Kodi Chipembedzo Chikukhutiritsa Zosoŵa Zanu?
MPWEYA, madzi, chakudya, nyumba—zinthu zimenezi zimazindikiridwa padziko lonse kukhala zosoŵa za munthu. Popanda izo mungakhale aumphaŵi ndi kufa. Komabe, kalekale, mtsogoleri wina Wachiisrayeli Mose anasonyeza chosoŵa china cha munthu, chofunikadi kwambiri kuposa chakudya kapena madzi. Mose anati: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.”—Deuteronomo 8:3.
Ndi mawu atanthauzo lalikulu ameneŵa, Mose anasonyeza kufunika kwa kukhutiritsa zosoŵa zathu zachipembedzo kapena zauzimu. Iye anasonyeza kuti miyoyo yathu yeniyeniyo imadalira pa kuzikhutiritsa! Mkati mwa ulendo wawo wa m’chipululu wa zaka 40, Aisrayeli anakhaladi ndi moyo ndi “zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.” Iwo anapulumuka chimene mwina chikanakhala tsoka lochititsa imfa. Mulungu atalamula, chakudya china chotchedwa mana chinagwa mozizwitsa kuchokera kumwamba. Madzi anatuluka pamatanthwe kuthetsa ludzu lawo. Koma Mulungu anachita zoposa kugaŵira zosoŵa zawo zakuthupi. Mose anati: “Monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.”—Deuteronomo 8:4, 5; Eksodo 16:31, 32; 17:5, 6.
Aisrayeli sanangosiyidwa kuti azidziŵire okha ponena za chabwino kapena choipa, mwamakhalidwe kapena mwachipembedzo. Iwo analandira chitsogozo kuchokera kwa Mulungu mwini. Iye anawapatsa Chilamulo cha Mose, mpambo wa malamulo wapadera umene unandandalitsa chakudya chopatsa thanzi, malamulo ofunika kwambiri a ukhondo, ndi malamulo a mkhalidwe a makhalidwe abwino ndi chipembedzo. Chotero Mulungu anachirikiza ubwino wa Israyeli wa thanzi ndi wauzimu. Iwo anakhala ndi moyo ndi “zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.”
Motero Israyeli anakhala wosiyana kwambiri ndi mitundu ina. M’tsiku la Mose Igupto analamulira monga ulamuliro waukulu koposa wa dziko. Anali dziko lopembedza kwambiri. Buku lotchedwa World Book Encyclopedia likunena kuti: “Aigupto akale anakhulupirira kuti milungu yosiyanasiyana (milungu yachimuna ndi yachikazi) inasonkhezera mbali iliyonse ya chilengedwe ndi ntchito iliyonse ya munthu. Chifukwa chake iwo analambira milungu yambiri. . . . Mumzinda uliwonse ndi tauni ya Aigupto, anthu a mmenemo analambira mulungu wawo wapadera kuwonjezera pa milungu ina yaikulu.”
Kodi kulambira milungu yambirimbiri kumeneku kunakhutiritsa zosoŵa zauzimu za Aigupto? Ayi. Igupto anakhala dziko loyedzamira kwambiri pamatsenga ndi machitachita a kugonana koluluzika. Mmalo mochirikiza moyo ndi thanzi, moyo wa Aigupto unawatsogolera ku “nthenda zoipa.” (Deuteronomo 7:15) Pamenepa, mposadabwitsa kuti Baibulo linasimba za milungu ya Igupto moipidwa nayo, likumaitcha “mafano [onyansa].”—Ezekieli 20:7, 8.
Mkhalidwe wofananawo ulipo lerolino. Anthu ochuluka ali ndi chikhulupiriro cha chipembedzo chinachake; oŵerengeka okha anganene kuti ali osapembedza. Komabe, mwachionekere, chipembedzo kwakukulukulu chalephera kukhutiritsa zosoŵa zauzimu za mtundu wa anthu. Kodi mavuto a nkhondo, kusankhana mafuko, njala, ndi umphaŵi wosatha akanakhalapo lerolino ngati anthu akanakhaladi ndi moyo “ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova”? Kutalitali! Komabe ngakhale zili choncho, anthu oŵerengeka okha ndiwo angalingalire zosintha chipembedzo chawo. Eetu, ena samafuna ngakhale kukambitsirana chabe nkhani yachipembedzo kapena kumvetsera malingaliro ena achipembedzo atsopano!
Mwachitsanzo, mwamuna wina wa ku Ghana, West Africa, anauza mtumiki wina Wachikristu kuti: “Ndikhulupirira kuti Mulungu wadzivumbula yekha kwa anthu a mu Afirikafe kupyolera mwa ansembe athu achimuna ndi achikazi amphamvu, monga momwedi anadzivumbulira kwa Ayuda kupyolera mwa aneneri awo. Nkomvetsa chisoni kuti ena a anthu a mu Afirikafe timalephera kuvomereza ansembe athu koma mmalo mwa amenewo timalankhula za Yesu, Muhammad, ndi ena.”
M’zitaganya zambiri za mwambo za mu Afirika, Chikristu chimaonedwa monga chipembedzo cha azungu—chipembedzo choloŵetsedwa kuchokera kwina chimene chavulaza anthu mmalo mwa kuwachitira zabwino. Koma kodi mkhalidwe wa maganizo wotsekereza malingaliro ena udzakuthandizani kapena udzadodometsa zoyesayesa zanu za kukhutiritsa zosoŵa zanu zauzimu? Mwambi wina wa mu Afirika umati: “Usaloŵetse manja onse m’mbizi ya chakudya kokha chifukwa chakuti uli ndi njala.” Chizoloŵezi cha kadyedwe chotero chili ponse paŵiri chopanda ulemu ndi chaupandu—makamaka ngati inu simudziŵa chimene chili m’mbiziyo! Komabe, ambiri amasankha chipembedzo chawo, osati pamaziko a kupenda mosamalitsa, koma pamaziko a kutengeka maganizo kapena a mwambo wabanja.
Kulambira kumene kumakhutiritsa zosoŵa zanu zauzimu kuyenera kukhala “utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kuganiza.” (Aroma 12:1, NW) Kuyenera kukhala chosankha chozindikiridwa bwino, chanzeru. Chifukwa chake tiyeni tipende nkhani ya kusankha chipembedzo cha munthu tili ndi lingaliro la munthu wa mu Afirika. Komabe, zimene zikutsatirazo zidzakhala zokondweretsa kwa oŵerenga okhala kulikonse.
[Chithunzi patsamba 3]
Mose anasonyeza kufunika kwa kukhutiritsa chosoŵa chathu chauzimu
[Chithunzi patsamba 4]
Zochitika za amishonale a Dziko Lachikristu mu Afirika zatsekereza maganizo a ena kudziŵa za Baibulo