Muziphunzitsa Ana Anu Aang’ono Kuti Azitumikira Yehova
“Lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”—OWER. 13:8.
1. Kodi Manowa anachita chiyani atauzidwa kuti adzakhala ndi mwana?
MKAZI wa Manowa anali wosabereka koma tsiku lina anauza mwamuna wake nkhani yodabwitsa. Mngelo wa Yehova anali atamuuza kuti adzakhala ndi mwana. Manowa ayenera kuti anasangalala kwambiri atauzidwa nkhaniyi, koma ankaganiziranso udindo waukulu wolera mwanayo. Pa nthawiyo, Aisiraeli ambiri ankachita zoipa choncho zinali zovuta kuti alere bwino mwana wawo. Ndiyeno Manowa anachonderera Yehova ponena kuti: “Lolani kuti munthu wa Mulungu woona [mngeloyo] amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”—Ower. 13:1-8.
2. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo? (Onani bokosi lakuti, “Anthu Ofunika Kwambiri Kuwaphunzitsa Baibulo.”)
2 Ngati muli ndi ana muyenera kuti mukumvetsa zimene Manowa anapemphazi. Inunso muli ndi udindo waukulu wothandiza ana anu kudziwa Yehova ndiponso kumukonda. (Miy. 1:8) Choncho muyenera kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse. Koma kungophunzitsa ana kamodzi pa mlungu si kokwanira. Pali zinthu zambiri zimene makolo ayenera kuchita pothandiza ana awo kuti mfundo za m’Baibulo ziziwafika pamtima. (Werengani Deuteronomo 6:6-9.) M’nkhaniyi ndiponso yotsatira tiona zimene makolo angachite potsanzira Yesu. N’zoona kuti Yesu analibe mwana koma makolo angaphunzire zambiri pa chitsanzo chake. Yesu ankaphunzitsa ophunzira ake mwachikondi, modzichepetsa ndiponso mozindikira. Tiyeni tikambirane zimene tingachite pomutsanzira.
MUZIKONDA ANA ANU
3. Kodi Yesu ankasonyeza bwanji kuti ankakonda ophunzira ake?
3 Yesu ankakonda kuuza ophunzira ake kuti amawakonda. (Werengani Yohane 15:9.) Iye ankasonyezanso chikondi pocheza nawo kawirikawiri. (Maliko 6:31, 32; Yoh. 2:2; 21:12, 13) Sikuti ankangokhalira kuwapatsa malangizo koma ankamasuka nawo. Choncho iwo sankakayikira kuti iye amawakondadi. Kodi inuyo mungatsanzire bwanji Yesu pa nkhani imeneyi?
4. Kodi mungatani kuti ana anu azidziwa kuti mumawakonda? (Onani chithunzi patsamba 3.)
4 Nanunso muziuza ana anu kuti mumawakonda ndiponso mumawaona kuti ndi ofunika kwambiri. (Miy. 4:3; Tito 2:4) M’bale wina wa ku Australia dzina lake Samuel ananena kuti: “Ndili mwana, bambo anga ankandiwerengera Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo tsiku lililonse ndisanakagone ndiponso kuyankha zimene ndinkawafunsa. Kenako ankandikumbatira n’kundigoneka. Ndinadabwa nditamva kuti makolo awo sankawachitira zimenezi. Koma iwo ankayesetsa kundisonyeza chikondi. Zimenezi zinachititsa kuti tizikondana kwambiri ndipo ndinkamva kuti ndine wotetezeka komanso ndinkasangalala.” Ana anunso akhoza kumamva choncho mukamawauza kuti mumawakonda. Muziwasonyeza chikondi pocheza nawo, kudya nawo ndiponso kusewera nawo.
5, 6. (a) Kodi Yesu amachita chiyani kwa anthu amene amawakonda? (b) Kodi kulangiza ana mwachikondi kumawathandiza bwanji?
5 Yesu ananena kuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.”a (Chiv. 3:19) Ngakhale kuti ophunzira ake ankakangana mobwerezabwereza kuti wamkulu ndani, Yesu sanasiye kuwathandiza. Pamene ankalephera kutsatira malangizo ake, iye ankasankha nthawi ndi malo abwino kuti awalangize mwachikondi ndiponso mofatsa.—Maliko 9:33-37.
6 Nanunso muzisonyeza kuti mumakonda ana anu powalangiza. Nthawi zina mukhoza kungowafotokozera ubwino ndi kuipa kwa zinthu zina. Koma nthawi zina ana amalephera kutsatira zimene mwawauza. (Miy. 22:15) Zimenezi zikachitika muzitsanzira Yesu. Muzisankha nthawi ndi malo abwino kuti muwalangize mwachikondi ndiponso mofatsa. Mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Elaine ananena kuti: “Makolo anga sankasinthasintha popereka malangizo. Akanena kuti andipatsa chilango chinachake ndikalakwa, ankachitadi zomwezo. Koma sankandilanga atapsa mtima ndipo nthawi zonse ankandiuza chifukwa chimene akuperekera chilangocho. Izi zinandithandiza kudziwa kuti makolo anga amandikonda. Ndinkadziwanso bwino zimene ndiyenera kuchita komanso zimene sindiyenera kuchita.”
MUZISONYEZA KUTI NDINU WODZICHEPETSA
7, 8. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa popemphera? (b) Kodi mapemphero anu angathandize bwanji ana kuti azidalira Mulungu?
7 Yesu atatsala pang’ono kuphedwa anapemphera kuti: “Abba, Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”b (Maliko 14:36) Kodi mukuganiza kuti ophunzira a Yesu anamva bwanji atadziwa zimene Yesu anapemphazi? Iwo ayenera kuti anazindikira zoti ngati Mwana wa Mulungu wangwiro anapempha thandizo modzichepetsa, nawonso ayenera kuchita zimenezi.
8 Kodi ana anu amaphunzira chiyani akamva mapemphero anu? N’zoona kuti cholinga cha pemphero si kuphunzitsa ana. Koma mukamapemphera modzichepetsa, anawo amazindikira kuti ayenera kudalira Yehova. Mlongo wina wa ku Brazil dzina lake Ana anati: “Agogo akadwala, kapena pakakhala vuto lililonse, makolo anga ankapempha Yehova kuti awapatse mphamvu kuti apirire vutolo komanso azisankha zochita mwanzeru. Ngakhale pamene apanikizika kwambiri ankaonetsetsa kuti atulira Yehova nkhawa zawo. Izi zinandithandiza kuti nanenso ndizidalira Yehova.” Mukamapemphera limodzi ndi ana anu musamangowapempherera iwowo, koma muzipemphanso Yehova kuti akuthandizeni inuyo. Mwachitsanzo, mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kupempha abwana anu kuti mupite kumsonkhano kapena kuti mulimbe mtima n’kulalikira anthu amene mwayandikana nawo nyumba. Mukamadalira Yehova modzichepetsa, ana anu akhoza kuchitanso chimodzimodzi.
9. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji ophunzira ake kuti azitumikira ena modzichepetsa? (b) Kodi ana angaphunzire chiyani akaona kuti mumayesetsa kuthandiza anthu ena?
9 Zimene Yesu ankachita komanso kulankhula, zinkathandiza ophunzira ake kudziwa kuti ayenera kutumikira ena modzichepetsa. (Werengani Luka 22:27.) Iye anaphunzitsa atumwi ake kuti ayenera kudzipereka potumikira Yehova komanso Akhristu anzawo. Nanunso mukhoza kuphunzitsa ana anu ngati mumachita zinthu modzipereka ndiponso modzichepetsa. Mlongo wina dzina lake Debbie ali ndi ana awiri ndipo ananena kuti: “Ana athu ali aang’ono, mwamuna wanga ankatanganidwa ndi kuthandiza anthu a mumpingo chifukwa choti ndi mkulu. Koma sindinkadandaula chifukwa ankayesetsanso kupeza nthawi yocheza ndiponso kusamalira banja lathu.” (1 Tim. 3:4, 5) Mwamuna wa mlongoyu dzina lake Pranas, ananenanso kuti: “Ana athu ankafunitsitsa kuchita utumiki wosiyanasiyana pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito zosiyanasiyana m’gulu la Yehova. Zimenezi zinawathandiza kuti azisangalala ndiponso kudziwana ndi abale ndi alongo ambiri.” Panopa banja lonseli likuchita utumiki wa nthawi zonse. Makolo akamachita zinthu modzipereka ndiponso modzichepetsa, nthawi zambiri ana awo amachitanso zomwezo.
MUZIKHALA OZINDIKIRA
10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wozindikira?
10 Yesu anasonyeza kuti ndi wozindikira ndipo ankadziwa zimene anthu ena akuganiza. Mwachitsanzo, anthu ena amene ankamumvetsera ku Galileya, ankaoneka kuti akufuna kukhala ophunzira ake. (Yoh. 6:22-24) Koma popeza kuti iye ankadziwa zimene zinali m’mitima yawo, anazindikira kuti ankangofuna chakudya chimene ankawapatsa osati zimene ankawaphunzitsa. (Yoh. 2:25) Iye atazindikira zimenezi, anawalangiza moleza mtima n’kuwauza zimene ayenera kuchita.—Werengani Yohane 6:25-27.
11. (a) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuzindikira ngati ana anu amakonda kulalikira kapena ayi? (b) Kodi mungatani kuti ana anu azikonda utumiki?
11 Ngakhale kuti simungadziwe zimene zili mumtima wa mwana wanu, mukhoza kuzindikira ngati amakondadi kulalikira. Mwachitsanzo, ana ambiri amakonda kusewera ndi anzawo akakhala mu utumiki. Choncho mukhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi tikakhala mu utumiki, mwana wangayu amakonda kulalikira kapena amangokonda kusewera ndi anzake?’ Mukazindikira kuti mwana wanu amakonda kusewera, muziyesetsa kuchita zinthu zomuthandiza kuti azisangalala ndi ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, mungamuuze zinthu zomwe angachite mu utumiki kuti azimva kuti akulalikira nawo.
12. (a) Kodi malangizo amene Yesu anapereka anasonyeza bwanji kuti anali wozindikira? (b) N’chifukwa chiyani malangizowa anali ofunika pa nthawiyo?
12 Yesu anasonyezanso kuti ndi wozindikira chifukwa ankadziwa zinthu zimene zingachititse kuti munthu achimwe. Mwachitsanzo, ophunzira ake ankadziwa kuti kuchita chiwerewere n’koipa. Koma Yesu anawachenjeza kuti azipewa zinthu zimene zingachititse munthu kuchita chiwerewere. Iye ananena kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mat. 5:27-29) Malangizo amenewa analidi oyenera kwa Akhristu amene ankalamuliridwa ndi Aroma. Tikutero chifukwa choti katswiri wina wa mbiri yakale analemba kuti m’mabwalo a zamasewero a ku Roma anthu ankaonera zinthu zoipa. Ndipo zinthu zonyansa kwambiri ndi zimene anthu ankasangalala nazo. Choncho Yesu anasonyeza chikondi komanso kuzindikira pochenjeza ophunzira ake kuti asamayang’ane zinthu zomwe zikanawachititsa kuti achimwe.
13, 14. Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azipewa zinthu zolaula?
13 Kukhala wozindikira kungakuthandizeni kuti muteteze ana anu kuti asachite zinthu zimene zingawononge ubwenzi wawo ndi Yehova. Masiku ano, ngakhale ana aang’ono akhoza kuona zinthu zolaula. N’zoona kuti Akhristu amauza ana awo kuti ayenera kupewa zinthu zoipa. Koma makolo akakhala ozindikira amatha kudziwa zimene zingakope mwana wawo kuti ayambe kuchita chidwi ndi zinthu zolaula. Iwo angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi n’chiyani chingachititse kuti mwana wanga akopeke ndi zinthu zolaula? Kodi amadziwa bwinobwino kuopsa kwa zolaula? Kodi timamasukirana moti angandifotokozere ngati atayesedwa kuti aonere zoipazi? Mungachite bwino kuyamba kumuthandiza adakali wamng’ono. Mwina mungamuuze kuti: “Tsiku lina ukadzakhala ndi kamtima kofuna kuonera zinthu zinazake zoipa, udzandiuze. Usadzachite manyazi chifukwa ndidzakuthandiza.”
14 Inunso muyenera kukhala ozindikira posankha zosangalatsa. Pranas amene tamutchula kale uja anati: “Ana amaona zimene makolofe timakonda kumvera, kuonera kapena kuwerenga ndipo amatsatira zimenezo kuposa malangizo amene timawapatsa.” Koma ana akaona kuti mumasankha bwino zosangalatsa, nawonso amachita zomwezo.—Aroma 2:21-24.
MULUNGU WOONA ADZAYANKHA MAPEMPHERO ANU
15, 16. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova angathandize makolo polera ana awo? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
15 N’chiyani chinachitika Manowa atapempha kuti Mulungu amuthandize kulera mwana wake? Baibulo limati: “Mulungu woona anamvetsera mawu a Manowa.” (Ower. 13:9) Yehova adzayankhanso mapemphero anu ndipo adzakuthandizani kulera ana anu. Iye adzakuthandizani kuti muziwaphunzitsa mwachikondi, modzichepetsa ndiponso mozindikira.
16 M’nkhaniyi taona kuti Yehova angathandize makolo kuti aziphunzitsa ana awo aang’ono. Koma m’nkhani yotsatira tidzaona kuti Yehova angathandizenso makolo pophunzitsa ana awo achinyamata kuti azimutumikira. Tidzakambirana zimene makolowo angachite potsanzira Yesu akamaphunzitsa anawo mwachikondi, modzichepetsa ndiponso mozindikira.
a Mawu amene anawamasulira kuti ‘kulanga’ pa Chivumbulutso 3:19 amatanthauza kutsogolera mwachikondi, kuphunzitsa komanso kulangiza. Nthawi zina angatanthauzenso kupereka chilango koma osati mwankhanza.
b Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti mawu oti “Abba” ndi amene ana ankagwiritsa ntchito poitana bambo awo. Mawuwa ankasonyeza kuti anawo ankakonda komanso kulemekeza bambo awo.