Madalitso Kapena Matemberero—Pali Chosankha!
“Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo.”—DEUTERONOMO 30:19.
1. Kodi anthu anapangidwa ndi kukhoza kotani?
YEHOVA MULUNGU anatipanga—zolengedwa zake zanzeru zaumunthu—kuti tikhale odzisankhira. Sitinalengedwe monga ziŵiya zodzichitira zinthu zosaganiza, kapena maloboti, koma tinapatsidwa mwaŵi ndi thayo la kudzisankhira. (Salmo 100:3) Anthu oyamba—Adamu ndi Hava—anali ndi ufulu wakusankha zochita zawo, ndipo anali ndi mlandu wodziŵerengera kwa Mulungu chifukwa cha chosankha chawo.
2. Kodi Adamu anapanga chosankha chotani, ndi chotulukapo chotani?
2 Mlengiyo wapereka madalitso osatha ochuluka pa moyo wa munthu m’paradaiso wa padziko lapansi. Kodi nchifukwa ninji chifuno chimenecho chili chosakwaniritsidwabe? Chifukwa chakuti Adamu anasankha molakwa. Yehova anapereka lamulo ili pa munthuyo: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Ngati Adamu akanasankha kumvera, makolo athu oyambawo akanadalitsidwa. Kusamvera kunabweretsa imfa. (Genesis 3:6, 18, 19) Chotero mbadwa za Adamu zonse anazipatsira uchimo ndi imfa.—Aroma 5:12.
Madalitso Achititsidwa Kukhala Otheka
3. Kodi Mulungu anapereka motani chitsimikiziro chakuti chifuno chake kwa anthu chidzakwaniritsidwa?
3 Yehova Mulungu anayambitsa njira mwa imene potsirizira pake chifuno chake kaamba ka kudalitsa anthu chidzakwaniritsidwamo. Iye mwiniyo ananeneratu za Mbewu, akumalosera mu Edene kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Pambuyo pake Mulungu analonjeza kuti madalitsowo adzafikira anthu omvera mwa njira ya Mbewu imeneyi, mbadwa ya Abrahamu.—Genesis 22:15-18.
4. Kodi Yehova wapanga makonzedwe otani odalitsira anthu?
4 Mbewu yolonjezedwa ya dalitsoyo inadzakhala Yesu Kristu. Ponena za mbali ya Yesu m’makonzedwe a Yehova odalitsira anthu, mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Anthu aja ochimwa amene amamvera Mulungu ndi kugwiritsira ntchito nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndiwo adzalandira madalitso. (Machitidwe 4:12) Kodi mudzasankha kumvera ndi madalitso? Kusamvera kudzabala kanthu kena kosiyana kwambiri.
Bwanji Nanga za Matemberero?
5. Kodi tanthauzo la liwu lakuti “temberero” nlotani?
5 Chinthu chosiyana ndi dalitso ndicho temberero. Liwulo “temberero” limatanthauza kunenera wina zoipa kapena kumuitanira tsoka. Liwu lachihebri lakuti qela·lahʹ latengedwa ku verebu yaikulu yakuti qa·lalʹ, kwenikweni lotanthauza “luluzika.” Komabe, pamene ligwiritsiridwa ntchito mophiphiritsira, limatanthauza ‘kuitanira tsoka pa’ kapena ‘kuchitira chipongwe.’—Levitiko 20:9, NW; 2 Samueli 19:43, NW.
6. Kodi ndi chochitika chotani m’nkhani ya Elisa chimene chinachitika pafupi ndi Beteli wakale?
6 Lingalirani za chitsanzo chochititsa chidwi cha kuchitapo kanthu panthaŵi yomweyo chonena za temberero. Zimenezi zinachitika pamene mneneri wa Mulungu Elisa anali paulendo kuchokera ku Yeriko kumka ku Beteli. Nkhaniyo imati: “Ndipo iye ali chikwerere m’njiramo, munatuluka anyamata aang’ono m’mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi! Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m’dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anayi mphambu aŵiri.” (2 Mafumu 2:23, 24) Mawu enieni amene Elisa ananena m’temberero limenelo loitanira tsoka pa ana osekawo samadziŵika. Komabe, mawu amenewo anabala zipatso chifukwa chakuti ananenedwa m’dzina la Yehova ndi mneneri wa Mulungu wochita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
7. Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa ana amene anaseka Elisa, ndipo chifukwa ninji?
7 Chifukwa chachikulu cha kusekako chichita ngati kuti chinali chakuti Elisa anali atavala chofunda cha Eliya chodziŵika cha udindo, ndipo anawo sanafune kuona woloŵa malo mneneri aliyense. (2 Mafumu 2:13) Kuti ayankhe kudereredwa kwake kwa kukhala woloŵa m’malo wa Eliya ndi kuphunzitsa ana ameneŵa ndi makolo awo ulemu woyenerera mneneri wa Yehova, Elisa anaitanira tsoka pa gulu losekalo m’dzina la Mulungu wa Eliya. Yehova anasonyeza kuvomereza kwake Elisa monga mneneri wake mwa kuchititsa zimbalangondo ziŵiri zazikazi kutuluka m’thengo ndi kupwetedza 42 a omsekawo. Yehova anachitapo kanthu motsimikizira chifukwa cha kupandiratu kwawo ulemu pa njira ya kulankhulana imene anali kugwiritsira ntchito padziko lapansi panthaŵiyo.
8. Kodi anthu a Israyeli anavomereza kuchitanji, ndipo ndi ziyembekezo zotani?
8 Zaka zambiri zimenezi zisanachitike, Aisrayeli anasonyeza kupanda ulemu kofananako kulinga ku makonzedwe a Mulungu. Zinachitika motere: Mu 1513 B.C.E., Yehova anasonyeza chiyanjo pa mtundu wa Israyeli mwa kuwalanditsa ku ukapolo wa Igupto monga ngati “pa mapiko a [chiombankhanga, NW].” Posapita nthaŵi pambuyo pake, iwo analonjeza kumvera Mulungu. Taonani mmene kumvera kunali kogwirizana mwamphamvu ndi kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu. Yehova kupyolera mwa Mose anati: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.” Pambuyo pake, mtunduwo unayankha motsimikiza, ukumati: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eksodo 19:4, 5, 8; 24:3) Aisrayeli ananena kuti anakonda Yehova, anadzipatulira kwa iye, ndipo anaŵinda kumvera mawu ake. Kuchita zimenezo kukanabweretsa madalitso aakulu.
9, 10. Kodi Aisrayeli anachitanji pamene Mose anali m’phiri la Sinai, ndipo ndi zotulukapo zotani?
9 Komano, mfundo zazikulu za panganolo zisanazokotedwe pamagome amiyala ndi “chala cha Mulungu,” matemberero a Mulungu anali ofunikira. (Eksodo 31:18) Kodi nchifukwa ninji chilango chotero chinafunikira? Kodi Aisrayeli sanasonyeze kufuna kuchita zonse zimene Yehova ananena? Inde, mu mawu iwo anafuna madalitso, koma anasankha njira imene inafunikira matemberero ndi zochita zawo.
10 Mkati mwa nyengo ya masiku 40 pamene Mose anali m’phiri la Sinai akumalandira Malamulo Khumi, Aisrayeli anaswa pangano lawo la kukhulupirika kwa Yehova. “Koma,” nkhaniyo imatero, “pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m’phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Aigupto, sitidziŵa chomwe chamgwera.” (Eksodo 32:1) Chimenechi chili chitsanzo china cha mzimu wopanda ulemu ku nthumwi zimene Yehova anali kugwiritsira ntchito panthaŵiyo kutsogolera ndi kulangiza anthu ake. Aisrayeli ananyengedwa kutsanzira kupembedza mafano kwa Aigupto ndipo anatuta zipatso zoŵaŵa pamene 3,000 a iwo anaphedwa ndi lupanga m’tsiku limodzi.—Eksodo 32:2-6, 25-29.
Chilengezo cha Madalitso ndi Matemberero
11. Kodi Yoswa anapereka malangizo otani ponena za madalitso ndi matemberero?
11 Zaka 40 za ulendo wa Israyeli m’chipululu zitatsala pang’ono kutha, Mose anafotokoza za madalitso amene adzawapeza mwa kusankha njira ya kumvera Mulungu. Anawatchuliranso za matemberero amene Aisrayeli adzalandira ngati adzasankha kusamvera Yehova. (Deuteronomo 27:11–28:10) Israyeli atangoloŵa kumene m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa anapereka malangizo a Mose okhudza madalitso ndi matemberero ameneŵa. Mafuko asanu ndi limodzi a Israyeli anaima mmunsi mwa phiri la Ebala, ndipo ena asanu ndi limodzi anaima pandunji pa phiri la Gerizimu. Alevi anaima m’chigwa chimene chinali pakati pake. Mafuko amene anaima pandunji pa phiri la Ebala angakhale atanena kuti “Amen!” pa matemberero amene anaŵerengedwa molunjikana nawo. Enawo anavomereza madalitso amene Alevi anawaŵerengera molunjikana nawo mmunsi mwa phiri la Gerizimu.—Yoswa 8:30-35.
12. Kodi ndi matemberero ena otani amene anatchulidwa ndi Alevi?
12 Tangoganizani kuti inu mukumva Alevi akunena kuti: “Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m’malo a m’tseri. . . . Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mayi wake. . . . Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. . . . Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m’njira. . . . Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. . . . Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. . . . Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. . . . Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. . . . Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. . . . Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m’tseri. . . . Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. . . . Wotembereredwa iye wosavomereza mawu a chilamulo ichi kuwachita.” Atatchula temberero lililonse, mafuko oima pandunji pa phiri la Ebala akunena kuti, “Amen”!—Deuteronomo 27:15-26.
13. Kodi mungafotokoze motani madalitso ena amene Alevi anawatchula m’mawu anu?
13 Tsono taganizani kuti mukumva awo amene aima pandunji pa phiri la Gerizimu akumavomereza mwamphamvu dalitso lililonse pamene Alevi akunena mokweza kuti: “Mudzakhala odala m’mudzi, ndi odala kubwalo. Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoŵeta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Zidzakhala zodala mtanga wanu, ndi choumbiramo mkate wanu. Mudzakhala odala poloŵa inu, mudzakhala odala potuluka inu.”—Deuteronomo 28:3-6.
14. Kodi Aisrayeli akanalandira madalitso pamaziko otani?
14 Kodi maziko a kulandira madalitso ameneŵa anali otani? Nkhaniyo imati: “Mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi; ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.” (Deuteronomo 28:1, 2) Inde, mfungulo yopezera madalitso a Mulungu inali kumvera Mulungu. Komano bwanji za ife lerolino? Kodi aliyense payekha adzasankha madalitso ndi moyo mwa kupitiriza ‘kumvera mawu a Yehova’?—Deuteronomo 30:19, 20.
Kuonetsetsa
15. Kodi ndi mfundo yotani imene inanenedwa pa dalitso lolembedwa pa Deuteronomo 28:3, ndipo tingapindule nayo motani?
15 Tiyeni tilingalire za madalitso ena amene Mwisrayeli akanakhala nawo chifukwa chomvera Yehova. Mwachitsanzo, Deuteronomo 28:3 amati: “Mudzakhala odala m’mudzi, ndi odala kubwalo.” Kudalitsidwa ndi Mulungu sikumadalira pa malo kapena gawo. Ena angamve kukhala atagwidwa m’mikhalidwe yawo, mwina chifukwa chakuti amakhala m’dera laumphaŵi kapena m’dziko losakazidwa ndi nkhondo. Ena angakhumbe kutumikira Yehova kumalo ena. Amuna ena achikristu angalefuke chifukwa chakuti sanaikidwe kukhala atumiki otumikira kapena kukhala akulu mumpingo. Nthaŵi zina, akazi achikristu amakhala osakondwa chifukwa chakuti sakhoza kuloŵa utumiki wanthaŵi yonse monga apainiya kapena amishonale. Komabe, aliyense ‘amene amamvera mawu a Yehova Mulungu kuchita malamulo ake onse’ adzadalitsidwa tsopano lino ndi kuumuyaya wonse.
16. Kodi pulinsipulo la pa Deuteronomo 28:4 likuchitika motani m’gulu la Yehova lerolino?
16 Deuteronomo 28:4 amati: “Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoŵeta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.” Kugwiritsiridwa ntchito kwa m’loŵa m’malo wachihebri ameneyo wotembenuzidwa “zanu” kumasonyeza kuti zimenezi zidzakhala chochitika cha munthu mwini kwa Mwisrayeli womvera. Bwanji nanga za atumiki a Yehova omvera lerolino? Chiwonjezeko chapadziko lonse ndi chifutukuko chimene chikuchitika m’gulu la Mboni za Yehova zili zotulukapo za dalitso la Mulungu pa zoyesayesa za olengeza mbiri yabwino ya Ufumu oposa 5,000,000. (Marko 13:10) Ndipo kuthekera kwa chiwonjezeko china chokulirapo nkwachionekere chifukwa chakuti oposa 13,000,000 anafika pa kusungidwa kwa Chakudya cha Madzulo cha Ambuye cha 1995. Kodi mukusangalala ndi madalitso a Ufumu?
Chosankha cha Israyeli Chinali Nkanthu
17. Kodi ‘kupezedwa’ ndi madalitso kapena matemberero kunadalira pa chiyani?
17 Kwenikweni, madalitso akanadza kwa Mwisrayeli womvera. Kunalonjezedwa kuti: “Madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani.” (Deuteronomo 28:2) Mofananamo, ananenanso za matemberero kuti: “Matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.” (Deuteronomo 28:15) Mukanakhala Mwisrayeli wa nthaŵi zakale, kodi ‘mukanapezedwa’ ndi madalitso kapena matemberero? Zimenezo zikanadalira pa kumvera kwanu Mulungu kapena pakusamumvera.
18. Kodi Aisrayeli akanapeŵa motani matemberero?
18 Pa Deuteronomo 28:15-68, zotulukapo zopweteka za kusamvera zafotokozedwa kukhala matemberero. Zina ndizo zosiyana kwambiri ndi madalitso a kumvera ofotokozedwa pa Deuteronomo 28:3-14. Kaŵirikaŵiri, anthu a Israyeli anatuta zipatso zoŵaŵa za matemberero chifukwa chakuti anasankha kulambira konyenga. (Ezara 9:7; Yeremiya 6:6-8; 44:2-6) Ha, nzachisoni chotani nanga! Akanapeŵa zotulukapo zimenezo mwa kupanga chosankha chabwino, chija cha kumvera malamulo ndi mapulinsipulo abwino a Yehova, amene amafotokoza momveka ponena za zabwino ndi zoipa. Lerolino ambiri amakumana ndi mavuto ndi tsoka chifukwa chakuti asankha kuchita mosiyana ndi mapulinsipulo a Baibulo mwa kutsatira chipembedzo chonyenga, kuchita chisembwere, kugwiritsira ntchito mankhwala oletsedwa, kumwetsa zakumwa zaukali, ndi zina zotero. Monga momwe zinalili mu Israyeli ndi Yuda wakale, kupanga zosankha zoipa zimenezo kumakwiyitsa Mulungu ndi kuvutika mtima kosayenera.—Yesaya 65:12-14.
19. Fotokozani mikhalidwe imene anapeza pamene Yuda ndi Israyeli anasankha kumvera Yehova.
19 Madalitso ambiri ndi bata zinalipo kokha pamene Israyeli anamvera Yehova. Mwachitsanzo, ponena za Mfumu Solomo, timaŵerenga kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera. . . . Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.” (1 Mafumu 4:20-25) Ngakhale m’nthaŵi ya Mfumu Davide, mmene analimbana kwambiri ndi adani a Mulungu, mtunduwo unali ndi thandizo ndi dalitso la Yehova pamene unasankha kumvera Mulungu wa choonadi.—2 Samueli 7:28, 29; 8:1-15.
20. Kodi Mulungu ali ndi chidaliro chotani ponena za anthu?
20 Kodi mudzamvera Mulungu, kapena simudzamumvera? Aisrayeli anali ndi chosankha. Ngakhale kuti tonsefe tili ndi choloŵa cha chikhoterero cha uchimo kuchokera kwa Adamu, talandiranso mphatso yaulere ya kusankha mwaufulu. Ngakhale kuti pali Satana, dziko loipali, ndi kupanda ungwiro kwathu, tingathe kupanga chosankha chabwino. Ndiponso, Mlengi wathu ali ndi chidaliro chakuti pamene tiyang’anizana ndi mayesero alionse, padzakhala awo amene amapanga chosankha chabwino, osati ndi mawu okha komanso ndi ntchito. (1 Petro 5:8-10) Kodi mudzakhala pakati pawo?
21. Kodi tidzapendanji m’nkhani yotsatira?
21 M’nkhani yotsatira, tidzakhala okhoza kupenda mikhalidwe yathu ndi machitidwe poyerekezera ndi zitsanzo zakale. Aliyense wa ife alabadiretu mothokoza mawu a Mulungu mwa Mose akuti: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo.”—Deuteronomo 30:19.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
◻ Kodi Yehova wachititsa motani madalitso kukhala otheka kwa anthu ochimwa?
◻ Kodi matemberero nchiyani?
◻ Kodi Aisrayeli akanalandira motani madalitso m’malo mwa matemberero?
◻ Kodi Israyeli anali ndi madalitso otani chifukwa cha kumvera Mulungu?
[Chithunzi patsamba 15]
Aisrayeli anaima pandunji pa phiri la Gerizimu ndi phiri la Ebala
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.