Kodi Mukudziwa?
N’chifukwa chiyani Ayuda m’nthawi ya Yesu anali omwazikana?
Yesu atauza anthu amene ankamumvetsera kuti kumene iye anali kupita iwo sakanatha kupitako, Ayudawo anafunsana kuti: “Ameneyu akufuna kupita kuti . . . ? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda omwazikana mwa Agiriki?” (Yohane 7:32-36) Pasanapite nthawi, amishonale achikhristu analalikira uthenga wabwino kwa Ayuda amene anali m’malo osiyanasiyana m’dera lonse lochita malire ndi nyanja ya Mediterranean.—Machitidwe 2:5-11; 9:2; 13:5, 13, 14; 14:1; 16:1-3; 17:1; 18:12, 19; 28:16, 17.
Ayuda anamwazikana chifukwa chakuti mitundu ina inawagonjetsa ndi kuwatengera kuukapolo. Oyamba kuwagonjetsa anali Asuri, mu 740 B.C.E., ndipo kenako Ababulo, mu 607 B.C.E. Ndipo ndi Ayuda ochepa okha amene anabwerera ku Isiraeli koma ena onse anakakhala m’madera osiyanasiyana.—Yesaya 10:21, 22.
Pachifukwa chimenechi, m’zaka za m’ma 400 B.C.E., Ayuda ankapezeka m’zigawo 127 za ufumu wa Perisiya. (Estere 1:1; 3:8) Ayudawa anali akhama potembenuza anthu kuti ayambe Chiyuda. Zimenezi zinachititsa kuti pamapeto pake anthu ambiri adziweko za Yehova ndi Chilamulo chimene iye anawapatsa. (Mateyo 23:15) Ayuda ochokera m’madera osiyanasiyana anafika ku Yerusalemu mu 33 C.E., ku Chikondwerero cha Pentekosite. Ndipo kumeneko anamva uthenga wabwino wonena za Yesu. Choncho, kupezeka kwa Ayuda mu ufumu wonse wa Roma kunathandiza kuti Chikhristu chifalikire mofulumira.
Kodi Mfumu Solomo inali ndi golide wochuluka bwanji?
Malemba amanena kuti Hiramu mfumu ya ku Turo, inatumiza matani anayi a golide kwa Solomo ndipo mfumukazi ya ku Seba inaperekanso matani anayi a golide. Komanso zombo za Solomo zinkabweretsa matani oposa 14 a golide kuchokera ku Ofiri. Baibulo limati: “Kulemera kwake kwa golidi anafika kwa Solomo chaka chimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi.” Amenewa ndi matani oposa 22. (1 Mafumu 9:14, 28; 10:10, 14) Kodi zimenezi ndi zoona? Kodi panthawi imeneyo nkhokwe za golide za mafumu zinali zazikulu bwanji?
Zolemba zakale, zimene akatswiri amati ndi zodalirika, zimanena kuti Farao Thutmose III wa ku Iguputo (yemwe anakhalako zaka pafupifupi 3,500 zapitazo) anapereka matani pafupifupi 12 a golide ku kachisi wa Amun-Ra ku Karnak. Cha m’ma 700 B.C.E., mfumu ya Asuri Tigilati Pilesere III, inalandira matani anayi a golide kuchokera ku Turo ngati msonkho, ndipo Sarigoni II anaperekanso matani anayi ngati mphatso kwa milungu ya ku Babulo. Mfumu Filipo II ya ku Makedoniya (359-336 B.C.E.) akuti inkakumba matani oposa 25 a golide chaka chilichonse m’migodi ya Pangaeum ku Thrace.
Mwana wa Filipo, Alesandro Wamkulu (336-323 B.C.E.) atalanda mzinda wa ku Perisiya wotchedwa Susa, akuti anatenga matani pafupifupi 1,070 a golide. Iye anatenganso matani oposa 6,000 kuchokera ku Perisiya konse. Choncho, tikayerekezera ndi zitsanzo zimenezi, zimene Baibulo limanena zokhudza golide wa Mfumu Solomo si kukokomeza.