Kodi Muyenera Kukhala Okhulupirika kwa Ndani?
Dziko lathu: . . . Lizikhala lolondola nthaŵi zonse; kaya likulondola kapena likulakwitsa, lizikhalabe dziko lathu nthaŵi zonse.—Stephen Decatur, mkulu wa asilikali a panyanja wa ku United States, 1779-1820.
N’ZOSACHITA kufunsa kuti anthu ambiri amaona kukhulupirika ku dziko lawo kukhala kofunika kwambiri kuposa china chilichonse. Ena anganene mawu a Stephen Decatur motere: ‘Chipembedzo changa chizikhala cholondola nthaŵi zonse, kaya chikulondola kapena chikulakwitsa, n’chipembedzo changabe basi nthaŵi zonse.’
Kunena zoona, kukhala okhulupirika ku dziko kapena ku chipembedzo nthaŵi zambiri kumadalira malo amene munthu unabadwira. Koma kusankha kukhulupirika kwa winawake ndi nkhani yofunika zedi moti siingadalire zinthu zochitika mwamwayi. Komabe, kusiya kukhulupirika pa zinthu zomwe munthu wakula nazo kumafuna kulimba mtima komanso kumabweretsa mavuto.
Chiyeso cha Kukhulupirika
Mayi wina yemwe anakulira ku Zambia anati: “Ndinkakonda chipembedzo kwambiri kuyambira ndili wamng’ono. Kupemphera tsiku lililonse m’chipinda chopatulika cha makolo anga, kusunga masiku achipembedzo, ndiponso kupita ku kachisi nthaŵi zonse, ndiwo ena mwa malangizo omwe ndinkalandira ndili mwana. Chipembedzo changa ndiponso kulambira kwanga, zinali zogwirizana kwambiri ndi miyambo yathu, dera lathu, ndiponso banja lathu.”
Komabe, atakula kufika zaka zothamangira m’ma 20, iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo posakhalitsa anaganiza zosintha chipembedzo chake. Kodi kuchita zimenezo kunali kusakhulupirika?
Zlatko anakulira ku Bosnia, ndipo kwanthaŵi yaitali ndithu anamenya nawo nkhondo yomwe inali m’dziko lake. Nayenso anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsopano amakana kumenya nkhondo. Kodi iye ndi wosakhulupirika?
Mayankho anu pa mafunso ameneŵa angadalire maganizo anu pankhaniyi. Mayi yemwe tamutchula kale uja anati: “M’dera lakwathu kusintha chipembedzo kunali kochititsa manyazi. Kuchita zimenezo ankati n’kusakhulupirika, kupandukira banja lako ndiponso dera lako.” Mofananamo, asilikali omwe kale ankamenya nkhondo limodzi ndi Zlatko, ankaona anthu okana kumenya nkhondo monga opanduka. Mayi tamutchula uja ndiponso Zlatko anaona kuti kukhulupirika kwa Mulungu, komwe n’koposa china chilichonse, ndiko kofunika kwambiri pa moyo wawo. Mfundo yofunika kwambiri n’njakuti, kodi Mulungu amawaona bwanji anthu amene amafuna kukhala okhulupirika kwa iye?
Kukhulupirika Kwenikweni Kumasonyeza Chikondi
Mfumu Davide inauza Yehova Mulungu kuti: “Kwa munthu wokhulupirika inunso mudzakhala wokhulupirika.” (2 Samueli 22:26, NW) Liwu lachihebri lomwe alimasulira pano kuti ‘kukhulupirika’ limatanthauza kukoma mtima komwe mwachikondi kumasonyezedwa kwa munthu mpaka cholinga chake chitakwaniritsidwa. Popeza ali ndi mtima ngati wa mayi amene ali ndi mwana woyamwa, Yehova mwachikondi amakhala paubwenzi weniweni ndi amene ali okhulupirika kwa iye. Yehova ananena kwa atumiki ake okhulupirika mu Israyeli wakale kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde aŵa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” (Yesaya 49:15) Mulungu akutsimikizira amene amadzipereka kukhala okhulupirika kwa iye kuti adzawasamalira mwachikondi.
Chikondi ndicho maziko a kukhala okhulupirika kwa Yehova. Kukhulupirika koteroko kumachititsa munthu kukonda zomwe Yehova amakonda ndiponso kudana ndi zinthu zoipa zomwe Yehova amadana nazo. (Salmo 97:10) Popeza khalidwe lalikulu la Yehova ndi chikondi, kukhala okhulupirika kwa Mulungu kumathandiza munthu kusachita zinthu mopanda chikondi kwa ena. (1 Yohane 4:8) Chotero ngati munthu wasintha chipembedzo chake chifukwa chofuna kukhala wokhulupirika kwa Mulungu sindiye kuti wasiya kukonda banja lake ayi.
Kukhala Wokhulupirika kwa Mulungu Kumapindulitsa
Mayi yemwe tamutchula kale uja anafotokoza zomwe anachita motere: “Chifukwa chophunzira Baibulo, ndinazindikira kuti Yehova ndiye Mulungu weniweni, ndipo ndinakulitsa ubwenzi wanga ndi iye. Yehova ndi wosiyana ndi milungu yomwe ndinkailambira poyamba. Iye ali ndi chikondi changwiro, chilungamo, nzeru, ndiponso mphamvu. Popeza Yehova amafuna kulambira kosagaŵanika, ndinasiya kulambira milungu inayo.
“Makolo anga ankandiuza mobwerezabwereza kuti sakukondwa mpang’ono pomwe ndi zochita zanga ndiponso kuti ndikuwakhumudwitsa kwambiri. Zimenezi zinkandiwawa kwambiri chifukwa ndinkafuna kuti ndizigwirizana ndi makolo anga. Koma n’tadziŵa kwambiri choonadi cha m’Baibulo, chosankha changa chinali chodziŵikiratu. Sindikanatha kumukana Yehova.
“Kusankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova m’malo mwa miyambo yachipembedzo sikutanthauza kuti ndine wosakhulupirika kwa makolo ndi achibale anga. Ndimayesetsa kuwasonyeza mwa zomwe ndimalankhula ndiponso zochita zanga kuti ndimamvetsa madandaulo awo. Koma ngati n’tasiya kukhulupirika kwa Yehova, ndiye kuti iwo sangamudziŵe iye, ndipo kuchita zimenezo ndiko kusakhulupirika kwenikweni.”
Mofananamo, munthu sakhala wopanduka ngati atakana kuloŵa m’ndale kapena kumenya nawo nkhondo chifukwa chofuna kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Zlatko anafotokoza zomwe anachita motere: “Ngakhale kuti ndinakulira m’Chikristu cha dzina lokha, ndinakwatira mkazi yemwe sanakulire m’Chikristu. Nkhondo itaulika, ndinafunika kukhala wokhulupirika ku mbali zonse ziŵiri. Ndinakakamizika kusankha kuimira gulu limodzi. Ndinamenya nkhondo zaka zitatu ndi theka. M’kupita kwa nthaŵi, ine ndi mkazi wanga tinathaŵira ku Croatia, komwe tinakumana ndi Mboni za Yehova.
“Chifukwa chophunzira Baibulo, tinazindikira kuti choyamba tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova ndiponso kuti iye amafuna kuti tizikonda anzathu mosaganizira za chipembedzo chawo kapena mtundu wawo. Tsopano ine ndi mkazi wanga tikulambira Yehova mogwirizana ndipo ndaphunzira kuti sizingatheke kukhala wokhulupirika kwa Mulungu uku n’kumamenyana ndi anzanga.”
Kukhala Okhulupirika Chifukwa Chodziŵa Zolondola
Popeza Yehova ndiye Mlengi, n’koyenera kuti choyamba tikhale okhulupirika kwa iye kuposa zina zonse. (Chivumbulutso 4:11) Komabe, kuti tipeŵe kuchititsa kukhulupirika kwathu kwa Mulungu kukhala mphamvu yotisonkhezera kuumirira miyambo ndiponso kuvulaza ena, tiyenera kudziŵa zolondola. Baibulo limatilangiza kuti: “Musandulike mukhale atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu . . . ndi kukhulupirika kwenikweni.” (Aefeso 4:23, 24, NW) Munthu wotchuka yemwe analemba mawu ouziridwa ameneŵa analimba mtima kufufuza kukhulupirika kwake pa zinthu zomwe anakula nazo. Kufufuza kwakeko kunamuchititsa kusintha komwe anapindula nako.
Inde, Saulo anakumana ndi chiyeso cha kukhulupirika, monga mmene achitira ambiri m’nthaŵi yathu ino. Saulo anakulira m’banja lotsatira miyambo kwambiri ndipo anakhala wokhulupirika kwambiri ku chipembedzo cha makolo ake. Kukhulupirika kwake ku ziphunzitso zachipembedzo chakecho kunam’sonkhezera kuchitira nkhanza anthu amene sankagwirizana ndi maganizo ake. Saulo anali wotchuka chifukwa chogwira Akristu m’nyumba zawo n’kuwapereka kuti alangidwe ngakhale kuphedwa kumene.—Machitidwe 22:3-5; Afilipi 3:4-6.
Komabe, Saulo atadziŵa zolondola kuchokera m’Baibulo, anachita zomwe anzake ambiri ankaganiza kuti sangayerekeze kuchita. Iye anasintha chipembedzo chake. Saulo amene anadzatchedwa mtumwi Paulo, anasankha kukhala wokhulupirika kwa Mulungu m’malo mokhala wokhulupirika ku miyambo. Kukhulupirika kwake kwa Mulungu chifukwa chodziŵa zolondola kunam’limbikitsa Saulo kukhala wololera, wachikondi, ndiponso wolimbikitsa ena, zimene zinasiyana kwambiri ndi khalidwe lake lakale lakupha ndiponso loumirira miyambo.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Okhulupirika?
Mwachidziŵikire ngati kukhulupirika kwathu kuli kogwirizana ndi miyezo ya Mulungu tidzapindula kwambiri. Mwachitsanzo, lipoti la chaka cha 1999 la gulu lofufuza nkhani za mabanja la Australian Institute of Family Studies linanena kuti, “kudalirika ndi kukhulupirika . . . [ndiponso] mkhalidwe wauzimu,” ndi zina mwa zinthu zofunika kwambiri kuti mabanja azikhala nthaŵi yaitali komanso osangalatsa. Kafukufuku yemweyo anapezanso kuti “mabanja okhazikika ndiponso osangalatsa” amathandiza amuna ndi akazi kukhala achimwemwe, a thanzi labwino, ndiponso amakhala ndi moyo nthaŵi yaitali. Ana nawonso amakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo wachimwemwe.
M’dziko losakhazikika lamakonoli, kukhulupirika tingakuyerekezere ndi chingwe chopulumutsira munthu amene akusambira movutika kuti apulumuke chomwe achimangirira ku sitima yopulumutsa anthu pa ngozi. Ngati munthu yemwe ‘akusambirayo’ sanagwire chingwe chilichonse ndiye kuti azingotengekatengeka ndi mafunde ndiponso mphepo. Koma ngati wagwira chingwe cholakwika, zili ngati kuti chingwecho achimangirira ku sitima yomwe ikumira. Monga Saulo, munthu woteroyo atha kumachita zinthu zovulaza. Mosiyana ndi zingwe zimenezi, kukhala okhulupirika kwa Yehova chifukwa chodziŵa zolondola, kuli ngati chingwe chomwe chingatithandize kukhala olimba ndiponso kupulumuka.—Aefeso 4:13-15.
Yehova akulonjeza amene ali okhulupirika kwa iye kuti: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa, asungika kosatha.” (Salmo 37:28) Posachedwapa, onse amene ali okhulupirika kwa Yehova adzaloŵa m’dziko lapansi la paradaiso, momwe adzasangalala ndi moyo wopanda chisoni, zowawa, komanso wopanda mikangano yachipembedzo ndiponso yandale.—Chivumbulutso 7:9, 14; 21:3, 4.
Ngakhale pakalipano, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse aona kuti chimwemwe chenicheni chimapezeka chifukwa chokhala okhulupirika kwa Yehova. Bwanji osauza Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni kupenda maganizo anu pankhani ya kukhulupirika mounikiridwa ndi choonadi cha m’Baibulo? Baibulo limatiuza kuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.”—2 Akorinto 13:5.
Kufufuza chikhulupiriro chathu ndiponso kuona chifukwa chomwe timakhalira okhulupirika kumafuna kulimba mtima. Komabe, kuchita zimenezi kungakhale kopindulitsa kwambiri ngati pamapeto pake titakhala mabwenzi enieni a Yehova Mulungu. Mayi yemwe tamutchula kale uja anafotokoza maganizo a anthu ambiri pomwe anati: “Ndazindikira kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi miyezo yake, kumatithandiza kuchita zinthu mwanzeru ndi achibale athu ndiponso kukhala anthu abwinopo m’dera lathu. Ngakhale titakumana ndi ziyeso zotani, ngati ndife okhulupirika kwa Yehova, iye adzakhalanso wokhulupirika kwa ife nthaŵi zonse.”
[Zithunzi patsamba 6]
Kudziŵa zolondola kunam’limbikitsa Saulo kusiya kukhala wokhulupirika ku miyambo
[Chithunzi patsamba 7]
Bwanji osapenda zinthu zomwe mumazisonyeza kukhulupirika kwanu mounikiridwa ndi choonadi cha m’Baibulo?
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Churchill, pamwamba chakumanzere: Chithunzi cha U.S. National Archives; Joseph Göbbels, chakumanja: Library of Congress