“Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa”
‘Ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti . . . uyende modzichepetsa ndi Mulungu wako?’—MIKA 6:8.
1, 2. Kodi kudzichepetsa n’chiyani, ndipo kumasiyana motani ndi kudzikuza?
MTUMWI wotchuka wakana kudzitamandira. Woweruza wolimba mtima wachiisrayeli akudzitcha wamng’ono m’nyumba ya atate wake. Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako akuvomereza kuti ulamuliro wake si umene uli wapamwamba koposa. Aliyense wa amuna ameneŵa akusonyeza kudzichepetsa.
2 Kudzichepetsa n’kosiyana ndi kudzikuza. Munthu wodzichepetsa amaona maluso ake ndi chuma chake moyenera ndipo samadzitukumula kapena kudzikweza. M’malo mokhala wonyada, wodzitamandira, kapena wofunitsitsa malo apamwamba, munthu wodzichepetsa amadziŵa bwino lomwe za zofooka zake. Chotero, amalemekeza ndi kulingalira mosamalitsa mmene ena amamvera mumtima ndi maganizo awo.
3. Kodi nzeru “ili ndi odzichepetsa” m’njira yotani?
3 Pa chifukwa chabwino Baibulo limati: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa n’ngwanzeru chifukwa chakuti amatsata njira imene Mulungu amavomereza, ndipo amapeŵa mzimu wodzikuza umene ungam’dzetsere manyazi. (Miyambo 8:13; 1 Petro 5:5) Nzeru ya kudzichepetsa yatsimikizirika m’moyo wa atumiki angapo a Mulungu. Tiyeni tipende zitsanzo zitatu zotchulidwa m’ndime yoyamba ija.
Paulo—‘Mtumiki’ Komanso ‘Mdindo’
4. Kodi Paulo anasangalala ndi madalitso apadera otani?
4 Paulo anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa Akristu oyambirira, ndipotu m’pomveka. M’kati mwa utumiki wake, anayenda makilomita ochuluka panyanja ndi pamtunda pomwe ndipo anayambitsa mipingo yambirimbiri. Komanso, Yehova anadalitsa Paulo ndi masomphenya ndi mphatso ya kulankhula m’malilime. (1 Akorinto 14:18; 2 Akorinto 12:1-5) Mulungu anauziranso Paulo kulemba makalata 14 omwe tsopano ali mbali ya Malemba Achigiriki Achikristu. Mwachionekere, tingatero kuti ntchito yomwe Paulo anagwira inaposa ya atumwi ena onse.—1 Akorinto 15:10.
5. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti sanali kudziona ngati wapamwamba?
5 Popeza kuti Paulo anali mtsogoleri wantchito zachikristu, mwina ena angayembekeze kuti anali kusangalala chifukwa cha kutchukako, ngakhalenso kuonetsera udindo wake modzitama. Koma Paulo sanachite zimenezo popeza kuti anali wodzichepetsa. Anadzitcha “wamng’ono wa atumwi,” akumawonjezera kuti: “Ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.” (1 Akorinto 15:9) Paulo yemwe kale anali wozunza Akristu, sanaiŵale kuti kunali kokha mwa chisomo kuti anatha kupanga ubwenzi ndi Mulungu, makamakanso kusangalala ndi mwayi wapadera wa utumiki. (Yohane 6:44; Aefeso 2:8) Choncho Paulo sanadzimve kuti zomwe ankachita mwachipambano muutumiki zinam’panga kukhala wapamwamba kwa ena.—1 Akorinto 9:16.
6. Kodi Paulo anasonyeza motani kudzichepetsa pochita ndi Akorinto?
6 Kudzichepetsa kwa Paulo kunali kuonekera makamaka momwe anali kuchitira ndi Akorinto. Zikuoneka kuti ena a iwo ankakonda kwambiri omwe anali kuŵalingalira kuti anali oyang’anira otchuka kuphatikizapo Apolo, Kefa, ndi Paulo yemwe. (1 Akorinto 1:11-15) Koma Paulo sanapemphe Akorintowo kuti adzim’tamanda kapena kutengerapo mwayi pa kukopeka kwawoko. Pamene anali kuŵachezera, sanalankhule kwa iwo “ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru.” M’malo mwake, ponena za iye mwini ndi anzake Paulo anati: “Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Kristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.”a—1 Akorinto 2:1-5; 4:1.
7. Kodi Paulo anasonyeza motani kudzichepetsa ngakhale popereka uphungu?
7 Paulo anasonyezanso kudzichepetsa popereka uphungu wamphamvu ndi malangizo. Iye anachonderera Akristu anzakewo “mwa zifundo za Mulungu” ndinso “mwa chikondi” osati chifukwa cha kukula kwa udindo womwe anali nawo monga mtumwi. (Aroma 12:1, 2; Filemoni 8, 9) Kodi Paulo anachitiranji zimenezi? Chifukwa chake n’chakuti analidi kudziona monga wantchito ‘wothandizana’ ndi abale akewo, osati monga ‘wochita ufumu pa chikhulupiriro chawo.’ (2 Akorinto 1:24) Mosakayika kunali kudzichepetsa kwa Pauloku komwe kunathandiza kuti akhale wokondedwa kwambiri ndi mipingo yachikristu ya m’zaka za zana loyamba.—Machitidwe 20:36-38.
Kuona Maudindo Athu Modzichepetsa
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudziona modzichepetsa? (b) Kodi omwe ali ndi udindo wakutiwakuti angasonyeze motani kudzichepetsa?
8 Paulo anapereka chitsanzo chabwino zedi kwa Akristu lerolino. Kaya tapatsidwa maudindo otani, palibe chifukwa chakuti wina aliyense wa ife azidziona ngati wopambana kuposa ena onse. “Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe,” analemba motero Paulo, “adzinyenga yekha.” (Agalatiya 6:3) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ‘onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.’ (Aroma 3:23; 5:12) Inde, tisaiŵale kuti tonsefe tinalandira uchimo ndi imfa kuchokera kwa Adamu. Maudindo apadera samatikweza kutichotsa m’mkhalidwe wathu wotsika wauchimowu. (Mlaliki 9:2) Monga momwedi zinalili kwa Paulo, ndi kupyolera mwa chisomo kuti anthu angapange ubwenzi ndi Mulungu, ndi kupatsidwa mwayi wa kum’tumikira m’maudindo ena apadera.—Aroma 3:12, 24.
9 Pozindikira zimenezi, munthu wodzichepetsa sanyadira udindo wake momkitsa kapena kudzitamandira akachita zinthu zina mwachipambano. (1 Akorinto 4:7) Popereka uphungu kapena malangizo, amachita motero monga wantchito mnzawo—osati monga mbuye wawo. Ndithudi, kungakhale kulakwa kuti munthu amene akuchita bwino pa ntchito inayake achite kupempha chitamando kwa okhulupirira anzake kapena kupezerapo mwayi pa kukopeka kwawo ndi kuchita bwino kwakeko. (Miyambo 25:27; Mateyu 6:2-4) Chitamando chokhacho chomwe n’choyeneradi pa china chilichonse chimachokera kwa ena—ndipo chimaperekedwa osati chifukwa chakuti mwapempha. Pamene chabwera, tisalole kuti chitichititse kulingalira mopambanitsa za ife eni koposa mmene tiyenera kudzilingalira.—Miyambo 27:2; Aroma 12:3.
10. Fotokozani momwe ena amene angaoneke ngati otsika angakhalire “olemera ndi chikhulupiriro.”
10 Pamene tapatsidwa udindo wakutiwakuti, kudzichepetsa kudzatithandiza kupeŵa kudziona monga opambana kwambiri, kukhala ndi lingaliro lakuti mpingo ukuyenda bwino chifukwa cha khama ndi maluso a ife tokha. Mwachitsanzo, mwinamwake tingapatsidwe mphatso ya kuphunzitsa. (Aefeso 4:11, 12) Koma ngati ndife odzichepetsa, tidzazindikira kuti ena mwa maphunziro akuluakulu ophunziridwa pa msonkhano wampingo samaperekedwa kuchokera pa pulatifomu. Kodi sim’malimbikitsidwa, mwachitsanzo, kuona kholo lopanda mnzake wa muukwati lomwe nthaŵi zonse limafika ku Nyumba ya Ufumu limodzi ndi ana? Kapena anthu opsinjika maganizo omwe mokhulupirika amabwera kumisonkhano mosasamala kanthu kuti nthaŵi zonse amamva kukhala opanda pake mumtima? Kapena achinyamata omwe mosagwedera akupita patsogolo mwauzimu ngakhale kuti amakumana ndi zisonkhezero zoipa ku sukulu ndi kwina kulikonse? (Salmo 84:10) Anthu ameneŵa angakhale osadziŵika kwenikweni mumpingomo. Mokulira, ena saona n’komwe kuyesedwa kwa chikhulupiriro cha anthu ameneŵa. Komabe, angakhale “olemera ndi chikhulupiriro” mofanana ndi omwe ali otchuka kwambiri. (Yakobo 2:5) Ndiiko komwe, n’kukhulupirikatu basi komwe Yehova amafuna.—Mateyu 10:22; 1 Akorinto 4:2.
Gideoni—“Wamng’ono” M’nyumba ya Atate Wake
11. Kodi Gideoni anasonyeza motani kudzichepetsa polankhula ndi mngelo wa Mulungu?
11 Gideoni, mnyamata wamphamvu wa fuko la Manase, anakhala ndi moyo m’nthaŵi yovuta kwambiri m’mbiri ya Israyeli. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, anthu a Mulungu anazunzika mu ulamuliro wankhanza wa Amidyani. Koma, tsopano nthaŵi inakwana yakuti Yehova awombole anthu ake. Chotero, mngelo anaonekera kwa Gideoni nati: “Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.” Gideoni anali wodzichepetsa, choncho sanakhutire momkitsa ndi ulemerero wa matamando aulemu osayembekezerekawo. M’malo mwake, anauza mngeloyo mwaulemu kuti: “Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi?” Mngeloyu anamveketsa nkhaniyo bwino lomwe nati kwa Gideoni: ‘Udzapulumutsa Israyeli m’dzanja la Midyani.’ Kodi Gideoni anachitanji? M’malo mojijirikira ntchitoyo, akumaona ngati mwayi wakuti adziŵike monga ngwazi yadziko lonse, Gideoni anayankha nati: “Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israyeli ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka m’Manase, ndipo ine ndine wamng’ono m’nyumba ya atate wanga.” Kudzichepetsatu kwenikweni!—Oweruza 6:11-15.
12. Kodi Gideoni anasonyeza motani nzeru pogwira ntchito yomwe anapatsidwa?
12 Asanatumize Gideoni ku nkhondo, Yehova anam’yesa. Motani? Gideoni anauzidwa kuphwasula guwa la nsembe la atate wake la Baala, ndi kudula mlongoti wopatulika womwe anauimika cha pafupi ndi guwalo. Ntchito imeneyi inafuna kulimba mtima, koma Gideoni anaigwira mosonyeza kudzichepetsa ndi nzeru. M’malo modzionetsera kwa onse, Gideoni anagwira ntchitoyo usiku pomwe mwachidziŵikire anali wokhoza kuchita chilichonse popanda wina aliyense kumuona. Komanso, Gideoni anagwira ntchito yakeyo mwa ukatswiri zedi. Anatenga anyamata ake khumi—mwinamwake kuti ena adzikalondera pamene enawo akum’thandiza kuphwasula guwa la nsembe ndi mlongoti wopatulikawo.b Mulimonse mmene zinalili, mwa madalitso a Yehova, Gideoni anachita ntchito yake, ndipo m’kupita kwa nthaŵi Mulungu anam’gwiritsa ntchito kuwombola Aisrayeli m’manja mwa Amidyani.—Oweruza 6:25-27.
Kusonyeza Kudzichepetsa ndi Nzeru
13, 14. (a) Kodi tingasonyeze motani kudzichepetsa pamene tapatsidwa mwayi wa utumiki? (b) Kodi Mbale A. H. Macmillan anapereka chitsanzo chabwino chotani posonyeza kudzichepetsa?
13 Pali zambiri zomwe tingaphunzire pa kudzichepetsa kwa Gideoni. Mwachitsanzo, kodi timachita motani tikapatsidwa udindo wautumiki? Kodi timalingalira kaye choyamba za kukhala kwathu apamwamba kapena kutchuka komwe kudzatsatira? Kapena kodi timalingalira modzichepetsa ndi mwapemphero ngati tingakwaniritse zolinga zofunika za ntchitoyo? Mbale A. H. Macmillan, yemwe anamaliza moyo wake wa padziko lapansi m’chaka cha 1966, anapereka chitsanzo chabwino pambali imeneyi. C.T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, nthaŵi inayake anafunsa Mbale Macmillan kuti amve malingaliro ake ponena za amene angadzakhale wotsogolera ntchito iye kulibe. M’kukambirana kwawo kotsatirapo, Mbale Macmillan sanadzichemerere, ngakhale kuti ikanakhala nthaŵi yabwino yochitira zimenezo. Pamapeto pake, Mbale Russell anapempha Mbale Macmillan kulingalira mosamalitsa kuti iyeyo avomere udindowu. “Ndinangoima chilili n’tagwira njakata,” Mbale Macmillan analemba choncho pambuyo pa zaka zingapo. “Ndinalingalira za nkhaniyo mozama kwambiri, ndi kuipempherera kwa kanthaŵi ndithu ndisanamuuze kuti ndidzakondwa kuchita chilichonse chomwe ndingathe kuti ndim’thandize.”
14 Pasanapite nthaŵi yaitali, Mbale Russell anamwalira, kusiya ofesi ya pulezidenti wa Watch Tower Society ili yopanda munthu. Popeza kuti Mbale Macmillan n’njemwe anali woyang’anira m’kati mwa ulendo wotsiriza wa ulaliki wa Mbale Russell, mbale wina anamuuza kuti: “Mac, uli ndi mwayi waukulu wa kulandira udindo wa upulezidenti. Unali woimira wapadera wa Mbale Russell pamene anali atachoka, ndipo anatiuza tonsefe kuchita zonse zimene iwe unganene. Ndithudi, anapita ndipo sanabwererenso. Zikuoneka kuti iweyo ndiye munthu amene adzatenga malo ake.” Mbale Macmillan anayankha nati: “Mbale, nkhani imeneyi sitiyenera kuiona motero. Iyi ndi ntchito ya Ambuye ndipo udindo umene umalandira m’gulu la Ambuye, ndi wokhawo womwe Ambuyewo aona kuti n’koyenera kuti akupatse; ndipo ndine wotsimikiza kuti sindine amene ndidzagwira ntchito imeneyo.” Kenako Mbale Macmillan anatchula munthu wina ndikuti ameneyo ali woyenera kudzatenga udindo umenewo. Mofanana ndi Gideoni, anali wodzichepetsa—n’khalidwe loyeneradi kulitsanzira.
15. Kodi tingagwiritse ntchito kuzindikira m’njira zina ziti zothandiza pamene tikulalikira kwa ena?
15 Nafenso tiyenera kukhala odzichepetsa pamene tikugwira ntchito yomwe tapatsidwa. Gideoni anali wanzeru, ndipo anayesetsa kuti asakwiyitse om’tsutsa mwachisawawa. Mofananamo, pa ntchito yathu yolalikira, tikhaletu odzichepetsa ndi anzeru m’kulankhula kwathu ndi ena. Zoonadi, tili m’nkhondo yauzimu yolimbana ndi “malinga” komanso “matsutsano.” (2 Akorinto 10:4, 5) Koma malankhulidwe athu sayenera kukhala onyoza ena kapena kuŵapatsa chifukwa chilichonse chokhumudwira ndi uthenga wathu. M’malo mwake, tiyenera kulemekeza maganizo awo, kugogomezera chinthu chomwe tingagwirizane nawo, ndipo kenako tingasumike pa mbali za uthenga wathuwu zomwe zingaŵasangalatse.—Machitidwe 22:1-3; 1 Akorinto 9:22; Chivumbulutso 21:4.
Yesu—Chitsanzo Chapamwamba cha Kudzichepetsa
16. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kudziona modzichepetsa?
16 Chitsanzo chabwino koposa cha kudzichepetsa ndicho cha Yesu Kristu.c Ngakhale kuti anali ndi unansi wabwino kwambiri ndi Atate wake, Yesu sanazengereze kunena poyera kuti analibe ulamuliro wochitira zinthu zina. (Yohane 1:14) Mwachitsanzo, pamene amake a Yakobo ndi Yohane anapempha kuti ana awo aŵiriwo adzakhale wina kudzanja lamanja la Yesu ndi wina kulamanzere mu ufumu wake, Yesu anati: “Kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa.” (Mateyu 20:20-23) Nthaŵi inayake, Yesu momasuka anavomereza kuti: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha . . . Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.”—Yohane 5:30; 14:28; Afilipi 2:5, 6.
17. Kodi Yesu anasonyeza motani kudzichepetsa m’kachitidwe kake ndi ena?
17 Yesu anali wapamwamba kwa anthu opanda ungwiro pa chilichonse, ndipo anali ndi ulamuliro wochuluka kuposa wa munthu wina aliyense, wochokera kwa Atate ake, Yehova. Ngakhale kuti zinali choncho, Yesu anali wodzichepetsa pochita ndi otsatira ake. Sanaŵazizwitse mwa kuŵaonetsera chidziŵitso chake chochulukacho. Anasonyeza kudera nkhaŵa ndi chifundo ndipo anali kulingalira zosoŵa zawo zaumunthu. (Mateyu 15:32; 26:40, 41; Marko 6:31) Choncho, ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, analibe malingaliro akuti chilichonse chichitike mwangwiro. Sanauzepo ophunzira akewo kuchita zomwe sakanatha kukwanitsa, ndipo sanaŵapatse zomwe sakanatha kuzisenza. (Yohane 16:12) N’chifukwa chaketu ambiri anali kukapeza mpumulo kwa iye!—Mateyu 11:29.
Tsanzirani Chitsanzo cha Yesu cha Kudzichepetsa
18, 19. Kodi tingatsanzire motani kudzichepetsa kwa Yesu pa (a) momwe timadzionera, ndi (b) mmene timachitira ndi ena?
18 Ngati munthu wamkulu kuposa onse omwe anakhalako anasonyeza kudzichepetsa, kuli bwanji ife. Kaŵirikaŵiri anthu opanda ungwiro safuna n’komwe kuvomereza kuti alibe ulamuliro pa chilichonse. Komabe, potsanzira Yesu, Akristu amayesetsa kudzichepetsa. Sali onyada kotero kuti n’kulephera kupereka udindo kwa omwe ali oyenerera kuulandira; kapena sali ouma mtima ndi osafuna kumvera malangizo ochokera kwa omwe ali ndi udindo wopereka malangizo. Posonyeza mzimu wogwirizana, amalola zinthu zonse mu mpingo kuchitika ‘moyenera ndi molongosoka.’—1 Akorinto 14:40.
19 Kudzichepetsa kudzatisonkhezera kusayembekezera zomkitsa kwa ena ndi kulingalira zosoŵa zawo zazikulu. (Afilipi 4:5) Tingakhoze kukhala ndi maluso ena ake ndi nyonga zomwe ena alibe. Komabe, ngati ndife odzichepetsa, sitidzayembekezera kuti nthaŵi zonse ena achite zinthu monga momwe ife tingafunire. Podziŵa kuti munthu aliyense ali ndi zofooka zake, tonsefe tidzavomereza modzichepetsa zophophonya za ena. Petro analemba kuti: “Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.”—1 Petro 4:8.
20. Kodi tingatani kuti tigonjetse chizoloŵezi chilichonse cha kudzikuza?
20 Monga momwe taphunzirira, nzeru zilidi ndi odzichepetsa. Koma nanga bwanji ngati mwaona kuti muli ndi chizoloŵezi cha kudzikuza kapena kudzitama? Musakhumudwe. M’malo mwake tsanzirani chitsanzo cha Davide, yemwe anapemphera kuti: “Muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine.” (Salmo 19:13) Mwa kutsanzira chikhulupiriro cha amuna monga Paulo, Gideoni, ndiponso—kuposa wina aliyense—Yesu Kristu, ndithudi aliyense payekha tidzazindikira kuona kwa mawu akuti: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.”—Miyambo 11:2.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “atumiki” angaimire kapolo wopalasa ngalawa yaikulu pogwiritsa ntchito zopalasira zakunthungo m’ngalawamo. Mosiyana ndi zimenezo, “adindo” angapatsidwe maudindo ambiri, mwinamwake kuyang’anira munda waukulu. Komabe, kwa olamulira ambiri, mdindo sanali kum’siyanitsa ndi mtumiki wopalasa ngalawayo.
b Kuchita mwanzeru ndi mochenjera kwa Gideoni sikuyenera kulingaliridwa molakwa n’kumati chinali chizindikiro cha mantha. M’malo mwake, kulimba mtima kwakeko kwatsimikiziridwa pa Ahebri 11:32-38, pamene akutchula Gideoni limodzi ndi ena omwe “analimbikitsidwa” ndi amenenso “anakula mphamvu kunkhondo.”
c Popeza kuti kudzichepetsa kumaphatikizapo kudziŵa zinthu zimene sungathe kuchita, ndithudi sitingati Yehova n’ngwodzichepetsa, kuchita ngati pali china chilichonse chimene sangathe kuchita. Koma, n’ngwofatsa.—Salmo 18:35.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi kudzichepetsa n’chiyani?
• Kodi tingatsanzire motani kudzichepetsa kwa Paulo?
• Kodi tingaphunzirenji ponena za kudzichepetsa m’chitsanzo cha Gideoni?
• Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo chapamwamba cha kudzichepetsa?
[Chithunzi patsamba 15]
Kudzichepetsa kwa Paulo kunam’pangitsa kukhala wosiririka kwa Akristu anzake
[Chithunzi patsamba 17]
Gideoni anagwiritsa ntchito nzeru pochita chifuno cha Mulungu
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu, Mwana wa Mulungu, amasonyeza kudzichepetsa pa zonse zimene amachita