Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Anachita Zinthu Mwanzeru
ABIGAYELI anaona kuti mmodzi wa anyamata ake anali ndi mantha kwambiri, ndipo zinali zomveka chifukwa moyo wawo unali pangozi. Nthawi imeneyo n’kuti asilikali 400 ali m’njira kudzapha munthu aliyense wamwamuna wa pakhomo pa Nabala, mwamuna wa Abigayeli. Komano n’chifukwa chiyani asilikaliwo ankafuna kudzachita zimenezi?
Zonsezi zinayambika chifukwa cha Nabala yemwe anali wakhalidwe loipa kwambiri. Iye anali wankhanza ndiponso wamwano. Koma panthawiyi anaputa munthu wolakwika, chifuwa anali mtsogoleri wa asilikali wodziwa nkhondo kwambiri. Komabe, mmodzi wa anyamata a Nabala, yemwe mwina anali mbusa wa nkhosa, anauza Abigayeli zimene zinachitikazo. Anachita zimenezi chifukwa ankakhulupirira kuti Abigayeli akhoza kuganizira njira inayake yowapulumutsira. Komano kodi mzimayi mmodzi akanakwanitsa kulimbana ndi gulu la asilikali?
Choyamba tiyeni tikambirane kaye za mzimayi wochititsa chidwi ameneyu. Kodi Abigayeli anali ndani? Nanga kodi mavutowa anayambika bwanji? Ndipo ifeyo tingaphunzirepo chiyani pa chikhulupiriro cha mayiyu?
‘Mkazi Wanzeru Kwambiri Ndiponso Wokongola’
Abigayeli ndi Nabala anali osayenerana. Abigayeli anali wakhalidwe labwino kwambiri koma anakwatiwa ndi mwamuna wachabechabe. Mwamunayu anali wolemera ndipo ankadziona kuti anali munthu wofunika kwambiri. Koma kodi anthu ena ankamuona bwanji? M’Baibulo lonse, palibe munthu amene amatchulidwa ndi mayina oipa kuposa Nabala. Ndipo dzina lakuti Nabala limatanthauza “Wopanda nzeru” kapena “Wopusa.” Kodi makolo ake ndi omwe anam’patsa dzinali kapena anachita kupatsidwa ndi anthu ena chifukwa cha khalidwe lake loipa? Sizikudziwika, koma dzinali linali logwirizana kwambiri ndi khalidwe lake chifukwa iye anali wouma mtima ndiponso wokonda kuchita zinthu zoipa. Analinso chidakwa komanso wankhanza moti anthu ambiri ankamuopa kwambiri ndipo sankagwirizana naye.—1 Samueli 25:2, 3, 17, 21, 25.
Koma Abigayeli anali wosiyana kwambiri ndi mwamuna wake. Dzina lake limatanthauza kuti, “Bambo Anga Asangalala.” Abambo ambiri amasangalala akabereka mwana wamkazi wokongola, koma anzeru amasangalala kwambiri chifukwa cha khalidwe labwino la mwana wawoyo. Ndipo nthawi zambiri, munthu wokongola kwambiri amaona kuti kukhala munthu woganiza bwino, wanzeru, wolimba mtima kapenanso wachikhulupiriro n’kosafunika. Koma zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi Abigayeli chifukwa Baibulo limati iye ‘anali wanzeru kwambiri ndiponso wokongola.’—1 Samueli 25:3.
Ena angadabwe kuti, ‘N’chifukwa chiyani mkazi wanzeru ngati ameneyu analola kukwatiwa ndi Nabala, yemwe anali munthu wachabechabe?’ Kumbukirani kuti kale, makolo ambiri ankasankhira ana awo munthu woti akwatirane naye. Nthawi zina munthu ankasankha yekha munthu womanga naye banja, komabe makolo ndi amene ankapereka chilolezo choti mwana wawoyo alowe m’banja. Kodi makolo a Abigayeli ndi amene anakonza zoti mwana wawo akwatiwe ndi Nabala chifukwa choti Nabalayo anali munthu wotchuka komanso wachuma? Kapena kodi umphawi ndi umene unawachititsa zimenezi? Sizikudziwika, koma mfundo ndi yakuti, ndalama sizinachititse Nabala kukhala mwamuna wabwino.
Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo kuti aziona kuti ukwati ndi wopatulika. Choncho, iwo salimbikitsa anawo kuti akwatiwe ndi winawake chifukwa choti munthuyo ndi wolemera. Ndiponso sakakamiza anawo kuti akhale ndi chibwenzi adakali aang’ono n’cholinga choti azipeza ndalama zothandizira makolowo. (1 Akorinto 7:36) Komabe popeza Abigayeli anali atakwatiwa kale, zinali zosatheka kuti aganizire mfundo zimenezi. Kaya iye anakwatiwa ndi Nabala pa zifukwa zotani, koma chodziwika n’choti ankayesetsa kupirira mavuto a m’banja.
“Anawakalipira”
Nabala anachita zinthu zoipa zimene zinakhumudwitsa kwambiri Abigayeli. Iye ananyoza kwambiri Davide, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Komanso Davide anali atadzozedwa ndi mneneri Samueli n’cholinga choti adzakhale mfumu yolowa m’malo mwa Sauli mogwirizana ndi mmene Mulungu anafunira. (1 Samueli 16:1, 2, 11-13) Pothawa Sauli, amene anali mfumu yansanje komanso yoopsa kwambiri, Davide anakakhala m’chipululu ndi asilikali ake okwana 600.
Nabala ankakhala m’mudzi wa Maoni koma zikuoneka kuti anali ndi malo ena kufupi ndi mudzi wa Karimeli, komwe ankagwirako ntchito.a Midzi imeneyi inali m’madera okwera ndipo kunkapezeka udzu wobiriwira. Choncho antchito a Nabala ankadyetsako nkhosa zake zokwana 3,000. Komabe, derali linali losalimidwa ndipo chakum’mwera kunali chipululu chachikulu cha Parana. Chakum’mawa, kufupi ndi Nyanja ya Mchere, kunali dera la zigwembe ndiponso lamapanga. Davide ndiponso anthu amene anali nawo ankavutika kwambiri kudera limeneli kuti apeze chakudya komanso ankakumana ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri iwo ankakumana ndi anyamata omwe ankaweta nkhosa za Nabala.
Kodi asilikaliwa ankatani akakumana ndi abusawo? Zinali zosavuta kuti aziba nkhosa za Nabala, koma iwo sankachita zimenezi. M’malomwake, iwo ankateteza nkhosazo ndiponso abusawo. (1 Samueli 25:15, 16) Abusa pamodzi ndi nkhosa zawo ankakumana ndi mavuto ambirimbiri. Mwachitsanzo, m’derali munali zilombo zambiri zolusa. Komanso kuderali kunali kufupi ndi malire a kum’mwera a dziko la Isiraeli ndipo akuba ochokera m’madera ena ankabwera kuderali pafupipafupi.b
Davide ayenera kuti anali ndi udindo waukulu kwambiri wopezera chakudya anthu ake, omwe anali nawo m’chipululumo. Motero tsiku lina iye anatumiza anyamata ake 10 kuti akapemphe chakudya kwa Nabala. Nthawi imene Davide anasankha kutumiza anyamatawa inali yabwino chifukwa inali nthawi yometa ubweya wankhosa ndiponso yamadyerero. Ndipo panthawiyi anthu ankakonda kugawana zinthu. Komanso Davide anasankha bwino mawu oti anyamata ake akalankhule ndi Nabala. Iye anawauza kuti akalankhule naye mwaulemu kwambiri, mpaka anawalangiza kukanena kuti Davide ndi “mwana wanu,” mwina posonyeza kuti akudzindikira zoti Nabala ndi munthu wamkulu. Koma kodi Nabala anatani?—1 Samueli 25:5-8.
Iye anakwiya kwambiri moti mnyamata wake pouza Abigayeli za nkhaniyi, ananena kuti Nabala “anawakalipira kwambiri” anyamata a Davide. Nabala anali munthu womana kwambiri moti anawalalatira powauza kuti sangawononge mkate, madzi ndiponso nyama kupatsa Davide ndi anyamata ake. Iye ananyoza Davide ponena kuti anali wachabechabe ndiponso anali ngati kapolo amene wathawa mbuye wake. N’kutheka kuti Nabala ankaona Davide mofanana ndi mmene Sauli ankamuonera Davideyo. Sauli ankadana kwambiri ndi Davide ndipo iye komanso ndi Nabala sankaona Davide ngati mmene Yehova ankamuonera. Mulungu ankakonda kwambiri Davide ndipo ankamuona kuti ndi mfumu ya mtsogolo ya Isiraeli, osati chigawenga.—1 Samueli 25:10, 11, 14.
Ndiyeno anyamata a Davide atamuuza zimene Nabala ananena, iye anapsa mtima kwambiri ndipo analamula asilikali ake kuti: “Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake.” Davide pamodzi ndi asilikali ake 400 ananyamula zida ndipo anayamba ulendo wopita kukapha Nabala ndiponso munthu wina aliyense wamwamuna pakhomo pake. (1 Samueli 25:12, 13, 21, 22) Zinali zomveka kuti Davide akwiye koma zimene ankafuna kuchita posonyeza mkwiyo wakewo zinali zolakwika. Baibulo limati: “Mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” (Yakobe 1:20) Komano kodi Abigayeli akanatani kuti apulumutse anthu a m’banja mwake?
“Kudalitsike Kuchenjera Kwako”
M’maganizo mwathu tingathe kuona Abigayeli akuganizira zimene angachite kuti akonze zinthu. Mosiyana ndi mwamuna wake Nabala, Abigayeli anali wofunitsitsa kumvetsera. Ponena za Nabala, mnyamatayo anati: “Iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.”c (1 Samueli 25:17) N’zomvetsa chisoni kuti khalidwe lodzikonda la Nabala linamuchititsa kuti asamamve za ena. N’chimodzimodzinso masiku ano, anthu ambiri safuna kumva za ena. Koma mnyamatayo ankadziwa kuti Abigayeli anali munthu wabwino kwambiri, ndipo mwina n’chifukwa chake anaganiza zomuuza nkhaniyi.
Abigayeli anaganiza mwanzeru n’kuchita zinthu mwachangu. Baibulo limati: “Pomwepo Abigayeli anafulumira.” Mu nkhaniyi, mawu onena za mzimayiyu akuti “anafulumira” amapezeka kanayi. Iye anakonza mphatso zokapatsa Davide ndi anthu ake. Zina mwa mphatsozo zinali mikate, vinyo, nkhosa, tirigu wokazinga, mikate yamphesa ndiponso mikate ya nkhuyu. N’zoonekeratu kuti Abigayeli ankadziwa bwino zinthu zimene anali nazo ndiponso ankadziwa kusamalira bwino udindo wake wapakhomo mofanana ndi mkazi wanzeru wotchulidwa m’buku la Miyambo. (Miyambo 31:10-31) Abigayeli anatumiza anyamata ake kuti atsogole ndi mphatsozo ndipo iye anatsatira pambuyo ali yekha. Koma Baibulo limati “sanauza mwamuna wake Nabala.”—1 Samueli 25:18, 19.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Abigayeli sankagonjera mwamuna wake yemwe anali mutu wabanjalo? Ayi sizinali choncho. Nabala anali atachita zinthu zoipa kwa mtumiki wodzozedwa wa Yehova ndipo zimenezi zikanamuphetsa pamodzi ndi anthu ambiri osalakwa a panyumba pake. Komanso ngati Abigayeli akanapanda kuchita chilichonse ndiye kuti akanakhala ngati akugwirizana ndi zimene mwamuna wake anachita. Choncho, iye anaona kuti anayenera kugonjera Mulungu m’malo mogwirizana ndi zolakwika zimene mwamuna wake anachita.
Posapita nthawi, Abigayeli anakumana ndi Davide ndi asilikali ake. Apanso iye anafulumira kutsika pabulu wake n’kudzichepetsa pamaso pa Davide. (1 Samueli 25:20, 23) Kenako anachonderera Davide mochokera pansi pa mtima kuti achitire chifundo mwamuna wake pamodzi ndi banja lake. Kodi chinam’thandiza n’chiyani kuti alankhule mogwira mtima?
Abigayeli analankhula ngati walakwitsa ndi iyeyo ndipo anapempha Davide kuti am’khululukire. Ankadziwanso kuti mwamuna wake ndi wopanda nzeru, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake. Motero, mwina anapempha Davide, yemwe anali waulemu wake, kuti asalimbane ndi munthu wopanda nzeruyo. Iye analankhula mosonyeza kuti ankadziwa zoti Davide ndi mtumiki wa Yehova ndiponso kuti akumenya “nkhondo za Yehova.” Abigayeli anasonyezanso kuti ankadziwa zoti Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa ufumu. Tikutero chifukwa polankhula ndi Davide, iye anati: “Yehova . . . adzaika inu mukhale kalonga wa Isiraeli.” Kenako anapempha Davide kuti asachite chilichonse chimene chingam’chititse kuti akhale ndi mlandu wamagazi kapena zimene zikanam’chititsa kuti patsogolo ‘adzakhale ndi chomudodometsa,’ kutanthauza kuti chikumbumtima chake chikanam’vutitsa kwambiri. (1 Samueli 25:24-31) Mawu amenewa analidi achifundo ndiponso othandiza munthu kuganiza.
Ndiyeno kodi Davide anachita chiyani? Iye analandira zimene Abigayeli anamubweretsera ndipo ananena kuti: “Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi.” Davide anayamikira kwambiri Abigayeli chifukwa cholimba mtima n’kupita mwachangu kukakumana naye ndiponso chifukwa chomuthandiza kuti asachite zinthu zimene zikanachititsa kuti akhale ndi mlandu wamagazi. Kenako Davide anauza Abigayeli kuti: “Ukwere kwanu mumtendere,” ndipo anamuuzanso modzichepetsa kuti “ndamvera mawu ako.”—1 Samueli 25:32-35.
“Onani, Mdzakazi Wanu”
Atasiyana, Abigayeli ayenera kuti ankaganizirabe zimene anakambirana ndi Davide ndipo anatha kuona kuti Davide anali munthu wokhulupirika ndiponso wokoma mtima mosiyana ndi mwamuna wake yemwe anali wankhanza kwambiri. Komabe sikuti iye ankangokhalira kuganizira zimenezi. Kenako, Baibulo limati: “Abigayeli anafika kwa Nabala.” Iye anabwerera kwa mwamuna wake ndi mtima wofunitsitsa kusamalira banja lake mmene angathere. Komabe anafunika kuuza mwamuna wakeyo za mphatso zimene anapatsa Davide ndi anthu ake, chifukwa monga mutu wabanja, anayenera kudziwa zimene zinachitika. Abigayeli anafunika kufotokoza yekha zimenezi kwa mwamuna wake kuopera kuti mwamuna wakeyo akanachita manyazi akanamva nkhaniyi kwa anthu ena. Komabe, panthawiyi zinali zosatheka kumuuza nkhaniyi chifukwa Nabala anali paphwando lalikulu ngati la mfumu ndipo anali ataledzera kwambiri.—1 Samueli 25:36.
Pamenepanso Abigayeli anasonyeza kuti anali wolimba mtima komanso woganiza bwino chifukwa anadikira mpaka m’mawa kuti alankhule ndi mwamuna wakeyo ali bwinobwino. Iye anadziwa kuti mwamuna wake angamvetsere bwino panthawiyi ngakhale kuti zinali zoopsa chifukwa anali wosachedwa kupsa mtima. Ngakhale zinali choncho, iye anauza mwamuna wake zonse zimene zinachitika. Mwina Abigayeli ankayembekezera kuti mwamuna wake alusa kwambiri mwinanso kufika pomumenya. Koma Nabala sanachite zimenezi, m’malomwake anangokhala phee, osachita chilichonse.—1 Samueli 25:37.
Kodi chinam’chitikira n’chiyani? Baibulo limati: “Mtima wake unamyuka mkati mwake, iye nasanduka ngati mwala.” Mwina anadwala matenda a sitiroko chifukwa cha mantha. Komano iye anamwalira patapita masiku 10, osati chifukwa cha matenda, koma chifukwa choti “Yehova anam’kantha.” (1 Samueli 25:38) Nabala atafa, mavuto am’banja amene Abigayeli ankakumana nawo anatha. Ngakhale kuti masiku ano Yehova sapha anthu ngati mmene anachitira ndi Nabala, nkhaniyi ikutiphunzitsa mfundo yoti Yehova amadana ndi mawu achipongwe ndiponso kuchitirana nkhanza m’banja. Panthawi yake yoyenerera mtsogolo muno, iye adzapereka chilango kwa anthu ochita makhalidwe oipawa.
Kuonjezera pa kutha kwa mavuto am’banja lake, Abigayeli anapezanso madalitso ena. Davide atangomva kuti Nabala wafa, anatumiza anthu kuti akamufunsirire ukwati. Abigayeli anayankha kuti: “Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.” Apa, n’zoonekeratu kuti iye sanayambe kudzikweza chifukwa choti wapeza mwayi wokhala mkazi wa Davide. M’malomwake, ananena kuti anali woyenera kusambitsa mapazi a akapolo a Davide. Zitatero, Baibulo limafotokozanso kuti ‘anafulumira’ kupita kwa Davide.—1 Samueli 25:39-42.
Komabe zimenezi sizinatanthauze kuti tsopano moyo wa Abigayeli ukhala wopanda mavuto aliwonse, chifukwa Davide anali ndi mkazi wina dzina lake Ahinowamu. Ndiponso n’zosakayikitsa kuti akazi okhulupirika omwe anali pa mitala ankakumana ndi mavuto ambiri.d Komanso panthawiyi Davide anali asanakhale mfumu ndipo panali mavuto ambiri amene ankakumana nawo. Koma Abigayeli ankathandiza ndiponso kulimbikitsa Davide ndi mtima wake wonse ndipo anam’berekera mwana wamwamuna. Abigayeli ankaonanso kuti mwamuna wakeyo amam’lemekeza, amam’konda ndiponso amamuteteza. Ndipotu panthawi inayake, Davide anapulumutsa mkazi wakeyu kwa anthu omwe anamuba. (1 Samueli 30:1-19) Choncho, Davide ankachita zinthu motsanzira Yehova Mulungu, yemwe amakonda ndiponso kulemekeza akazi oganiza bwino, olimba mtima ndiponso okhulupirika ngati mmene analili Abigayeli.
[Mawu a M’munsi]
a Karimeli ameneyu si phiri lotchuka lomwe linali kumpoto kwa chipululu cha Parana. Koma ndi mudzi umene unali kufupi ndi chipululuchi.
b Zikuoneka kuti Davide ankaona kuti kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo kunali kutumikira Yehova Mulungu. Masiku amenewo, m’derali munkakhala mbadwa Abulahamu, Isake ndi Yakobo chifukwa ndi zimene Yehova anakonza. Choncho ndi zoonadi kuti kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo unali utumiki wopatulika.
c Mawu omwe mnyamatayo anagwiritsira ntchito ponena za Nabala amatanthauzanso kuti “mwana wa beliyali (wachabechabe).” Pavesi limeneli, mabaibulo ena amati Nabala anali “munthu wosamva za ena,” ndipo “sichinali chinthu chanzeru kulankhula naye.”
d Onani nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?” patsamba 30.
[Chithunzi patsamba 19]
Mosiyana ndi mwamuna wake, Abigayeli ankamva zonena za ena
[Chithunzi patsamba 20]
Polankhula ndi Davide, Abigayeli anasonyeza kuti anali wodzichepetsa, wolimba mtima ndiponso wanzeru