Ehudi Mwamuna Wachikhulupiriro ndi Wolimba Mtima
PANALI patapita zaka zambiri kuchokera pamene Aisrayeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Mose ndi womloŵa malo, Yoswa, anali atamwalira kalekale. Posakhalapo amuna achikhulupiriroŵa, anthu ambiri anasiya kulambira koyera. Aisrayeli anayambanso kutumikira Abaala ndi milongoti yopatulika.a Chifukwa cha zimenezo, Yehova anapereka anthu ake m’manja mwa Aaramu zaka zisanu ndi zitatu. Ndiyeno Aisrayeli anafuula kwa Mulungu kaamba ka thandizo. Mwachifundo, anamvetsera. Yehova anaukitsa woweruza, Otiniyeli, kuti alanditse anthu Ake.—Oweruza 3:7-11.
Zochitikazi zikanaphunzitsa Aisrayeli choonadi choyambirira—kumvera Yehova kumadzetsa madalitso, pamene kusamvera kumadzetsa matemberero. (Deuteronomo 11:26-28) Komabe, anthu a Israyeli analephera kutengapo phunziro limeneli. Patapita zaka 40 zamtendere, iwo anasiyanso kulambira koyera.—Oweruza 3:12.
Moabu Awaukira
Panopo Yehova analola kuti anthu ake agwere m’manja mwa Mfumu Egiloni ya Moabu. Baibulo limamfotokoza kuti anali “munthu wonenepa ndithu.” Mothandizidwa ndi Amoni ndi Amaleki, Egiloni anaukira Israyeli ndi kukhazikitsa nyumba ya mfumu m’Yeriko, “mudzi wa m’migwalangwa.” Kunali kodabwitsa chotani nanga kuti mzinda wachikanani woyamba kugonjetsedwa ndi Israyeli tsopano unali likulu la munthu amene anali kulambira mulungu wonyenga Kemosi!b—Oweruza 3:12, 13, 17.
Egiloni anatsendereza Aisrayeli zaka 18 zotsatira, mwachionekere ndi kufuna mtulo waukulu kwa iwo. Mwa kufuna mtulo nthaŵi ndi nthaŵi, Moabu analemera akumatapa chuma cha Israyeli. Ndipo anthu a Mulungu anayeneradi kulilira mpumulo, ndipo kachiŵirinso Yehova anamvetsera. Anawaukitsira mpulumutsi winanso—nthaŵi ino wa m’fuko la Benjamini wotchedwa Ehudi. Kuti athetse ulamuliro wotsendereza wa Egiloni pa Israyeli, Ehudi anakonzekera kukachitapo kanthu tsiku lokapereka mtulo wotsatira.—Oweruza 3:14, 15.
Pokonzekera cholinga chake molimba mtima, Ehudi anapanga lupanga lakuthwa konsekonse lautali wamkono. Ngati umenewu unali mkono waufupi, chidacho chinali ngati masentimita 38 utali wake. Ena angachione ngati chigwandali. Mwachionekere panalibe chopingasa pakati pa mpeni wake ndi chigumbu chake. Choncho, Ehudi anatha kubisa lupanga lake laling’onolo m’zovala zake. Ndiponso, popeza kuti Ehudi anali wamanzere, iye anamangirira lupanga lake kulamanja lake—malo osazoloŵereka a chida.—Oweruza 3:15, 16.
Njira ya Ehudi inalinso ndi ngozi zake. Mwachitsanzo, bwanji ngati atumiki a mfumu anampapasa Ehudi kuti aone ngati ali ndi zida? Ngakhale ngati sakanatero, ndithudi iwo sakanasiya mfumu yawo ili yokha ndi Mwisrayeli! Koma ngati akanatero ndipo Egiloni nkuphedwa, kodi Ehudi akanathaŵa bwanji? Akanathaŵa mtunda wautali chotani atumiki a Egiloni asanadziŵe zimene zachitika?
Mosakayikira Ehudi analingalira pa zinthu zimenezi, mwinamwake ndi kulingalira zotsatirapo zake zingapo zatsoka. Komabe, iye anapitiriza kukonzekera kwake, nasonyeza kulimba mtima ndi kukhulupirira Yehova.
Ehudi Aonana ndi Egiloni
Tsiku lopereka mtulo wotsatira linafika. Ehudi ndi anyamata ake analoŵa m’bwalo la mfumu. Posapita nthaŵi, anali ataimirira pamaso pa Mfumu Egiloni iye mwini. Koma nthaŵi yoti Ehudi akanthe inali isanafike. Atapereka mtulowo, Ehudi analola onyamula mtulowo kuchoka.—Oweruza 3:17, 18.
Kodi nchifukwa ninji Ehudi anazengereza kukantha Egiloni? Kodi anachita mantha? Kutalitali! Kuti akwaniritse cholinga chake, Ehudi anafunikira kulankhula ndi mfumu payokha—mwaŵi umene sanapatsidwe pakuonana koyambaku. Ndiponso, Ehudi adzafunikira kuzemba mwamsanga. Munthu mmodzi angathaŵe mosavuta kuposa gulu lonse la onyamula mtulo. Choncho, Ehudi anadikira nthaŵi yabwino. Kuonana ndi Egiloni kwa kanthaŵi kochepa kumeneko kunamthandiza kulidziŵa bwino bwalolo ndi kuona kukula kwa chitetezo cha mfumu.
Atafika “pamafano osema ali ku Giligala,” Ehudi anasiya anyamata akewo nabwerera kumka kubwalo la Egiloni. Kuyenda mtunda wa makilomita ngati aŵiri kunampatsa kanthaŵi Ehudi koti alingalire za ntchito yake ndi kupempherera dalitso la Yehova.—Oweruza 3:19.
Ehudi Abwerera
Zikuoneka kuti Ehudi anamlandiranso m’bwalolo. Mwinamwake mtulo waukulu umene anali atapereka poyamba unamkondweretsa Egiloni. Mwinamwake ngakhale paulendo woyamba sanakhalitse, Ehudi anapeza mpata wokwanira woti adziŵane ndi mfumu. Mulimonse mmene zinalili, Ehudi analinso pamaso pa Egiloni.
“Ndili nawo mawu achinsinsi kwa inu, mfumu,” anatero Ehudi. Kungofika pano patali chonchi chinali chizindikiro chakuti Yehova anali kumtsogolera. Komabe, panali vuto. “Mawu achinsinsi” amene Ehudi anali nawo sakanatchulidwa atumiki a mfumu ali pompo. Ngati Yehova anayenera kuloŵererapo, Ehudi anafuna thandizo limenelo pomwepo. “Khalani chete,” inalamula mfumuyo. Popeza kuti Egiloni sanafune kuti ena amveko “mawu achinsinsi” ameneŵa, anauza atumiki ake kuchoka. Mmene mtima wa Ehudi unakhalira m’malo!—Oweruza 3:19.
Egiloni anali atakhala m’chipinda chake chosanja pamene Ehudi anadza kwa iye ndi kunena: “Ndili nawo mawu a Mulungu akukuuzani.” Potchula “Mulungu,” kodi Ehudi anali kutanthauza Kemosi? Mwinamwake ndi zimene Egiloni anaganiza. Atachita chidwi, anauka pampando wake wachifumu naimirira moyembekezera kumva mawuwo. Ehudi anayandikira, mwinamwake akumayenda mosamala kuti mfumu isadziŵe kuti adzaikantha. Kenako, mwamsanga, “Ehudi anatulutsa dzanja lake lamanzere nagwira lupanga kuntchafu ya kulamanja nampyoza [Egiloni] m’mimba mwake; ndi chigumbu chake chinaloŵa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolola lupanga m’mimba mwake; [ndipo tubzi tunayamba kutuluka, NW].”—Oweruza 3:20-22.
Atumiki a mfumu, akumazengereza chapafupi, sanadziŵe kalikonse. Koma Ehudi anali adakali pangozi. Nthaŵi iliyonse atumiki a Egiloni angaloŵe ndi kupeza mtembo wa mfumu yawo yakufa. Ehudi anafunikira kuthaŵa mwamsanga! Atafungulira zitseko, anathaŵira poloŵera mphepo m’chipinda chosanja.—Oweruza 3:23, 24a.
Kudziŵa ndi Kugonjetsedwa
Posapita nthaŵi atumiki a Egiloni anatekeseka. Komabe, anaopa kusakondweretsa mfumu mwa kusokoneza msonkhano wake wamtseri. Kenako anaona kuti zitseko za chipinda chosanja zinali zofungulira. “Angophimba mapazi m’chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo,” iwo analingalira motero. Komabe, patapita nthaŵi kutekeseka wamba kunakhala nkhaŵa yaikulu. Atumiki a Egiloni sanathenso kuyembekezera. “Pamenepo anatenga mfungulo natsegula [zitseko za chipinda chosanja]; ndipo taonani, mbuye wawo wagwa pansi, wafa.”—Oweruza 3:24b, 25.
Pamenepo nkuti Ehudi wathaŵa. Anapitirira mafano osema a ku Giligala nafika ku Seira, malo a kumapiri a Efraimu. Ehudi anamema amuna a Israyeli nawatsogolera kukakantha Amoabu mogwirizana. Nkhaniyo imasimba kuti “anakantha Amoabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onseŵa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuka ndi mmodzi yense.” Atagonjetsa Moabu, dziko la Israyeli linapumula zaka 80.—Oweruza 3:26-30.
Kuphunzira pa Chitsanzo cha Ehudi
Kukhulupirira Mulungu kunamsonkhezera Ehudi. Ahebri m’chaputala cha 11 samamtchula mwachindunji monga munthu “amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, . . . anakula mphamvu kunkhondo, anapitikitsa magulu a nkhondo yachilendo.” (Ahebri 11:33, 34) Koma ngakhale zili choncho, Yehova anachirikiza Ehudi pamene anachita zinthu mwachikhulupiriro nalanditsa Israyeli ku mphamvu yopondereza ya Mfumu Egiloni.
Kulimba mtima kunali umodzi wa mikhalidwe ya Ehudi. Anafunikira kulimba mtima kuti agwiritsire ntchito lupanga lenileni mwaluso. Ifeyo monga atumiki amakono a Mulungu, sitimagwiritsira ntchito lupanga lotero. (Yesaya 2:4; Mateyu 26:52) Komabe, timagwiritsira ntchito “lupanga la Mzimu,” Mawu a Mulungu. (Aefeso 6:17) Ehudi anagwiritsira ntchito chida chake mwaluso. Ifenso tifunikira kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu mwaluso polalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mateyu 24:14) Phunziro la Baibulo laumwini, kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse, kuchita nawo utumiki wakumunda mwachangu, ndi kudalira Atate wathu wakumwamba mwapemphero kudzatithandiza kutsanzira mikhalidwe imene Ehudi anasonyeza, munthudi wachikhulupiriro ndi wolimba mtima.
[Mawu a M’munsi]
a Milongoti yopatulika ingakhale inali zizindikiro za mpheto yachimuna. Anali kuigwiritsira ntchito pamapwando achisembwere chosaneneka.—1 Mafumu 14:22-24.
b Kemosi ndiye anali mulungu wamkulu wa Amoabu. (Numeri 21:29; Yeremiya 48:46) Pazochitika zina, ana ayenera kuti anaperekedwa nsembe kwa mulungu wonyansa ndi wonyenga ameneyu.—2 Mafumu 3:26, 27.
[Chithunzi patsamba 31]
Ehudi ndi anyamata ake anapereka mtulo kwa Mfumu Egiloni
[Mawu a Chithunzi]
Chotengedwa mu llustrirte Pracht - Bibel/Heilige Schrift des Alten und Neuen Testaments, nach der deutschen Uebersetzung D. Martin Luther’s