Khalani ndi Mtima Wovomerezeka kwa Yehova
“Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.”—SALMO 51:10.
1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi mtima wathu?
ANALI wamtali ndiponso wokongola. Mneneri Samueli atangomuona, anachita naye chidwi ndipo anaganiza kuti mwana wamwamuna woyamba wa Jese ameneyu ndi amene Mulungu anamusankha kuti akhale mfumu m’malo mwa Sauli. Koma Yehova anati: “Usayang’ane nkhope [ya mwana ameneyo], kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye; . . . munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” Yehova anasankha mwana wamwamuna womaliza wa Jese, Davide, amene anali “munthu wa pamtima pake.”—1 Samueli 13:14; 16:7.
2 Mulungu angadziŵe zimene zili m’mitima ya anthu, monga mmene kenako anafotokozera kuti: “Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndim’patse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.” (Yeremiya 17:10) Inde, “Yehova ayesa mitima.” (Miyambo 17:3) Koma kodi ndi mtima wanji wa munthu umene Yehova amayesa? Ndipo kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima wovomerezeka kwa iye?
“Munthu Wobisika Wamtima”
3, 4. Kodi liwu lakuti “mtima” m’Baibulo analigwiritsira ntchito makamaka m’lingaliro lotani? Perekani zitsanzo.
3 Liwu lakuti “mtima” limapezeka nthaŵi pafupifupi 1000 m’Malemba Opatulika. Malo ambiri analigwiritsa ntchito mophiphiritsa. Mwachitsanzo, Yehova anauza mneneri Mose kuti: “Lankhula ndi ana a Israyeli, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake um’funitsa mwini.” Ndipo amene anabweretsa zopereka, “anadza, aliyense wofulumidwa mtima.” (Eksodo 25:2; 35:21) Motero, mbali ina ya mtima wophiphiritsa ndiyo chilimbikitso—mphamvu yam’kati imene imatilimbikitsa kuchita zinthu. Mtima wathu wophiphiritsa umasonyezanso malingaliro athu, zokhumba zathu, ndiponso zinthu zimene timakonda kwambiri. Mtima ungadzaze ndi mkwiyo kapena mantha, ungavutike ndi nkhaŵa kapena kudzala ndi chimwemwe. (Salmo 27:3; 39:3; Yohane 16:22; Aroma 9:2) Ungakhale wonyada kapena wodzichepetsa, wachikondi kapena waudani.—Miyambo 16:5; Mateyu 11:29; 1 Petro 1:22.
4 Motero, “mtima” nthaŵi zambiri umagwirizana ndi chilimbikitso ndi mmene tikumvera mumtima mwathu, pamene “maganizo” nthaŵi zambiri amagwirizana ndi nzeru. Ameneŵa ndiwo matanthauzo a mawu aŵiriŵa akapezeka m’Lemba limodzimodzi. (Mateyu 22:37; Afilipi 4:7) Komabe mtima ndi maganizo si zosiyana kwenikweni. Mwachitsanzo, Mose anauza Aisrayeli kuti: “Mukumbukire m’mtima mwanu, [kapena, “mukumbukire m’maganizo mwanu,” NW mawu a m’munsi] kuti Yehova ndiye Mulungu.” (Deuteronomo 4:39) Yesu anauza alembi amene anali kufuna kumupha kuti: “Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m’mitima yanu?” (Mateyu 9:4) “Kumvetsa,” “kudziŵa,” ndi “kuganiza” zingagwirizanenso ndi mtima. (1 Mafumu 3:12; Miyambo 15:14; Marko 2: 6) Choncho, mtima wophiphiritsa ungaphatikizeponso nzeru, yomwe ili maganizo athu.
5. Kodi mtima wophiphiritsa umaimira chiyani?
5 Malinga ndi zomwe buku lina limanena, mtima wophiphiritsa umaimira “pakati penipeni pa chinthu. Motero, umatanthauza munthu wam’kati amene amadzionetsera m’zochita zake zosiyanasiyana, m’zokhumba zake, zimene amakonda, mmene akumvera mumtima mwake, zolinga zake, maganizo ake, nzeru zake, zimene akudziŵa, luso lake, zimene amakhulupirira, chikumbumtima chake.” Mtima umaimira zimene ife tili m’kati mwathu, “munthu wobisika wamtima.” (1 Petro 3:4) Zimenezo n’zimene Yehova amaona ndi kuyesa. N’chifukwa chake Davide anapemphera kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.” (Salmo 51:10) Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima woyera?
“Ikani Mitima Yanu” pa Mawu a Mulungu
6. Kodi Mose anawalangiza chiyani Aisrayeli atasonkhana pamodzi m’Chigwa cha Moabu?
6 Mose, polangiza ana a Israyeli amene anasonkhana m’Chigwa cha Moabu asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, anati: “Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi.” (Deuteronomo 32:46) Aisrayeli anafunika “kumvetsera mwatcheru.” (Knox) Akanatha kuphunzitsa ana awo malamulo a Mulungu kokha ngati makolowo akanadziŵa bwino malamulowo.—Deuteronomo 6:6-8.
7. Kodi ‘kuika mtima wathu’ pa Mawu a Mulungu kumafuna kuchitanji?
7 Chofunika kwambiri kuti tikhale ndi mtima woyera ndicho kudziŵa zolondola zokhudza zofuna ndi zolinga za Mulungu. Tingadziŵe zimenezo kudzera m’Mawu ouziridwa a Mulungu basi. (2 Timoteo 3:16, 17) Komabe, kungodziŵa kokha sikungatithandize kuti tikhale ndi mtima umene umakondweretsa Yehova. Kuti zimene tadziŵazo zikhudze umunthu wathu wam’kati, tiyenera ‘kuika mtima wathu’ kapena “kusunga mumtima,” zimene tikuphunzirazo. (Deuteronomo 32:46, An American Translation) Kodi tingachite bwanji zimenezo? Wamasalmo Davide akufotokoza kuti: “Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.”—Salmo 143:5.
8. Kodi tingasinkhesinkhe mafunso ati pamene tikuphunzira?
8 Ifenso tizisinkhasinkha moyamikira pa zimene Yehova amachita. Poŵerenga Baibulo kapena zofalitsa zofotokoza Baibulo, tifunika kusinkhasinkha mafunso onga aŵa: ‘Kodi zimenezi zikundiphunzitsanji za Yehova? Kodi ndi khalidwe la Yehova liti limene alisonyeza pamenepa? Kodi nkhani imeneyi ikundiphunzitsa chiyani chokhudza zinthu zimene Yehova amakondwera nazo ndi zimene amadana nazo? Kodi kuchita zimene Yehova amafuna kuli ndi zotsatira zotani poyerekeza ndi kuchita zimene iye amadana nazo? Kodi zimene ndaphunzirazi zikugwirizana motani ndi zimene ndikuzidziŵa kale?’
9. Kodi phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha n’zofunika motani?
9 Lisa wa zaka 32a akufotokoza mmene anayambira kuyamikira kufunika kophunzira n’cholinga ndiponso kusinkhasinkha. Akuti: “Nditabatizidwa mu 1994, ndinali wokangalika m’choonadi kwa zaka pafupifupi ziŵiri. Ndinali kupezeka pamisonkhano yonse yachikristu, ndinali kuthera maola 30 kapena 40 mu utumiki wakumunda mwezi uliwonse, ndipo ndinali kucheza ndi Akristu anzanga. Ndiyeno ndinayamba kubwerera mmbuyo. Ndinazilala kwambiri moti mpaka ndinaswa lamulo la Mulungu. Koma ndinazindikira kulakwa kwanga ndipo ndinaganiza za kukonzanso moyo wanga. Ndikusangalalatu kwambiri kuti Yehova anazindikira kulapa kwanga ndi kundilandiranso. Ndakhala ndikudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndinabwerera m’mbuyo?’ Yankho limene ndimalipeza nthaŵi zonse n’lakuti ndinanyalanyaza kuphunzira n’cholinga ndiponso kusinkhasinkha. Choonadi cha Baibulo sichinandifike mumtima. Kuyambira tsopano ndizichita phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha nthaŵi zonse.” Pamene tikupitiriza kudziŵa zambiri zokhudza Yehova, Mwana wake, ndi Mawu ake, n’kofunikatu kwambiri kupatula nthaŵi ya kusinkhasinkha kwaphindu.
10. N’chifukwa chiyani n’kofunika kuchita changu kupatula nthaŵi yochitira phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha?
10 M’dziko lino limene anthu amakhala otanganidwa, n’kovuta kupeza nthaŵi yophunzira ndi kusinkhasinkha. Komabe, Akristu lerolino ali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa lomwe lili dziko latsopano lolungama la Mulungu. (2 Petro 3:13) Zochitika zodabwitsa, monga kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu” ndi kuukira anthu a Yehova kwa “Gogi, wa ku dziko la Magogi,” zatsala pang’ono kuchitika. (Chivumbulutso 17:1, 2, 5, 15-17; Ezekieli 38:1-4, 14-16; 39:2) Zimene zili kutsogolo zingayese kukonda kwathu Yehova. Tsopano lino n’kofunika kuchitatu changu kupatula nthaŵi ndi kuika mtima wathu pa Mawu a Mulungu.—Aefeso 5:15, 16.
‘Konzekeretsani Mtima Wanu Kufuna Mawu a Mulungu’
11. Kodi mtima wathu tingaufanizire ndi nthaka motani?
11 Mtima wophiphiritsa tingaufanizire ndi nthaka mmene mbewu za choonadi zingabzalidwe. (Mateyu 13:18-23) Nthaka yeniyeni amaitipula, kuikonzekeretsa kuti mbewu zidzakule bwino. Mofananamo, tiyenera kukonzekeretsa mtima wathu kuti uthe kulandira bwino Mawu a Mulungu. Ezara wansembe “adaikiratu [“anakonzekeretsa,” NW] mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita.” (Ezara 7:10) Kodi tingaukonzekeretse bwanji mtima wathu?
12. Kodi n’chiyani chingathandize kukonzekeretsa mtima pofuna kuphunzira?
12 Kupemphera kochokera pansi pa mtima ndiko kukonzekeretsa mtima kwabwino kwambiri pamene tikufuna Mawu a Mulungu. Misonkhano yachikristu ya olambira oona imayamba ndi kumaliza ndi pemphero. N’koyeneratu kuti tizipemphera moona mtima tisanayambe phunziro la Baibulo laumwini ndiyeno n’kuchita mogwirizana ndi pempherolo m’kati mwa phunziro lonselo.
13. Kodi tichite chiyani kuti tikhale ndi mtima wovomerezeka kwa Yehova?
13 Mtima wophiphiritsa tiyenera kuukonzekeretsa kuti tichotse malingaliro amene tinali nawo kale. Atsogoleri a chipembedzo a m’nthaŵi ya Yesu sanafune kuchita zimenezi. (Mateyu 13:15) Koma Mariya, mayi ake a Yesu analingalira “mumtima mwake” choonadi chimene anamva. (Luka 2:19, 51) Anakhala wophunzira wokhulupirika wa Yesu. Lidiya wa ku Tiyatira anamvetsera zimene Paulo anali kunena, ndipo “mtima wake Ambuye anatsegula, kuti amvere.” Iyenso anakhala wokhulupirira. (Machitidwe 16:14, 15) Tisaumirire pa maganizo athu okha kapena ziphunzitso zomwe timazikonda. M’malo mwake, tiyeni tifunitsitse kulola kuti “Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama.”—Aroma 3:4.
14. Kodi tingaukonzekeretse bwanji mtima wathu kuti timvetsere pa misonkhano yachikristu?
14 Kukonzekeretsa mtima wathu kuti timvetsere pamisonkhano yachikristu n’kofunika kwambiri. Kuganiza zina kungatilepheretse kumvetsera mosamala zimene akukamba pa msonkhanopo. Zimene akukambazo sitingapindule nazo ngati tatanganidwa kuganiza zinthu zimene zachitika tsiku limenelo kapena kuganizira zimene tidzachite mawa. Tifunika kutsimikiza mtima kumvetsera ndi kuphunzira ngati tikufuna kuti tipindule ndi nkhani zimene akukambazo. Tidzapindulatu kwambiri ngati tikufunitsitsa kumvetsa malemba amene akuwafotokoza ndi kuwatanthauzira.—Nehemiya 8:5-8, 12.
15. Kodi kudzichepetsa kumatithandiza motani kuti tikhale ophunzitsika?
15 Monga mmene kulili kuti kuika zinthu zina zofunika m’nthaka kumawonjezera chonde, kudzichepetsa, kulakalaka zinthu zauzimu, kukhulupirira, kuopa ndi kukonda Mulungu zingawonjezerenso chonde cha mtima wathu wophiphiritsa. Kudzichepetsa kumafeŵetsa mtima, zimene zimatithandiza kukhala ophunzitsika. Yehova anauza mfumu yachiyuda Yosiya kuti: “Popeza mtima wako n’ngowoloŵa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera ine . . . ndi kulira misozi pamaso panga, inenso ndakumvera.” (2 Mafumu 22:19) Mtima wa Yosiya unali wodzichepetsa ndiponso womvera. Kudzichepetsa kunathandiza ophunzira a Yesu “osaphunzira ndi opulukira” kumvetsa ndi kugwiritsa ntchito choonadi chauzimu chimene anthu “anzeru ndi ozindikira” sanachimvetse. (Machitidwe 4:13; Luka 10:21) Tiyeni “tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu” pamene tikuyesetsa kuti tikhale ndi mtima wovomerezeka kwa Yehova.—Ezara 8:21.
16. Kodi n’chifukwa chiyani pamafunika khama kuti tikulitse chilakolako cha chakudya chauzimu?
16 Yesu ananena kuti: “Odala ali osauka mumzimu [“ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu,” NW]. (Mateyu 5:3) Ngakhale kuti tapatsidwa mwayi wodziŵa zinthu zauzimu, zochitika m’dziko loipa lino kapena ulesi zingatilepheretse kuzindikira zimene tikufunikira. (Mateyu 4:4) Tikulitsetu chilakolako chabwino cha chakudya chauzimu. Ngakhale kuti poyamba sizikutisangalatsa kuŵerenga Baibulo ndi kuchita phunziro laumwini, koma ngati tichita khama tidzaona kuti zimene tadziŵa ‘zidzakondweretsa moyo wathu,’ moti tidzafunitsitsa kuchita phunzirolo nthaŵi zonse.—Miyambo 2:10, 11.
17. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kumukhulupirira kotheratu? (b) Kodi tingatani kuti timukhulupirire kwambiri Mulungu?
17 Mfumu Solomo inalangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Mtima wokhulupirira Yehova umadziŵa kuti zimene Iye amatiuza kuti tichite kapena kutitsogolera kudzera m’Mawu ake ndi zolondola nthaŵi zonse. (Yesaya 48:17) Inde, Yehova ndi woyenera kum’khulupirira kotheratu. Iye amatha kukwaniritsa zolinga zake zonse. (Yesaya 40:26, 29) Ndipotu dzina lake lenilenilo limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala,” zimene zikutichititsa kukhulupirira kuti adzakwaniritsa zimene walonjeza. Iye ali “wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.” (Salmo 145:17) Inde, kuti timukhulupirire kwambiri, tifunika ‘kulaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino’ mwa kugwiritsa ntchito m’moyo wathu zimene tikuphunzira m’Baibulo ndiponso mwa kusinkhasinkha phindu la zimenezi.—Salmo 34:8.
18. Kodi kuopa Mulungu kumatithandiza motani kuti tithe kulandira malangizo ake?
18 Solomo, pofotokoza khalidwe linanso limene limachititsa mtima wathu kulandira malangizo a Mulungu, anati: “Opa Yehova, nupatuke pa zoipa.” (Miyambo 3:7) Yehova ponena za Israyeli wakale anati: “Ha! mwenzi akadakhala nawo mtima wotere wakundiopa ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana awo nthaŵi zonse!” (Deuteronomo 5:29) Inde, amene amaopa Mulungu, amamumvera. Yehova amatha “kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye” ndi kulanga anthu amene sakumumvera. (2 Mbiri 16:9) Kuopa kusakondweretsa Mulungu kutitsogolere pa zonse zimene timachita ndi kuganiza.
‘Kondani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse’
19. Kodi chikondi chimathandiza motani kuchititsa mtima wathu kulandira malangizo a Yehova?
19 Chikondi chimaposa makhalidwe ena onse pothandiza kuti mtima wathu uthe kumvera malangizo a Yehova. Mtima wokonda Mulungu umachititsa munthu kufunitsitsa kuphunzira zimene zimakondweretsa Mulungu ndi zimene sizimukondweretsa. (1 Yohane 5:3) Yesu anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Tiyeni timukonde kwambiri Mulungu mwa kusinkhasinkha ubwino wake nthaŵi zonse, mwa kulankhula naye nthaŵi zonse ngati bwenzi lapamtima, ndiponso mwa kuuza ena za iye mofunitsitsa.
20. Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima wovomerezeka kwa Yehova?
20 Mongobwereza zimene taphunzira, taona kuti: Kukhala ndi mtima wovomerezeka kwa Yehova kumafuna kulola kuti Mawu a Mulungu alimbikitse umunthu wathu wam’kati, munthu wobisika wamumtima. Phunziro laumwini la Malemba lokhala ndi cholinga ndiponso kusinkhasinkha moyamikira n’zofunika kwambiri. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiyenera kukonzekeretsa mtima wathu—kuchotsa malingaliro amene tinali nawo kale ndi kukhala ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tikhale ophunzitsika. Inde, ndi chithandizo cha Yehova, tingakhale ndi mtima movomerezeka kwa iye. Komabe, kodi tingatani kuti titchinjirize mtima wathu?
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha dzina.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi mtima wophiphiritsa umene Yehova amayesa n’chiyani?
• Kodi ‘tingaike mtima wathu’ pa Mawu a Mulungu motani?
• Kodi tingaukonzekeretse bwanji mtima wathu pofuna Mawu a Mulungu?
• Pamene mwamaliza kuphunzira nkhaniyi, kodi mukumva kuti yakulimbikitsani kuchita chiyani?
[Chithunzi patsamba 17]
Davide anali kusinkhasinkha moyamikira zinthu zauzimu. Kodi inunso mumatero?
[Zithunzi patsamba 18]
Konzekeretsani mtima wanu musanayambe kuphunzira Mawu a Mulungu