Ogwirizana Pansi pa Mbendera ya Chikondi
“Koposa zonse, mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha.”—1 PETRO 4:8.
1. Ndi mtundu wanji wachikondi umene timawona pakati pa anthu a Mulungu lerolino, ndipo nchiyani chimene Akristu odzozedwa akhala akulalikira chiyambire 1922?
KODI timawona mtundu umenewo wa chikondi pakati pa anthu a Mulungu lerolino? Ndithudi timatero! Chimenechi ndi chikondi chimene chimazikidwa mozungulira pa kuzindikira ndi kuchirikiza ulamuliro wa Yehova, mongadi mmene Davide anauchirikizira iwo. Mozindikirika chiyambire chaka cha 1922, abale odzozedwa a Yesu Kristu, “Mwana wa Davide,” akhala akulalikira pa dziko lonse lapansi kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi ndi kuti ngwazi za kulamulira kotsendereza kwa Satana zikuyang’anizana ndi chiŵeruzo ndi Woŵeruza woikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu.—Mateyu 21:15, 42-44; Chibvumbulutso 19:11, 19-21.
2. Nchifukwa ninji Davide anatchedwa ‘munthu wa pa mtima pa Yehova’?
2 Davide anali ‘munthu wa pa mtima pa Yehova.’ Ichi chinali chowonekera m’chikondi chake kaamba ka Yehova ndi chilungamo Chake—zikhoterero zomwe ngakhale mwa mantha Mfumu Sauli anavomereza kuti zinali mwa Davide—inde, m’mikhalidwe yake ya kupanda mantha, kudzipereka kwa mtima wonse kwa Yehova, ulamuliro, ndi kugonjera kodzichepetsa ku dongosolo la teokratiki.—1 Samueli 13:14; 16:7, 11-13; 17:33-36; 24:9, 10, 17.
3. Nchiyani chomwe chinali mkhalidwe wa Jonatani kulinga kwa Davide, ndipo nchifukwa ninji?
3 Kutsatira chipambano chake pa Goliati, Davide anasimba kwa Sauli. Panali pamenepo pamene wokonda wina wa chilungamo anabwera. Iye anali Jonatani, mwana wamkulu koposa wa Mfumu Sauli. “Ndipo kunali, pakutsiriza [Davide] kulankhula ndi Sauli, mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.” (1 Samueli 18:1) M’malo mwa kulimba mtima kwa kuthupi ndi kukhala ndi luso la choponyera mwala, chinali changu chotentha cha Davide cha kuchotsa chitonzo pa dzina la Mulungu, kudzipereka kwake, ndi kudalira kwake kotheratu pa Yehova kumene kunakoka kukhumbira kochokera ku mtima kwa Jonatani.—Yerekezani ndi Salmo 8:1, 9; 9:1, 2.
4. Nchiyani chimene Jonatani anachita m’kuzindikira za kukhala kwa Davide yemwe anadzozedwa kukhala mfumu?
4 Ngakhale kuti Jonatani anali wokulirapo ndi zaka 30 kuposa Davide, iye anakhala wogwirizana ndi wankhondo wachichepere ameneyu m’chomangira chosatha cha ubwenzi. “Pamenepo Jonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha. Ndipo, Jonatani anavula malaya ake anali nawo nampatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake ndi uta wake ndi lamba lake.” (1 Samueli 18:3, 4) Ndi chiwonetsero chowonekera chotani nanga cha kuzindikira ku mbali ya Jonatani! Jonatani mwachibadwa akakhala m’lowa m’malo wa Sauli. Komabe iye anasonyeza chikondi chotentha, chokhala ndi prinsipulo kaamba ka Davide ndi kugonjera kwa iye monga mmodzi wodzozedwa kukhala mfumu, mmodzi amene mwachiwonekere anali wokhoterera pa kumamatira ku dzina la Yehova ndi ulamuliro.—2 Samueli 7:18-24; 1 Mbiri 29:10-13.
5. Nchiyani chimene Jonatani anazindikira pamene chinabwera ku nkhondo ya teokratiki?
5 Jonatani iyemwini analinso womenyera wa chilungamo. Iye analengeza kuti “palibe chomuletsa Yehova kupulumutsa ngakhale ndi ambiri kapena oŵerengeka.” Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti Jonatani anazindikira kuti pali nthaŵi zonse chifuno cha kufuna chitsogozo chaumulungu kaamba ka chipambano munkhondo ya teokratiki. Pamene Jonatani mosadziŵa anapanga cholakwa kaamba ka chimene Sauli anamuŵeruza iye ku imfa, modzichepetsa analandira chiŵeruzocho. Mwachimwemwe, anthu anamupulumutsa iye.—1 Samueli 14:6, 9, 10, 24, 27, 43-45.
Kusonyeza Chikondi Chokhulupirika
6. Ndimotani mmene chikondi chokhulupirika cha Jonatani chinabwerera ku chipulumutso cha Davide?
6 Sauli anachita nsanje ndi kutchuka kwa Davide monga wankhondo ndi kufunafuna kumupha iye, koma chikondi chokhulupirika cha Jonatani chinabwera ku chipulumutso! Cholemberacho chimaŵerenga kuti: “Koma Jonatani, mwana wa Sauli, anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Jonatani anauza Davide, nati: ‘Sauli atate wanga alikufuna kukupha. Chifukwa chake tsono uchenjere, m’mawa, nukhale m’malo mosadziŵika, nubisale.’” Pa chochitika chimenecho, Jonatani anatonthoza Sauli, kotero kuti Davide anapulumutsidwa. Koma zipambano zowonjezereka za Davide “m’kumenyana ndi Afilisti ndi kuwakantha iwo ndi kupha kwakukulu” zinadzutsanso udani wa Sauli. Kachiŵirinso iye anagamulapo kupha Davide, kotero kuti Davide anathaŵa.—1 Samueli 19:2-10.
7. Pamene Jonatani anakumana ndi Davide wothaŵa kwawo, nchiyani chimene ananena kwa wina ndi mnzake m’kulimbikitsanso pangano?
7 M’kupita kwa nthaŵi, Davide wothaŵa kwawoyo kachiŵirinso anakumana ndi Jonatani, yemwe analengeza kuti: “Chirichonse mtima wako unena ndidzakuchitira.” Aŵiriwo analimbikitsanso pangano lawo pamaso pa Yehova, ndipo Davide analonjeza kuti sadzachotsa chikondi chokoma mtima kuchoka ku nyumba ya Jonatani—lonjezo limene iye analisunga mokhulupirika. “Ndipo Jonatani anamulumbiritsa Davide kachiŵiri chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.”—1 Samueli 20:4-17; 2 Samueli 21:7.
8. Nchifukwa ninji Jonatani ndi Davide anakumana mwamseri m’munda, ndipo nchiyani chomwe chinachitika pa chochitikacho?
8 Mfumu Sauli anakhala wotsimikiza m’chigamulo chake cha kupha Davide. Nkulekeranji, popeza kuti Sauli anaponya mkondo pa mwana wake weniweni Jonatani pamene uyu analankhulira mokomera Davide! Chotero Jonatani anakumana ndi Davide mwachinsinsi m’munda. “Davide, . . . nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana nalirirana, kufikira Davide analiritsa. Ndipo Jonatani ananena kwa Davide: ‘Muka mu mtendere, popeza tonsefe, tinalumbira, m’dzina la Yehova, kuti, “Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe ndi pakati pa mbewu yanga ndi mbewu yako nthaŵi zamuyaya.”’” Chotero analekana, ndipo Davide anakhala wothaŵa kwawo m’chipululu cha Zifi.—1 Samueli 20:41, 42.
9, 10. (a) Ndimotani mmene Jonatani mowonjezereka analimbikitsira Davide pa kumene mwinamwake kunali kukumana komalizira pakati pa aŵiriwo? (b) Pamene Jonatani ndi Sauli anaphedwa ndi Afilisti, ndi nyimbo yamaliro yotani imene Davide anapanga, ndipo ndimotani mmene anaifikitsira pachimake?
9 Mwachikondi, Jonatani anapitiriza kulimbikitsa Davide. Monga mmene cholemberacho chikunenera: “Jonatani mwana wa Sauli ananyamuka napita kwa Davide ku [Horesi, NW], namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu. Ndipo iye ananena naye: ‘Usawopa; chifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza, iwe udzakhala mfumu ya Israyeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe; ichinso Sauli atate wanga achidziŵa.’ Ndipo aŵiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova.”—1 Samueli 23:15-18.
10 Mwachidziŵikire, kumeneko kunali kukumana komalizira pakati pa Davide ndi mnzake wokhulupirika Jonatani. Pambuyo pake, pamene onse aŵiri Jonatani ndi Sauli anaphedwa mu nkhondo ndi Afilisti, Davide anapanga nyimbo ya maliro, “Uta.” Mu iyo iye anasonyeza ulemu kaamba ka Sauli monga wodzozedwa wa Yehova koma anafikitsa pachimake nyimbo yake ndi mawu awa: “Jonatani anaphedwa pamisanje pako! Ndipsyinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani, wondikomera kwambiri. Chikondi chako ndinadabwa nacho chinaposa chikondi cha anthu akazi. Ha! amphamvuwo anagwa ndi zida zankhondo zinawonongeka.” (2 Samueli 1:18, 21, 25-27) Davide kenaka anadzozedwa kwa nthaŵi yachiŵiri, monga mfumu pa Yuda.
Kufanana Nako kwa Makono
11, 12. (a) Ndi mtundu wotani wa chikondi umene Davide ndi Jonatani anasonyeza? (b) Nchiyani chimene chikondi chenicheni pakati pa Davide ndi Jonatani chinaimira?
11 Popeza kuti “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso,” nchiyani chomwe tikuphunzira ku cholembera chonena za Davide ndi Jonatani? (2 Timoteo 3:16) Tikudziŵa kuti pali chikondi “chokomera . . . kuposa chochokera kwa anthu akazi.” Zowona, “chikondi chochokera kwa anthu akazi” chingakhale chosangalatsa ndi chokwaniritsa pamene malamulo a Yehova ponena za ukwati alemekezedwa. (Mateyu 19:6, 9; Ahebri 13:4) Koma Davide ndi Jonatani anachitira chitsanzo mbali yabwino koposa ya chikondi, m’chigwirizano ndi lamulo iri: “Imvani, Israyeli: Yehova Mulungu wathu Yehova ndiye mmodzi. Ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu yanu yonse.”—Deuteronomo 6:4, 5.
12 Davide ndi Jonatani anali ogwirizana m’kusonyeza chikondi chimenecho pamene anamenyera kuchotsa chitonzo chonse pa dzina la Yehova chimene adani Ake anachiika pa ilo. M’kuchita ichi, iwo anakulitsanso ‘chikondano chenicheni kaamba ka wina ndi mnzake.’ (1 Petro 4:8) Ubwenzi umene anasangalala nawo mwanjirayi unapyola ngakhale lamulo la pa Levitiko 19:18: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” Ndithudi, chinachitira chithunzi mtundu wa chikondi wosonyezedwa mu “lamulo latsopano, [la Yesu] kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” Chikondi cha Yesu chinali chodzipereka nsembe osati kokha m’kugonjera kwake kotheratu ku chifuno cha Yehova komanso m’kufunitsitsa kwake ngakhale “kutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.”—Yohane 13:34; 15:13.
“Gulu” Limodzi Logwirizana
13. Ndi gulu liti la olalikira Ufumu limene lawonekera pa chochitika makamaka kuyambira 1935, ndipo ndi umodzi wotani umene Akristu odzozedwa ali nawo ndi iwo?
13 Akristu odzozedwa a “kagulu ka nkhosa” atenga chitsogozo cha nkhondo m’kulimbana ndi Goliati wamakono. Chiyambire 1935, ngakhale kuli tero, iwo agwirizana ndi olalikira a Ufumu a “gulu” lina ndipo lokulirapo. “Nkhosa zina” zimenezi zakhala zogwirizana ndi otsalira a “nkhosa” zodzozedwa monga “gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi,” “Mwana wa Davide,” m’chomangira chokulira cha chikondi cha umodzi—chonga chija chomwe chinalipo pakati pa Jonatani ndi Davide.—Luka 12:32; Yohane 10:16; Ezekieli 37:24.
14. Nchiyani chomwe chinalingana ndi zoyesera za Sauli za kupha Davide, ndi kudzizindikiritsa kwa chikondi kwa Jonatani ndi Davide?
14 Ngakhale pamene gulu la Jonatani limeneli linali kuyamba kuwonjezeka kufika ku khamu lalikulu, Nkhondo ya Dziko ya II inawulika, kotero kuti ponse paŵiri odzozedwa ndi mabwenzi awo anayesedwa mowopsya. Izo zinali zaka za chizunzo chowopsya, kaŵirikaŵiri chosonkhezeredwa ndi atsogoleri a chipembedzo. Ichi chinafanana ndi zoyesera za Sauli za kupha Davide wodzozedwayo ndipo, pambuyo pake, Jonatani pamene womalizirayo mwachikondi anadzizindikiritsa iyemwini limodzi ndi Davide. Ndi chikondi chenicheni chotani nanga chimene magulu a Davide ndi Jonatani anasonyeza kulinga kwa wina ndi mnzake mkati mwa nyengo imeneyo! Fanizo la Yesu pa Mateyu 25:35-40 kaŵirikaŵiri linali ndi kukwaniritsidwa kwenikweni.a
15. (a) Ndi njira yotani yotengedwa ndi Mboni yomwe imasiyana ndi ija yotengedwa ndi gulu la Sauli lamakono? (b) Nchiyani m’tsiku lathu chimene chingafanane ndi “mzimu woipa wochokera kwa Yehova” womwe unazunza Mfumu Sauli?
15 Ndimotani nanga mmene kusunga umphumphu kwa Mboni za Yehova kumasiyanirana ndi njira ya gulu la Sauli wamakono! Mbonizo, zomwe tsopano “siziri mbali ya dziko,” zamvera lamulo la Yesu la “kukondana wina ndi mnzake” pa maziko a dziko lonse. (Yohane 15:17-19) Ku mbali ina, mu nkhondo ziŵiri za dziko atsogoleri a chipembedzo cha Chikristu cha Dziko ku mbali zonse ziŵiri anapemphera kwa “mulungu” wawo kaamba ka chipambano, pamene mamiliyoni a asilikali anali kuphedwa ndi mabwenzi awo a chipembedzo a mitundu ina. “Mzimu woipa wochokera kwa Yehova” womwe unazunza Sauli ungafanane bwino ndi chotulukapo cha kutsanula kwa mngelo miliri ya Chibvumbulutso mutu 8. Chiri chachiwonekere kuti atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko alibe mzimu woyera wa Yehova.—1 Samueli 16:14; 18:10-12; 19:10; 20:32-34.
16. (a) Ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo anagwiritsira ntchito nkhondo ziŵiri za dziko kutsendereza anthu a Yehova? (b) M’zaka za posachedwapa, nchifukwa ninji chinganenedwe kuti Sauli wamakono wawumirira m’kuvutitsa anthu a Mulungu?
16 Mu 1918 atsogoleri a chipembedzo anagwiritsira ntchito kuwopsya kwa nkhondo kukakamiza mphamvu za ndale zadziko mu United States kutenga kachitidwe molimbana ndi akulu akulu a thayo a Watch Tower Society ndipo potsirizira pake kuziika iwo m’ndende. (Ophunzira Baibulo amenewa pambuyo pake anamasulidwa kotheratu.) Mkati mwa nkhondo ya dziko yachiŵiri, Mboni za Yehova zinaletsedwa mu ulamuliro wa mphamvu Zazikulu ndi maiko ambiri a British Commonwealth, kaŵirikaŵiri monga chotulukapo cha chitsenderezo cha chipembedzo. Mwachitsanzo, onani kalata yofanana nayo yotsatirayo yolembedwa ndi Archbishopu wa Sydney (pambuyo pake cardinal) kokha kuletsedwa kwa Mboni za Yehova kusanachitike mu Australia. Pamene chiletso m’dziko limenelo chinatsutsidwa m’Bwalo Lamilandu Lapamwamba la Australia, woŵeruza wozenga mlanduyo, Mr. Justice Starke, analongosola icho monga “kaduka, kuphonya maziko ndi kutsendereza.” Chiletsocho chinachotsedwa pa June 14, 1943, ndipo boma linawuzidwa kulipira zotaikazo. M’zaka zaposachedwapa, chitsenderezo cha chipembedzo pa unyinji wa maboma mu Africa ndi Asia chatulukapo m’chitsenderezo cha nkhalwe pa Mboni za Yehova. Chotero Sauli wamakono—atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko—awumirira m’kuzunza anthu a Mulungu.
17. (a) Ndimotani mmene Mboni za Yehova zakumanizirana ndi zitsenderezo zomapitirizabe za ndale zadziko ndi chipembedzo? (b) Nchiyani chomwe chasonyezedwa ndi kugwirizana kwa dziko lonse kwa Mboni?
17 Mkati mwa ma 1980, ndimotani mmene Mboni za Yehova zakumanizirana ndi zitsenderezo zopitabe patsogolo za ndale zadziko ndi chipembedzo? Nkulekeranji, mongadi mmene Davide anakumanizana ndi Goliati, ndipo Davide ndi Jonatani kwa Mfumu Sauli! Iwo ali opanda mantha ndipo ogamulapo kusunga umphumphu m’chigwirizano ndi nkhani ya ulamuliro, popeza kuti iwo akudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzapambana. (Danieli 2:44) M’chiyang’aniro cha chizunzo, iwo amawonetsabe kupita patsogolo kogwirizana, kulimbikitsana wina ndi mnzake m’chomangira cha mitundu yonse cha chikondi chonga chimene dziko silinawonepo chikhalire. Monga auchete m’nthaŵi za nkhondo, iwo sakhetsa mwazi wa akhulupiriri anzawo m’mitundu ina. (Mika 4:3, 5) Chotero iwo amasonyeza kuti ali gulu limene Yesu analozerako pamene ananena kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Monga ubale wa dziko lonse, Mboni za Yehova ‘zadziveka ndi chikondi, chomangira changwiro,’ chomangira chomwe chimaposa malire onse a ufuko, manenedwe, ndi utundu.—Akolose 3:14.
Kusonyeza “Chikondi Chenicheni”
18. (a) Ndi kufanana kotani komwe kulipo m’chikondi cha Jonatani kaamba ka Davide, ndipo ichi chikusonyezedwa motani? (b) Nchiyani chomwe chatulukapo pa dziko lonse kuchokera ku kaimidwe kosagonjera ka gulu la Davide?
18 Kumbukirani kuti “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.” Ndi kufanana kosangalatsa kotani nanga kumene kwakhalapo mu “masiku otsiriza” awa! (2 Timoteo 3:1, 14) Mkati mwa chiwawa chopanda pake cha mbadwo wachiwawa uno, pakhala gulu limodzi, Mboni za Yehova, lomwe lasungirira umodzi wa dziko lonse wa chikondi. Monga Akristu a uchete, iwo alemekeza Mlengi wawo monga Mfumu Ambuye wa mtundu wonse wa anthu. (Salmo 100:3) Oh, Refaimu wamakono—mabwenzi a ndale zadziko a “Goliati”—angapitirize kutonza Israyeli wauzimu. (2 Samueli 21:21, 22) Ndipo Sauli wamakono—atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko—angapitirize kupanga mavuto kaamba ka magulu a Davide ndi Jonatani. (1 Samueli 20:32, 33) Koma “Yehova ndi mwini nkhondo.” Monga Mfumu Ambuye, iye adzapeza chipambano chotsirizira kaamba ka atumiki ake okhulupirika. Akumawona kaimidwe kosagonjera ka gulu la Davide, mamiliyoni—m’maiko onse—a gulu la Jonatani, ngakhale kuphatikizapo omwe kalelo anali azunzi, agwirizana nawo pansi pa ‘mbendera yachikondi’ ya Kristu.b—1 Samueli 17:47; Nyimbo ya Solomo 2:4.
19, 20. (a) Ndi ziti zomwe ziri zina za mfundo zazikulu za ntchito ya Mboni monga momwe zasonyezedwera ndi chati pa masamba 4-7? (b) Ndi liti lomwe linali liŵiro la kukula kwa Mboni mkati mwa zaka khumi za 1979-88? (c) Nchifukwa ninji chinganenedwe kuti Mboni ziri anthu ogwirizana mowonadi pa dziko lonse, ndipo chotero ndi funso lotani limene likubuka?
19 Mungabwereremo mu ntchito yofutukula ya mamiliyoni a Mboni zimenezi mwa kuwona chati pa masamba 4-7 a maganizi ino. Mkati mwa zaka khumi za 1979-88, unyinji wa olalikira a mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu wawonjezeka kuchokera ku 2,186,075 kufika ku 3,592,654, kukula kwa 64.3-peresenti. Pa dziko lonse, awa ali anthu amene mowonadi agwirizana m’kugawana chikhulupiriro chofala chimodzi, utumiki wofala umodzi kwa Mulungu, ndi kudzipereka kumodzi kokhazikika ku maprinsipulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Liri gulu logwirizana kotheratu la mitundu yonse limeneli ku limene mawu a Yesu amagwira ntchito lerolino: “Ngati musunga malamulo anga, mudzakhala m’chikondi changa, monga ine ndasunga malamulo a Atate wanga ndipo ndikhala m’chikondi chake.”—Yohane 15:10; yerekezani ndi 1 Akorinto 1:10.
20 Ngakhale kuti iwo amalalikira mu malirime oposa 200 osiyanasiyana, mboni zimenezi za Yehova zimalankhula “chinenero choyera” cha chowonadi pamene zikutumikira Mulungu “ndi cholinga chimodzi.” Mu ichi, iwo amatsanzira chitsanzo chachikondi cha Davide ndi Jonatani. (Zefaniya 3:9; 1 Samueli 20:17; Miyambo 18:24) Ngati simuli kale ogwirizana ndi anthu a Mulungu, kodi simungakonde kukhala mbali ya gulu la Jonatani wamakono? Mungapange chimenecho kukhala chonulirapo chanu, ndipo Mboni za Yehova zidzasonyeza chikondi chenicheni m’kuthandiza inu kufikira icho.
[Mawu a M’munsi]
a Chitsanzo chabwino cha ichi chalongosoledwa mu 1972 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, kuyambira pa tsamba 216, ndime 3, mpaka tsamba 217, ndime 3.
b Onani 1988 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 150-4.
Mafunso kaamba ka Kubwereramo
◻ Ndimotani mmene Jonatani anasonyezera chikondi chokhulupirika kaamba ka Davide?
◻ Ndi mtundu wanji wachikondi womwe unachitiridwa chithunzi ndi chikondi pakati pa Davide ndi Jonatani?
◻ Ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko achitira monga Mfumu Sauli pamene anavutitsa Davide?
◻ Nchiyani lerolino chomwe chiri chofanana ndi chikondi cha Jonatani kaamba ka Davide?
◻ Nchiyani chimene kugwirizana kwa Mboni dziko lonse kumasonyeza?
[Bokosi patsamba 27]
St. Mary’s Cathedral
Sydney
August 20, 1940.
The Rt. Hon. W. M. Hughes, M.H.R.,K.C.,
Attorney General,
CANBERRA.
Dear Mr. Hughes:
Ndikuyamikani kaamba ka kalata yanu ya pa 9 yonena za kuimiridwa kopangidwa kwa inu ndi Mr. Jennings, M.P.
Chiri, ndithudi, choyamikiridwa kuti kusamala kwakukulu kothekera kuyenera kuchitidwa ndi inu mu nkhani yovuta chotereyi monga ija yonena za amene kuimiridwa kunapangidwa.
Ngati, ngakhale kuli tero, kukaikira kokha komwe muli nako kumabuka kuchokera ku chenicheni chakuti anthu amenewa amadzinenera kukhala akuwanditsa ziphunzitso za Chikristu, ndingakhoze mwaulemu kwenikweni kulingalira kuti kuŵeruza kwanu kwa kuchita kwawo chimenechi kuzikidwe, osati pa kudzinenera kwawo, koma pa nsonga. Ponena za nsonga, ndikupereka zofalitsidwa zawo zenizeni ndi mawu awo ndi zochita, zotsimikizidwa ndi Apolisi a ku New South Wales. Chirichonse chosiyana ndi Chikristu, chingakhale chovuta kuchilingalira.
Nduna Yaikulu ya Apolisi mu N.S.W. yalongosola chiyembekezo chake chakuti maulamuliro a Commonwealth adzalengeza sosaite yomwe yakaikiridwayo kukhala bungwe lopanda lamulo kotero kuti Apolisi angakhale m’malo a kutenga kachitidwe kogwira ntchito kwenikweni kulinga ku iyo.
With every good wish, I remain,
Yours faithfully,
ARCHBISHOP OF SYDNEY