-
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
19, 20. (a) N’chifukwa chiyani Boazi sanakwatire Rute nthawi yomweyo? (b) Kodi Boazi anachita chiyani posonyeza kuti sankafuna kuti mbiri ya Rute iwonongeke?
19 Boazi anapitiriza kuuza Rute kuti: “Tsopano usachite mantha mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene wanena, chifukwa aliyense mumzinda wathu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri.” (Rute 3:11) Iye anasangalala ndi nkhani yoti angathe kukwatira Rute, ndipo mwina sanadabwe kwenikweni ndi zimene Rute anamuuza kuti iyeyo anali womuwombola. Komabe Boazi anali munthu wolungama ndipo sanafune kuchita zinthu zongomukomera iyeyo. Choncho anafotokozera Rute kuti panali wachibale wina wapafupi wa ku banja la malemu mwamuna wa Naomi amene akanatha kumuwombola. Boazi anamuuza kuti ayenera kuonana kaye ndi munthuyo n’kumufunsa ngati ali wokonzeka kukwatira Rute.
Rute ankadziwika kuti anali mkazi wabwino chifukwa choti anali wokoma mtima komanso waulemu
-
-
Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
21. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Rute azidziwika kuti anali “mkazi wabwino kwambiri,” nanga tingatsanzire bwanji chitsanzo chake?
21 Rute ayenera kuti ankasangalala kwambiri akaganizira zimene Boazi ananena zoti anthu onse ankamudziwa kuti ndi “mkazi wabwino kwambiri.” Zinali zoyeneradi kuti iye azidziwika ndi mbiri imeneyi chifukwa anali ndi cholinga chodziwa Yehova komanso kumutumikira. Iye anasonyezanso kuti ankadera nkhawa ndiponso kukomera mtima Naomi ndi anthu a mtundu wake ndipo anali wofunitsitsa kutsatira miyambo yawo, yomwe mosakayikira inali yosiyana kwambiri ndi yakwawo. Kutsanzira chikhulupiriro cha Rute kungatithandize kuti nafenso tizilemekeza kwambiri anthu ena komanso miyambo ndi chikhalidwe chawo. Tikamachita zimenezi, ifenso tidzakhala ndi mbiri yoti ndife anthu abwino kwambiri.
-