PHUNZIRO 48
Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
Anzathu apamtima amatithandiza kuti tizisangalala komanso amatilimbikitsa tikamakumana ndi mavuto. Koma Baibulo limatichenjeza kuti tizisamala tikamasankha anthu ocheza nawo. Ndiye kodi mungasankhe bwanji anthu abwino oti muzicheza nawo? Mungachite bwino kuganizira mafunso omwe ali m’munsiwa.
1. Kodi zochita za anthu amene mungasankhe kucheza nawo zingakukhudzeni bwanji?
Anthufe timatengera zochita za anthu amene timacheza nawo. Zimenezi zikutanthauza kuti tikhoza kutengera makhalidwe abwino kapena oipa a anthu amene timacheza nawo pamasom’pamaso kapena pa intaneti. Mpake kuti Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa [anthu omwe sakonda Yehova] adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mukamacheza ndi anthu omwe amakonda komanso kulambira Yehova, angakuthandizeni kuti nanunso mukhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti muzisankha zinthu mwanzeru. Koma kucheza kwambiri ndi anthu amene sakonda Yehova, kungachititse kuti tisiye kumukonda. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Tikamacheza ndi anthu omwe amakonda Mulungu, timatengera zochita zawo zabwino ndipo nawonso amatengera zochita zathu zabwino. Choncho, ‘timapitiriza kutonthozana ndi kulimbikitsana.’—1 Atesalonika 5:11.
2. Kodi Yehova angamve bwanji ngati mutasankha kumacheza ndi anthu oipa?
Yehova amasamala posankha anthu amene akufuna kuti akhale anzake. Baibulo limanena kuti iye “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Kodi Yehova angamve bwanji ngati titasankha kumacheza ndi anthu omwe samamukonda? Iye angakhumudwe kwambiri. (Werengani Yakobo 4:4.) Komabe, Yehova angasangalale kwambiri ndipo angatisankhe kuti tikhale anzake tikamapewa kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa n’kumacheza ndi anthu omwe amamukonda.—Salimo 15:1-4.
FUFUZANI MOZAMA
Onani chifukwa chake mufunika kusankha anzanu mwanzeru komanso zimene mungachite kuti muzicheza ndi anthu amene angakulimbikitseni kumachita zinthu zabwino.
3. Muzipewa kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa
Anthu amakhalidwe oipa ndi amene sakonda Mulungu ndiponso satsatira mfundo zake pa moyo wawo. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi tingayambe bwanji kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa mosazindikira?
Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi munthu wamakhalidwe ati amene sangakhale mnzanu wabwino? N’chifukwa chiyani mukutero?
Werengani Salimo 119:63, kenako mukambirane funso ili:
Kodi muyenera kusankha anthu otani kuti akhale anzanu?
4. Anthu amene timasiyana nawo zinthu zina akhoza kukhala anzathu abwino
Baibulo limafotokoza za Davide ndi Yonatani omwe anali mabwenzi apamtima. Iwo ankagwirizana kwambiri ngakhale kuti Yonatani anali wamkulu kwa Davide komanso anali mwana wa mfumu. Werengani 1 Samueli 18:1, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani anzathu sayenera kukhala anthu okhawo amene timafanana nawo msinkhu komanso zinthu zina?
Werengani Aroma 1:11, 12, kenako mukambirane funso ili:
Kodi anthu amene amakonda Yehova amalimbikitsana bwanji?
Muvidiyoyi, onani mmene wachinyamata wina anapezera anzake kudera limene anasamukira. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
N’chifukwa chiyani makolo a Akil ankadera nkhawa za anthu amene ankacheza nawo kusukulu?
N’chiyani chinachititsa kuti Akil ayambe kugwirizana ndi anthu amenewa?
N’chiyani chinamuthandiza kuti apeze anzake?
5. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mupeze anzanu abwino?
Onani zimene mungachite kuti mupeze anzanu abwino ndiponso zomwe mungachite kuti mukhale munthu amene anthu ena angakonde kumacheza naye. Onerani VIDIYO.
Werengani Miyambo 18:24 ndi 27:17, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mabwenzi enieni amathandizana m’njira ziti?
Kodi inuyo muli ndi anzanu abwino ngati amenewo? Ngati mulibe anzanu oterewa, kodi mungatani kuti muwapeze?
Werengani Afilipi 2:4, kenako mukambirane funso ili:
Kuti mupeze anzanu abwino, nanunso muyenera kukhala munthu wabwino yemwe anthu angakonde kucheza naye. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
ZIMENE ENA AMANENA: “Palibe vuto kumacheza ndi wina aliyense, kusiyana ndi kungokhaliratu opanda mnzako.”
Inuyo mungayankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Tikamasankha bwino anthu ocheza nawo, timasangalatsa Yehova ndiponso ifeyo timakhala osangalala.
Kubwereza
Kodi Yehova angamve bwanji ngati mutasankha kumacheza ndi anthu oipa?
Kodi tiyenera kupewa kucheza ndi anthu otani?
Mungatani kuti mupeze anthu abwino ocheza nawo?
ONANI ZINANSO
Onani mmene anzathu abwino angatithandizire tikamakumana ndi mavuto.
“Pezani Anzanu Apamtima Mapeto Asanafike” (Nsanja ya Olonda, November 2019)
Onani zimene mungachite kuti mupeze anzanu abwino.
Kodi muyenera kudziwa zotani pa nkhani yocheza ndi anthu pa intaneti?
Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti (4:12)
Munkhani yakuti, “Ndinkalakalaka Nditapeza Bambo,” onani chifukwa chake bambo wina anaganiza zosintha anthu ocheza nawo.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2012)