MUTU 11
“Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zopanda chilungamo ziti zimene zinachitikira Yosefe? (b) Kodi Yehova anachita chiyani pothetsa zinthu zopanda chilungamozo?
MNYAMATA wina anachitiridwa zinthu zomwe sizinali zachilungamo ngakhale pang’ono. Mnyamata ameneyu anali wooneka bwino kwambiri ndipo sanalakwe chilichonse, koma anali m’ndende chifukwa chomunamizira kuti ankafuna kugwiririra mkazi. Komatu aka sikanali koyamba kuti achitiridwe zinthu zopanda chilungamo. M’mbuyomo ali ndi zaka 17, mnyamatayu yemwe dzina lake ndi Yosefe, azichimwene ake enieni ankafuna kumupha ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo kudziko lina. Kumeneko mkazi wa abwana ake ankamunyengerera kuti agone naye koma iye anakana. Mkaziyo ataona kuti Yosefe wamukana, anamunamizira kuti amafuna kumugwiririra ndipo zimenezi ndi zimene zinachititsa kuti atsekeredwe m’ndende. Zinali zomvetsa chisoni chifukwa zinkaoneka ngati palibe aliyense amene akanamuthandiza.
2 Komabe, Mulungu yemwe “amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera” ankaona zonsezo. (Salimo 33:5) Yehova anachitapo kanthu kuti athetse zinthu zopanda chilungamozo ndipo Yosefe anamasulidwa. Kuwonjezera pamenepo, Yosefe yemwe anali mkaidi, anapatsidwa udindo waukulu kwambiri ndiponso ulemu wapadera. (Genesis 40:15; 41:41-43; Salimo 105:17, 18) Pamapeto pake anthu anadziwa kuti Yosefe analibe mlandu ndipo iye anagwiritsa ntchito udindo wake wapamwambawu pothandiza kuti zofuna za Mulungu zichitike.—Genesis 45:5-8.
Yosefe anakumana ndi zinthu zopanda chilungamo m’ndende
3. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti tonsefe timafuna kuti tizichitiridwa zinthu mwachilungamo?
3 Nkhani ya Yosefe imatilimbikitsa kwambiri chifukwa tonsefe ena anatichitirapo zinthu zopanda chilungamo kapena tinaonapo ena zikuwachitikira. Zoonadi, aliyense amafuna azichitiridwa zinthu moyenera komanso mosakondera. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Yehova anatilenga m’njira yoti tizisonyeza makhalidwe ake, ndipo chilungamo ndi limodzi mwa makhalidwe ake akuluakulu. (Genesis 1:27) Kuti timudziwe bwino Yehova, tifunika kumvetsa mmene amaonera chilungamo. Zimenezi zingatithandize kuti tiyambe kusangalala ndi mmene amachitira zinthu komanso kuti akhale mnzathu wapamtima.
Kodi Chilungamo N’chiyani?
4. Kodi nthawi zambiri anthu amaona kuti chilungamo n’chiyani?
4 Nthawi zambiri anthu amaona kuti chilungamo ndi kugwiritsa ntchito malamulo mosakondera. Buku lina limanena kuti “chilungamo chimakhudza malamulo, zimene munthu amaloledwa kuchita, zimene ayenera kuchita ndiponso mfundo yoti munthu ayenera kupatsidwa mphoto kapena kulangidwa pa zimene wachita.” (Right and Reason—Ethics in Theory and Practice) Koma chilungamo cha Yehova sichimangotanthauza kugwiritsa ntchito malamulo chifukwa choti akufunika kugwira ntchito kapenanso chifukwa choti iye ali ndi udindo wogwiritsa ntchito malamulowo.
5, 6. (a) Kodi mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawamasulira kuti “chilungamo” amatanthauza chiyani? (b) Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Mulungu ndi wachilungamo?
5 Tingamvetse bwino chilungamo cha Yehova tikaganizira mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawagwiritsa ntchito m’Baibulo pofotokoza mawu akuti chilungamo. Mawu amene anawagwiritsa ntchitowa angatanthauze “zoyenera” kapena “kuchita zabwino.”—Genesis 18:25; Amosi 5:24.
6 Choncho Baibulo likamanena kuti Mulungu ndi wachilungamo, limasonyeza kuti iye amachita zinthu zoyenera ndipo nthawi zonse amazichita mopanda tsankho. (Aroma 2:11) Sitingayembekezere kuti iye angachite zosiyana ndi zimenezi. Elihu, yemwe anali wokhulupirika, anati: “N’zosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.” (Yobu 34:10) N’zosathekadi kuti Yehova achite zinthu zopanda chilungamo. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa ziwiri zikuluzikulu.
7, 8. (a) N’chifukwa chiyani Yehova sangachite zinthu zopanda chilungamo? (b) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azichitira anthu zinthu zachilungamo?
7 Choyamba, iye ndi woyera. Monga tinaonera m’Mutu 3, Yehova ndi woyera kwambiri ndiponso wolungama. Choncho sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Popeza Yehova yemwe ndi Bambo athu ndi woyera, tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti sangatichitire zoipa. Yesu ankakhulupirira kwambiri zimenezi. Pa usiku wake womaliza padzikoli, anapemphera kuti: “Atate Woyera, ayang’anireni (kutanthauza ophunzira ake) chifukwa cha dzina lanu.” (Yohane 17:11) M’Malemba, ndi Yehova yekha amene amatchulidwa kuti “Atate Woyera.” Zimenezi n’zoyenera, chifukwa palibe bambo aliyense amene angafanane ndi Yehova pa nkhani yokhala woyera. Yesu ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova, yemwe ndi woyera pa chilichonse ndipo alibiretu uchimo, adzateteza ophunzira ake.—Mateyu 23:9.
8 Chachiwiri, Mulungu ndi wosadzikonda ndipo nthawi zonse amasonyeza chikondi. Chikondi chimenechi chimamupangitsa kuti azichitira ena zinthu mwachilungamo. Koma anthu opanda chilungamo amachitira ena zoipa chifukwa cha dyera komanso kudzikonda, zomwe ndi zosiyana ndi chikondi. Ponena za Mulungu wachikondi, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ndi wolungama. Iye amakonda ntchito zolungama.” (Salimo 11:7) Ponena za iyeyo, Yehova anati: “Ine Yehova ndimakonda chilungamo.” (Yesaya 61:8) Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu wathu amasangalala kuchita zoyenera, kapena kuti zachilungamo?—Yeremiya 9:24.
Chifundo Ndiponso Chilungamo cha Yehova
9-11. (a) Kodi chilungamo cha Yehova chimagwirizana bwanji ndi chifundo chake? (b) Kodi mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa zimasonyeza bwanji kuti ndi wachilungamo ndiponso wachifundo?
9 Mofanana ndi ena mwa makhalidwe, Yehova amasonyeza chilungamo m’njira yabwino kwambiri. Mose anatamanda Yehova kuti: “Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita zinthu zopanda chilungamo. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” (Deuteronomo 32:3, 4) Nthawi zonse Yehova akamasonyeza chilungamo, salakwitsa zinazake. Iye si wolekerera komanso sachita zinthu mwankhanza.
10 Chilungamo cha Yehova n’chogwirizana kwambiri ndi chifundo chake. Lemba la Salimo 116:5 limati: “Yehova ndi wokoma mtima komanso wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo.” Zoonadi, Yehova ndi wachifundo ndiponso wachilungamo. Makhalidwe awiriwa si otsutsana. Yehova akasonyeza chifundo, sizitanthauza kuti akanapanda kuchita zimenezi chilungamo chake chikanachititsa kuti apereke chiweruzo chokhwima. M’malomwake, iye amasonyeza makhalidwe awiri onsewa pa nthawi imodzi. Taganizirani chitsanzo ichi.
11 Tonsefe tinatengera uchimo kwa Adamu, choncho timayenera kulandira chilango cha uchimowo chomwe ndi imfa. (Aroma 5:12) Koma Yehova sasangalala ndi imfa ya anthu ochimwa. Iye ndi ‘Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo ndiponso wachifundo.’ (Nehemiya 9:17) Komabe popeza ndi woyera, sangalekerere zinthu zosalungama. Ndiye kodi angasonyeze bwanji chifundo kwa anthu omwe anatengera uchimo? Mfundo ina yofunika kwambiri ya choonadi yopezeka m’Mawu a Mulungu imatithandiza kupeza yankho. Mfundoyi ndi yakuti Yehova anapereka dipo kuti apulumutse anthu. Tidzaphunzira zambiri pa nkhaniyi m’Mutu 14. Zimene Yehova anachitazi zimasonyeza kuti ndi wachilungamo komanso wachifundo kwambiri. Pogwiritsa ntchito dipoli iye angachitire chifundo anthu ochimwa omwe alapa, kwinaku akutsatirabe mfundo zake zokhudza chilungamo.—Aroma 3:21-26.
Chilungamo cha Yehova Chimatichititsa Kuti Tizimukonda
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilungamo cha Yehova chimatichititsa kuti tizifuna kuti akhale mnzathu? (b) Kodi Davide ananena chiyani zokhudza chilungamo cha Yehova, nanga zimenezi zingatilimbikitse bwanji?
12 Chilungamo cha Yehova sichichititsa kuti tizichita naye mantha, koma ndi khalidwe labwino limene limatichititsa kufuna kuti akhale mnzathu. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova amasonyeza chilungamo chake mwachifundo. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina zolimbikitsa pa nkhaniyi.
13 Chilungamo cha Yehova, chomwe amachisonyeza mosalakwitsa chilichonse, chimamuchititsa kukhala wokhulupirika kwa atumiki ake. Wolemba masalimo Davide anaona umboni wa zimenezi. Kuchokera pa zimene zinamuchitikira ndiponso zimene anaphunzira zokhudza Yehova, iye anati: “Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Salimo 37:28) Amenewatu ndi mawu olimbikitsa kwambiri. Mulungu wathu sadzasiya ngakhale pang’ono atumiki ake okhulupirika. Choncho tingamukhulupirire kuti amakhala nafe pafupi komanso amatikonda. Izi zili choncho chifukwa choti iye ndi wachilungamo.—Miyambo 2:7, 8.
14. Kodi Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli chimasonyeza bwanji kuti iye amadera nkhawa anthu ovutika?
14 Chilungamo cha Mulungu chimamuchititsa kuti azichita zinthu moganizira anthu ovutika. Mfundo yoti Yehova amadera nkhawa anthu ovutika imaoneka bwino m’Chilamulo chimene anapatsa Aisiraeli. Mwachitsanzo, m’Chilamulochi munali malamulo apadera omwe ankathandiza kuti akazi amasiye ndi ana amasiye azisamaliridwa. (Deuteronomo 24:17-21) Podziwa kuti moyo wa mabanja amenewa umakhala wovuta, Yehova, yemwe “amachitira chilungamo ana amasiye ndi akazi amasiye,”a anakhala Woweruza wawo ndiponso Bambo wowateteza. (Deuteronomo 10:18; Salimo 68:5) Yehova anachenjeza Aisiraeli kuti ngati angazunze akazi ndi ana opanda owateteza, adzamva kulira kwawo. Iye anati: “Mkwiyo wanga udzakuyakirani.” (Ekisodo 22:22-24) Ngakhale kuti kukwiya si limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yehova, chilungamo chake chimamuchititsa kukwiya ngati mwadala anthu akuchitira ena zinthu zopanda chilungamo, makamaka otsika ndiponso osowa owathandiza.—Salimo 103:6.
15, 16. Fotokozani mfundo yochititsa chidwi yosonyeza kuti Yehova alibe tsankho.
15 Yehova amatitsimikiziranso kuti “sakondera munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.” (Deuteronomo 10:17) Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amene ali ndi udindo kapena mphamvu amachita, Yehova sakopeka ndi chuma kapena mmene munthu akuonekera. Iye sakondera komanso alibe tsankho ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo yochititsa chidwi iyi yosonyeza kuti zimenezi ndi zoona. Mwayi wokhala atumiki ake, omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha, sunaperekedwe kwa anthu apadera ochepa okha. M’malomwake, “iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Munthu aliyense angakhale ndi chiyembekezo chimenechi mosatengera kuti ndi wotani, ali ndi khungu lamtundu wanji komanso amachokera dziko liti. Kodi chilungamo chingapose pamenepa?
16 Palinso njira ina imene Yehova amasonyezera chilungamo chake yomwenso tiyenera kuiganizira. Njirayi ndi yokhudza mmene amachitira zinthu ndi anthu amene aphwanya mfundo zake zachilungamo.
Amapereka Chilango
17. Fotokozani chifukwa chake zoipa zomwe zikuchitika m’dzikoli si umboni wakuti Yehova si wachilungamo.
17 Ena angafunse kuti: ‘Popeza Yehova sasangalala ndi zinthu zopanda chilungamo, nanga n’chifukwa chiyani masiku ano anthu osalakwa akuvutika komanso makhalidwe oipa ali paliponse m’dzikoli?’ Komatu zoipa zimenezi si umboni wakuti Yehova si wachilungamo. Zinthu zambiri zopanda chilungamo zomwe zimachitika m’dziko loipali ndi zotsatirapo za uchimo womwe anthu anatengera kwa Adamu. M’dzikoli mumachitika zinthu zopanda chilungamo chifukwa choti anthu ambiri asankha kumachita zoipa, komabe zimenezi zitha posachedwapa.—Deuteronomo 32:5.
18, 19. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova sadzalekerera mpaka kalekale anthu amene amaphwanya mwadala malamulo ake olungama?
18 Ngakhale kuti Yehova amasonyeza chifundo chachikulu kwa anthu amtima wabwino omwe akufuna kukhala anzake, sadzalola kuti dzina lake lizinyozedwa mpaka kalekale. (Salimo 74:10, 22, 23) Mulungu wachilungamo sapusitsika ndipo sadzalola kuti anthu omwe samumvera mwadala asalandire chilango chomwe akuyenera kulandira. Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi, . . . koma sadzalekerera wolakwa osam’patsa chilango.” (Ekisodo 34:6, 7) Mogwirizana ndi mawu amenewa, nthawi zina Yehova amaona kuti m’pofunika kulanga anthu amene amaphwanya mwadala malamulo ake olungama.
19 Mwachitsanzo, taganizirani za Aisiraeli. Nthawi zambiri ankachita zinthu zosakhulupirika ngakhale pamene anakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Zochita zawo zoipa ‘zinkakhumudwitsa’ Yehova, komabe iye sanawasiye nthawi yomweyo. (Salimo 78:38-41) M’malomwake, ankawachitira chifundo ndipo ankawapatsa mwayi woti asinthe zochita zawo. Anawachonderera kuti: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa asinthe zochita zake n’kupitiriza kukhala ndi moyo. Bwererani! Bwererani n’kusiya zinthu zoipa zimene mukuchita. Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?” (Ezekieli 33:11) Poona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, Yehova anatumiza aneneri ake mobwerezabwereza kuti mwina Aisiraeli angasiye makhalidwe awo oipa. Koma ambiri anaumitsa mitima yawo ndipo sanalape. Pamapeto pake Yehova anawapereka m’manja mwa adani awo pofuna kuteteza dzina lake loyera komanso zonse zimene dzinalo limaimira.—Nehemiya 9:26-30.
20. (a) Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? (b) N’chifukwa chiyani n’zoyenera kuti mkango ndi chizindikiro cha chilungamo cha Yehova?
20 Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? Tikuphunzira kuti maso ake omwe amaona chilichonse, amaonanso zinthu zosalungama ndipo zimene amaonazo zimamukhudza kwambiri. (Miyambo 15:3) N’zolimbikitsanso kudziwa kuti amasonyeza chifundo ngati pali chifukwa chochitira zimenezi. Komanso tikuphunzirapo kuti amaleza mtima ndipo amapereka mwayi kwa anthu kuti asinthe. Chifukwa choti Yehova ndi woleza mtima, anthu ambiri amaganiza molakwika kuti sadzaweruza anthu oipa. Koma zimenezi si zoona, chifukwa mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi Aisiraeli zimatiphunzitsanso kuti kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Nthawi zonse Yehova amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Mosiyana ndi anthu, omwe nthawi zambiri amalephera kuchita chilungamo, Yehova amalimba mtima n’kuchita zinthu mwachilungamo. Mpake kuti Baibulo limagwiritsa ntchito mkango, womwe ndi nyama yolimba mtima, ngati chizindikiro cha chilungamo cha Yehova.b (Ezekieli 1:10; Chivumbulutso 4:7) Choncho tisamakayikire kuti adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzachotsa zinthu zopanda chilungamo padzikoli. Mwachidule tinganene kuti iye amaweruza chonchi: amachita zinthu molimba mtima pamene pakufunika kutero, ndipo amasonyeza chifundo ngati zingatheke.—2 Petulo 3:9.
Yesetsani Kuti Mulungu Wachilungamo Akhale Mnzanu
21. Tikamaganizira mmene Yehova amasonyezera chilungamo, kodi tizimuona kuti ndi wotani, nanga n’chifukwa chiyani?
21 Tikamaganizira mmene Yehova amasonyezera chilungamo, tisamaone kuti iye ali ngati woweruza wosaganizira ena yemwe amangofuna kupereka chilango kwa olakwa. M’malomwake, tizimuona ngati bambo wachikondi koma wolimba mtima, amene nthawi zonse amachita zinthu ndi ana ake m’njira yabwino kwambiri. Popeza Yehova ndi Bambo wachilungamo, sasunthika pa nkhani yochita chilungamo koma pa nthawi imodzimodziyo amasonyezanso chifundo kwa ana ake apadziko lapansi, omwe amafunika kuwathandiza ndiponso kuwakhululukira.—Salimo 103:10, 13.
22. Chifukwa cha chilungamo chake, kodi Yehova anakonza zoti tikhale ndi chiyembekezo chotani, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
22 Tikuthokoza chifukwa sikuti Mulungu amasonyeza chilungamo chake polanga anthu olakwa basi. Chifukwa cha chilungamo chake, Yehova anakonza zoti tiziyembekezera kudzakhala ndi moyo wangwiro komanso wosatha m’dziko limene ‘mudzakhale chilungamo.’ (2 Petulo 3:13) Zimenezi zikusonyeza kuti chifukwa choti Yehova ndi wachilungamo, amafuna kupulumutsa anthu, osati kuwalanga. Zoonadi, tikamvetsa bwino zokhudza chilungamo cha Yehova, timafunitsitsa kuti akhale mnzathu. M’mitu yotsatirayi, tiphunzira mmene Yehova amasonyezera khalidwe labwino kwambiri limeneli.
a Mawu akuti “mwana wamasiye” akusonyeza kuti Yehova amadera nkhawa kwambiri ana onse amasiye, kaya aamuna kapena aakazi. Yehova anaonetsetsa kuti m’Chilamulo mwalembedwa zokhudza chigamulo chomwe chinaperekedwa pa nkhani ya ana aakazi a Tselofekadi omwe anali amasiye. Chigamulo chimenechi chinakhala lamulo ndipo chinkateteza ufulu wa ana aakazi amasiye.—Numeri 27:1-8.
b N’zochititsa chidwi kuti Yehova anadziyerekezera ndi mkango pamene ankapereka chiweruzo kwa Aisiraeli osakhulupirika.—Yeremiya 25:38; Hoseya 5:14.