“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
“Ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wamakamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli, amene iwe unawanyoza.”—1 SAMUELI 17:45.
1, 2. (a) Ndi chitokoso chotani chomwe chikuyang’anizana ndi gulu lankhondo la Israyeli pansi pa ulamuliro wa Mfumu Sauli? (b) Ndimotani mmene amuna a gulu lankhondo la Aisrayeli akuchitira ku chitokoso cha Goliati, ndipo ndani tsopano yemwe akuwonekera pa chochitikacho?
MAGULU ankhondo aŵiri amphamvu ayang’anizana lina ndi linzake modutsa chigwa cha Ela, kum’mwera cha kumadzulo kwa Yerusalemu. Kumbali imodzi kuli gulu lankhondo la Israyeli, lotsogozedwa ndi Mfumu Sauli woikidwa chatsopano. Kumbali ina kuli gulu lankhondo la Afilisti ndi ngwazi yake yaikulu, Goliati. Mwachidziŵikire, dzina la Goliati limatanthauza “Wobisika.” Iye ali wamtali mamita 2.7 ndipo ali wokonzekeretsedwa kotheratu. Goliati akufuula kutonza kwa mwano pa Israyeli.—1 Samueli 17:1-11.
2 Ndani yemwe adzakumanizana ndi chitokoso cha Goliati? “Ndipo Aisrayeli onse, pakumuwona munthuyo, anathaŵa, nawopa kwambiri.” Koma tawonani—kokha mwana womakula awonekera pa chochitikacho! Dzina lake ndi Davide, lomwe limatanthauza “Wokondedwa.” Iye anatsimikiziranso kukhala “wokondedwa” kwa Yehova chifukwa cha kudzipereka kwake kolimba mtima ku chilungamo. Samueli wadzoza kale Davide kukhala mfumu ya mtsogolo ya Israyeli, ndipo mzimu wa Yehova ukugwira ntchito mwamphamvu pa iye.—1 Samueli 16:12, 13, 18-21; 17:24; Salmo 11:7; 108:6.
3. Ndimotani mmene Davide akudzikonzekeretsera iyemwini kaamba ka nkhondo, koma ndimotani mmene Goliati wadzikonzekeretsera?
3 Pa kumva Goliati “akutonza ankhondo a Mulungu wa moyo,” Davide adzipereka iyemwini kumenyana ndi chimphonacho. Pamene Sauli avomereza, Davide anyamuka koma osati ndi chikopa cha mwambo ndi zida zoperekedwa ndi Sauli. Iye akonzekeretsedwa kokha ndi ndodo, choponyera miyala, ndi miyala yosalala isanu—m’kusiyanitsa ndi Goliati, yemwe akunyamula lupanga la mutu wolemera makilogramu 7 ndipo akuvala cha pachifuwa cha mkuwa cha makilogramu 57! Pamene Goliati wamphamvu ndi wonyamula chikopa chake akuyandikira kutsogolo, ‘Mfilistiyo atukwana Davide natchula milungu yake.’—1 Samueli 17:12-44.
4. Ndimotani mmene Davide akuyankhira ku chitokoso cha chimphonacho?
4 Ndimotani mmene Davide akuyankhira? Iye akutsekereza chitokoso cha chimphonacho, akumafuula kuti: “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga ndi mkondo ndi nthungo, koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli, amene iwe unawanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa, ndipo ndidzakukantha ndi kukuchotsera mutu wako; ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena ndi mkondo, pakuti YEHOVA NDIYE MWINI NKHONDO, ndipo iye adzakuperekani inu m’manja athu.”—1 Samueli 17:45-47.
5. Nchiyani chomwe chiri chotulukapo cha nkhondoyo, ndipo ndi kwa ndani kumene kukupita chiyamikiro?
5 Davide molimba mtima akupita kutsogolo ku nkhondo. Mwala wake woponyedwa uwulukira kulinga ku chandamale chake, ndipo Goliati agwa pansi. Inde, Yehova wafupa chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa Davide mwa kutsogoza chida chaching’ono chimenecho mosaphonya pa mphumi pa chimphonacho! Davide athamangira kutsogolo, kusolola lupanga lake la Goliati, ndi kuchotsa mutu wa wotonzayo. Afilisti athaŵa m’kusokonezeka. Zowonadi, chinganenedwe kuti: “YEHOVA NDIYE MWINI NKHONDO”!—1 Samueli 17:47-51.
6. (a) Nchifukwa ninji Yehova wasunga tsatanetsatane wa nkhondo yakale imeneyi? (b) Ndi chitsimikozo chotani chimene atumiki a Mulungu akufunikira pamene akupirira chizunzo kuchokera kwa adani omwe angayerekezedwe ndi Goliati?
6 Nchifukwa ninji Yehova wasunga cholembera chokanthana cha tsatanetsatane chimenechi m’Mawu ake, ngakhale kuti nkhondoyo inamenyedwa zaka 3,000 zapitazo? Mtumwi Paulo akutiuza ife kuti: “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Lerolino, atumiki okhulupirika ambiri a Mulungu akupirira chitonzo ndi chizunzo chapoyera chochokera kwa adani omwe angayerekezedwe ndi Goliati. Pamene zididikizo za adani zikuwonjezeka, tonsefe tifunikira chitsimikiziro chotonthoza chakuti “YEHOVA NDIYE MWINI NKHONDO.”
Nkhani ya Ulamuliro
7. Ndi nkhani yotani imene iri yodetsa nkhaŵa kwa anthu onse a Mulungu m’mitundu yonse, ndipo nchifukwa ninji?
7 Goliati anayenda m’kutonza Mulungu wa Israyeli. Mofananamo, m’zana la 20 iri dongosolo la ndale zadziko la boma lolamulira labwera kutsogolo, kutokosa ulamuliro wa Yehova ndi kuyesera kukakamiza atumiki ake m’kugonjera kolambira kwa Boma. Nkhaniyi iri yodetsa nkhaŵa kwa anthu a Mulungu m’mitundu yonse. Nchifukwa ninji ziri tero? Chifukwa Nthaŵi za Akunja zoloseredweratu, kapena “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu,” zinatha mu 1914, kubweretsa nyengo iripoyi ya “nsautso ya mitundu, ndi kuzizwitsidwa.” (Luka 21:24-26; NW, King James Version) Nthaŵi za Akunja zinayamba pamene mitundu inayamba kupondereza pa Yerusalemu wa pa dziko lapansi mu 607 B.C.E. ndipo zinakwaniritsa zaka 2,520 zotsatirazo kufika ku 1914, pamene Yehova anaika pa mpando wachifumu Yesu monga Mfumu yake ya Umesiya mu Yerusalemu wa kumwamba.—Ahebri 12:22, 28; Chibvumbulutso 11:15, 17.a
8. (a) Ndimotani mmene mafumu a dziko lapansi amavomerezera ku lamulo la ulosi la “kutumikira Yehova ndi mantha”? (b) Ndi ngwazi zakudziko zotani lerolino zomwe zikutonza Yehova ndi kunyoza mboni zake?
8 Kusintha kwakukulu kunachitika mu 1914. Mitundu ya Akunja sikanalamuliranso popanda kulowerera kwa umulungu. Koma kodi “mafumu” olamulira pa nthaŵiyo anamvera lamulo la ulosi la “kutumikira Yehova ndi mantha,” kuvomereza Mfumu yake yoikidwa chatsopanoyo? Ayi! M’malomwake, iwo “achita upo pamodzi kutsutsana naye Yehova ndi wodzozedwa wake,” Yesu. Akumatsatira zofuna zawozawo, iwo anafikira kukhala “m’phokoso” mu Nkhondo Yaikulu ya 1914-18. (Salmo 2:1-6, 10-12) Kufikira ku tsiku lino, ulamuliro wa dziko uli nkhani yaikulu pamaso pa mtundu wa anthu. Dziko la Satana likupitirizabe kutulutsa ngwazi za ndale zadziko, zofanana ndi mabwenzi a Goliati, Arafa. Olamulira a nkhanza amenewa amatonza Yehova ndi kuyesera kunyoza mboni zake kufikira ku kugonjera, koma monga mwa nthaŵi zonse, nkhondo ndi chipambano ndi za Yehova.—2 Samueli 21:15-22.
“Sauli” Wamakono
9. Ndani lerolino amene anafanana ndi mtundu wa kachitidwe wa Mfumu Sauli, ndipo m’njira zotani?
9 Ndi kuti kumene Mfumu Sauli akubwera m’chithunzichi? Kumayambiriro, chifukwa cha kupanduka kwake, Yehova anagamulapo ‘kuchotsa kwa iye ulamuliro wachifumu wa Israyeli.’ (1 Samueli 15:22, 28) Tsopano, Sauli analephera kuchirikiza ulamuliro wa Yehova m’chiyang’aniro cha chitokoso cha Goliati. M’kuwonjezerapo, iye potsatira anapitiriza kuzunza Davide, wogonjetsa wa Goliati ndi mmodzi yemwe anadzozedwa ndi Yehova kulowa m’malo mzera wa kulamulira wa Sauli. Ndi mosangalatsa chotani nanga mmene atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko ayenerera mtundu uwu wa kachitidwe! Iwo awukira motsutsana ndi chowonadi cha Baibulo, akumakhala mbali ya mpatuko waukulu umene ‘sumvera mbiri yabwino’ ponena za Ambuye wathu Yesu ndi Ufumu wake womwe ukudza. Iwo alephera kotheratu kupititsa patsogolo ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova ndipo azunza mowopsya mboni zodzozedwa za Yehova ndi mabwenzi awo, khamu lalikulu. Yehova adzachotsa ampatuko amenewa ‘mu mkwiyo wake.’—2 Atesalonika 1:6-9; 2:3; Hoseya 13:11.
10. (a) Mu 1918, ndi chiwonetsero cha malingaliro chotani chomwe chinafalitsidwa mu London ndi gulu la atsogoleri a chipembedzo otchuka? (b) M’malo mwa kutsatira chisonyezero cha malingaliro cha 1918, ndi njira yotani imene atsogoleri achipembedzo analondola?
10 Mkati mwa nkhondo ya dziko yoyamba, njira zogonjera za atsogoleri a Chikristu cha Dziko zinakhala zachiwonekere. Mwachidziŵikire, ulosi wa Yesu mu Mateyu mitu 24 ndi 25, ndi Luka mutu 21 unali kukwaniritsidwa. M’chenicheni, mu 1918 gulu la atsogoleri achipembedzo otchuka mu London, England, akumaimira Matchalitchi a Baptist, Congregational, Presbyterian, Episcopal, ndi Methodist, anafalitsa chiwonetso chapoyera cha malingaliro awo. Ichi chinanena kuti: “Nsautso iripoyi imaloza kulinga ku kutha kwa nthaŵi za Akunja.” Koma iwo sanatsatire pa chilengezo chimenecho. Kalekale, atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko anakhala odzilowetsamo mozama kuchirikiza mbali zonse ziŵiri za nkhondo yoyamba ya dziko. M’malo mozindikira kukhalapo kwa Yesu m’mphamvu ya Ufumu, iwo anagonjera ku kulingalira kwa mitundu ya pa dziko—kuti anthu ayenera kupitiriza kulamuliridwa ndi mphamvu Zakunja zogawanika za ndale zadziko, ngakhale ozunza onga Goliati, m’malo mwa kugwirizana pansi pa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 25:31-33.
Palibe Kugonja!
11. Ndani yemwe sanagonje pa nkhani ya ulamuliro, ndipo ndi chitsanzo cha ndani chomwe akutsatira?
11 Kodi atumiki odzipereka a Mulungu amagonja pa nkhani imeneyi ya ulamuliro? Kutalitali, monga mmene cholembera cha Baibulo chikusonyezera mowonekera! (Danieli 3:28; 6:25-27; Ahebri 11:32-38; Chibvumbulutso 2:2, 3, 13, 19) Akristu okhulupirika lerolino amasungirira ulamuliro wa Yehova ndi Ufumu mosasamala kanthu za chitonzo cha nkhanza ndi chizunzo chomwe Goliati wamakono wotonza akuwunjika pa iwo. Chotero, iwo amatsatira m’mapazi a Yesu, “Mwana wa Davide,” yemwe molimba mtima anamenya nkhondo yauzimu m’malo mwa ulamuliro wa Yehova, pamene pa nthaŵi imodzimodziyo anasungirira uchete wotheratu kulinga ku mikangano ya dziko ndi ndale zadziko. Mu pemphero kwa Atate wake, Yesu ananena kuti otsatira ake, Akristu owona, nawonso sali “mbali ya dziko lapansi.”—Mateyu 4:8-10, 17; 21:9; Yohane 6:15; 17:14, 16; 18:36, 37; 1 Petro 2:21.
12. (a) Ndani omwe akantha Goliati wamakono, ndipo tero motani? (b) Kuwona kwawo “Goliati” monga wakufa kwakhala ndi chiyambukiro chotani pa anthu a Yehova?
12 Otsalira a Akristu odzozedwa onga Davide lerolino akantha Goliati wamakono. Tero motani? M’chakuti adzilengeza iwo eni mogwirizana kotheratu kukhala ku mbali ya Yehova ya mkangano wa ulamuliro wa dziko. “CHIGAMULO (Chotengedwa ndi International Bible Students Association mu Msonkhano pa Cedar Point, Ohio, Sande, September 10, 1922)” chimakhazikitsa chitsanzocho. Icho chinaphatikizapo zotsatirazi:
“10. Ife mowonjezereka tikusunga ndi kuchitira umboni kuti iri ndi tsiku la kubwezera la Mulungu motsutsana ndi ufumu wa Satana wowoneka ndi wosawoneka;
“11. Kuti kukhazikitsidwanso kwa dziko lakale kapena dongosolo kuli kosatheka; kuti nthaŵi iri pano kaamba ka kukhazikitsa kwa ufumu wa Mulungu kupyolera mwa Kristu Yesu; ndi kuti mphamvu zonse ndi magulu omwe modzifunira sadzigonjetsera ku ulamuliro wolungama wa Ambuye adzawonongedwa.”
“Mwana wa Davide,” monga Mutu wa mpingo Wachikristu, mosakaikira anatsogoza kugwetsedwa kwa “mwala” umenewo wa chowonadi cha Ufumu. (Mateyu 12:23; Yohane 16:33; Akolose 1:18) Zigamulo zotengedwa pa misonkhano ya pa chaka kuyambira 1922 mpaka 1928 zinagogomezera kaimidwe kameneka. Kuchokera ku kawonedwe ka anthu a Yehova, “Goliati” anagona wakufa, wodulidwa mutu. Ulamuliro wa nkhalwe wa umunthu wakhala wopanda mphamvu kutsekereza opititsa patsogolo olimba mtima a ulamuliro wa Yehova kufika ku kugonja.—Yerekezani ndi Chibvumbulutso 20:4.
13. (a) Ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko anagonjera mkati mwa chitsenderezo mu Germany wa Hitler? (b) Nchiyani chimene bukhu la Mothers in the Fatherland limasimba ponena za Mboni zosagonja?
13 Chitsanzo chamakono chowonekera cha kutonza kochitidwa ndi ulamuliro wa ndale zadziko wonga wa Goliati kunachitika mu Germany wa Hitler. Zipembedzo zotchuka, ponse paŵiri za Chikatolika ndi Chiprotestanti, zinagonjera momvetsa chisoni m’kupereka ulemu ku chiNazi, kupanga fano führer, kupereka sawatcha ku mbendera yake ya swastika, ndi kudalitsa magulu ake ankhondo pamene anali kupita kukaphana ndi akhulupiriri anzawo m’mitundu yoyandikana nayo. Otchedwa Akristu a zikhulupiriro zonse—koma osati Mboni za Yehova—anagwidwa m’chiyanjo cha utundu. Bukhu lakuti Mothers in the Fatherland linasimba kuti: “[Mboni za Yehova] zinatumizidwa ku misasa yachibalo, chikwi cha iwo chinaphedwa, ndipo chikwi china chinafa pakati pa 1933 ndi 1945. . . . Akatolika ndi Aprotestanti anamva atsogoleri awo achipembedzo akuwafulumiza iwo kugwirizana ndi Hitler. Ngati iwo anakana, anachita tero motsutsana ndi malamulo ochokera ponse paŵiri ku tchalitchi ndi boma.” Ndi zaliwongo la mwazi chotani nanga mmene ponse paŵiri Tchalitchi ndi Boma zakhalira!—Yeremiya 2:34.b
14. Nchifukwa ninji Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimazunzidwa?
14 Kufikira tsiku lino, chitsenderezo cha nkhalwe cha Mboni za Yehova chikupitiriza m’maiko ambiri, monga mmene Yesu ananeneratu. Koma pansi pa mikhalidwe yonseyi, Akristu amenewa mwachangu akupitiriza kulalikira “mbiri imeneyi yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:9, 13, 14) Mbali yoseketsa ya mkhalidwe iri yakuti Mboni zimazindikiridwa m’maiko ambiri monga nzika zowona mtima, za makhalidwe oyera, zopereka chitsanzo m’kusungirira lamulo ndi chilongosoko. (Aroma 13:1-7) Komabe izo kaŵirikaŵiri zimazunzidwa. Nchifukwa ninji? Popeza kulambira kuli kotheratu kwa Yehova, izo zimakana kugwadira mafano a Boma kapena kuwatamanda iwo. (Deuteronomo 4:23, 24; 5:8-10; 6:13-15) Mosagonjera, izo zimalambira Yehova, “iye yekha,” kumpanga Yehova Mfumu Ambuye wa miyoyo yawo. (Mateyu 4:8-10; Salmo 71:5; 73:28) Posakhala “mbali ya dziko,” izo zimasungirira uchete Wachikristu kulinga ku ndale ndi nkhondo za dziko.—Yohane 15:18-21; 16:33.
15, 16. (a) Ndi chitsanzo cha ndani chimene Mboni za misinkhu yonse zingatsatire pamene Goliati wamakono awawopsyeza iwo, ndipo ndimotani mmene ichi chinachitidwira chitsanzo ndi mtsikana Wachikristu wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa? (b) Makolo Achikristu amafuna kuphunzitsa achichepere awo kukhala monga ndani?
15 Goliati wamakono kaŵirikaŵiri amawopsyeza osunga umphumphu amenewa, omwe amaika kulambira kwa Yehova patsogolo pa machitachita a mafano. (Yerekezani ndi Chibvumbulutso 13:16, 17.) Koma Mboni, zachichepere ndi zachikulire, zingatsatire chitsanzo cha Davide mwa kuyankha mopanda mantha chitokosocho. Mu dziko la Latin-America, mtsikana Wachikristu wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa analandira kuphunzitsa kwabwino panyumba kuchokera ku ubwana. (Yerekezani ndi Aefeso 6:4; 2 Timoteo 3:14, 15.) Ichi chinathandizira m’kumupanga iye kukhala wophunzira wabwino kwambiri m’kalasi yake ku sukulu. Koma chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo chinampangitsa iye kukana kutenga mbali m’mapwando a m’kalasi olambira mafano. Pamene iye analongosola kaimidwe kake, aphunzitsi anafuula kuti mtsikana wa msinkhu wake anali wam’ng’ono koposa kukhala ndi chikumbumtima! Wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwayo anatsimikizira mphunzitsiyo kukhala wolakwa mwa kupereka umboni wokhumbirika.
16 Chikuyembekezeredwa kuti makolo onse Achikristu aphunzitse achichepere awo kotero kuti awa angatsatire chitsanzo cha Davide wachichepere mwa kutenga kaimidwe kawo pamene ulamuliro wakudziko wonga Goliati uwopsyeza iwo. Lolani kuti akhale monga ana Achihebri atatu okhulupirika, monga Danieli ndi ena ambiri a cholembera cha Baibulo ‘m’kusungirira chikumbumtima chabwino’ molimba mtima m’chigwirizano ndi maprinsipulo a Baibulo.—1 Petro 2:19; 3:16; Danieli 3:16-18.
Mmene Akatswiri a Mbiri Yakale Amaiwonera
17. (a) Katswiri wa mbiri yakale wa Chingelezi Toynbee anachenjeza za kuchitika kwa chiyani? (b) Ndimotani mmene gulu la Goliati wamakono limayesera kukhulupirika kwa anthu a Mulungu?
17 Katswiri wa mbiri yakale wodziwika bwino wa Chingelezi Arnold Toynbee anachenjeza za zochitika m’nthaŵi yathu ya “kuyambika kochepera kwa kulambira kwachikunja kwa maboma olamulira a utundu,” akumalongosola ichi monganso “chotupitsa chowawa cha vinyo watsopano wa democracy m’mabotolo akale a ufuko.” Awo odzinenera kuti mtundu wawo uli wapamwamba kuposa ena, ngakhale ku nsonga ya kulambira Boma, akhala akusonkhezeredwa ndi olamulira ndi kuikidwa m’gulu lankhondo ndi cholinga chofuna kuchirikiza malamulo awo, kaya ndi abwino kapena oipa. Monga chotulukapo, gulu la Goliati lawuka kuyesa kukhulupirika kwa anthu a Mulungu, omwe amakonda dziko lawo lobadwira koma amakana kulambira Boma ndi ziphiphiritso zake.
18. Ndi mafunso ofufuza otani amene Mkristu weniweni afunikira kuyankha?
18 Monga mmene inaliri nkhani mu Nazi Germany, lerolino pali mafunso ofufuza kaamba ka Mkristu weniweni kuwayankha: Kodi ndiyenera kukhulupirira kuti mtundu umene ndimakhalamo uli wokondedwa ndi Mulungu kuposa wina uliwonse? Makamaka tsopano, m’nyengo yowopsya kwambiri ya mbiri ya anthu, kodi chiri chanzeru ndi cholingalirika kuwona mbali imodzi yaing’ono ya dziko lapansi kukhala yapamwamba kuposa mbali zina zonse? Kapena kuwona mbali imodzi ya banja la munthu kukhala yapamwamba kuposa mbali zina zonse?
19. Nchiyani chimene Katswiri wa Mbiri Yakale wamkulu pa onse, Yehova, akutiuza ife ponena za kulingalira ndi kuchita ngati kuti mtundu umodzi wa anthu unali wopambana kuposa mtundu wina uliwonse?
19 Tiyeni tilingalire kawonedwe ka Katswiri wa Mbiri Yakale wamkulu koposa—Yehova Mulungu, Mkonzi wa Baibulo. Mtumwi Petro akutiuza ife kuti: “Nzowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho, koma m’mitundu yonse wakumuwopa iye ndi kuchita chilungamo alandiridwa naye.” Ndipo kodi ife nthaŵi zonse sitiyenera kuchita m’chigwirizano ndi ndemanga yowuziridwa ya mtumwi Paulo kuti Mulungu “ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi”? Nchifukwa ninji mtundu umodzi wa anthu uyenera kulingalira ndi kuchita ngati kuti unali wapamwamba ku mitundu yonse? Akumalankhula za anthu onse, Paulo ananena kuti: “Tiri mbadwa za Mulungu.”—Machitidwe 10:34, 35; 17:26, 29.
20. Kodi anthu a Mulungu sadzatokosedwanso ndi chiyani m’dongosolo la zinthu latsopano la Yehova, ndipo nchiyani chimene phunziro lathu lotsatira lidzakambitsirana?
20 M’dongosolo la zinthu latsopano la Yehova, okonda chilungamo sadzakhalanso akutokosedwa ndi madongosolo a ndale zadziko olamulira onga Goliati, popeza kuti kunyada kwa atsatiri okangalika ndi udani zidzakhala zinthu zakale. (Salmo 11:5-7) Kulikonse kumene amakhala pa dziko lapansi, anthu a Mulungu aika kale utundu woterowo kumbuyo kwawo, m’kumvera ku lamulo la Yesu la ‘kukondana wina ndi mnzake monga anawakondera iwo.’ (Yohane 13:34, 35; Yesaya 2:4) Phunziro lathu lotsatira lidzasonyeza mtundu wachikondi umene icho chiri!
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka kukambitsirana kwa tsatanetsatane kwa dongosolo la nthaŵi za Baibulo kumeneku, onani masamba 129-39 a bukhu la “Let Your Kingdom Come,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kaamba ka zitsanzo zochititsa nthumanzi za umphumphu wa Mboni za Yehova, zachichepere ndi zachikulire, m’kuyankha chitokoso cha “Goliati” wa chiNazi, onani 1974 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 117-21, 164-9.
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi chimphona chonyoza Goliati?
◻ Ndi m’njira zotani mmene atumiki a Mulungu samasonyezera kugonja pa nkhani ya ulamuliro?
◻ Nchifukwa ninji anthu a Mulungu anganene kuti Goliati wamakono wakanthidwa?
◻ Ndani omwe akutsatira mtundu wa kachitidwe wa Mfumu Sauli, ndipo motani?
◻ Ndimotani mmene anthu a Yehova achitira monga Davide m’chiyang’aniro cha kutsendereza kwa onga Goliati?