Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Sanasunthike Pakulambira Koona
ELIYA anayang’ana gulu la anthu amene anali kukwera movutika phiri la Karimeli. Anthuwa anali kuonekeratu kuti anali anjala ngakhale kuti kunali kusanache. Njala imene inatha zaka zitatu ndi theka, inasiya anthuwa m’mavuto aakulu.
Pagulu la anthuwa, panali aneneri a Baala 450, amene anali onyada ndi odzikweza komanso odana kwambiri ndi Eliya yemwe anali mneneri wa Yehova. Mfumukazi Yezebeli anali atapha atumiki a Yehova ambiri, komabe Eliya sanasiye kulimbana ndi olambira Baala. Koma kodi akanakwanitsa kulimbana nawo? N’kutheka kuti ansembe a Baala ankaganiza kuti munthuyu sangapambane popeza anali yekha. (1 Mafumu 18:3, 19, 20) Mfumu Ahabu anapitanso ku phiriku pa galeta lake lachifumu. Iyenso ankamuda Eliya.
Panthawiyi wolambira woona anali mneneriyu basi ndipo anatsala pang’ono kuona zinthu zapadera kwambiri. Pamene Eliya ankaona anthuwa akukwera phirili, iye anadziwa kuti n’chiyambi cha kulimbana kwakukulu pakati pa kulambira koona ndi konyenga kumene sikunachitikepo n’kale lonse. Kodi iye anamva bwanji nthawiyi itafika? Iye anachita mantha, popeza “anali munthu monga ife tomwe.” (Yakobe 5:17) Ndipo zikuoneka kuti Eliya anadzimvadi kuti anali yekhayekha ataona anthu osakhulupirirawa, ndi mfumu yawo yopandukayo ndiponso ansembe awo omwe ankapha anthu.—1 Mafumu 18:22.
Koma kodi zinakhala bwanji kuti Aisiraeli afike mpaka pamenepa? Ndipo kodi masiku ano tingaphunzirepo chiyani pankhani imeneyi? Baibulo limatilimbikitsa kuyang’anitsitsa zochita za atumiki odzipereka a Mulungu kuti ‘titsanzire chikhulupiriro chawo.’ (Aheberi 13:7) Tsopano onani chitsanzo cha Eliya.
Kulimbana Kwanthawi Yaitali Kufika Pachimake
Pazaka zambiri za moyo wake, palibe chimene Eliya akanachita pamene anthu ankanyalanyaza ndi kupondereza kulambira Yehova komwe kunali chinthu chofunika kwambiri m’dzikomo. Kwanthawi yaitali, Aisiraeli anali pankhondo yoti asankhe pakati pa kulambira koona ndi konyenga, ndiponso pakati pa kulambira Yehova Mulungu kapena mafano amene mitundu imene inali nawo pafupi imalambira. M’masiku a Eliya, kulimbana kumeneku kunali kutafika poipa kwambiri.
Mfumu Ahabu anakwatira Yezebeli, mwana wa mfumu ya ku Sidoni. Yezebeli anatsimikiza mtima kufalitsa kulambira Baala m’dziko la Isiraeli ndiponso kuthetseratu kulambira Yehova. Ndipo Ahabu sanachedwe kukhalanso ndi mtima womwewu. Iye anamangira Baala kachisi ndi guwa la nsembe ndipo anatsogolera anthu kulambira mulungu wonyenga ameneyu. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri Yehova.—1 Mafumu 16:30-33.a
Kodi n’chiyani chinapangitsa kulambira Baala kukhala koipitsitsa? Chifukwa chakuti kunakopa Aisiraeli ambiri kusiya kulambira Mulungu woona. Kunalinso konyenga ndiponso kwa nkhanza. Kunkakhala ndi mahule achimuna ndi achikazi pakachisi, mapwando amene cholinga chake chinali kugonana mwachisawawa, ngakhalenso kupereka ana nsembe kumene. Yehova analowererapo mwa kutumiza Eliya kwa Ahabu kuti akanene za njala imene idzatha pokhapokha mneneri wa Mulungu akadzalengeza kuti ithe. (1 Mafumu 17:1) Panatha zaka zambiri kuti Eliya aonanenso ndi Ahabu n’cholinga choti amuuze kuti asonkhanitse anthu ndi aneneri a Baala ku phiri la Karimeli.
Koma kodi masiku ano tikupindulapo chiyani pa nkhani ya kulimbana kwa Eliya ndi aneneri a Baala? Ena anganene kuti nkhani ya kulambira Baala ilibe phindu masiku ano, popeza tilibe akachisi a Baala ndi maguwa ake a nsembe. Komabe nkhani imeneyi sikuti yangokhala mbiri ya kale basi. (Aroma 15:4) Mawu akuti “Baala” amatanthauza kuti “mwiniwake” kapena “mbuye.” Yehova anauza anthu ake kuti ayenera kumusankha iye kukhala “baala” wawo, kapena kuti mwamuna wawo. (Yesaya 54:5) Kodi simukuvomereza kuti masiku anonso anthu akutumikira ambuye osiyanasiyana osati Mulungu Wamphamvuyonse? Ndithudi, ngati anthu pamoyo wawo amangokhalira kufunafuna ndalama, ntchito, zosangalatsa, zakugonana, kapena milungu ina iliyonse imene anthu amalambira osati Yehova, ndiye kuti asankha zimenezi kukhala mbuye wawo. (Mateyo 6:24; Aroma 6:16) Choncho, tingati zinthu zambiri zokhudza kulambira Baala n’zofala masiku ano. Nkhani imeneyi ya kulimbana pakati pa Yehova ndi Baala ingatithandize kusankha mwanzeru woti timutumikire.
Kodi ‘Anakayikakayika’ Motani?
Pamwamba penipeni paphiri la Karimeli anthu ankatha kuona dziko la Isiraeli lonse, kuyambira kuchigwa cha Kisoni mpaka ku Nyanja Yaikulu (Mediterranean) imene inali pafupi ndi mapiri a Lebano cha kumpoto kwenikweni kwa dzikoli.b Koma dzuwa likukwera patsiku lapadera limeneli, dziko lonseli linayamba kuonekeratu kuti linali louma. Dziko limene Yehova anapatsa ana a Abrahamu, poyamba linali la chonde koma tsopano linali litaumiratu. M’dzikoli tsopano munali chilala chadzaoneni, chifukwa cha kusaganiza bwino kwa anthu enieni a Mulungu. Anthu amenewo atasonkhana pamodzi, Eliya anawayandikira ndi kuwauza kuti: “Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, m’tsateni iye; ngati Baala, mum’tsate iyeyo.”—1 Mafumu 18:21.
Kodi Eliya ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “mukayikakayika kufikira liti”? Anthu amenewo sankadziwa kuti anafunika kusankha chimodzi, kulambira Yehova kapena kulambira Baala. Iwo ankaganiza kuti angathe kuchita zonsezi, kusangalatsa Baala pochita miyambo yake yoipayo ndiponso kupempha Yehova Mulungu kuti awathandize. Mwina ankaganiza kuti Baala azidalitsa mbewu ndi ziweto zawo, ndipo “Yehova wa makamu” aziwateteza pankhondo. (1 Samueli 17:45) Iwo anaiwala mfundo yofunika kwambiri imene anthu ambiri saidziwa masiku ano yakuti, Yehova sagawana kulambira ndi milungu ina. Iye amafuna ndiponso ndi woyenera kulambiridwa mosagawanika. Iye savomereza komanso amadana ndi kulambira kwina kulikonse konyenga.—Eksodo 20:5.
Choncho Aisiraeli amenewo anali ‘kukayikakayika’ ngati munthu amene akufuna kuyenda njira ziwiri nthawi imodzi. Masiku anonso anthu ambiri amalakwitsa zinthu monga mmene Aisiraeli anachitira. Iwo amayamba kuchita zinthu zina zokhudza kulambira konyenga, moti zimenezi zimawachititsa kusiya kulambira Mulungu. Mawu ochenjeza ndi omveka bwino a Eliya oti siyani kukayikakayika, angatithandize kuonanso bwinobwino zinthu zimene timaika patsogolo ndiponso mmene kulambira kwathu kulili.
Mayeso Apadera
Ndiyeno Eliya anaganiza kuti pakhale mayeso. Ndipo mayeso ake anali osavuta. Ansembe a Baala anafunika kumanga guwa la nsembe ndi kuikapo nsembe; ndiyeno anafunika kupemphera kwa mulungu wawo kuti apsereze nsembeyo. Eliya nayenso anafunika kuchita chimodzimodzi. Iye anati: “Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu.” Eliya ankadziwa bwino kwambiri yemwe anali Mulungu woona. Iye anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri moti analolera kuti olambira Baala ndiwo ayambe kupempha kwa mulungu wawo. Iye anawapatsa adani akewo mwayi wonse, wosankha ng’ombe yamphongo imene akufuna kupereka nsembe ndiponso woyamba kupempha Baala.c—1 Mafumu 18:24, 25.
Sitikukhala mu nthawi ya zozizwitsa. Komabe, Yehova sanasinthe ndipo tingamukhulupirire monga anachitira Eliya. Mwachitsanzo, ngati ena sakukhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa, tisamaope koma tiziwalola kunena maganizo awo. Mofanana ndi Eliya, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Mulungu. Ndipo timachita zimenezi osati mwa kudzidalira tokha koma mwa kudalira Mawu ake ouziridwa amene analembedwa kuti ‘awongole zinthu.’—2 Timoteyo 3:16.
Aneneri a Baala anaika nsembe yawo ija ndipo anayamba kupempha mulungu wawo. Iwo anafuula mobwerezabwereza amvekere: “Baala, timvereni ife.” Iwo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka nthawi n’kumatha. Ndipo Baibulo limati: “Koma panalibe mawu kapena wovomereza.” Ndipo masana Eliya anayamba kuwaseka akumati mwina Baala ayenera kuti watanganidwa ndi zinazake, kapena wapita kuchimbudzi. Mwinanso wagona, ndipo muyenera kum’dzutsa. Kenako Eliya analimbikitsa anthu onyengawo kuti: “Kwezani mawu.” Ndithudi, iye ankadziwa kuti olambira Baala ndi onyenga enieni, koma ankafuna kuti anthu a Mulungu adzionere okha kuti Baala analidi wonyenga.—1 Mafumu 18:26, 27.
Zitatero ansembe a Baala anakwiya kwambiri, “anakwezadi mawu, nadzitema monga makhalidwe awo ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wawo unali chuchuchu.” Koma zonsezi sizinaphule kanthu. “Panalibe mawu, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.” (1 Mafumu 18:28, 29) Ndithudi kunalibe Baala. Satana anangopeka kuti kuli Baala n’cholinga choti anthu asiye kulambira Yehova. Monga zinalili kale, masiku anonso ngati tisankha mbuye wina osati Yehova tidzakhumudwa ndiponso tidzachita manyazi.—Salmo 25:3; 115:4-8.
Zotsatira za Mayeso
Chakumadzulo, inafika nthawi yoti Eliya nayenso achite mbali yake. Iye anakonzanso guwa la nsembe la Yehova limene linagumulidwa. Mwachionekere linagumulidwa ndi anthu amene ankadana ndi kulambira koona. Pokonza guwali, iye anagwiritsa ntchito miyala 12, mwina pofuna kukumbutsa anthu ambiri a ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli kuti anafunika kutsatira Chilamulo chimene chinaperekedwa kwa mafuko onse khumi ndi awiri a Isiraeli. Ndiyeno anaika nsembe yakeyo paguwapo n’kuithira madzi ambiri, mwina ankawatunga mu nyanja ya Mediterranean imene inali pafupi ndi malowa. Ndipo anakumba ngalande mozungulira guwalo, n’kudzazamonso madzi. Monga mmene anapatsira aneneri a Baala mwayi wonse wochita zilizonse kuti zimene iwo ankafunazo ziyende, iye anachita zonse zimene zikanachititsa kuti motowo usayake. Iye anachita izi chifukwa anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu wake sangalephere.—1 Mafumu 18:30-35.
Zinthu zonse zitakonzedwa, Eliya anapemphera. Pemphero lake linali lomveka bwino ndi losavuta ndipo linasonyeza chimene chinali chofunika kwambiri kwa iye. Choyamba, iye ankafuna kwambiri kuti anthu adziwe kuti Yehova ndiye “Mulungu wa Isiraeli,” osati Baala. Chachiwiri, iye ankafuna kuti anthu onse adziwe kuti ntchito yake inali yotumikira Yehova, ndipo Mulungu ndi amene ayenera kupatsidwa ulemerero. Chomaliza, anasonyeza kuti ankaganizirabe anthu a mtundu wake, chifukwa ankafunitsitsa kuti Yehova ‘abwezenso mitima yawo.’ (1 Mafumu 18:36, 37) Eliya ankawakondabe anthuwo ngakhale kuti anabweretsa mavuto ambiri chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. Tikamapemphera kwa Mulungu, tiyenera kudera nkhawa dzina la Mulungu, komanso tiyenera kudzichepetsa ndi kumvera chifundo anthu ovutika.
Eliya asanapemphere, khamu la anthulo liyenera kuti linkaganiza kuti Yehova awakhumudwitsanso monga anachitira Baala. Koma zimene anthuwa anaona Eliya atangomaliza kupemphera, zinawapangitsa kuti asakayikenso. Nkhaniyi imati: “Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mum’tchera.” (1 Mafumu 18:38) Ili linalidi yankho lothetsa makani. Kodi anthu anachita bwanji ataona zimenezi?
Onse anafuula amvekere: “Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.” (1 Mafumu 18:39) Pomaliza pake anthuwa anadziwa choonadi pankhaniyo. Komabe, iwo anali asanasonyezebe chikhulupiriro chilichonse. Kunena zoona, kuvomereza kuti Yehova ndi Mulungu woona ataona moto wochokera kumwamba chifukwa cha pemphero la Eliya si umboni weniweni wakuti anthuwo anali ndi chikhulupiriro. Choncho Eliya anawapempha kuti asonyeze m’njira ina kuti anali ndi chikhulupiriro. Iye anawauza kuti atsatire Chilamulo cha Yehova, zimene anafunika kuchita zaka zambiri zapitazo. Chilamulo cha Mulungu chinati aneneri onyenga ndi olambira mafano anayenera kuphedwa. (Deuteronomo 13:5-9) Aneneri a Baala amenewa anali adani enieni a Yehova Mulungu popeza ankachita dala zinthu zimene iye amadana nazo. Kodi anayenera kuwachitira chifundo? Chabwino, kodi iwo anachitira chifundo ana osalakwa amene ankawaotcha ali amoyo powapereka nsembe kwa Baala? (Miyambo 21:13; Yeremiya 19:5) Panalibe ndi mmodzi yemwe mwa aneneri amenewa amene anayenera kuchitiridwa chifundo. Choncho, Eliya analamula kuti iwo aphedwe, ndipo anaphedwadi.—1 Mafumu 18:40.
Masiku ano, anthu ena otsutsa amati zimene zinachitika pa phiri la Karimeli sizinathe mwachilungamo. Ena amada nkhawa kuti zimene zinachitika pa phirili zingachititse kuti anthu ena otengeka maganizo pankhani zachipembedzo aziukirana. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano pali anthu ambiri otere amene amachita zachiwawa m’dzina la chipembedzo. Komatu Eliya sanali ngati anthu otengekawa. Iye anachita zinthu zimene Yehova ankafuna ndipo anapereka chilango choyenera. Komabe, Akhristu enieni amadziwa kuti sangachite zimene Eliya anachitazi mwa kupha anthu oipa. Chibwerereni Mesiya, Akhristu onse oona amatsatira mfundo imene Khristu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyo 26:52) M’tsogolo muno Yehova adzauza mwana wake kuweruza anthu mwachilungamo.
Mkhristu woona aliyense ayenera kukhala ndi chikhulupiriro. (Yohane 3:16) Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kutsanzira anthu okhulupirika ngati Eliya. Iye analambira Yehova ndi mtima wonse ndipo analimbikitsa ena kuchita chimodzimodzi. Eliya anatsutsiratu poyera chipembedzo chonyenga chimene Satana ananyengera anthu kusiya kulambira Yehova. Ndipo anadalira Yehova kuti athetse nkhaniyo m’malo modalira nzeru zakezake. Ndithudi, Eliya sanasunthike pakulambira koona. Choncho, aliyense wa ife atsanzire chikhulupiriro chake.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri pankhani ya zimene Eliya anachitapo ndi Ahabu, onani nkhani yakuti “Kodi Muli ndi Chikhulupiriro Chonga cha Eliya?” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1992.
b Phiri la Karimeli nthawi zambiri limakhala lobiriwira komanso kumawomba kamphepo kayeziyezi kochokera m’nyanja ndipo zimenezi zimachititsa kuti kawirikawiri kuzigwa mvula ndi mame ambiri. Chifukwa chakuti anthu ankanena kuti Baala ndi amene amabweretsa mvula, mwachionekere phiri limeneli ndi limene linali malo ofunika kwambiri pa kulambira Baala. Koma panthawiyi zinasonyezeratu kuti Baala ndi mulungu wonyenga chifukwa phiri la Karimeli linauma ndiponso linali lopanda zomera.
c Chochititsa chidwi n’chakuti Eliya anawauza kuti: “Musasonkhepo moto” pa nsembeyo. Akatswiri ena a Baibulo amati opembedza mafano amenewa nthawi zina ankagwiritsa ntchito maguwa ansembe amene ankakhala ndi bowo kunsi kumene amabisako moto n’cholinga choti anthu aziona ngati kuti milungu yawo ndiyo yayatsa motowo.
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Tikasankha mbuye wina osati Yehova tidzakhumudwa
[Chithunzi patsamba 21]
‘Yehova ndiye Mulungu woona’