Chipulumutso ncha Yehova
“Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso.”—SALMO 68:20.
1, 2. (a) Nchifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndiye Gwero la chipulumutso? (b) Kodi lemba la Miyambo 21:31 mungalifotokoze motani?
YEHOVA ndi Mpulumutsi wa anthu amene amamkonda. (Yesaya 43:11) Davide, mfumu yotchuka ya Israyeli, anadziŵa chimenechi mwa zimene anakumana nazo, moti anaimba ndi mtima wonse kuti: “Chipulumutso ncha Yehova.” (Salmo 3:8) Mneneri Yona analankhula mawu ofananawo m’pemphero lake lochokera pansi pa mtima pamene anali m’mimba mwa nsomba yaikulu.—Yona 2:9.
2 Ngakhalenso Solomo mwana wa Davide, anadziŵa kuti Yehova ndiye Gwero la chipulumutso, pakuti anati: “Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.” (Miyambo 21:31) Ku Middle East wakale, ng’ombe zinkakoka chikhasu, abulu ankanyamula akatundu, anthu ankakwera nyulu, ndipo akavalo ankagwiritsidwa ntchito pankhondo. Komabe Aisrayeli asanakaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu analamula kuti mfumu yawo yam’tsogolo ‘isakachulukitse akavalo.’ (Deuteronomo 17:16) Akavalo ankhondo sanafunikirenso chifukwa Yehova akalanditsa anthu ake.
3. Ndi mafunso ati amene tiyenera kuwaganizira?
3 Ambuye Mfumu Yehova ndi “Mulungu wa chipulumutso.” (Salmo 68:20) Ha, kulimbikitsa kwake kwa ganizo limenelo! Koma kodi ndi “chipulumutso” chotani chimene Yehova wakhala akuchipereka? Ndipo ndayani amene iye wapulumutsa?
Yehova Amapulumutsa Olungama
4. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amapulumutsa anthu aumulungu?
4 Onse olondola njira yolungama monga atumiki a Mulungu odzipatulira atha kupeza chitonthozo m’mawu a mtumwi Petro akuti: “Ambuye [“Yehova,” NW] adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” Potsimikizira mfundo imeneyi, Petro anati Mulungu “sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.”—2 Petro 2:5, 9.
5. Kodi Nowa anatumikira m’mikhalidwe yotani monga “mlaliki wa chilungamo”?
5 Dziyerekezeni kuti muli pakati pa mikhalidweyo m’tsiku la Nowa. Ziŵandazo zovala matupi a anthu zili pompano padziko lapansi. Ana obadwa kwa angelo opandukawo akuchitira anthu mwankhanza kwambiri, moti ‘dziko lapansi ladzala ndi chiwawa’ chokhachokha. (Genesis 6:1-12) Komabe, pomthupsa Nowa iwo alephera kumusiyitsa kutumikira Yehova. M’malo mwake, iye ndi “mlaliki wa chilungamo.” Limodzi ndi banja lake akumanga chingalawa asakukayika konse zakuti kuipa konse kudzachotsedwa m’nthaŵi ya moyo wawo. Chikhulupiriro cha Nowa chikulitsutsa dzikolo. (Ahebri 11:7) Mikhalidwe ya lerolino ikufanana ndi ya m’tsiku la Nowa, ndipo ikusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu. (Mateyu 24:37-39; 2 Timoteo 3:1-5) Monga Nowa panthaŵi ijayo, kodi inu mudzakhalabe wokhulupirika monga mlaliki wa chilungamo, mukumatumikira limodzi ndi anthu a Mulungu poyembekezera chipulumutso cha Yehova?
6. Kodi lemba la 2 Petro 2:7, 8 limatsimikizira motani kuti Yehova amapulumutsa olungama?
6 Petro akupereka umboni wina wakuti Yehova amapulumutsa olungama. Mtumwiyo akuti: “[Mulungu] anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja (pakuti wolungamayo pokhala pakati pawo, ndi kuona ndi kumva zawo, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika).” (2 Petro 2:7, 8; Genesis 19:1-29) M’masiku ano otsiriza, chiwerewere changokhala moyo wa anthu mamiliyoni ambiri. Monga Loti, kodi inuyo ‘mukuzunzika m’moyo wanu ndi ntchito zosayeruzika’ za anthu ambiri lerolino? Ngati mukutero, ndipo ngati mukutsata chilungamo, mungadzakhale pakati pa awo odzapulumutsidwa ndi Yehova podzawononga dongosolo lino la zinthu.
Yehova Amapulumutsa Anthu Ake kwa Opsinja
7. Kodi mmene Yehova anachitira ndi Aisrayeli m’Aigupto zimatsimikizira motani kuti iye amalanditsa anthu ake ku chipsinjo?
7 Malinga ngati dongosolo lakaleli lidakalipobe, atumiki a Yehova adzakumanabe ndi chizunzo ndi chipsinjo cha adani. Koma iwo angakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzawalanditsa, chifukwa kumbuyoku wakhala akupulumutsa anthu ake opsinjidwa. Tayerekezani kuti ndinu Mwisrayeli wopsinjidwa ndi Aigupto a m’tsiku la Mose. (Eksodo 1:1-14; 6:8) Ndiyeno Mulungu akantha Igupto ndi milili yotsatanatsatana. (Eksodo 8:5–10:29) Pamene mlili wachikhumi wapha ana achisamba achiigupto, Farao alola Israyeli amuke koma pambuyo pake asonkhanitsa magulu ake ankhondo nawathamangira. Komabe posakhalitsa, iye limodzi ndi asilikali ake awonongedwa m’Nyanja Yofiira. (Eksodo 14:23-28) Tayerekezani kuti mukuimba limodzi ndi Mose ndi Aisrayeli onse nyimbo iyi: “Yehova ndiye wankhondo; Dzina lake ndiye Yehova. Magareta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m’nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira m’Nyanja Yofiira. Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala.” (Eksodo 15:3-5) Tsoka ngati limenelo lili patsogolopa kwa onse opsinja anthu a Mulungu m’masiku ano otsiriza.
8, 9. Kuchokera m’buku la Oweruza, perekani chitsanzo chotsimikizira kuti Yehova amapulumutsa anthu ake kwa opsinja.
8 Kwa zaka zambiri Aisrayeli ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, oweruza awo anasungitsa chilungamo pakati pawo. Nthaŵi zina anthuwo ankapsinjidwa ndi mitundu ina, komabe Mulungu ankagwiritsa ntchito oweruza kuwalanditsa iwo. Mofananamo, ifenso ngati ‘tingabuule chifukwa cha otipsinja ndi otitsendereza,’ Yehova adzatipulumutsa pokhala atumiki ake okhulupirika. (Oweruza 2:16-18; 3:9, 15) Ndi iko komwe, buku la m’Baibulo la Oweruza limatitsimikizira za chimenechi ndi za chipulumutso chachikulu chimene Yehova adzapereka mwa Woweruza wake woikika, Yesu Kristu.
9 Tiyeni tibwererenso m’mbuyo kumasiku a Woweruza Baraki. Chifukwa cha kulambira kwawo konyenga ndi kutayikidwa chiyanjo cha Mulungu, Aisrayeli apsinjika kwa zaka 20 za ulamuliro woŵaŵa wa Mfumu yachikanani, Yabini. Sisera ndiye kazembe wamkulu wa chigulu chankhondo cha Akanani. Koma, ‘chikopa kapena nthungo sizitha kuoneka mwa zikwi makumi anayi a Israyeli,’ ngakhale kuti mtunduwo uyenera kuti unali ndi anthu pafupifupi mamiliyoni anayi. (Oweruza 5:6-8) Aisrayeli akufuulira Yehova molapa. Monga momwe Mulungu walangizira kudzera mwa mneneri wamkazi Debora, Baraki akusonkhanitsa amuna 10,000 pa Phiri la Tabori, ndipo Yehova akukwezera gulu lankhondolo kuchigwa m’munsi mwa Tabori wamtaliyo. Pakumveka chipokoso chachikulu, kenako magulu ankhondo a Sisera limodzi ndi magareta 900 atulukira akuthamanga chodutsa m’chidikhamo ndi m’khwaŵa la mtsinje wa Kidron. Koma chimvula chachikulu chikuvumba ndipo Kidron akusefukira ndi madzi ochuluka. Pamene Baraki ndi asilikali ake atsika m’Phiri la Tabori atabisika ndi mvulayo, akuona ndi maso awo tsoka losaneneka pamene Yehova atsanulira mkwiyo wake. Ndipo amuna a Baraki akukantha Akanani amene akuthaŵa pochita mantha, moti palibe ndi mmodzi yemwe wopulumukapo. Ha, ati chenjezo lake nanga kwa otipsinjawo omwe akulimbana ndi Mulungu!—Oweruza 4:3-16; 5:19-22.
10. Nchifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzapulumutsa atumiki ake amakono kwa owapsinja onse?
10 Yehova adzapulumutsanso atumiki ake amakono kwa adani awo owapsinja, monga mmene anapulumutsira Israyeli woopa Mulungu m’nthaŵi zowawitsa. (Yesaya 43:3; Yeremiya 14:8) Mulungu analanditsa Davide “m’dzanja la adani.” (2 Samueli 22:1-3) Choncho ngakhale ngati tipsinjidwa kapena kuzunzidwa pokhala anthu a Yehova, tiyeni tilimbike mtima, chifukwa Mfumu yake yaumesiya idzatilanditsa kuchipsinjo. Inde, “adzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.” (Salmo 72:13, 14) Chilanditso chimenecho chili posachedwa pompa.
Mulungu Amapulumutsa Omdalira
11. Kodi Davide wachinyamatayo anapereka chitsanzo chotani chodalira Yehova?
11 Kuti tione chipulumutso cha Yehova, tiyenera kumdalira molimba mtima. Davide anasonyeza kudalira Mulungu molimba mtima pamene anakakumana ndi Goliati, chimphona chija. Tangoganizirani chimfilisti chachitali ndi chojintcha chimenecho chitayang’anizana ndi Davide, amene akufuula kuti: “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo.” Posapita nthaŵi, Goliati anali kwala atakanthidwa ndi kufa pomwepo, ndipo Afilisti agonjetsedwa. Mwachionekere, Yehova ndiye anapulumutsa anthu ake.—1 Samueli 17:45-54.
12. Nchifukwa chiyani kungakhale kothandiza kukumbukira Eleazara, mwamuna wamphamvu wa Davide?
12 Poyang’anizana ndi ozunza, timafunikira kukhala ‘olimbika mtima’ ndi kudalira Mulungu kwathunthu. (Yesaya 46:8-13; Miyambo 3:5, 6) Taganizirani chochitikacho kumalo otchedwa Pasidamimu. Israyeli wathaŵa poopa magulu ankhondo achifilisti. Koma Eleazara, mmodzi wa amuna amphamvu a Davide sakusunthika ndi mantha. Iye waima chilili m’munda wa balere ndipo yekhayekha akukantha ndi kupha Afilistiwo ndi lupanga. Motero ‘awapulumutsa Yehova ndi chipulumutso chachikulu.’ (1 Mbiri 11:12-14; 2 Samueli 23:9, 10) Sikuti ifenso tikafunikira kugonjetsa gulu la nkhondo tili tokha ayi. Komabe, nthaŵi zina adani atha kutipanikiza tili tokhatokha. Kodi tidzadalira Yehova mwapemphero, Mulungu wa ntchito zopulumutsa? Kodi tidzapempha kuti atithandize kuti tisapereke okhulupirira anzathu kwa ozunza?
Yehova Amapulumutsa Okhulupirika
13. Nchifukwa chiyani kunali kovuta kukhala wokhulupirika kwa Mulungu mu ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli?
13 Kuti Yehova atipulumutse, tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa iye zivute zitani. Anthu a Mulungu a m’nthaŵi zakale anakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Talingalirani zimene mukanakumana nazo mukanakhalako mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Nkhanza za Rehabiamu zinachititsa mafuko khumiwo kumgalukira ndi kukapanga ufumu wakumpoto wa Israyeli. (2 Mbiri 10:16, 17; 11:13, 14) Pakati pa mafumu a Israyeli ambiri, Yehu ndiye anachita bwino kopambana, ngakhale kuti iyenso ‘sanasamalire kuyenda m’chilamulo cha Yehova ndi mtima wake wonse.’ (2 Mafumu 10:30, 31) Komabe, ufumu wa mafuko khumiwo unali nawo anthu ena okhulupirika. (1 Mafumu 19:18) Iwo anaonetsa chikhulupiriro mwa Mulungu, ndipo Mulungunso anakhaladi nawo. Ngakhale kuti inunso mumakumana ndi ziyeso za chikhulupiriro chanu, kodi mukukhalabe wokhulupirika kwa Yehova?
14. Kodi Yehova anapereka chipulumutso chotani m’nthaŵi ya Mfumu Hezekiya, ndipo nchiyani chinatheketsa Ababulo kugonjetsa Yuda?
14 Kunyalanyaza Chilamulo cha Mulungu kofalako kunagwetsera ufumu wa Israyeli m’tsoka. Asuri atagonjetsa ufumuwo mu 740 B.C.E., anthu ena ochokera ku mafuko ake khumi anathaŵira ku ufumu wa Yuda wa mafuko aŵiri, kumene iwo anatha kulambira Yehova pakachisi wake. Pamafumu 19 a Yuda a mzere wa Davide, anayi okha—Asa, Yehosafati, Hezekiya, ndi Yosiya—ndiwo anali odzipereka kwambiri kwa Mulungu. M’masiku a Hezekiya wokhulupirikayo, Asuri anatsikira Yuda ndi khamu lalikulu lankhondo. Poyankha kuchonderera kwa Hezekiya, Mulungu anagwiritsa ntchito mngelo mmodzi yekha kupha Asuri 185,000 usiku umodzi wokha, napulumutsa alambiri Ake! (Yesaya 37:36-38) Pambuyo pake, anthuwo polephera kusunga Chilamulo ndi kunyalanyaza machenjezo a aneneri a Mulungu, Ababulo anagonjetsa Yuda ndi kuwononga likulu lake, Yerusalemu, mu 607 B.C.E., limodzi ndi kachisi wake.
15. Kodi nchifukwa chiyani Ayuda omwe anali akapolo ku Babulo anafunikira kupirira, ndipo potsirizira pake Yehova anawalanditsa bwanji?
15 Chipiriro chinali chofunika kwa Ayuda okhala m’dziko la ndendewo kuti akhalebe okhulupirika kwa Mulungu pamene anali muukapolo ku Babulo kwa zaka 70 zomvetsa chisonizo. (Salmo 137:1-6) Mmodzi wodziŵika kwambiri pakukhulupirika kwake anali mneneri Danieli. (Danieli 1:1-7; 9:1-3) Tangoganizani chisangalalo chake Danieli, pamene Koresi, Mfumu ya Peresiya anapereka lamulo mu 537 B.C.E., lolola Ayuda kubwerera ku Yuda kukamanganso kachisi! (Ezara 1:1-4) Danieli limodzi ndi anzake ena anapirira zaka zambiri, koma pomalizira pake anaona kugwa kwa Babulo ndi kulanditsidwa kwa anthu a Yehova. Zimenezo ziyenera kutithandiza kupirira pamene tikuyembekezera kugwa kwa “Babulo Wamkulu,” ufumu wa padziko lonse wa chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 18:1-5.
Yehova Amapulumutsa Anthu Ake Nthaŵi Zonse
16. Kodi Mulungu anapereka chipulumutso chotani m’masiku a Mfumukazi Estere?
16 Yehova nthaŵi zonse amapulumutsa anthu ake pamene akhala okhulupirika ku dzina lake. (1 Samueli 12:22; Yesaya 43:10-12) Tabwererani m’mbuyo ndi kuganiza za Mfumukazi Estere—m’zaka za zana lachisanu B.C.E. Mfumu Ahaswero (Aritasasta I) waika Hamani kukhala nduna yaikulu ya boma lake. Hamani atapsa mtima chifukwa Myuda wotchedwa Moredekai wakana kumuŵeramira, akukonza chiwembu choti amuphe limodzi ndi Ayuda ena onse a m’dziko la Ufumu wa Peresiya. Akuwanamizira kukhala oswa malamulo, ndiponso ayesa kunyengerera mfumuyo ndi ndalama, moti aloledwa kugwiritsa ntchito mphete ya pachala cha mfumu monga umboni wovomereza chikalata cholamula kuti Ayuda onse anyongedwe. Molimba mtima Estere akuulula pamaso pa mfumuyo kuti iye ndi mbadwa yachiyuda navumbulanso chiwembu chambanda cha Hamani. Posapita nthaŵi Hamani ali pachikike pamtengo umene anali atakonzera kunyongerapo Moredekai. M’malo mwake Moredekai akuikidwa nduna yaikulu ya boma, napatsidwa mphamvu yolola Ayuda kudziteteza pamlanduwo. Iwo akulakika kotheratu pa adani awowo. (Estere 3:1–9:19) Chochitika chimenechi chiyenera kulimbikitsa chikhulupiriro chathu chakuti Yehova adzachita ntchito zopulumutsa atumiki ake omvera amakono.
17. Kodi kumvera kunatheketsa motani kuti Akristu achiyuda a m’zaka za zana loyamba apulumuke?
17 Chifukwa china chimene Mulungu amapulumutsira anthu ake nchakuti amamumvera iye limodzi ndi Mwana wake. Tayerekezani kuti munali mmodzi wa ophunzira a Yesu achiyuda a m’zaka za zana loyamba. Iye akuwauza kuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.” (Luka 21:20-22) Zaka zikudutsa, ndipo muyamba kudabwa kuti nanga mawuwo akwaniritsidwa liti. Kenako Ayuda akugaluka mu 66 C.E. Magulu ankhondo achiroma motsogozedwa ndi Cestius Gallus akuzinga Yerusalemu ndipo aguba mpaka m’malinga a kachisi. Mwadzidzidzi, Aromawo akubwerera pachifukwa chosadziŵika bwinobwino. Kodi Akristu achiyuda atani pamenepo? M’buku lake lotchedwa Ecclesiastical History (Buku III, chaputala V, 3), Eusebius ananena kuti iwo anathaŵamo m’Yerusalemu ndi m’Yudeya. Anapulumuka chifukwa anamvera ulosi wochenjeza wa Yesu. Kodi inunso mumalabadira msanga chitsogozo cha m’Malemba choperekedwa kudzera mwa “mdindo wokhulupirika” woikidwa kuyang’anira “zonse ali nazo”?—Luka 12:42-44.
Chipulumutso cha ku Moyo Wosatha
18, 19. (a) Kodi imfa ya Yesu inatheketsa chipulumutso chotani, ndipo kwa ndani? (b) Kodi mtumwi Paulo anali wotsimikiza mtima kuchitanji?
18 Kulabadira chenjezo la Yesu kunapulumutsa miyoyo ya Akristu achiyudawo m’Yudeya. Koma imfa ya Yesu imatheketsa chipulumutso cha ku moyo wosatha kwa “anthu onse.” (1 Timoteo 4:10) Mtundu wa anthu unafunikira chipulumutso pamene Adamu anachimwa, ndi kudzitayira moyo wake ndi kugulitsa mtundu wa anthu mu ukapolo ku uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12-19) Nsembe za nyama zoperekedwa m’nthaŵi ya Chilamulo cha Mose zinali kokha chizindikiro cha kukhululukira machimo. (Ahebri 10:1-4) Popeza Yesu analibe tate waumunthu ndipo mzimu woyera wa Mulungu ndiwo ‘unaphimba’ Mariya kuchokera nthaŵi imene anaima mpaka kubadwa kwa Yesu, Yesuyo anabadwa wopanda uchimo uliwonse wa choloŵa kapena kupanda ungwiro kulikonse. (Luka 1:35; Yohane 1:29; 1 Petro 1:18, 19) Yesu atafa monga wokhulupirika wangwiro, anapereka moyo wake wangwiro kuwombola ndi kumasula mtundu wa anthu. (Ahebri 2:14, 15) Chotero Kristu “anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse.” (1 Timoteo 2:5, 6) Si onse amene adzazipindulitsa ndi makonzedwe amenewa a chipulumutso, koma Mulungu wavomereza kuti onse okhulupirira makonzedwe amenewo apindule nawo.
19 Mwa kupereka mtengo wa nsembe yake ya dipo kwa Mulungu kumwamba, Kristu anazigulanso mbadwa za Adamu. (Ahebri 9:24) Choncho Yesu akupeza Mkwatibwi, amene ndi otsatira ake odzozedwa okwanira 144,000, oukitsidwa ku moyo wakumwamba. (Aefeso 5:25-27; Chivumbulutso 14:3, 4; 21:9) Iye akukhalanso “Atate Wosatha” kwa awo ovomereza nsembe yake ndi kulandira moyo wosatha wa padziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7; 1 Yohane 2:1, 2) Ha, chikondi chake cha makonzedwe amenewo! Chiyamikiro cha Paulo pa zimenezo chikuoneka m’kalata yake youziridwa yachiŵiri ku Mpingo wa Akorinto, monga mmene nkhani yotsatira idzasonyezera. Ndi iko komwe, Paulo anali wotsimikiza mtima kusalola china chilichonse kumlepheretsa kuthandiza anthu kuti apindule ndi makonzedwe odabwitsa a Yehova opulumutsira ku moyo wosatha.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi pali umboni wotani wa Malemba wosonyeza kuti Mulungu amapulumutsa anthu ake olungama?
◻ Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amapulumutsa aja omdalira ndi okhulupirika?
◻ Kodi Mulungu wapanga makonzedwe otani opulumutsira ku moyo wosatha?
[Chithunzi patsamba 12]
Davide anadalira Yehova, “Mulungu wa chipulumutso.” Kodi inu mumatero?
[Chithunzi patsamba 15]
Yehova amapulumutsa anthu ake nthaŵi zonse, monga anachitira m’tsiku la Mfumukazi Estere