Yehova Amakondwera Mukamamumvera
“Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga.”—MIYAMBO 27:11.
1. Kodi dziko masiku ano ladzala ndi mzimu wotani?
MASIKU ano, dziko ladzala ndi mzimu wosafuna kuuzidwa chochita ndi wa kusamvera. Mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake m’kalata yopita kwa Akhristu a ku Efeso. Anati: “Munali kuyenda . . . mogwirizana ndi dongosolo la zinthu la m’dzikoli, momveranso wolamulira wa mphamvu ya mumpweya, mzimu umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:1, 2) Zoonadi, tingati Satana Mdyerekezi, “wolamulira wa mphamvu ya mumpweya,” waipitsa dziko lonse ndi mzimu wa kusamvera. Ankachita zimenezi nthawi ya atumwi, ndipo wakhala akuchitabe zimenezi kwambiri kuchokera pamene anathamangitsidwa kumwamba m’zaka za nkhondo yoyamba ya padziko lonse.—Chivumbulutso 12:9.
2, 3. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Yehova?
2 Ngakhale zili choncho, Akhristufe timadziwa kuti tifunika kumvera Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse chifukwa chakuti iye ndi Mlengi wathu, Wolamulira wathu wachikondi, Mlanditsi wathu, ndiponso amene amasamalira moyo wathu. (Salmo 148:5, 6; Machitidwe 4:24; Akolose 1:13; Chivumbulutso 4:11) Masiku a Mose, Aisiraeli ankadziwa kuti Yehova ndiye anawapatsa moyo ndiponso anali Mpulumutsi wawo. N’chifukwa chake Mose anawauza kuti: “Muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani.” (Deuteronomo 5:32) Ndithudi, iwo anafunika kumvera Yehova. Koma patangopita nthawi yochepa, iwo analeka kumvera Wolamulira wawo.
3 Kumvera Mlengi wa chilengedwe chonse ndi kofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Panthawi ina Mulungu analamula Samueli kuuza Mfumu Sauli kuti: “Kumvera ndiko kokoma koposa nsembe.” (1 Samueli 15:22, 23) Kodi kumvera kumaposa bwanji nsembe?
Kumvera ‘Kumaposa Nsembe’
4. Kodi ndi chiyani chimene tingamuchitire Yehova?
4 Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi, zinthu zonse zimene tili nazo ndi zake. Ndiyeno, kodi pali chilichonse chimene tingamuchitire? Inde, chilipo ndipo ndi chamtengo wapatali. Tingamuchitire chiyani? Tikupeza yankho pamalangizo otsatirawa akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Zimene tingamuchitire Mulungu ndi kumumvera basi. Ngakhale kuti tinabadwira kosiyanasiyana ndipo tili ndi moyo wosiyanasiyana, ifeyo mwa kumvera, tingatsutse bodza lamkunkhuniza la Satana Mdyerekezi lakuti anthufe sitingakhale okhulupirika kwa Mulungu poyesedwa. Ndithudi, Mulungu watilemekeza zedi potipatsa mwayi wotsutsa zimenezi!
5. Kodi Mlengi amamva bwanji ngati anthu sakumumvera? Perekani chitsanzo.
5 Mulungu ali ndi chidwi ndi zimene timachita. Tikapanda kumvera, sasangalala. Zimamupweteka kuona munthu akuchita zinthu zopanda nzeru ngati zimenezo. (Salmo 78:40, 41) Zimenezi tingaziyerekezere ndi munthu wodwala matenda a shuga amene waleka kutsatira malangizo a kadyedwe amene dokotala anamupatsa ndipo akudyabe zinthu zimene anamuletsa. Kodi dokotalayo angamve bwanji? Yehovanso zimamupweteka anthu akapanda kumumvera, chifukwa chakuti amadziwa zotsatira zake munthu akamanyalanyaza malangizo ake opatsa moyo.
6. Kodi ndi chiyani chingatithandize kumvera Mulungu?
6 Kodi ndi chiyani chingathandize aliyense wa ife kukhala womvera? Tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse “mtima womvera,” monga Mfumu Solomo. Iye anapempha mtima umenewo kuti athe ‘kuzindikira pakati pa zabwino ndi zoipa’ ndi cholinga choti athe kuweruza Aisiraeli anzake. (1 Mafumu 3:9) Ifenso tifunikira kukhala ndi “mtima womvera” kuti tizitha kuzindikira pakati pa zabwino ndi zoipa m’dziko lodzala ndi mzimu wa kusamverali. Mulungu watipatsa Mawu ake, mabuku ofotokoza Baibulo, misonkhano yachikhristu, ndi akulu achikondi mumpingo kuti tikhale ndi “mtima womvera.” Kodi tikugwiritsa ntchito bwino zinthu zothandiza zimenezi?
7. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amakonda kwambiri kumvera kuposa nsembe?
7 Kumbukiraninso kuti kale Yehova anauza anthu ake kuti kumvera ndi kofunika kuposa nsembe za nyama. (Miyambo 21:3, 27; Hoseya 6:6; Mateyo 12:7) N’chifukwa chiyani ananena zimenezo? Kodi si Yehova yemweyo amene analamula anthu ake kupereka nsembe zotero? Apa nkhani yagona pa cholinga cha munthu amene akupereka nsembeyo. Kodi cholinga chake ndi kukondweretsa Mulungu? Kapena kodi akungochita mwamwambo? Ngati munthu akufunadi kukondweretsa Mulungu, amayesetsa kumvera malamulo onse a Mulungu. Mulungu safuna nsembe za nyama, koma kumvera ndiko chinthu chamtengo wapatali chimene tingamuchitire.
Chitsanzo Chotichenjeza
8. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anakana kuti Sauli asapitirize kukhala mfumu?
8 Nkhani ya m’Baibulo yonena za Mfumu Sauli imasonyeza kuti kumvera ndi kofunika kwambiri. Poyamba, Sauli anali mfumu yodzichepetsa ndipo anadziyesa ‘wamng’ono m’maso mwake.’ Koma patapita nthawi, anayamba kunyada ndi kukhala ndi maganizo olakwika pazochita zake. (1 Samueli 10:21, 22; 15:17) Nthawi ina, Sauli akukamenyana ndi Afilisti, Samueli anamuuza kuti amudikire kuti iye adzapereke nsembe kwa Yehova ndiponso kuti adzapatse mfumuyo malangizo ena. Koma Samueli anachedwa kubwera ndipo anthu anayamba kubalalika. Ataona zimenezo, Sauli “anapereka nsembe yopserezayo.” Zimenezi Yehova sanakondwere nazo. Samueli atabwera, mfumu inapereka zifukwa pofuna kulungamitsa kusamvera kwake. Inafotokoza kuti ‘inadzifulumiza’ ndi kupereka nsembe yopsereza kupembedzera Yehova chifukwa chakuti Samueli anachedwa. Mfumu Sauli anaona kuti kupereka nsembeyo kunali kofunika kwambiri kuposa kumvera malangizo oti adikire Samueli kudzapereka nsembe. Samueli anamuuza kuti: “Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene iye anakulamulirani.” Mapeto ake, Sauli anataya ufumu wake chifukwa chosamvera Yehova.—1 Samueli 10:8; 13:5-13.
9. Kodi Sauli anasonyeza bwanji kuti anali ndi chizolowezi chosamvera Mulungu?
9 Kodi mfumuyo inatengerapo phunziro pa zimene zinachitikazo? Ayi ndithu. Nthawi ina, Yehova analamula Sauli kuwononga mtundu wa Amaleki, amene m’mbuyomo anaukira Isiraeli popanda chifukwa. Sauli sanafunikire kusunga ngakhale ziweto zawo. Anamvera ndithu chifukwa “anakantha Aamaleki, kuyambira pa Havila, [mpaka] dera la ku Suri.” Samueli atafika kudzakumana naye, mfumuyi inakondwera chifukwa chopambana nkhondo ndipo inati: “Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.” Koma mosemphana ndi malangizo omveka bwino amene analandira, Sauli ndi anthu ake anasunga Mfumu Agagi ndi “nkhosa zokometsetsa, ndi ng’ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse.” Mfumu Sauli inalungamitsa kusamvera kwake mwa kunena kuti: “Anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng’ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.”—1 Samueli 15:1-15.
10. Kodi Sauli analephera kuphunzira chiyani?
10 Samueli atamva zimenezo, anauza Sauli kuti: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.” (1 Samueli 15:22) Popeza kuti Yehova anali atalamula kuti nyamazo ziwonongedwe, sizikanakhalanso nsembe zovomerezeka.
Khalani Omvera M’zinthu Zonse
11, 12. (a) Kodi Yehova amaona bwanji tikamayesetsa kumukondweretsa pa kulambira kwathu? (b) Kodi munthu angadzinyenge bwanji ndi kumaona kuti akuchita chifuniro cha Mulungu koma kwenikweni ali wosamvera?
11 Yehova amakondwera kwambiri akaona atumiki ake okhulupirika akulimbikirabe ngakhale akuzunzidwa. Amakondweranso kuwaona akulalikirabe za Ufumu ngakhale kuti anthu ambiri alibe chidwi, komanso amakondwera kuwaona akusonkhanabe ngakhale kuti amavutika podzipezera zosowa zawo. Kumvera kwathu pankhani zofunika kwambiri zimenezi pamoyo wathu wauzimu kumakondweretsa mtima wake. Zonse zimene timachita polambira Yehova zimakhala zamtengo wapatali pamaso pake ngati timazichita ndi mtima wachikondi. Anthu angaiwale ntchito yaikulu imene tachita, koma Mulungu amaona nsembe zathu zochokera pansi pa mtima ndipo amazikumbukira.—Mateyo 6:4.
12 Komabe, kuti timukondweretse Mulungu mokwanira, tiyenera kukhala omvera m’zochita zathu zonse. Tisadzinyenge tokha ndi kuganiza kuti tingathe kunyalanyaza mfundo za Mulungu malinga ngati tikumulambira pa zinthu zina. Mwachitsanzo, munthu angadzinyenge yekha ndi kuganiza kuti malinga ngati akuchita zinthu zina zokhudza kulambira, ndiye kuti angachite chiwerewere kapena machimo ena akuluakulu popanda kulangidwa. Maganizo amenewa ndi olakwika.—Agalatiya 6:7, 8.
13. Kodi tingayesedwe bwanji pa kumvera Yehova tili kwatokha?
13 Ndi mfundo imeneyi, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikumvera Yehova pazochita zanga za tsiku ndi tsiku, ngakhale ngati ndikuganiza kuti ena sakundiona?’ Yesu anati: “Munthu wokhulupirika m’chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu, ndipo munthu wosalungama m’chaching’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Kodi ‘tikuyenda ndi mtima wangwiro,’ ngakhale ‘m’nyumba mwathu,’ m’mene anthu ena sakutiona? (Salmo 101:2) N’zoona kuti kukhulupirika kwathu kungayesedwe ngakhale pamene tili m’nyumba zathu. Osati kale kwambiri, anthu akafuna kuonera zithunzi zolaula, ankapita kumalo achisangalalo. Koma masiku ano kumayiko kumene anthu ambiri ali ndi makompyuta m’nyumba zawo, m’posavuta kuonera zithunzi zolaula chifukwa munthu amangotabwanya mabatani basi. Kodi ife tikumvera mawu a Yesu akuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake”? Inde, kodi timakana ngakhale kuyang’ana zithunzi zolaula? (Mateyo 5:28; Yobu 31:1, 9, 10; Salmo 119:37; Miyambo 6:24, 25; Aefeso 5:3-5) Nanga bwanji za mapulogalamu a pa TV achiwawa? Kodi tikugwirizana ndi Mulungu wathu, amene moyo wake ‘umada iye wakukonda chiwawa’? (Salmo 11:5) Nanganso bwanji za kumwa mowa mopitirira muyezo kwatokha? Baibulo limaletsa kuledzera, komanso limachenjeza Akhristu kuti asamamwe “vinyo wambiri.”—Tito 2:3; Luka 21:34, 35; 1 Timoteyo 3:3.
14. Kodi tingasonyeze bwanji kumvera Mulungu pankhani ya ndalama?
14 Mbali inanso imene tifunika kusamala nayo ndi nkhani ya ndalama. Mwachitsanzo, kodi timatsatira njira zokhudzana pang’ono ndi chinyengo pofuna kulemera mwachangu? Kodi timachita ukamberembere polipira msonkho? Kapena kodi timamvera ndi mtima wonse lamulo lakuti “perekani kwa onse zimene amafuna, kwa amene amafuna msonkho, perekani msonkho”?—Aroma 13:7.
Timamvera Mulungu Chifukwa Chomukonda
15. Kodi n’chifukwa chiyani inuyo mumamvera malamulo a Yehova?
15 Kumvera malamulo a Mulungu kuli ndi madalitso ake. Mwachitsanzo, popeza kuti sitisuta fodya, ndipo tili ndi makhalidwe abwino, komanso timaona magazi kukhala opatulika, timapewa matenda ambiri. Mwa kutsatira choonadi cha m’Baibulo, timapindulanso m’njira zina chifukwa timadziwa kugwiritsa ntchito bwino ndalama, timakhala bwino ndi anzathu, komanso timakhala ndi mabanja osangalala. (Yesaya 48:17) Tingatero kuti, madalitso amenewa amasonyeza kuti malamulo a Mulungu ndi othandiza. Ngakhale zili choncho, timamvera Yehova kwenikweni chifukwa chakuti timamukonda. Sititumikira Mulungu ndi cholinga choti tipeze phindu. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Mulungu anatipatsa ufulu wosankha amene tikufuna kumumvera. Ife timamvera Yehova chifukwa chakuti timafuna kumukondweretsa ndiponso kuchita zabwino.—Aroma 6:16, 17; 1 Yohane 5:3.
16, 17. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anamvera Mulungu chifukwa chomukonda ndi mtima wonse? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?
16 Yesu anapereka chitsanzo changwiro chomvera Yehova chifukwa chomukonda ndi mtima wonse. (Yohane 8:28, 29) Ali pa dziko lapansi, Yesu “anaphunzira kumvera mwa mavuto amene anakumana nawo.” (Aheberi 5:8, 9) Motani? Yesu “anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa, inde, imfa ya pamtengo wozunzikirapo.” (Afilipi 2:7, 8) Yesu anali womvera ali kumwamba. Koma kumvera kwake kunayesedwa kwambiri padziko lapansi. Tikutsimikiza kuti Yesu ndi woyenerera kwambiri kukhala Mkulu wa Ansembe wa abale ake auzimu komanso anthu ena onse okhulupirira iye.—Aheberi 4:15; 1 Yohane 2:1, 2.
17 Nanga bwanji ifeyo? Kuti titsanzire Yesu, kumvera chifuniro cha Mulungu kuyenera kukhala patsogolo. (1 Petulo 2:21) Timasangalala ngati, chifukwa chokonda Yehova, timamvera malamulo ake ngakhale panthawi imene tili m’mavuto kapena tikuyesedwa. (Aroma 7:18-20) Zimenezi zikuphatikizapo kukhala ndi mtima womvera malangizo operekedwa ndi anthu amene akutsogolera pa kulambira koona, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. (Aheberi 13:17) Kumvera kwathu malamulo a Mulungu tili kwatokha, ndi kwamtengo wapatali pamaso pa Yehova.
18, 19. Kodi chimachitika ndi chiyani tikamamvera Mulungu ndi mtima wonse?
18 Masiku ano, kumvera kwathu Yehova kungafune kuti tipirire chizunzo ndi kukhalabe okhulupirika. (Machitidwe 5:29) Ndiponso, kumvera kwathu lamulo la Yehova lakuti tilalikire ndi kuphunzitsa ena kumafuna kupirira mpaka mapeto a dongosolo la zinthuli. (Mateyo 24:13, 14; 28:19, 20) Timafunikanso kupirira kuti tizisonkhana ndi abale athu, ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto m’dzikoli. Mulungu wathu wachikondi akudziwa kuti tikuyesetsa kukhala omvera pazinthu zimenezi. Komabe, kuti kumvera kwathu kukhale kwachikwanekwane, tifunika kulimbana ndi thupi lathu lochimwa ndi kupewa zoipa n’kumakonda zinthu zabwino.—Aroma 12:9.
19 Tikamatumikira Yehova chifukwa chomukonda ndiponso chifukwa chokhala ndi mtima woyamikira, iye “amakhala [kwa ife] wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Ndi zoona kuti nsembe zabwino n’zofunika, koma Yehova amakondwera kwambiri ngati tikumumvera m’zonse chifukwa chomukonda.—Miyambo 3:1, 2.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chifukwa chiyani tikunena kuti pali chimene tingamuchitire Yehova?
• Kodi Sauli analakwitsa zinthu zotani?
• Kodi mungasonyeze bwanji kuti inuyo mukukhulupirira kuti kumvera kumaposa nsembe?
• N’chifukwa chiyani inuyo mumamvera Yehova?
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi dokotala wabwino angamve bwanji ngati wodwala akudya zakudya zimene anamuletsa?
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakwiya ndi Mfumu Sauli?
[Zithunzi patsamba 30]
Kodi mumamvera malamulo a Mulungu mukakhala nokha m’nyumba mwanu?