Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
“Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko”
YEREKEZERANI kuti mukuona Rute ndi apongozi ake a Naomi akuyenda okhaokha m’chigwa cha Mowabu. Kenako Rute pozindikira kuti kunja kwatsala pang’ono kuda, akuyamba kuganiza za kumene angapeze malo oti iyeyo ndi apongozi ake agone. Rute ankawakonda kwambiri apongozi ake ndipo anali wokonzeka kuchita chilichonse kuti awasamalire.
Azimayi awiri onsewa anali ndi chisoni chachikulu. Panali patapita zaka zambiri kuchokera pamene mwamuna wa Naomi anamwalira. Koma pa nthawiyi, Naomi analinso ndi chisoni chifukwa cha imfa ya ana ake awiri, Kiliyoni ndi Maloni. Nayenso Rute anali ndi chisoni ndi imfa ya Maloni chifukwa anali mwamuna wake. Rute ndi apongozi akewo anali pa ulendo wopita ku Betelehemu m’dziko la Isiraeli. Ku Betelehemu kunali kwawo kwa Naomi koma Rute anali wa ku Mowabu. Choncho Rute ankapita kudziko lachilendo ndipo anali atasiya abale ake komanso miyambo ndi milungu ya kwawo.—Rute 1:3-6.
Kodi n’chiyani chinachititsa Rute kuti apite nawo kudziko lachilendolo? Nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire imfa ya mwamuna wake komanso kuti athe kusamalira apongozi ake? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kuona mmene tingatsanzirire chikhulupiriro cha Rute. Choyamba, tiyeni tione zimene zinachititsa azimayi awiriwa kuti apezeke ali pa ulendo wopita ku Betelehemu.
Banja la Naomi Linakumana ndi Mavuto
Rute anakulira m’dziko la Mowabu lomwe lili kum’mawa kwa Nyanja Yakufa. Derali linali lokwera ndipo linali ndi mitengo patalipatali komanso maphedi. Dzikoli linali lachonde moti ngakhale pa nthawi imene ku Isiraeli kunali njala, m’dzikoli munali chakudya chokwanira. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti Rute akumane ndi Maloni ndi abale ake.—Rute 1:1.
Njala imene inagwa ku Isiraeli inachititsa kuti Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi, atenge mkazi ndiponso ana ake awiri aamuna kupita kukakhala m’dziko la Mowabu monga alendo. Zimenezi ziyenera kuti zinali zovuta kwa onsewa chifukwa Aisiraeli anali ndi nthawi zimene ankafunika kulambira Yehova. Iwo ankayenera kuchita zimenezi pamalo amene Yehova anasankha ndipo malo amenewo anali ku Isiraeli. (Deuteronomo 16:16, 17) Komabe ngakhale pamene Elimeleki anamwalira, Naomi anapitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Mulungu.—Rute 1:2, 3.
Patapita nthawi iye ayenera kuti anamvanso chisoni pamene ana ake aja anakwatira akazi achimowabu. (Rute 1:4) Naomi ankadziwa kuti Abulahamu, yemwe anali tate wa fuko lawo, anayesetsa kupezera mwana wake Isaki mkazi wolambira Yehova. (Genesis 24:3, 4) Komanso Chilamulo cha Mose chinkaletsa Aisiraeli kulola ana awo aamuna kapena aakazi kukwatirana ndi anthu amitundu ina. Chinkaletsa zimenezi poopa kuti Aisiraeliwo angayambe kulambira mafano.—Deuteronomo 7:3, 4.a
Naomi ayenera kuti anakhumudwa Maloni ndi Kiliyoni atakwatira akazi achimowabu, omwe mayina awo anali Rute ndi Olipa. Komabe iye ankawakonda azipongozi akewo. Mwina iye anali ndi chikhulupiriro choti nthawi ina nawonso adzayamba kulambira Yehova. Kaya Naomi ankakhulupiriradi zimenezi kapena ayi, koma zikuoneka kuti Olipa ndi Rute ankawakondanso kwambiri apongozi awowa. Ndipo kukondana kumeneku kunawathandiza kwambiri pa nthawi imene anakumana ndi mavuto. Azimuna awo a atsikanawa anamwalira iwo asanabereke n’komwe ana.—Rute 1:5.
N’zokayikitsa ngati chipembedzo cha Rute chinamuthandiza kudziwa zoyenera kuchita pa nthawi ya mavutowa. Amowabu ankalambira milungu yambiri ndipo mulungu wawo wamkulu anali Kemosi. (Numeri 21:29) Zikuoneka kuti Amowabu nawonso ankachita nawo zinthu zankhanza zimene zinali zofala pa nthawiyo kuphatikizapo kupereka nsembe ana. Zimene Rute anaphunzira kwa Maloni ndiponso Naomi zokhudza Yehova, Mulungu wa Aisiraeli, ziyenera kuti zinamuthandiza kuona kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi milungu ya Amowabu. Iye anaphunzira kuti Yehova ndi wachikondi komanso wachifundo ndipo anthu amamulambira chifukwa chomukonda osati chifukwa cha mantha. (Deuteronomo 6:5) Pa nthawi imene Rute anali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mwamuna wake, ayenera kuti ankacheza kwambiri ndi Naomi ndipo ankamvetsera zimene apongozi akewo ankafotokoza zokhudza ntchito zazikulu za Yehova, chikondi chake komanso chifundo chimene amachitira anthu ake.
Pa nthawi yonse imene Naomi ankakhala ku Mowabu ankafunitsitsa kumva mmene zinthu zinalili ku Isiraeli. Tsiku lina iye anamva kuti ku Isiraeli kunalibenso njala ndipo ayenera kuti anamva zimenezi kuchokera kwa anthu amalonda. Yehova anali atakumbukira anthu ake kumeneko. Tsopano ku Betelehemu kunali chakudya chokwanira ndipo izi zinali zogwirizana ndi dzina loti Betelehemu, lomwe limatanthauza “Nyumba ya Chakudya.” Choncho Naomi anaganiza zobwerera kwawo.—Rute 1:6.
Popeza Rute ndi Olipa anazolowerana kwambiri ndi apongozi awowa, kodi iwo anatani atamva kuti apongozi awo akufuna kubwerera kwawo? Baibulo limanena kuti iwo anaganiza zopitira nawo limodzi ku Yuda. (Rute 1:7) Ngakhale kuti atsikana onsewa ankakonda apongozi awowa, zikuoneka kuti Rute ankawakonda kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwawo komanso chikhulupiriro chawo pa Yehova.
Nkhani ya Rute imatikumbutsa kuti mavuto amagwera anthu onse, abwino ndi oipa omwe. (Mlaliki 9:2, 11) Nkhaniyi ikutiphunzitsanso kuti tikakhala pa mavuto, ndi bwino kumacheza ndi anthu ena, makamaka amene amadalira Yehova, Mulungu amene Naomi ankalambira.—Miyambo 17:17.
Rute Anali ndi Chikondi Chosatha
Azimayiwa atayenda mtunda wautali ndithu, Naomi anayamba kuda nkhawa. Iye anayamba kuganizira za azipongozi akewo komanso chikondi chimene anamusonyeza iyeyo ndiponso ana ake aja. Iye anaona kuti si bwino kuti awawonjezerenso mtolo wina. Naomi anadziwa kuti akakafika ndi azipongozi akewo ku Betelehemu palibe chimene akawachitire.
Ataganizaganiza nkhaniyi, Naomi anauza azipongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.” Iye anasonyezanso kuti ankakhulupirira kuti Yehova awadalitsa powapatsa amuna ena. Baibulo limanena kuti atatero “anawapsompsona. Pamenepo iwo anayamba kulira mokweza mawu.” Zinali zovuta kwa Rute ndi Olipa kuti asiyane ndi apongozi awowo chifukwa iwo anali mayi wokoma mtima komanso woganizira ena. Choncho Rute ndi Olipa anakana kubwerera ndipo anauza Naomi kuti: “Ayi musatero, ife tipita nanu kwanu.”—Rute 1:8-10.
Koma Naomi anapitirizabe kuwakakamiza kuti abwerere. Iye anawafotokozera kuti panalibe chifukwa choti apitire limodzi ku Isiraeli popeza iye analibe mwamuna woti azikawasamalira, analibe ana oti angakawakwatire ndipo panalibe chiyembekezo choti iyeyo angadzakhalenso ndi ana ena. Iye ananenanso kuti zinkamuwawa kwambiri akaganiza kuti panalibe chimene akanachita kuti awathandize.—Rute 1:11-13.
Olipa anaona kuti zimene apongozi ake ananenazi zinali zoona. Iye anaona kuti ndi bwinodi kuti atsale ku Mowabu chifukwa n’kumene kunali abale ake, amayi ake komanso nyumba. Choncho, mwachisoni iye anapsompsona apongozi akewo ndipo kenako anabwerera.—Rute 1:14.
Koma kodi Rute anatani? Iyenso anaona kuti zimene apongozi ake ananena zinali zoona. Koma Baibulo limati: “Rute anawaumirirabe.” Mwina Naomi ankaganiza kuti onse abwerera, koma atayang’ana m’mbuyo anaona kuti Rute akumutsatirabe. Choncho Naomi anati: “Taona m’bale wako wamasiye wabwerera kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake. Bwerera naye limodzi.” (Rute 1:15) Mawu amene Naomi ananenawa akutiuza zambiri. Sikuti Olipa anangobwerera kwa anthu a kwawo, koma iye anabwereranso kwa “milungu yake.” Iye analolera kukapitiriza kulambira Kemosi komanso milungu ina. Koma kodi Rute ankaonanso kuti palibe vuto ngati angabwerere kuti akapitirize kulambira milungu ya kwawo?
Rute ankaona kuti sangachite zimenezo. Iye ankakonda kwambiri Naomi komanso Mulungu amene Naomiyo ankalambira. Choncho iye anauza Naomi kuti: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, pakuti kumene inu mupite inenso ndipita komweko, kumene inu mugone inenso ndigona komweko. Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko, ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri ngati chinachake kupatulapo imfa chingandilekanitse ndi inu.”—Rute 1:16, 17.
Mawu amene Rute ananenawa ndi osaiwalika moti anthu ambiri amawakumbukirabe ngakhale kuti papita zaka 3,000 kuchokera pamene ananenedwa. Mawuwa akusonyeza khalidwe lina lofunika kwambiri limene Rute anali nalo, lomwe ndi chikondi chosatha. Iye ankakonda kwambiri Naomi moti palibe chimene chikanawalekanitsa, kupatulapo imfa. Rute ankayembekezera kuti anthu a mtundu wa Naomi ndi amene akhale anthu a mtundu wake choncho anali wokonzeka kusiya chilichonse ku Mowabu, kuphatikizapo milungu yake. Mosiyana ndi Olipa, Rute ananena ndi mtima wonse kuti akufuna kuti Yehova, Mulungu wa Naomi, akhalenso Mulungu wake.b
Choncho azimayi awiriwa anapitiriza ulendo wawo wopita ku Betelehemu. Anthu ena amanena kuti mwina ulendowu unatenga mlungu wathunthu. Popeza awiri onsewa anali ndi chisoni chifukwa cha zimene zinawachitikira zija, ayenera kuti pa ulendo wawowu ankalimbikitsana.
Anthu ambiri masiku ano amakumananso ndi mavuto. Baibulo limanena kuti, tikukhala ino ndi “nthawi yapadera komanso yovuta” ndipo timakumana ndi zinthu zosiyanasiyana zomvetsa chisoni. (2 Timoteyo 3:1) Choncho khalidwe limene Rute anasonyeza ndi lofunika kwambiri masiku ano. Munthu akakhala ndi chikondi chosatha pa munthu wina, amamumamatira kwambiri munthuyo ndipo salola kuti asiyane naye. Chikondi choterechi n’chothandiza kwambiri m’dziko lamavutoli. N’chofunika kwambiri m’banja, mu mpingo, kwa mabwenzi komanso kwa anthu apachibale. Tikamayesetsa kusonyeza chikondi choterechi, ndiye kuti tikutengera chitsanzo chabwino cha Rute.
Zimene Zinachitika Rute ndi Naomi Atafika ku Betelehemu
Munthu sangangonena ndi pakamwa kuti ali ndi chikondi, zochita zake n’zimene zingasonyeze kuti alidi ndi chikondi. Rute anali ndi mwayi woti asonyeze kuti amakonda kwambiri Naomi komanso Yehova, Mulungu amene anasankha kumutumikira.
Kenako azimayi awiriwa anafika ku Betelehemu, mudzi womwe unali pa mtundu wa makilomita 10, kum’mwera kwa Yerusalemu. Banja la Naomi liyenera kuti linali lodziwika kwambiri m’tauniyi chifukwa iye atangofika anthu onse ankakamba za iyeyo. Azimayi ambiri ankamuyang’anitsitsa n’kumanena kuti, “Kodi si Naomi uyu?” Zikuoneka kuti iye anali atasintha mmene ankaonekera poyamba chifukwa cha zimene anakumana nazo ku Mowabu ndipo nkhope yake inkasonyezeratu kuti anali ndi chisoni.—Rute 1:19.
Naomi anafotokozera achibale ake komanso anthu ena okhala nawo pafupi mavuto amene anakumana nawo ali ku Mowabu. Iye ankaona kuti sayenera kutchedwanso Naomi, kutanthauza “Chisangalalo Changa” koma ayenera kutchedwa Mara, kutanthauza “Zowawa.” Mofanana ndi Yobu, Naomi ankaona ngati Yehova Mulungu ndi amene wachititsa mavuto akewo.—Rute 1:20, 21; Yobu 2:10; 13:24-26.
Azimayiwa atakhazikika ku Betelehemu, Rute anayamba kuganiza zimene angachite kuti azipeza zosowa zake komanso kuti azisamalira apongozi ake. Iye anamva kuti Chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Aisiraeli chinaphatikizapo lamulo lothandiza anthu osauka. Lamuloli linkalola anthu osauka kuti azipita m’minda ya anthu pa nthawi yokolola n’kumakunkha zotsalira komanso mbewu zomera m’mbali mwa munda.c—Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19-21.
Nthawi yokolola balere itakwana, yomwe mwina munali mu April malinga ndi kalendala ya masiku ano, Rute anapita kumene kunali minda ya anthu n’cholinga choti akakunkhe m’munda mwa aliyense amene angamukomere mtima. Mwamwayi iye anafika m’munda mwa munthu wina wolemera dzina lake Boazi amenenso anali m’bale wake wa Elimeleki, mwamuna wa Naomi. Ngakhale kuti lamulo lija linkamulola kukunkha, Rute anayamba wapempha kaye mnyamata amene ankayang’anira anthu amene ankakolola m’mundamo. Mnyamatayo anamulola ndipo iye anayamba kukunkha.—Rute 1:22–2:3, 7.
Yerekezerani kuti mukumuona Rute akutsatira m’mbuyo mwa okololawo. Okololawo akamadula balere ndi zikwakwa zawo zamwala iye ankatola balere amene wagwa kapena amene watsala n’kumumanga mitolo ndipo ankapita naye pamalo amene ankakamupuntha. Ntchito imeneyi inali yowawa komanso yotopetsa makamaka dzuwa likamakwera. Koma Rute ankagwira ntchitoyi mwakhama kwinaku akupukuta thukuta ndipo ankangopuma kanthawi pang’ono “m’chisimba” kuti adye.
Anthu ankaona khama limene Rute ankasonyezali ngakhale kuti iye sankachita zimenezi n’cholinga choti anthu amuone. Mwachitsanzo, Boazi atamuona anazindikira kuti anali mtsikana wolimbikira ntchito. Boazi, yemwe anali munthu wachikhulupiriro, analonjera antchito akewo ndi mawu akuti: “Yehova akhale nanu.” Anthuwonso anamuyankha mawu ofanana ndi omwewo. Ena mwa antchitowo anali aganyu ndipo ena sanali Aisiraeli. Kenako Boazi, yemwe anali wachikulire komanso ankakonda kwambiri Yehova, anafunsa mnyamata amene ankayang’anira okolola aja za Rute.—Rute 2:4-7.
Boazi anatchula Rute kuti “mwana wanga” ndipo anamuuza kuti azibwerabe m’mundamo kudzakunkha. Anamulangizanso kuti azikhala pafupi ndi atsikana ake antchito poopera kuti anyamata antchito aja angamuchite chipongwe. Iye ankamuitaniranso chakudya chamasana ndipo anamuyamikira komanso kumulimbikitsa. Kodi anachita zimenezi motani?—Rute 2:8, 9, 14.
Rute atafunsa Boazi kuti zatheka bwanji kuti amuchitire chifundo iyeyo wokhala mlendo, Boazi anayankha kuti anamva zabwino zimene Ruteyo anachitira apongozi ake a Naomi. N’kutheka kuti Naomi ankayamikira Rute akamacheza ndi azimayi a ku Betelehemu ndipo Boazi anamva zimenezi. Iye anadziwanso zoti Rute anali atayamba kulambira Yehova, n’chifukwa chake anamuuza kuti: “Yehova akudalitse chifukwa cha zimene wachita, ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanira. Iye amene m’mapiko mwake wathawiramo ndi kupezamo chitetezo.”—Rute 2:12.
Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri Rute. Iye analidi atathawira m’mapiko a Yehova Mulungu, ngati mmene mwana wa mbalame amabisalira m’mapiko a mayi ake. Iye anayamikira Boazi chifukwa cholankhula mawu olimbikitsawa ndipo anapitirizabe kukunkha mpaka madzulo.—Rute 2:13, 17.
Chikhulupiriro chimene Rute anasonyeza ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe chifukwa timakumana ndi mavuto ambiri azachuma. Iye sankaona kuti anthu ena akumuthandiza chifukwa choti ndi udindo wawo, choncho ankayamikira chilichonse chimene ena amuchitira. Rute ankagwira mwakhama ntchito yooneka ngati yonyozeka n’cholinga choti azisamalira apongozi ake omwe ankawakonda ndipo sankachita manyazi kuchita zimenezi. Iye anatsatira malangizo amene Boazi anam’patsa omwe anathandiza kuti azicheza ndi anthu abwino ndiponso akhale wotetezeka. Komanso Rute nthawi zonse ankadalira Yehova Mulungu kuti azimuteteza, monga Atate ake.
Ifenso tikatengera chitsanzo cha Rute n’kukhala ndi chikondi chosatha, odzichepetsa, akhama pa ntchito komanso oyamikira, tidzakhala chitsanzo chabwino kwa ena. Koma kodi Yehova anadalitsa bwanji Rute ndi Naomi? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani ina imene idzatuluke kutsogoloku.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa—N’chifukwa Chiyani Mulungu Anauza Aisiraeli Kuti Asamakwatirane Ndi Anthu a Mitundu Ina?” patsamba 29.
b N’zochititsa chidwi kuti Rute sanangotchula kuti “Mulungu” ngati mmene anthu amene sankalambira Yehova ankachitira. M’malomwake iye anagwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova. Baibulo lina linanena kuti: “Pamenepa amene analemba buku la Rute anatsindika mfundo yoti ngakhale kuti Rute sanali Mwisiraeli, iye ankalambira Mulungu woona.”—The Interpreter’s Bible.
c Lamulo limeneli linali lachilendo kwambiri kwa Rute chifukwa kwawo kunalibe lamulo lotere. Kale ku Middle East akazi amasiye ankazunzika ndipo buku lina linati: “Mwamuna akamwalira, nthawi zambiri mkazi ankadalira ana ake aamuna. Ngati alibe ana, ankadzigulitsa ku ukapolo, apo ayi ankafunika kusankha kuyamba uhule kapena kungofa.”
[Bokosi patsamba 26]
Buku Laling’ono Koma Lolembedwa Mwaluso
Anthu amanena kuti buku la Rute linalembedwa mwaluso kwambiri ngakhale kuti ndi laling’ono. Nkhani zimene zili m’bukuli n’zosiyana ndi zimene zili m’buku la Oweruza lomwe lili m’mbuyo mwa bukuli. Komabe nkhani za m’buku la Oweruza zimatithandiza kudziwa nthawi imene zinthu zimene zili m’buku la Rute zinachitika. (Rute 1:1) Mabuku awiri onsewa analembedwa ndi mneneri Samueli ndipo tikamawerenga Baibulo timaona kuti buku la Rute linaikidwa pamalo abwino m’Baibulo. M’buku la Oweruza timawerenga nkhani zokhudza nkhondo komanso kufunkha katundu. Koma kenako timapeza buku la Rute limene limatikumbutsa kuti Yehova saiwala anthu okhulupirika amene akukumana ndi mavuto. Nkhani ya m’bukuli yomwe imanena za zochitika m’banja, imatiphunzitsa mfundo zofunika pa nkhani ya chikondi, chikhulupiriro komanso zimene tingachite tikaferedwa.
[Chithunzi patsamba 24]
Rute ankacheza kwambiri ndi Naomi pa nthawi imene anali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mwamuna wake
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
“Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga”
[Chithunzi patsamba 27]
Rute ankagwira mwakhama ntchito yooneka ngati yonyozeka n’cholinga choti azipeza zosowa zake komanso azisamalira Naomi