NKHANI YOPHUNZIRA 9
Aisiraeli Ankafunika Kusonyeza Chikondi ndi Chilungamo
“Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera. Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.”—SAL. 33:5.
NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi tonsefe timafuna chiyani? (b) Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?
TONSEFE timafuna kukondedwa komanso kuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Ngati zimenezi sizikuchitika, timayamba kudziona kuti ndife achabechabe ndipo timataya mtima.
2 Yehova amadziwa kuti anthufe timafuna chikondi ndi chilungamo. (Sal. 33:5) Tisamakayikire kuti Yehova amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizichitiridwa zinthu mwachilungamo. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chimatsimikizira mfundo imeneyi. Ngati mumaona kuti anthu sakukondani kapena anakuchitirani zinthu mopanda chilungamo, tikukupemphani kuti muganizire mmene Chilamulo cha Moseb chimasonyezera kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake.
3. (a) Malinga ndi Aroma 13:8-10, kodi tikamaphunzira Chilamulo cha Mose timazindikira chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
3 Tikamaphunzira Chilamulo cha Mose timatha kuzindikira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi kwambiri. (Werengani Aroma 13:8-10.) Munkhaniyi tikambirana malamulo ena amene anaperekedwa kwa Aisiraeli ndipo tiyankha mafunso awa: N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu anasonyeza chikondi popereka Chilamulo? N’chifukwa chiyani tinganene kuti Chilamulo chinkalimbikitsa chilungamo? Kodi akulu ndi oweruza ankayenera kutsatira bwanji Chilamulo? Nanga Chilamulo chinkateteza ndani makamaka? Mayankho a mafunso amenewa angatilimbikitse, kutipatsa chiyembekezo komanso kulimbitsa kwambiri ubwenzi wathu ndi Atate wathu wachikondi.—Mac. 17:27; Aroma 15:4.
MULUNGU ANASONYEZA CHIKONDI POPEREKA CHILAMULO
4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu anasonyeza chikondi popereka Chilamulo cha Mose? (b) Mogwirizana ndi zimene lemba la Mateyu 22:36-40 limanena, Kodi Yesu anatchula malamulo ati?
4 Tinganene kuti Mulungu anasonyeza chikondi popereka Chilamulo cha Mose chifukwa chilichonse chimene amachita, amachichita chifukwa cha chikondi. (1 Yoh. 4:8) Malamulo onse amene Mulungu anapereka anachokera pa mfundo ziwiri. Mfundo zake ndi zakuti uzikonda Mulungu komanso uzikonda mnzako. (Lev. 19:18; Deut. 6:5; werengani Mateyu 22:36-40.) Choncho malamulo oposa 600 amene Mulungu anapereka amasonyeza chikondi chake. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.
5-6. Kodi Yehova amafuna kuti anthu a pa banja azichita chiyani, nanga iye amadziwa chiyani? Perekani chitsanzo.
5 Muzikhala okhulupirika m’banja komanso muzisamalira bwino ana. Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azikondana kwa moyo wawo wonse. (Gen. 2:24; Mat. 19:3-6) Munthu akachita chigololo amasonyeza kuti alibiretu chikondi. M’pomveka kuti lamulo la nambala 7 pa Malamulo 10 linali loletsa chigololo. (Deut. 5:18) Munthu akachita chigololo amakhala kuti ‘wachimwira Mulungu’ komanso kuchitira nkhanza mkazi kapena mwamuna wake. (Gen. 39:7-9) Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo zikhoza kumupweteka kwa zaka zambiri.
6 Yehova amadziwa zimene anthu okwatirana amachitirana. Iye ankafuna kuti akazi a ku Isiraeli azikondedwa ndi amuna awo. Mwamuna amene ankalemekeza Chilamulo ankakonda kwambiri mkazi wake ndipo sakanathetsa banja popanda zifukwa zomveka. (Deut. 24:1-4; Mat. 19:3, 8) Koma ngati panali vuto lalikulu ndipo mwamunayo wasankha kuthetsa banja, ankafunika kumupatsa mkaziyo kalata yothetsera ukwati. Kalata imeneyi inkateteza mkaziyo kuti asamaimbidwe mlandu wochita chiwerewere. Komanso mwamuna asanapatse mkazi wake kalata yothetsera ukwati, ankayenera kukaonana ndi akuluakulu a mzinda, omwe ankayesetsa kuwathandiza kuti banja lisathe. Mwamuna akathetsa banja pa zifukwa zosamveka, sikuti Yehova ankalowerera nthawi zonse. Komabe ankaona misozi imene mkaziyo ankagwetsa ndipo ankadziwa mmene zinkamupwetekera.—Mal. 2:13-16.
7-8. (a) Kodi Yehova analamula makolo kuti azichita chiyani? (Onani chithunzi patsamba loyamba.) (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani?
7 Chilamulo chinkasonyezanso kuti Yehova amakonda kwambiri ana. Yehova analamula kuti makolo azisamalira ana awo mwakuthupi komanso mwauzimu. Makolo ankafunika kuyesetsa kuthandiza ana awo kuti azidziwa bwino Chilamulo cha Yehova komanso azimukonda kwambiri. (Deut. 6:6-9; 7:13) Chifukwa chimodzi chimene Yehova analangira Aisiraeli chinali chakuti makolo ankachitira ana awo nkhanza zoopsa. (Yer. 7:31, 33) Makolo ankayenera kuona ana awo ngati cholowa kapena kuti mphatso yochokera kwa Yehova ndipo ankayenera kuwakonda kwambiri.—Sal. 127:3.
8 Zimene tikuphunzirapo: Yehova amaona chilichonse chimene anthu a pa banja amachitirana. Iye amafunanso kuti makolo azikonda ana awo ndipo adzawaimba mlandu pa zimene amachita ndi anawo.
9-11. N’chifukwa chiyani Yehova anapereka lamulo loti musasirire?
9 Muzipewa kusirira. Lamulo lomaliza pa Malamulo 10 linali loletsa kusirira, kapena kulakalaka zinthu za munthu wina. (Deut. 5:21; Aroma 7:7) Yehova anapereka lamuloli pofuna kuphunzitsa anthu kuti ayenera kuteteza mitima yawo kapena maganizo awo. Iye amadziwa kuti zoipa zimene anthu amachita zimayambira mumtima. (Miy. 4:23) Munthu akayamba kulakalaka zinthu zoipa mumtima mwake amayambanso kuchita zinthu mopanda chikondi ndi anthu ena. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Davide. Nthawi zambiri iye ankachita zabwino. Koma nthawi ina anayamba kusirira mkazi wa munthu wina ndipo kenako anachimwa. (Yak. 1:14, 15) Paja Davide anachita chigololo, anayesetsa kupusitsa mwamuna wa mkaziyo kenako anakonza zoti mwamunayo aphedwe.—2 Sam. 11:2-4; 12:7-11.
10 Yehova amadziwa zamumtima choncho ankadziwa ngati munthu waphwanya lamulo lokhudza kusirira. (1 Mbiri 28:9) Lamulo loti musasirire linathandiza anthu ake kudziwa kuti ayenera kupewa maganizo amene angachititse munthu kuchita zoipa. Apa zikuonekeratu kuti Yehova ndi Atate wanzeru komanso wachikondi.
11 Zimene tikuphunzirapo: Yehova samangoona maonekedwe athu koma amaonanso zimene zili mumtima mwathu. (1 Sam. 16:7) Sitingabisire Yehova chilichonse chimene tikuganiza, kulakalaka kapena kuchita. Iye amayang’ana zabwino zimene timachita ndipo amatilimbikitsa kuchita zabwinozo. Koma amafunanso kuti tizindikire zinthu zoipa zimene tayamba kuganizira n’kusiya kuziganizira tisanafike pochita zoipazo.—2 Mbiri 16:9; Mat. 5:27-30.
CHILAMULO CHINKALIMBIKITSA CHILUNGAMO
12. Kodi Chilamulo cha Mose chimasonyeza chiyani?
12 Chilamulo cha Mose chimasonyeza kuti Yehova amakonda chilungamo. (Sal. 37:28; Yes. 61:8) Iye amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo. Aisiraeli akamamvera malamulo ake achilungamo, iye ankawadalitsa. Koma akapanda kumvera ankakumana ndi mavuto. Tiyeni tsopano tikambirane za malamulo ena awiri pa Malamulo 10 amene anawapatsa aja.
13-14. Kodi malamulo awiri oyambirira anali otani, nanga kumvera malamulowo kunkathandiza bwanji Aisiraeli?
13 Muzilambira Yehova yekha. Malamulo awiri oyambirira ankalimbikitsa Aisiraeli kuti azilambira Yehova yekha osati mafano. (Eks. 20:3-6) Malamulo amenewa anali othandiza anthuwo osati Yehova. Aisiraeliwo akakhala okhulupirika kwa Yehova zinthu zinkawayendera bwino. Koma akayamba kulambira milungu ya mitundu ina ankavutika kwambiri.
14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi anthu a ku Kanani. Iwo ankalambira mafano opanda moyo osati Mulungu woona komanso wamoyo. Izi zinachititsa kuti azichita zinthu zoipa kwambiri. (Sal. 115:4-8) Mwachitsanzo, polambira milunguyo ankachita chiwerewere komanso kupereka nsembe ana awo. Nawonso Aisiraeli akasiya Yehova n’kumalambira mafano ankachita zinthu zoipa kwambiri komanso kuzunzitsa mabanja awo. (2 Mbiri 28:1-4) Anthu olamulira sankatsatira mfundo zachilungamo za Yehova ndipo ankapondereza kwambiri anthu wamba. (Ezek. 34:1-4) Yehova anachenjeza Aisiraeli kuti adzalanga anthu onse amene ankazunza akazi ndi ana. (Deut. 10:17, 18; 27:19) Koma Yehova ankadalitsa kwambiri anthu ake akakhala okhulupirika komanso akamachitirana zinthu mwachilungamo.—1 Maf. 10:4-9.
15. Kodi taphunzira chiyani zokhudza Yehova?
15 Zimene tikuphunzirapo: Sitiyenera kuimba mlandu Yehova ngati anthu asiya kutsatira mfundo zake n’kumazunza anzawo. Yehova amatikonda kwambiri ndipo amadziwa ngati sitikuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Iye amazindikira mavuto athu kuposa mmene mayi amachitira ndi mwana wake wakhanda. (Yes. 49:15) Ngakhale kuti mwina sangathetse mavuto athuwo panopa, pa nthawi yoyenera adzalanga anthu osalapa amene amachitira nkhanza anzawo.
KODI AKULU NDI OWERUZA ANKAYENERA KUTSATIRA BWANJI CHILAMULO?
16-18. Kodi Chilamulo cha Mose chinkakhudza mbali ziti, nanga tikuphunzirapo chiyani?
16 Chilamulo cha Mose chinkakhudza mbali zosiyanasiyana za moyo wa Aisiraeli. Choncho kuti zinthu ziziyenda bwino pa moyo wa anthu, akulu ndi oweruza ankafunika kuchita zinthu mwachilungamo. Iwo ankafunika kuweruza anthu pa nkhani zokhudza kulambira komanso milandu yosiyanasiyana. Tiyeni tione zitsanzo pa nkhaniyi.
17 Munthu wa ku Isiraeli amene wapha mnzake sankaphedwa nthawi yomweyo. Akulu amumzinda umene ankakhala ankaifufuza nkhaniyo kuti adziwe ngati munthuyo ndi woyenera kuphedwa kapena ayi. (Deut. 19:2-7, 11-13) Akulu ankaweruzanso milandu yosiyanasiyana yokhudza katundu, mavuto a m’banja ndiponso nkhani zina. (Eks. 21:35; Deut. 22:13-19) Akuluwo akamachita zinthu mwachilungamo komanso Aisiraeli akamamvera malamulo, zinthu zinkawayendera bwino ndipo Yehova ankalemekezeka.—Lev. 20:7, 8; Yes. 48:17, 18.
18 Zimene tikuphunzirapo: Yehova amaona chilichonse chimene chikuchitika pa moyo wathu. Iye amafuna kuti tizichita zinthu mwachikondi komanso mwachilungamo. Mulungu amamva zimene timalankhula komanso kuona zimene timachita ngakhale m’banja lathu.—Aheb. 4:13.
19-21. (a) Kodi akulu ndi oweruza ankayenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu? (b) Kodi Yehova anatani pofuna kuti pakhale chilungamo, nanga tikuphunzirapo chiyani?
19 Yehova ankafuna kuteteza anthu ake kuti asatengere makhalidwe oipa a mitundu ina. Choncho ankafuna kuti akulu ndi oweruza azitsatira Chilamulo mosakondera. Koma ankafunika kuweruza moganizira anthu osati mwankhanza. Oweruzawo ankayenera kukonda chilungamo.—Deut. 1:13-17; 16:18-20.
20 Yehova ndi wachifundo choncho anapereka malamulo othandiza kuti anthu asamachitirane zinthu mopanda chilungamo. Mwachitsanzo, Chilamulo chinkathandiza kuti munthu asamanamiziridwe mlandu. Munthu woimbidwa mlandu anali ndi ufulu wodziwa munthu amene akumuimba mlanduwo. (Deut. 19:16-19; 25:1) Pankafunikanso anthu awiri kuti apereke umboni munthuyo asanaweruzidwe. (Deut. 17:6; 19:15) Ndiye kodi chinkachitika n’chiyani ngati panali mboni imodzi yokha pa mlandu winawake? Wopalamulayo sankayenera kuganiza kuti basi wapulumuka. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anaona zimene wachita. M’banja, bambo ankakhala ndi ulamuliro koma unali ndi malire. Pa nkhani zina zokhudza banja, akulu ankakhala ndi udindo woona nkhaniyo n’kupereka chiweruzo.—Deut. 21:18-21.
21 Zimene tikuphunzirapo: Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa chilichonse chimene amachita chimakhala chachilungamo. (Sal. 9:7) Iye amadalitsa anthu amene amatsatira mfundo zake mokhulupirika koma amalanga anthu amene amapondereza anzawo. (2 Sam. 22:21-23; Ezek. 9:9, 10) Anthu ena akachita zoipa zimaoneka ngati azemba chilango koma Yehova akaona kuti nthawi yabwino yafika amawalanga mwachilungamo. (Miy. 28:13) Ndipo ngati salapa, amadzazindikira kuti “kulandira chilango chochokera kwa Mulungu wamoyo n’chinthu choopsa.”—Aheb. 10:30, 31.
KODI CHILAMULO CHINKATETEZA NDANI MAKAMAKA?
22-24. (a) Kodi Chilamulo chinkateteza makamaka ndani, nanga tikuphunzirapo chiyani zokhudza Yehova? (b) Kodi pa Ekisodo 22:22-24 pamapezeka chenjezo lotani?
22 Chilamulo chinkateteza makamaka anthu amene sankatha kudziteteza monga ana ndi akazi amasiye komanso alendo. Oweruza a ku Isiraeli anauzidwa kuti: “Usapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye, ndipo usalande mkazi wamasiye chovala chake monga chikole.” (Deut. 24:17) Yehova ankaganizira kwambiri anthu amene ankaponderezedwa mosavuta. Ndipo ankalanga anthu amene ankawapondereza.—Werengani Ekisodo 22:22-24.
23 Chilamulo chinkateteza anthu kuti asachitiridwe nkhanza zokhudza kugonana ndi achibale awo. (Lev. 18:6-30) Anthu a mitundu ina ankalekerera nkhanza ngati zimenezi ndipo nthawi zina ankazilimbikitsa. Koma mosiyana ndi zimenezi, Aisiraeli anali ndi maganizo a Yehova pa nkhaniyi ndipo ankaona kuti ndi zoipa kwambiri.
24 Zimene tikuphunzirapo: Yehova amafuna kuti anthu amene wawapatsa udindo azichita zinthu mwachikondi ndi anthu amene akuwayang’anira. Iye amadana ndi nkhanza zokhudza kugonana ndipo amafuna kuti anthu onse, makamaka amene angaponderezedwe mosavuta, azitetezedwa komanso kuchitiridwa zinthu mwachilungamo.
CHILAMULO CHINALI ‘MTHUNZI WA ZINTHU ZABWINO ZIMENE ZINKABWERA’
25-26. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi ndi chilungamo zili ngati moyo ndi mpweya? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?
25 Chikondi ndi chilungamo zimayendera limodzi ngati moyo ndi mpweya padzikoli. China sichingakhalepo popanda chinzake. Tikamaona kuti Yehova amatichitira zinthu mwachilungamo timayamba kumukonda kwambiri. Ndipo tikamakonda Yehova ndi mfundo zake zachilungamo, timalimbikitsidwa kukonda anzathu komanso kuwachitira zinthu mwachilungamo.
26 Chilamulo cha Mose chinkathandiza kuti ubwenzi wa pakati pa Yehova ndi Aisiraeli ukhale wolimba. Koma Chilamulochi chinatha pamene Yesu anachikwaniritsa ndipo chinalowedwa m’malo ndi zinthu zina zabwino kwambiri. (Aroma 10:4) Mtumwi Paulo ananena kuti Chilamulo chinali ngati ‘mthunzi wa zinthu zabwino zimene zinkabwera.’ (Aheb. 10:1) Nkhani yotsatira idzafotokoza zina mwa zinthu zabwinozi komanso mmene tingasonyezere chikondi ndi chilungamo mumpingo wachikhristu.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima
a Iyi ndi nkhani yoyamba pa nkhani 4 zimene tikambirane zosonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri. Nkhani zina zidzatuluka mu Nsanja ya Olonda ya May 2019. Mitu ya nkhanizo ndi yakuti “Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo Mumpingo Wachikhristu,” “Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo M’dziko Loipali” ndiponso “Tizilimbikitsa Anthu Amene Achitiridwa Zoipa.”
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Malamulo oposa 600 amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose amatchedwa “Chilamulo,” “Chilamulo cha Mose” kapena “malamulo.” Mabuku oyambirira 5 a m’Baibulo (Genesis mpaka Deuteronomo) amatchedwanso Chilamulo. Nthawi zina mawu amenewa amagwiritsidwanso ntchito ponena za Malemba Achiheberi onse.
c CHITHUNZI PATSAMBA LOYAMBA: Yehova ankafuna kuti makolo azikonda ana awo komanso kuwaphunzitsa n’cholinga choti anawo azikhala otetezeka
MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mayi wachiisiraeli akucheza ndi ana ake uku akukonza chakudya. Chakumbuyo kwawo, bambo akuphunzitsa mwana wake kusamalira nkhosa.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Akulu apageti lamzinda akuthandiza mayi wamasiye ndi mwana wake amene aponderezedwa ndi munthu wabizinezi.