-
Anali Watcheru Ndiponso AnadikiraTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
17, 18. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira Eliya ali m’njira yopita ku Yezereeli? (b) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi ulendo wa Eliya wochokera ku Karimeli kupita ku Yezereeli? (Onaninso mawu a m’munsi.)
17 Mneneri wa Yehovayu anayamba ulendo wobwerera kwawo ndipo anadutsa njira imene Ahabu anadutsa. Ulendowu unali wautali, kunja kunali mdima wa mvula komanso mumsewu monse munali madzi okhaokha. Koma panachitika chinthu china chodabwitsa.
18 Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Dzanja la Yehova linali ndi Eliya, moti iye anakokera chovala chake m’chiuno n’kuchimanga, ndipo anayamba kuthamanga n’kupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.” (1 Maf. 18:46) Izi zikusonyeza kuti Yehova anathandiza Eliya modabwitsa chifukwatu Eliya anali wachikulire ndipo ulendo wokafika ku Yezereeli unali wa makilomita 30.a Yerekezerani kuti mukuona mneneriyo akukwinya chovala chake kuti azithamanga bwino. Ndiyeno akuthamanga m’njira yomwe inali madzi okhaokha mpaka kupeza galeta limene Ahabu anakwera n’kulipitirira.
19. (a) Kodi mphamvu zimene Eliya anapatsidwa zikutikumbutsa maulosi ati? (b) Pamene Eliya ankathamanga pa ulendo wake wopita ku Yezereeli, kodi ankadziwa chiyani zokhudza Atate wake?
19 Pamenepatu Eliya anadalitsidwa kwambiri. Zinali zinthu zolimbikitsa kwambiri kwa Eliya chifukwa anapatsidwa mphamvu zapadera zomwe mwina zinaposa zimene anali nazo ali wachinyamata. Zimenezi zikutikumbutsa maulosi amene amatitsimikizira kuti anthu okhulupirika adzakhala ndi thanzi labwino m’Paradaiso padziko lapansi. (Werengani Yesaya 35:6; Luka 23:43) Pamene Eliya ankathamanga pa ulendowu ankadziwa kuti Atate wake, yemwe ndi Mulungu woona, akusangalala naye.
-
-
Analimbikitsidwa ndi Mulungu WakeTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
1, 2. Kodi chinachitika n’chiyani pa tsiku lapadera kwambiri pa moyo wa Eliya?
ELIYA anali akuthamanga pa mvula pa ulendo wake wopita ku Yezereeli ndipo pa nthawiyi kunja n’kuti kuli mdima wamvulayo. Panali padakali ulendo wautali kuti akafike ku Yezereeli komanso anali munthu wachikulire. Ngakhale zinali choncho, iye ankathamanga osatopa chifukwa “dzanja la Yehova” linali naye. Pa nthawiyi, anali ndi mphamvu zoti sanakhalepo nazo chiyambire moti anathamanga mpaka kupitirira gulu la mahatchi amene ananyamula Mfumu Ahabu pa galeta lake lachifumu.—Werengani 1 Mafumu 18:46.
-