Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
RUTE, yemwe ankakhala ku Betelehemu, anagwada pafupi ndi mtolo wa balere amene anali atakunkha tsiku limenelo. Kunja kunali kutada ndipo anthu ambiri anali atayamba kubwerera kunyumba zawo, zomwe zinali m’dera lokwera. Rute anali atatopa kwambiri chifukwa anali atagwira ntchito tsiku lonse. Komabe iye anatenga kamtengo kopunthira n’kuyamba kupuntha balere wakeyo. Ngakhale kuti anali atatopa kwambiri, Rute anali wosangalala chifukwa ankaona kuti wapeza balere wambiri kusiyana ndi masiku onse.
Kodi zimenezi zinasonyeza kuti tsopano zinthu ziyamba kumuyendera bwino Rute, yemwenso anali mayi wamasiye? Iye anasankha kubwera ku Yerusalemu ndi apongozi ake, a Naomi ndipo analonjeza kuti azikhala nawo n’kumalambira Yehova, Mulungu wa a Naomiwo ngati Mulungu wake. Naomi nayenso anali mayi wamasiye ndipo poyamba azimayi awiriwa ankakhala ku Mowabu. Rute, yemwe anali Mmowabu, anamva kuti m’Chilamulo cha Yehova munali lamulo lothandiza anthu osauka mu Isiraeli kuphatikizapo alendo.a Ndipo pa nthawiyi anali ataona kuti anthu a Yehova omwe ankatsatira Chilamulochi, anali anthu amakhalidwe abwino komanso okoma mtima, ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kwambiri.
Mmodzi mwa anthu a makhalidwe abwino amenewa anali Boazi, yemwe anali wolemera komanso wachikulire ndipo Rute ankakunkha m’munda mwa munthu ameneyu. Boazi anachita chidwi ndi Rute chifukwa anali wamakhalidwe abwino ndipo anamuyamikira. Rute ankasangalala mumtima mwake akakumbukira mawu olimbikitsa amene Boazi ananena. Boazi anamuyamikira chifukwa choti ankasamalira apongozi ake omwe anali achikulire komanso chifukwa chosankha kuti azilambira Yehova.—Rute 2:11-13.
Komabe n’kutheka kuti Rute ankada nkhawa akaganiza za tsogolo lake. Popeza iye anali mlendo wosauka komanso analibe mwamuna kapena mwana, mwina ankaganiza kuti ndani adzamusamalire komanso kusamalira apongozi ake m’tsogolo. Kodi iwo azidzangodalirabe kukunkha? Nanga akadzakalamba, ndani azidzamusamalira? N’zomveka kukhala ndi maganizo amenewa. Masiku anonso, chifukwa cha mavuto azachuma, anthu ambiri amakhala ndi nkhawa zofanana ndi zimenezi. Tiyeni tikambirane mmene chikhulupiriro cha Rute chinamuthandizira pa nthawi yovutayi, ndipo tionanso mmene tingamutsanzirire.
Kodi Tikati Banja N’chiyani?
Rute atamaliza kupuntha balere wake uja n’kumuunjika pamodzi, anaona kuti akukwana efa yathunthu. Balere ameneyu anali wokwana makilogalamu 14. Atatero anaika balereyo pansalu n’kusenza ndipo anayamba ulendo wopita ku Betelehemu. Pa nthawiyi, kunja kunali kutada.—Rute 2:17.
Naomi anasangalala ataona mpongozi wakeyu, yemwe ankamukonda kwambiri, ndipo mwina anadabwa ataona kuchuluka kwa Balere amene Rute anakunkha. Rute anali atabweretsanso chakudya chimene chinatsala, chomwe Boazi anam’patsa pamene ankadya ndi anyamata ake. Rute ndi Naomi anayamba kudya chakudyachi. Ndiyeno Naomi anamufunsa kuti: “Kodi unakakunkha kuti lero? Adalitsike amene wakuganizirayo.” (Rute 2:19) Naomi ataona balere amene Rute anabweretsa, anadziwa kuti pali munthu wina amene anamukomera mtima Ruteyo kuti apeze balere wochuluka choncho.
Kenako Naomi ndi Rute anayamba kucheza ndipo Rute anafotokoza zabwino zimene Boazi anamuchitira. Atachita chidwi ndi zimene Boazi anachitazo, Naomi ananena kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha kwa amoyo ndi akufa, am’dalitse munthu ameneyu.” (Rute 2:19, 20) Iye anaona kuti zimene Boazi anachita, zinali zochokera kwa Yehova yemwe amachititsa atumiki ake kukhala owolowa manja. Yehova amalonjeza kuti adzadalitsa atumiki ake amene amakomera mtima anthu ena.b—Miyambo 19:17.
Naomi analangiza Rute kuti amvere zimene Boazi anamuuza zoti azikunkha m’minda yake komanso azikhala pafupi ndi atsikana ake antchito n’cholinga choti anyamata okolola asamamuvutitse. Rute anamvera malangizo amenewa. Komanso iye “anapitiriza kukhala ndi apongozi ake.” (Rute 2:22, 23) Zimene Rute anachitazi zikutithandizanso kuona kuti Rute analidi ndi chikondi chenicheni. Chitsanzo chake chiyenera kutipangitsa kuganizira ngati ifeyo timakonda kwambiri anthu a m’banja lathu posawataya ndiponso kuwathandiza akamavutika. Yehova amayamikira anthu amene amayesetsa kuchita zimenezi.
Kodi Naomi ndi Rute tingati sanali m’banja chifukwa choti analibe amuna? Anthu ena amaganiza kuti, m’banja “lenileni” mumayenera kukhala mwamuna, mkazi, mwana wamwamuna, mwana wamkazi, agogo ndi ena otero. Koma chitsanzo cha Naomi ndi Rute chikutiphunzitsa kuti ngakhale anthu ochepa okha apachibale, akhoza kupanga banja lokondana n’kumakomerana mtima. Choncho ngakhale zitakhala kuti tili ndi achibale ochepa ngati mmene zinaliri ndi Naomi ndi Rute, tiyenera kuyamikirabe chifukwa amenewa ndi anthu a m’banja lathu. Yesu anakumbutsa otsatira ake kuti, ngakhale anthu amene alibe wachibale aliyense, akhoza kupeza anthu amene angakhale ngati achibale awo mumpingo wachikhristu.—Maliko 10:29, 30.
“Ndi Mmodzi wa Otiwombola”
Kungoyambira mu April, yomwe ndi nthawi imene ankakolola balere, kukafika mu June, nthawi imene ankakolola tirigu, Rute ankakunkha m’minda ya Boazi. Patadutsa milungu ingapo kuchokera pamene Rute anayamba kukunkha, n’zosakayikitsa kuti Naomi anayamba kuganizira zimene angachite kuti athandize mpongozi wakeyo. Ali ku Mowabu, Naomi ankaona kuti sangathe kupezera Rute mwamuna wina woti amukwatire. (Rute 1:11-13) Koma tsopano Naomi anasintha maganizo. Iye anauza Rute kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera mpumulo?” (Rute 3:1) Pa nthawi imeneyi zinali zofala makolo kupezera ana awo anthu omanga nawo banja ndipo Naomi ankamuona Rute ngati mwana wake weniweni. Iye anafuna kupezera Rute “mpumulo” kutanthauza kuti ankafuna kuti Ruteyo akhale ndi nyumba yakeyake komanso mwamuna woti azimusamalira. Koma kodi Naomi akanathandiza bwanji Rute kuti apeze mwamuna?
Pamene Rute anatchula za Boazi, Naomi ananena kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu. Ndi mmodzi wa otiwombola.” (Rute 2:20) Kodi iye ankatanthauza chiyani? M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, munali lamulo lothandiza mabanja ovutika chifukwa cha umphawi kapena umasiye. Mayi amene mwamuna wake wamwalira asanam’berekere mwana wamwamuna, ankakhala wachisoni kwambiri chifukwa ankaona kuti dzina la mwamuna wakeyo lifa ndipo lithera pomwepo. Choncho Chilamulo cha Mulungu chinkati mchimwene wake wa munthuyo ayenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere mwana woti atenge dzina la bambo ake komanso kusamalira chuma cha banja.c—Deuteronomo 25:5-7.
Naomi anafotokozera Rute zoyenera kuchita kuti ukwati wotere utheke. Ziyenera kuti zinamudabwitsa kwambiri Rute chifukwa lamulo limeneli linali lachilendo kwa iye komanso ayenera kuti miyambo ina ya m’Chilamulo anali asanaimvetse bwino. Komabe iye ankalemekeza kwambiri Naomi moti anamvetsera zonse zimene ankamuuzazo. Ngakhale kuti zimene Rute anauzidwa kuti achite zinali zochititsa manyazi, iye anatsatira malangizo a Naomiwo. Rute ananena kuti: “Zonse zimene mwanena ndikachita.”—Rute 3:5.
Nthawi zina zimakhala zovuta kuti achinyamata amvere malangizo a anthu achikulire. Iwo amaganiza kuti achikulire sangamvetse mavuto amene achinyamata amakumana nawo. Koma chitsanzo cha Rute cha kudzichepetsa chimatithandiza kudziwa kuti kumvera anthu achikulire amene amatikonda komanso kutifunira zabwino, n’kopindulitsa kwambiri. Koma kodi Naomi analangiza Rute zotani, ndipo kodi Rute anapinduladi atatsatira malangizowo?
Zimene Rute Anachita Atafika Pamalo Opunthira Balere
Madzulo a tsiku limenelo, Rute anapita pamalo opunthira balere. Amenewa anali malo amene alimi ankapunthirako ndiponso kupeta mbewu zawo ndipo ankakhala afulati komanso ogangatika. Kawirikawiri malowa ankakhala paphiri pamene pankaomba mphepo kwambiri m’mamawa komanso madzulo. Alimi akamapeta mbewu, ankagwiritsa ntchito chifoloko chachikulu chimene ankachipisa pamulu wa mbewuzo n’kumachitukulira m’mwamba ndipo madeya ankauluzika, mbewuzo n’kumagwera pansi.
Rute anangokhala chapatali n’kumadikira kuti kude. Boazi ankayang’anira anyamata amene ankapeta balere wake omwe pomaliza anaunjika balereyo pamulu waukulu. Ndiyeno Boazi atadya n’kukhuta, anakagona chakumapeto kwa mulu wa balerewo. Anthu ambiri ankakonda kuchita zimenezi n’cholinga chofuna kuteteza mbewu zawo kuti zisabedwe. Rute anaonetsetsa pamene Boazi anagona ndipo anadziwa kuti imeneyi inali nthawi yoti achite zimene Naomi anamulangiza.
Rute anayenda mwakachetechete n’kukafika pamene Boazi anagona. Iye anaona kuti Boazi anali m’tulo tofa nato. Choncho Rute anachita zimene Naomi anamuuza, moti anavundukula mapazi a Boazi n’kugona. Atatero anadikirira ndipo pamene nthawi inkapita ankangoona kuchedwa. Ndiyeno pakati pa usiku Boazi anamva kuzizira choncho anayamba kufulukuta. Iye anadziwongola kuti afunditse mapazi ake koma anadzidzimuka ataona kuti kumapazi ake kuli munthu. Nkhaniyi imati iye “anadabwa kuona mkazi atagona kumapazi ake.”—Rute 3:8.
Boazi anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Ndiyeno Rute, mwamantha anayankha kuti: “Ndine Rute kapolo wanu. Mufunditse kapolo wanu chovala chanu, pakuti ndinu wotiwombola.” (Rute 3:9) Anthu ena potanthauzira vesili amanena kuti polankhula mawu amenewa, Rute, analankhula mokopa komanso ankachita zinthu zosonyeza kuti ankafuna kuti agone ndi Boazi. Koma anthu amenewa amaiwala mfundo ziwiri. Choyamba, zimene Rute anachitazi zinali zogwirizana ndi miyambo ya pa nthawiyo imene panopa imaoneka ngati yosayenera. Choncho kungakhale kulakwa kuganiza kuti zimene anachitazo sizinali zabwino poganizira mmene zinthu zilili masiku ano pamene anthu ambiri ali ndi khalidwe lachiwerewere. Chachiwiri, zimene Boazi anachita ataona Rute, zinasonyeza kuti sanaone kuti zimene Rute anachitazi zinali zosayenera.
N’zosakayikitsa kuti zimene Boazi analankhula zinamukhazika mtima pansi Rute. Iye anauza Rute kuti: “Yehova akudalitse, mwana wanga. Kukoma mtima kosatha kumene wasonyeza panopa kukuposa koyamba kuja, popeza sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera.” (Rute 3:10) Rute anasonyeza kukoma mtima “koyamba” pamene anachoka ku Mowabu ndi apongozi ake kupita ku Isiraeli n’kumakawasamalira. Kukoma mtima kwachiwiri kunaonekera pa zimene Rute anachita, kuti sanafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. Boazi ankadziwa kuti popeza Rute anali akadali mtsikana, akanatha kukwatiwa ndi mnyamata wa msinkhu wake. Koma iye anasankha kuchitira zabwino Naomi komanso mwamuna wa Naomi amene anamwalira n’cholinga choti dzina la mwamuna wa Naomiyo, lisafe. N’chifukwa chake Boazi anachita chidwi kwambiri ndi Rute.
Boazi anapitiriza kuuza Rute kuti: “Tsopano usachite mantha mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene wanena, chifukwa aliyense mumzinda wathu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri.” (Rute 3:11) Iye anasangalala ndi nkhani yoti angathe kukwatira Rute, ndipo mwina sanadabwe kwenikweni ndi zimene Rute anamuuza kuti iyeyo anali womuwombola. Komabe Boazi anali munthu wolungama ndipo sanafune kuchita zinthu zongomukomera iyeyo. Choncho anafotokozera Rute kuti panali wachibale wina wapafupi wa ku banja la malemu mwamuna wa Naomi amene akanatha kumuwombola. Boazi anati ayenera kuonana kaye ndi munthuyo n’kumufunsa ngati ali wokonzeka kukwatira Rute.
Ndiyeno Boazi anauza Rute kuti agone kufikira kutatsala pang’ono kucha, kenako anyamuke kusanachetsetse n’cholinga choti anthu asamuone. Iye anachita zimenezi pofuna kuteteza mbiri ya Ruteyo komanso yake. Boazi ankaopa kuti anthu akamuona Rute angayambe kuwaganizira zoipa. Rute anagonadi pafupi ndi mapazi a Boazi ndipo ziyenera kuti mtima wake unakhala m’malo tsopano chifukwa cha zimene Boazi anayankha. Ndiyeno kutatsala pang’ono kucha, Boazi anathira balere wambiri ndithu pansalu ya Rute n’kumuuza kuti abwerere kwawo.
Rute ayenera kuti ankasangalala kwambiri akaganizira zimene Boazi ananena zoti anthu onse ankamudziwa kuti iyeyo ndi “mkazi wabwino kwambiri.” Zinali zoyeneradi kuti iye azidziwika ndi mbiri imeneyi chifukwa anali ndi cholinga chodziwa Yehova komanso kumutumikira. Iye anasonyezanso kuti ankadera nkhawa ndiponso kukomera mtima Naomi ndi anthu a mtundu wake ndipo anali wofunitsitsa kutsatira miyambo yawo, yomwe mosakayikira inali yosiyana kwambiri ndi yakwawo. Kutsanzira chikhulupiriro cha Rute kungatithandize kuti nafenso tizilemekeza kwambiri anthu ena komanso miyambo ya chikhalidwe chawo. Tikamachita zimenezi, ifenso tidzakhala ndi mbiri yoti ndife anthu abwino kwambiri.
Rute Anapeza Mpumulo
Rute atafika kunyumba, Naomi anam’funsa kuti: “Ndiwe yani, mwana wanga?” Mwina Naomi anafunsa funsoli chifukwa choti kunja kunali kudakali mdima. Koma n’kuthekanso kuti iye ankafuna kudziwa ngati zayenda bwino moti Ruteyo akusangalala kuti mwina apeza banja. Rute anafotokozera apongozi akewo zonse zimene zinachitika. Iye anaonetsanso Naomi balere wochuluka amene Boazi anam’patsira kuti akapereke kwa Naomiyo.d—Rute 3:16, 17.
Naomi analangiza Rute kuti tsiku limeneli akhale pakhomo asapite kukakunkha. Iye anam’tsimikizira Rute kuti Boazi “sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi.”—Rute 3:18.
Naomi ananenadi zoona. Boazi anapita kuchipata cha mzinda kumene akulu a mzindawo ankakonda kukumana ndipo anadikira mpaka munthu amene anali wachibale wapafupi uja akudutsa. Ndiyeno pa maso pa mboni, Boazi anapatsa munthuyo mwayi wokwatira Rute ngati womuwombola. Koma munthuyo anakana ponena kuti kuchita zimenezo kukanachititsa kuti awononge cholowa chake. Ndiyeno pa maso pa mbonizo, Boazi ananena kuti awombola Rute. Iye anati agula munda wa Elimeleki, mwamuna wa Naomi ndiponso akwatira Rute yemwe anali mkazi wa Maloni, mwana wa Elimeleki. Boazi analankhulanso mawu osonyeza kuti anali ndi chiyembekezo choti zimenezi zichititsa kuti “dzina la mwamuna wake [wa Naomi] amene anamwalira libwerere pacholowa chake.” (Rute 4:1-10) Izi zikusonyezeratu kuti Boazi anali munthu wolungama komanso woganizira ena.
Zitatere, Boazi anakwatira Rute. Baibulo limati: “Yehova anam’dalitsa [Rute] ndipo anatenga pakati n’kubereka mwana wamwamuna.” Akazi a ku Betelehemu anayamba kudalitsa Naomi komanso kutamanda Rute kuti anachita zazikulu kwa Naomi zoposa zimene ana aamuna oposa 7 akanachita. Baibulo limasonyeza kuti mwana wa Rute anadzakhala kholo la Mfumu Davide. (Rute 4:11-22) Ndiyeno Davideyo anadzakhala kholo la Yesu Khristu.—Mateyu 1:1.e
Monga taonera m’nkhaniyi, Rute ndi Naomi anadalitsidwa kwambiri. Naomi ankathandiza kulera mwanayo moti ankangomuona ngati wake. Nkhani ya azimayi awiriwa imatikumbutsa kuti Yehova Mulungu saiwala anthu amene modzichepetsa, amayesetsa kupeza zofunika pa moyo wawo komanso amamutumikira mokhulupirika limodzi ndi anthu ake. Yehova amadalitsa anthu okhulupirika amene amayesetsa kukhala ndi mbiri yabwino ngati mmene Rute anachitira.
a Onani nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—‘Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko’” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2012.
b Monga Naomi ananenera, Yehova amasonyeza kukoma mtima kwa anthu, ngakhalenso amene anamwalira. Mwamuna wa Naomi komanso ana ake awiri anali atamwalira. Ndipo mmodzi mwa ana a Naomi amene anamwalirawo, anali mwamuna wake wa Rute. N’zosakayikitsa kuti amuna atatu onsewa ankakonda kwambiri Naomi ndi Rute. Choncho kukomera mtima Naomi ndi Rute tingati kunalinso kukomera mtima amunawo chifukwa iwo akanakonda kuti azimayiwa azisamalidwa.
c Monga zinaliri pa nkhani ya cholowa, mchimwene weniweni wa mwamuna womwalirayo ndi amene ankayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo. Koma ngati palibe wotereyu, achibale ake ena a mwamunayo ankayenera kukwatira mkaziyo.—Numeri 27:5-11.
d Boazi anapatsa Rute balere wokwana miyezo 6. Mwina iye anachita zimenezi posonyeza kuti, mofanana ndi mmene zinkakhalira kuti masiku 6 ogwira ntchito ankatsatana ndi tsiku la Sabata limene linali lopuma, Rute yemwe anakhala nthawi yaitali ali wamasiye anali atatsala pang’ono ‘kupuma,’ kutanthauza kuti ankayembekezera kupeza mwamuna n’kukhala ndi nyumba yakeyake. Koma n’kuthekanso kuti Boazi anapatsa Rute miyezo 6 chifukwa ndi imene Ruteyo akanatha kunyamula.
e Rute ndi mmodzi mwa akazi anayi amene Baibulo limatchula pa mzere wa makolo a Yesu. Wina ndi Rahabi, yemwe anali mayi ake a Boazi. (Mateyu 1:3, 5, 6) Mofanana ndi Rute, nayenso Rahabi sanali Mwisiraeli.