yemwe waikiratu tsiku kaamba ka kuweruza dziko lapansi?
6 Chabwino, Machitidwe 17:30 imasonyeza amene Paulo anali kulozerako—Mulungu weniweniyo yemwe akuwuza onse kulapa, Mpatsi wathu wa Moyo, Mlengi. Mwachibadwa, tingapeze zochulukira ponena za Mulungu kuchokera mu ntchito zake za kulenga. Koma miyezo yake ya chilungamo iri makamaka yowonekera kuchokera ku magwero ena, Baibulo, lomwe liri ndi mbiri ya zochita zake ndi anthu onga Mose ndi za malamulo a Mulungu kaamba ka Israyeli.
Ndi Mtundu Wanji wa Kuweruza ndi Chilungamo?
7. Mose akupereka umboni wotani ponena za Yehova ndi chilungamo?
7 Inu mungakhale odziŵa kuti kwa zaka makumi angapo Mose anali ndi zochita zathithithi ndi Yehova Mulungu, chapafupi kwenikweni chakuti Mulungu ananena kuti analankhula ndi Mose “pakamwa ndi pakamwa.” (Numeri 12:8) Mose anadziŵa mmene Yehova anachitira ndi iye, limodzinso ndi mmene Mulungu anachitira ndi anthu ena ndi mtundu wonse. Pafupi ndi mapeto a moyo wake, Mose anapereka kulongosola kwake kotsimikizirika uku: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro, pakuti njira zake zonse ndi [chilungamo, NW]. Mulungu wokhulupirika, ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”—Deuteronomo 32:4.
8. Nchifukwa ninji tiyenera kudziŵa za chimene Elihu ananena pa nkhani ya chilungamo?
8 Lingalirani, kachiŵirinso, umboni kuchokera kwa Elihu, munthu wodziŵika kaamba ka nzeru zake ndi kuzindikira. Inu mungakhale wotsimikizira kuti iye anali osati munthu yemwe anafikira mathedwe ongothamangira. M’malomwake, m’nkhani imodzi iye anakhala koposa mlungu umodzi pamene ankamvetsera pa kukangana kwa pakamwa kotalikira kuchokera ku mbali zonse ziŵiri. Tsopano, kuchokera ku chokumana nacho cha Elihu iyemwini ndi kuchokera m’kuphunzira kwake kwa njira za Mulungu, ndi mathedwe otani amene iye anafikira ponena za Mulungu? Iye analengeza kuti: “Chifukwa chake, mundimvere ine, eni nzeru inu. Nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama! Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake, napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake. Ndithu, zowonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipsye mlandu.”—Yobu 34:10-12.
9, 10. Nchifukwa ninji miyezo ya Mulungu kaamba ka oweruza a umunthu imatilimbikitsa ife? (Levitiko 19:15)
9 Dzifunseni inu eni: Kodi chimenecho sichimalongosola mwangwiro chomwe tikafuna kuchokera kwa woweruza, kuti iye amachitira munthu aliyense mogwirizana ndi machitidwe ake, kapena mikhalidwe, popanda tsankho kapena kupatutsa mlandu? Ngati inu munafunikira kuyang’anizana ndi woweruza waumunthu, kodi inu simungadzimve opumitsidwa ngati iye anali wofanana ndi amenewo?
10 Baibulo limalozera kwa Yehova kukhala “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Genesis 18:25) Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, iye amagwiritsira ntchito oweruza aumunthu. Nchiyani chomwe iye anayembekezera kwa oweruza a Chiisrayeli omwe anamuimira iye? Mu Deuteronomo 16:19, 20 timaŵerenga zitsogozo za Mulungu zomwe zinafikira ku kulongosola kwa ntchito kaamba ka oweruza: “Musamapotoza chiweruzo. Musamasamalira munthu kapena kulandira chokometsera mlandu, popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru nichiipsya mawu a [olunjika, NW]. Chilungamo—chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo.” Mafano owumba amakono osonyeza Chilungamo angakhoze modzifunira kusonyeza iwo kukhala otsekedwa maso kutanthauza kupanda tsankho, koma mungawone kuti Mulungu anapyola pamenepo. Iye m’chenicheni anafuna kupanda tsankho koteroko kwa oweruza aumunthu omwe anafunikira kumuimira iye ndi kuchirikiza malamulo ake.
11. Tingatsirize chiyani kuchokera ku kubwereramo m’chidziŵitso cha Baibulo chimenechi ponena za chilungamo?
11 Tsatanetsatane ameneyu ponena za kawonedwe ka Mulungu ka chilungamo amachitira umboni mwachindunji pachimake pa kulankhula kwa Paulo. Pa Machitidwe 17:31 Paulo analengeza kuti Mulungu “anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu [m’chilunjiko, NW].” Chimenecho ndi chenicheni chomwe tingayembekezere kuchokera kwa Mulungu—chilungamo, chilunjiko, kupanda tsankho. Ndiponso, anthu ena angakhale odera nkhaŵa chifukwa chakuti, mogwirizana ndi versi 31, Mulungu adzagwiritsira ntchito “munthu” kuweruza anthu onse. Ndani yemwe ali “munthu” ameneyo, ndipo kodi ndi chitsimikiziro chotani chomwe tiri nacho chakuti iye adzagwiririra ku miyezo yapamwamba ya Mulungu ya chilungamo?
12, 13. Ndimotani mmene timadziŵira “munthu” amene Mulungu adzagwiritsira ntchito kuweruza?
12 Machitidwe 17:18 imatiwuza ife kuti Paulo anakhala “akulalikira [mbiri yabwino ya, NW] Yesu ndi kuuka kwa akufa.” Chotero, pamapeto pa kulankhula kwake, opezekapo anadziŵa kuti Paulo anatanthauza Yesu Kristu pamene iye ananena kuti Mulungu akakhoza ‘kuweruza dziko lokhalamo anthu [m’chilunjiko, NW] ndi munthu amene anamuikiratu, ndipo Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa.’
13 Yesu anavomereza kuti Mulungu anali atamusankha iye kukhala woweruza yemwe anafikiritsa miyezo yaumulungu. Pa Yohane 5:22 iye ananena kuti: “Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana.” Pambuyo pa kutchula chiwukiriro chomwe chinkadza cha awo omwe ali m’manda a chikumbukiro, Yesu anawonjezera kuti: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha; monga momwe ndimva, ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.”—Yohane 5:30; Salmo 72:2-7.
14. Ndi mtundu wotani wa kachitidwe womwe tingayembekezere kuchokera kwa Yesu?
14 Ndi mwaubwino chotani nanga mmene chitsimikiziro chimenechi chikugwirizanirana ndi chomwe timaŵerenga pa Machitidwe 17:31! Pamenepo Paulo nayenso wapereka chitsimikiziro chakuti Mwana akakhoza “kuweruza dziko lokhalamo anthu [m’chilunjiko, NW].” Chimenecho ndithudi sichimalingalira chilungamo cholimba chirichonse, chosasinthasintha, ndi chopanda kudzimva, kodi chimatero? M’malomwake, kuweruza kolunjika kumaphatikizapo kusanganiza chilungamo ndi chifundo ndi kumvetsetsa. Lolani kuti tisanyalanyaze ichi: Ngakhale kuti Yesu tsopano ali m’mwamba, iye anakhalapo munthu. Chotero iye angakhale wachifundo. Pa Ahebri 4:15, 16 Paulo anakhudza pa ichi m’kulongosola Yesu kukhala wansembe wamkulu.
15. Ndimotani mmene Yesu amasiyanirana ndi oweruza aumunthu?
15 Pamene mukuŵerenga Ahebri 4:15, 16, lingalirani ponena za mpumulo umene tiyenera kudzimvera kukhala ndi Yesu monga Woweruza: “Pakuti sitiri naye mkulu wansembe wosatha [ndi woweruza], kumva chifundo ndi zofoka zathu, koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero, tilimbike mtima, poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi ya kusowa.” M’zipinda za bwalo lamilandu lerolino, chiri kaŵirikaŵiri chomvetsa mantha kuitanidwa patsogolo pa Benchi. Komabe, m’nkhani ya Kristu monga Woweruza, tingakhoze ‘kumufikira ndi ufulu wa kulankhula kotero kuti tikapeze chifundo, chisomo, ndi thandizo pa nthaŵi yoyenera.’ Ponena za nthaŵi, ngakhale kuli tero, muli ndi chifukwa chabwino cha kufunsira kuti, ‘Ndi liti pamene Yesu adzaweruza mtundu wa anthu [m’chilunjiko, NW]?’
“Tsiku” la Kuweruza—Liti?
16, 17. Ndimotani mmene timadziŵira kuti kuweruza kuchokera kumwamba kukuchitika tsopano?
16 Kumbukirani kuti Paulo ananena kuti Mulungu “anaikiratu tsiku” la kuweruza dziko ndi Woweruza Wake woikidwa. M’kuyembekezera “tsiku” la chiweruzo limenelo, Yesu akuchita ntchito yoweruza yofunika kwambiri lerolino, inde, tsopano lino. Nchifukwa ninji tinganene chimenecho? Osati kale kwambiri iye asanamangidwe ndi kukanidwa mosalungama ku imfa, Yesu anapereka ulosi wa m’mbiri womwe umaphatikiza tsiku lathu. Timaupeza uwo mu Mateyu mutu 24. Yesu analongosola zochitika zadziko zomwe zikazindikiritsa nyengo yotchedwa “mapeto a dongosolo la kachitidwe ka zinthu.” Nkhondo, kusoweka kwa chakudya, zivomezi, ndi zosautsa zina zomwe zachitika pa dziko lonse lapansi chiyambire Nkhondo ya Dziko ya I zimatsimikizira kuti ulosi wa Yesu ukukwaniritsidwa tsopano ndi kuti posachedwapa “mapeto adzafika.” (Mateyu 24:3-14) Mboni za Yehova kwa zaka makumi angapo zakhala zikulongosola chimenechi kuchokera m’Baibulo. Ngati mungafune umboni wowonjezereka ponena za chifukwa chimene timadziŵira kuti tiri m’masiku otsiriza a dongosolo la kachitidwe la chisalungamo iri, Mboni za Yehova zingapereke woterowo.
17 Santhulani, ngakhale ndi tero, theka lotsirizira la Mateyu mutu 25, yomwe iri mbali ya ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza. Mateyu 25:31, 32 imagwira ntchito mkati mwa nthaŵi yathu: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake [m’mwamba]. Ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse, ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Tsopano yang’anani pansipo pamene Yesu akulongosola ntchito yake ya, kulekanitsa, kapena kuweruza. Versi 46: “Ndipo amenewa [anthu amene iye akuweruza kukhala mbuzi] adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse, koma [olunjika, NW] [nkhosa] ku moyo wa nthaŵi zonse.”
18. Ndi kuchiyani kumene kuweruza m’tsiku lathu kudzatsogolera?
18 Chotero tikukhala m’nthaŵi yoipitsitsa kwenikweni ya chiweruzo. Awo ‘ofunafuna Mulungu ndi kumpezadi iye’ lerolino adzaweruzidwa monga “nkhosa” mu mzere wa kupulumuka mathedwe a dongosolo la kachitidwe lamakono ndi kuloŵa m’dziko latsopano lomwe lidzatsatira. Kenaka 2 Petro 3:13 idzazindikiridwa: “Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa [chilunjiko, NW].” Limenelo lidzakhala “tsiku” pamene mawu a Paulo pa Machitidwe 17:31 adzagwira ntchito mokwanira, nthaŵi kaamba ka kuweruzidwa kwa dziko lapansi m’chilunjiko.
19, 20. Ndani omwe adzayambukiridwa ndi Tsiku la Chiweruzo lomwe likudzalo?
19 Tsiku la Chiweruzo limenelo lidzaposa kokha kupulumuka kwa “nkhosa,” omwe adzakhala ataweruzidwa kale oyenerera kuloŵa m’dziko latsopano. Kumbukirani kuti pambuyo pa kunena kuti Atate wake anapereka chiweruzo kwa iye, Yesu analankhula za kudza kwa chiwukiriro. Ndiponso, pa Machitidwe 10:42, mtumwi Petro ananena kuti Yesu Kristu “ali Amene walamulidwa ndi Mulungu kuweruza amoyo ndi akufa.”
20 Mwakutero, ‘tsiku loikidwiratu’ limenelo lotchulidwa pa Machitidwe 17:31 pamene Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu “adzaweruza dziko lokhalidwa ndi anthu [m’chilunjiko, NW]” idzakhala nthaŵi kaamba ka kuwukitsidwa kwa akufa. Chidzakhala chisangalalo chotani nanga kuwona mphamvu zaumulungu zikusonyezedwa kugonjetsa imfa, yomwe kusakaza kwake kwakhala kaŵirikaŵiri chisalungamo chokulira. Anthu ena, monga kunaliri ndi Yesu iyemwini, aphedwa mopanda chilungamo ndi maboma kapena magulu ankhondo owukira. Ena atayikiridwa miyoyo yawo m’zochitika zosawonedweratu zonga ngati kugwa kwa nyumba, zivomezi, moto wa ngozi, ndi matsoka a mtundu wotero.—Mlaliki 9:11.
Chisalungamo cha Kumbuyo Chithetsedwa
21. Ndimotani mmene chisalungamo cha papitapo chidzagonjetsedwera m’dziko latsopano?
21 Talingalirani kukhala okhoza kuwona okondedwa athu akubweretsedwa kumoyo! Ambiri chotero adzakhala ndi mwaŵi wawo woyamba ‘kufunafuna Mulungu ndi kumpezadi iye’ ndipo kenaka adzakhala ndi “moyo wosatha” pamaso pawo womwe ungakhale mphoto ya “nkhosa.” Owukitsidwa ena, limodzinso ndi opulumuka a dongosolo la kachitidwe la chisalungamo iri, akhala minkhole ya chisalungamo chowonekera chonga ngati kulemala kobadwa nako, khungu, ugonthi, kapena kulemala kwa kalankhulidwe. Kodi zinthu zoterezi zidzakhala zoyenerera mu ‘dziko lapansi latsopano mmene [chilunjiko, NW] chidzakhala’? Yehova anagwiritsira ntchito Yesaya kupereka maulosi osiyanasiyana omwe adzakhala ndi kukwaniritsidwa kokulira kwenikweni mkati mwa Tsiku la Chiweruzo lomwe likudzalo. Onani chomwe tingayembekezere: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo opunduka adzadumpha ngati nswala, ndi lilime la osalankhula lidzayimba.”—Yesaya 35:5, 6.
22. Nchifukwa ninji Yesaya mutu 65 uli wolimbikitsa chotero ponena za chilungamo?
22 Bwanji ponena za chisalungamo china chomwe tsopano chimapangitsa chisoni chokulira? Yesaya mutu 65 uli ndi mayankho ena olimbikitsa mosangalatsa. Kuyerekeza kwa Yesaya 65:17 ndi 2 Petro 3:13 kumasonyeza kuti mutu umenewo nawonso umaloza ku nthaŵi ya “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” dongosolo la kachitidwe latsopano lolunjika. Ndiponso, nchiyani chomwe chidzachinjiriza oipa oŵerengeka kuipitsa mtendere ndi chilungamo? Cha patsogolo pang’ono, Yesaya 65 akuthetsa chomwe chingawonekere kukhala vuto.
23. Kwa anthu ena Tsiku la Chiweruzo lidzakhala ndi chotulukapo chothekera chotani?
23 Mkati mwa Tsiku la Chiweruzo lomwe liripoli, Yesu adzapitirizabe ntchito yake ya kuweruza anthu, kaya akuyenerera kaamba ka moyo wosatha. Ena sadzatero. Pambuyo pa kupatsidwa nthaŵi yokwanira, mwinamwake ngakhale “zaka zana limodzi,” za kufunafuna Mulungu, ena adzasonyeza kuti akukana kusonyeza chilunjiko. Molungama iwo adzataya moyo m’dziko latsopano limenelo, monga momwe tikuwonera mu Yesaya 65:20: “Ndipo wochimwa, pokhala wa zaka zana limodzi adzatembereredwa.” Oterowo oweruzidwa kukhala osayenerera moyo adzakhala ochepera. Tiri ndi chifukwa chirichonse cha kuyembekezera kuti ife—ndi ambiri ena—tidzasangalatsidwa kuphunzira ndi kusonyeza chilunjiko.—Yesaya 26:9.
24. Nchiyani chomwe chidzakhala mkhalidwe ponena za chisalungamo cha zachuma?
24 Kodi chimenecho chimatanthauza kuti sipadzakhala kusalungama komapitirizabe, osati ngakhale chisalungamo cha zachuma? Motsimikizirikadi! Yesaya 65:21-23 imaloza ku nsonga imeneyo: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka ndi wina kudya. Pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, kapena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.” Ndi kusintha kotani nanga kuchokera ku lerolino! Ndi dalitso lotani nanga!
25. Nchiyani chomwe chiri chiyembekezo chanu ndi chigamulo ponena za chilungamo kuchokera kwa Woweruza woikidwa ndi Mulungu?
25 Ndiponso, onse omwe amakhumba kaamba ka chilungamo chosatha angatenge kulimba mtima. Chiri chotsimikizirika kudza—mwamsanga. Tsopano, mkati mwa nthaŵi yochepera yotsalako m’nthaŵi ino ya chiweruzo, iri nthaŵi ya kugwirizana ndi Mboni za Yehova m’kufunafuna Mulungu ndi kumpezadi iye, mwa kukhala ndi madalitso osatha.
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndi umboni wotani womwe tiri nawo ponena za muyezo wa Mulungu wa chilungamo?
◻ Ndimotani mmene Yesu adzaphatikizidwira m’Tsiku la Chiweruzo lomwe likudzalo?
◻ Nchifukwa ninji yathu iri nthaŵi yoipitsitsa m’chigwirizano ndi chiweruzo chaumulungu?
◻ Ndimotani mmene chisalungamo chapapitapo chidzawongoleredwa m’dziko latsopano?
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.