TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | DEBORA
“Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli”
DEBORA ankachita chidwi ndi asilikali omwe anasonkhana pamwamba pa phiri la Tabori. Iye anasangalala kwambiri kuwaona atasonkhana molimba mtima. Pa nthawiyi, ankaganiziranso kulimba mtima kwawo komanso chikhulupiriro cha mtsogoleri wawo, Baraki. Ngakhale kuti asilikaliwa analipo 10,000 komanso anali amphamvu, zinthu sizinali bwino pa tsikuli. Ankafunika kumenya nkhondo ndi gulu lina la asilikali oopsa kwambiri, koma iwo anali ochepa ndiponso anali ndi zida zochepa zomenyera nkhondo. Ngakhale zinali choncho, iwo analimbabe mtima kumenya nkhondoyi chifukwa chakuti Debora anawalimbikitsa.
Tayerekezerani kuti mukuona Debora ndi Baraki omwe ali pamwamba pa phiri la Tabori ndipo kamphepo kakumenya pa zovala za Debora. Phirili linali lalitali mamita pafupifupi 400 ndipo pamwamba pake panali pafulati. Munthu akakhala pamwambapo ankatha kuona chigwa cha Esdraelon chomwe chili kumwera chakumadzulo. Ankaonanso Mtsinje wa Kisoni womwe umadutsa m’dambo lomwe lili mphepete mwa phiri la Karimeli ndipo umakathira m’Nyanja Yaikulu. Pa nthawiyi mtsinjewo unali utauma koma m’chigwachi munkanyezimira chifukwa cha zida za nkhondo za asilikali a Sisera amene anali atayandikira. Asilikaliwa ndi amene Sisera ankadalira kwambiri ndipo anakwera magaleta pafupifupi 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo. Sisera anatumiza asilikaliwa n’cholinga chofuna kuseseratu Aisiraeli omwe ankaoneka kuti alibiretu zida za nkhondo.
Debora ankadziwa kuti Baraki ndi asilikali ake amadikira kuti iyeyo awauze zochita. Kodi pa nthawiyi mzimayi anali yekha? Kodi iye ankamva bwanji poganizira udindo umene anali nawowu? Kodi sankadziwa zoyenera kuchita? Iye ankadziwa ndithu, chifukwa Mulungu wake Yehova ndi amene anamuuza kuti ayambe kumenya nkhondoyi. Anamuuzanso kuti adzagwiritsira ntchito mzimayi pothetsa nkhondoyi. (Oweruza 4:9) Kodi tingaphunzire chiyani kwa Debora komanso kwa asilikali olimba mtimawa pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro?
ANAUZIDWA KUTI AKAGUBE PAPHIRI LA TABORI
Baibulo likamayamba kufotokoza za Debora limamutchula kuti anali “mneneri wamkazi.” Ngakhale kuti udindo wa Deborawu unali wodabwitsa, panalinso aneneri ena aakazi.a Kungoti iyeyo anali wosiyana ndi aneneri ena aakazi chifukwa Yehova anamupatsa udindo woweruza milandu ya anthu.—Oweruza 4:4, 5.
Debora ankakhala m’dera lamapiri la ku Efuraimu, pakati pa mzinda wa Beteli ndi Rama. Iye ankakhala pansi pa mtengo wa kanjedza n’kumaweruza milandu ya anthu motsatira malangizo ochokera kwa Yehova. Udindo umene Debora anali nawowu unali wovuta ndithu, koma sunkamulepheretsa kugwira ntchito zina. Mwachitsanzo, Mulungu anamugwiritsanso ntchito polemba nyimbo yomwe imafotokoza za kusakhulupirika kwa anthu a mtundu wake. Iye analemba kuti: “Anayamba kusankha milungu yatsopano. Atatero m’pamene nkhondo inafika m’mizinda.” (Oweruza 5:8) Popeza kuti Aisiraeli anasiya Yehova n’kuyamba kutumikira milungu ina, iye analolera kuti azizunzidwa ndi adani awo. Choncho Yabini yemwe anali Mfumu ya Kanani anayamba kuwapondereza ndipo ankagwiritsa ntchito Sisera mtsogoleri wa nkhondo yemwe anali wamphamvu kwambiri.
Sisera anali wankhanza kwambiri ndipo Aisiraeli ankamuopa. Chikhalidwe komanso chipembedzo cha a Kanani chinkalimbikitsa zinthu zankhanza komanso zoipa monga kupereka ana awo nsembe ndiponso kuchita uhule pakachisi. N’zodziwikiratu kuti zinthu sizinali bwino ku Isiraeli chifukwa chakuti dzikoli linali m’manja mwa Akanani ankhanzawa. Nyimbo imene Debora analemba imasonyeza kuti kuyenda kunali kovuta kwambiri komanso anthu anathawa m’midzi yawo. (Oweruza 5:6, 7) Taganizirani kuti mukuona Aisiraeli akuyenda mwamantha podutsa m’nkhalango komanso m’mapiri. Iwo ankaopa kupita kumunda kapena kukhala m’midzi yopanda mipanda ndiponso kuyenda m’misewu. Ankachita zimenezi poopa kuti angaphedwe, ana awo angatengedwe kapena akazi awo angagwiriridwe.b
Aisiraeli anakhala mozunzika chonchi kwa zaka 20 kufikira pamene Yehova anaona kuti anthu ake omwe anali osamvera akufuna kusintha. Kapenanso mogwirizana ndi mawu a m’nyimbo ya Debora ndi Baraki: ‘Kufikira pamene Debora anauka monga mayi mu Isiraeli.’ Sitikudziwa ngati Debora, yemwe anali mkazi wa Lapidoti, anali ndi ana. Mawu amene ananenawa anali ophiphiritsa ndipo ankatanthauza kuti Yehova adzagwiritsa ntchito Debora poteteza Aisiraeli ngati mmene mayi amatetezera ana ake. Yehova anamutuma kuti akauze Baraki yemwe anali woweruza ndiponso anali wachikhulupiriro cholimba kuti akamenyane ndi gulu la nkhondo la Sisera.—Oweruza 4:3, 6, 7; 5:7.
Yehova anagwiritsa ntchito Debora pouza Baraki kuti akagube paphiri la Tabori. Baraki ankafunika kupita ndi amuna 10,000 a m’mafuko awiri a Isiraeli ndipo Debora anawauza lonjezo la Yehova lakuti akagonjetsa Sisera ndi gulu lake la nkhondo lomwe linali ndi magaleta 900. Baraki sanamvetse zimenezi chifukwa pa nthawiyi ku Isiraeli kunalibe gulu la nkhondo komanso analibe zida zankhondo. Baraki ananena kuti apita pokhapokha ngati Debora atapita nawo kuphiri la Tabori.—Oweruza 4:6-8; 5:6-8.
Anthu ena amaganiza kuti Baraki analibe chikhulupiriro chifukwa ankafuna kuti Debora apite naye. Koma zimenezi si zoona chifukwa iye sanapemphe Mulungu kuti am’patse zida zambiri. M’malo mwake anapempha kuti mneneri wa Yehova, Debora, apite naye n’cholinga choti azikalimbikitsa iyeyo ndi anthu amene anali nawo. (Aheberi 11:32, 33) Yehova analola Debora kuti apite nawo komanso anamuuza kuti alosere zoti munthu wamkazi ndi amene adzaphe Sisera.—Oweruza 4:9.
Masiku ano akazi amachitidwa nkhanza, kuponderezedwa komanso amachitidwa zinthu zopanda chilungamo. Ndipo nthawi zambiri salemekezedwa ngati mmene Mulungu amafunira. Komatu Mulungu amaona kuti akazi komanso amuna ndi ofunika kwambiri. (Aroma 2:11; Agalatiya 3:28) Chitsanzo cha Debora chikusonyeza kuti Mulungu amapatsa akazi udindo komanso kuwachitira zinthu zina zosonyeza kuti amawadalira komanso amawakonda. Choncho tizipewa kuona kuti akazi ndi osafunika, m’malo mwake tiziwalemekeza.
‘DZIKO LINAGWEDEZEKA NDIPO KUMWAMBA KUNAGWETSA MADZI’
Baraki anasonkhanitsa anthu olimba mtima okwana 10,000 kuti akamenyane ndi gulu la nkhondo la Sisera. Pamene ankapita ndi asilikali ake kuphiri la Tabori, Baibulo limati: “Debora nayenso anapita nawo.” (Oweruza 4:10) N’zosakayikitsa kuti Baraki ataona Debora, mtima wake unakhala m’malo. Komanso asilikali analimbikitsidwa kwambiri ataona kuti mayi wolimba mtimayu akupita nawo kuphiri la Tabori. Iye analolera kuika moyo wake pachiswe chifukwa chokhulupirira kwambiri Yehova Mulungu.
Sisera atazindikira kuti Aisiraeli asonkhana kuti amenyane naye, nthawi yomweyo anasonkhanitsa asilikali ake. Komanso mafumu ambiri a ku Kanani anagwirizana ndi Mfumu Yabini, yemwe ayenera kuti anali wamphamvu kwambiri pa mafumu onse a ku Kanani. Kenako phokoso la magaleta a Sisera linapangitsa kuti dziko ligwedezeke. Akananiwo sankakayikira ngakhale pang’ono kuti awina nkhondoyo ndipo ankaona kuti sizitenga nthawi kuti agonjetse Aisiraeliwo.—Oweruza 4:12, 13; 5:19.
Kodi mukuganiza kuti Baraki ndi Debora anayenera kutani asilikali a Sisera atayandikira phirilo? Baraki ndi asilikali ake akanati azimenya nkhondo ali m’mbali mwa phirilo, akanakhala ndi mwayi wowina chifukwa magaleta a Sisera ankafunika malo a fulati kuti amenye bwino nkhondo. Koma Baraki anadikira kuti Debora amuuze zochita chifukwa ankafunika kumenya nkhondoyi mogwirizana ndi malangizo a Yehova. Kenako Debora anafika ndipo anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.” Atamuuza zimenezi, Baibulo limati: “Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira.”—Oweruza 4:14.c
Asilikali a Isiraeli anatsika m’phirili n’kumalowera chakumene kunali zida zankhondo zoopsa za Akanani. Kodi pa nthawiyi Yehova anakhaladi patsogolo pa Baraki ngati mmene Debora analoserera? Inde. Baibulo limati: “Dziko linagwedezeka, kumwamba kunagwetsa madzi.” Apatu gulu la nkhondo la Sisera linasowa mtengo wogwira. Kunagwa chimvula chambiri moti posapita nthawi nthaka inafewa kwambiri. Kenako magaleta achitsulo amene ankadalira aja anawaona kuti ndi opanda ntchito chifukwa anayamba kutitimira m’matope.—Oweruza 4:14, 15; 5:4.
Baraki ndi asilikali ake sanachite mantha ndi chimvulachi chifukwa ankadziwa kuti Yehova ndi amene akuchititsa zimenezi. M’malo mwake anathamangira kumene kunali gulu la asilikali a Akananiwo. Aisiraeliwo anaseseratu asilikali onse a Sisera motsatira malangizo a Mulungu. Kenako Mtsinje wa Kisoni unasefukira ndipo unakokolola mitembo yonse ya asilikaliwa n’kukaitaya m’Nyanja Yaikulu.—Oweruza 4:16; 5:21.
Masiku ano Yehova sagwiritsanso ntchito atumiki ake kumenya nkhondo. Koma amafuna kuti azichita zofuna zake ndipo akamatero amakhala akumenya nkhondo yauzimu. (Mateyu 26:52; 2 Akorinto 10:4) Tikamayesetsa kumvera zimene Mulungu amatiuza, timasonyeza kuti tikumenya nawo nkhondoyi. Choncho atumiki a Mulungu ayenera kuyesetsa kuchita zinthu molimba mtima chifukwa akhoza kutsutsidwa kwambiri. Koma popeza Yehova sanasinthe, iye ndi wokonzeka kuteteza anthu amene amamukhulupirira monga mmene anatetezera Debora, Baraki ndi asilikali a ku Isiraeli omwe anali olimba mtima.
“WODALITSIKA PAKATI PA AKAZI ONSE”
Sisera yemwe ankazunza kwambiri anthu a Mulungu anathawa wapansi nkhondo ili mkati. Iye anasiya asilikali ake akungodzifera m’matope, n’kudutsa asilikali a Isiraeli n’kuthawira kunyumba kumene ankaganiza kuti angakamuteteze. Pothawapo ankangoti chewuchewu kuopera kuti asilikali a Isiraeli angamupeze ndipo anathawira ku mahema a Heberi Mkeni. Heberi anadzisiyanitsa ndi anthu a mtundu wake n’kukakhala kumwera komanso anapanga mgwirizano ndi Mfumu Yabini.—Oweruza 4:11, 17.
Sisera anakafika kuhema wa Heba ali wefuwefu koma anakapeza mkazi wake yekha chifukwa Heba anali atachoka. Sisera sankakayikira kuti mkazi wa Heba dzina lake Yaeli, amulandira ndi manja awiri chifukwa cha ubale umene unalipo pakati pa Heba ndi Mfumu Yabini. Iye sanaganizireko n’komwe kuti Yaeli angamuchite chipongwe. Komatu Sisera sanadziwe zamumtima mwa mkaziyu. N’zosakayikitsa kuti Yaeli ankadziwa bwino nkhanza zimene Akanani ankachitira Aisiraeli ndipo pa nthawiyi ankafunika kuchita zinthu mwanzeru. Popeza Sisera anali munthu woipa komanso ankazunza anthu a Mulungu, Yaeli anafunika kusankha pakati pomuthandiza kapena kumupha. Kodi anayenera kusankha chiyani pamenepa? Kodi mzimayiyu akanakwanitsa kupha msilikali wamphamvu komanso wankhanzayu?
Yaeli anafunika kuganiza mofulumira kwambiri. Iye anapatsa Sisera malo ogona ndipo Siserayo anamuuza kuti asauze aliyense kuti ali m’hemayo. Kenako Yaeli anamufunditsa bulangete ndipo atapempha madzi akumwa anamupatsa mkaka. Posakhalitsa Sisera anagona tulo tofa nato. Nthawi yomweyo Yaeli anatenga chikhomo cha hema ndi nyundo zomwe azimayi ambiri okhala m’mahema ankadziwa bwino kuzigwiritsa ntchito ndipo anayenda monyang’ama n’kufika pafupi ndi mutu wa Sisera. Tsopano ankafunika kugwira ntchito yoopsa yopereka chilango moimira Yehova. Yaeli akanangophonya Sisera n’kudzuka, akanaona zakuda. Kodi Yaeli anachita zimenezi chifukwa choganizira mmene Sisera anazunzira anthu a Mulungu kwa zaka zambiri? Kapena ankaganizira mwayi womwe anali nawo wogwiritsidwa ntchito ndi Yehova? Baibulo silimanena chilichonse pa nkhaniyi. Koma limasonyeza kuti Yaeli sanazengereze ndipo nthawi yomweyo anapha Sisera.—Oweruza 4:18-21; 5:24-27.
Kenako Baraki anayamba kufunafuna kumene kunali Sisera kuti aphedwe. Koma Yaeli atamuonetsa mtembo wa Sisera womwe unali ndi chikhomo cha hema, pompo anazindikira kuti ulosi umene unanenedwa ndi Debora uja wakwaniritsidwa. Debora anali ataneneratu kuti Sisera adzaphedwa ndi mkazi. Anthu ena amene sakhulupirira Baibulo, amatchula Yaeli mayina osonyeza kuti anali mzimayi wankhanza koma Debora ndi Baraki ankadziwa kuti zimene Yaeli anachitazi zinali zitaloseredwa. Chifukwa chakuti Yaeli anachita zinthu molimba mtima, Mulungu anauzira Debora ndi Baraki kuti alembe nyimbo yotamanda Yaeli. Iwo analemba kuti Yaeli ndi “wodalitsika pakati pa akazi onse.” (Oweruza 4:22; 5:24) Debora sanali munthu wodzikonda. Iye sanachitire nsanje Yaeli chifukwa chakuti anatamandidwa, koma anakumbukira kuti zimene Yaeli anachita zinakwaniritsa mawu a Yehova.
Sisera ataphedwa, Aisiraeli sankaopanso Mfumu Yabini ndipo Akanani anasiya kuzunza Aisiraeliwo. Iwo anakhala pa mtendere kwa zaka 40. (Oweruza 4:24; 5:31) Yehova anadalitsa kwambiri Debora, Baraki ndiponso Yaeli chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Tingatsanzire chikhulupiriro cha Debora potumikira Yehova molimba mtima komanso tikamalimbikitsa ena kuti azichita zimenezi. Tikamatero, Yehova adzatithandiza kuti tisamagonje tikakumana ndi zinthu zoyesa chikhulupiriro chathu komanso tidzakhala ndi mtendere wochuluka.
a Aneneri ena aakazi anali Miriamu, Hulida komanso mkazi wa Yesaya.—Ekisodo 15:20; 2 Mafumu 22:14; Yesaya 8:3.
b Nyimbo ya Debora imasonyeza kuti nthawi zambiri Sisera akamachoka kunkhondo, ankabwerako ndi zinthu zosiyanasiyana komanso atsikana moti nthawi zina msilikali aliyense ankapatsidwa atsikana angapo. (Oweruza 5:30) Zikuoneka kuti atsikanawa ankawatenga kuti azigonana nawo basi ndipo pa nthawiyi ku Kanani azimayi ambiri ankagwiriridwa.
c Nkhondoyi imafotokozedwa kawiri m’Baibulo. Koyamba inafotokozedwa ngati mbiri m’buku la Oweruza chaputala 4, kenako inafotokozedwa m’nyimbo imene Debora ndi Baraki analemba m’chaputala 5 cha buku lomweli. Nkhanizi n’zogwirizana koma iliyonse imafotokoza mfundo zina zomwe m’nkhani ina mulibe.