Pamene Ambiri Akhala Ooloŵa Manja
TINENE kuti mukufuna kupereka mphatso kwa mfumu, kodi mungaipatse chiyani? Bwanji ngati mfumuyo ndiyo wolamulira wolemera koposa komanso wanzeru koposa padziko lonse? Kodi mungalingalire za mphatso iliyonse imene ingam’sangalatse? Zaka ngati zikwi zitatu zapitazo, mfumu yaikazi ya ku Seba inaganizirapo mafunso amenewo pokonzekera kukachezera wolamulira woteroyo—Mfumu Solomo ya Israyeli.
Mphatso yake, Baibulo limatiuza motero, inaphatikizapo matalenti 120 a golidi “ndi zonunkhira zaunyinji, ndi timiyala ta mtengo wapatali.” Pamitengo yalero, golidi yekhayo anali ngati $40,000,000. Zonunkhirazo, mafuta onunkhira bwino amenenso ndi mankhwala, anali kuŵerengeredwa kukhala chinthu cha mtengo wapatali pamodzi ndi golidi. Pamene kuli kwakuti Baibulo silinena kuchuluka kwa mafuta amene mfumu yaikazi ya ku Seba inapatsa Solomo, ilo limatiuzabe kuti panalibenso mphatso ina yoposa yakeyo.—1 Mafumu 10:10.
Mosakayikira, mfumu yaikazi ya ku Seba inali mkazi wachuma ndi wooloŵa manja. Komanso, kuoloŵa manja kwake kunam’pindulitsa. Baibulo limati: ‘Mfumu Solomo anam’patsa mfumu yaikazi ya ku Seba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osaŵerengera zija adabwera nazo kwa mfumu.’ (2 Mbiri 9:12) Zoonadi, mwina unali mwambo wa mafumu kusinthana mphatso; komabe, Baibulo limatchula mwachindunji za “ufulu” wa Solomo. (1 Mafumu 10:13) Solomo iyemwini analemba kuti: “Mtima wamataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”—Miyambo 11:25.
Inde, mfumu yaikazi ya ku Seba inatheranso nthaŵi yaitali ndipo inayesetsa kwambiri kuti ikachezere Solomo. Mwachionekere, Seba anali m’dera la dziko lamakono la Republic of Yemen; chotero mfumuyo ndi ngamila zake zambiri anayenda ulendo wa makilomita 1,600 kupita ku Yerusalemu. Monga momwe Yesu ananenera, “anadza kuchokera ku malekezero a dziko.” Kodi mfumu yaikazi ya ku Seba inadzivutiranji choncho? Inangobwera “kudzamva nzeru za Solomo.”—Luka 11:31.
Mafumu Woyamba 10:1, 2 amanena kuti mfumu yaikazi ya ku Seba “[i]nadza kumuyesera [Solomo] ndi miyambi yododometsa. . . . [Mfumu yaikaziyo i]nakamba naye zonse za m’mtima mwake.” Kodi Solomo anatani? “Ndipo Solomo anam’yankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanam’fotokozera iye.”—1 Mafumu 10:3.
Pozizwa ndi zimene anamva ndi kuona, mfumu yaikaziyo inayankha kuti: “Odala anyamata anu akukhala nthaŵi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.” (1 Mafumu 10:4-8) Sananene kuti anyamata a Solomo anali odala chifukwa chakuti anazingidwa ndi chuma chamwanaalirenji—ngakhale kuti zinalidi motero. M’malo mwake, anyamata a Solomo anali odala chifukwa chakuti nthaŵi zonse anali kumvetsera nzeru za Solomo zopatsidwa ndi Mulungu. Mfumu yaikazi ya ku Seba ili chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu a Yehova lerolino, awo amene azingidwa ndi nzeru ya Mlengi iyemwini ndi ya Mwana wake, Yesu Kristu!
Mawu otsatira a mfumuyo kwa Solomo ndi ochititsanso chidwi: “Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu.” (1 Mafumu 10:9) Iye anaonadi dzanja la Yehova m’nzeru ya Solomo ndi chuma. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Israyeli poyamba. ‘Kusunga maweruzo anga,’ iye anatero, “ndi nzeru zanu ndi chidziŵitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.”—Deuteronomo 4:5-7.
Ponena za Wopereka Nzeru
M’nthaŵi zamakonozi, anthunso mamiliyoni ambiri akopeka ndi gulu la Yehova chifukwa aona kuti “Israyeli wa Mulungu” ndi “anthu anzeru ndi akuzindikira,” osati mwachibadwa, koma chifukwa chakuti akutsogozedwa ndi malamulo ndi mapulinsipulo angwiro a Mulungu. (Agalatiya 6:16) Ziŵerengero za amene akubatizidwa m’zaka zino zikusonyeza kuti chaka chilichonse ophunzira atsopano zikwi mazanamazana anena, kwa Israyeli wauzimu, kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Si mmenetu atsopano ameneŵa amadabwira poona phwando la chakudya chauzimu chimene Yehova wakonzera atumiki ake! Sanaonepo phwando ngati limeneli m’zipembedzo zawo zakale.—Yesaya 25:6.
Kupereka kwa Wopatsa Wamkulu
Pokhala alandira zambiri chonchi, mwachibadwa anthu oyamikira amasinkhasinkha zimene iwo tsopano angapereke kwa Mfumu ndi Wopatsa wamkulu koposa, Yehova Mulungu. Baibulo limatiuza kuti mphatso yabwino koposa imene tingapatse Yehova ndiyo “nsembe yakuyamika.” (Ahebri 13:15) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti nsembe imeneyi imakhudza mwachindunji kupulumutsa moyo, nkhani yofunika kwambiri kwa Yehova m’nthaŵi ino yachimaliziro. (Ezekieli 18:23) Kuwonjezera apo, kupatsa nyonga yako pothandiza odwala, opsinjika maganizo, ndi ena ili nsembe yolandirika.—1 Atesalonika 5:14; Ahebri 13:16; Yakobo 1:27.
Zopereka za ndalama zimathandiza kwambiri. Zimatheketsa kupangidwa kwa mabaibulo, zofalitsa zofotokoza Baibulo, ndi kupeza malo amene Akristu angamasonkhanirepo. (Ahebri 10:24, 25) Zopereka zimathandiziranso pathumba la chithandizo choperekedwa kwa amene akuvutika chifukwa cha nkhondo ndi masoka achilengedwe.
Mawu a Mulungu amapereka mapulinsipulo ena abwino otipatsa chitsogozo pankhani yopatsayi. Mwachitsanzo, amaphunzitsa kuti Akristu amapatsa, osati ndalama yaunyinji winawake woikika, koma imene angathe kupatsa, kuchita zimenezo modzifunira, ndi mtima wokondwera. (2 Akorinto 9:7) Ena angapereke zambiri; ena, monga mkazi wamasiye waumphaŵi wa m’nthaŵi ya Yesu, angathe kungoperekapo zochepa. (Luka 21:2-4) Kodi sizochititsa chidwi kuti Yehova, Mwiniwake chilengedwe chonse, amayamikira mphatso ndi nsembe iliyonse yoperekedwa m’dzina lake ndi zolinga zabwino?—Ahebri 6:10.
Kuti azipereka mokondwera, anthu a Yehova amadziŵitsidwa za zinthu zosiyanasiyana zimene zikufunika ndi njira zabwino zedi zokhutiritsira zofunika zimenezo. Kenako, mzimu woyera wa Yehova umasonkhezera mitima yofuna kuti ichitepo kanthu. M’Israyeli wakale anatsatira njira imeneyi pomanga chihema chokumanako ndiyeno pambuyo pake kachisi. (Eksodo 25:2; 35:5, 21, 29; 36:5-7; 39:32; 1 Mbiri 29:1-19) M’zaka za zana loyamba C.E., njira imodzimodziyo inatheketsa Akristu kukhala ndi zofunikira kuti atengere uthenga wabwino wa Ufumu kwa mitundu ndi kuti achirikize abale m’Israyeli pamene kunali njala.—1 Akorinto 16:2-4; 2 Akorinto 8:4, 15; Akolose 1:23.
Mofananamo, Yehova wadalitsa anthu ake lerolino ndipo adzapitirizabe kuwadalitsa, mwa kuwapatsa zomwe akufuna kuti amalize ntchito yaikulu koposa yolalikira ndi kuphunzitsa yomwe sinachitikepo ndi kalelonse padziko lapansi.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Kodi Pakufunika Zotani Lerolino?
M’zaka zaposachedwapa Mboni za Yehova zaloledwa m’mayiko ambiri kumene kale ntchito yawo inali yoletsedwa. Chotero, chiŵerengero cha ofalitsa m’mayiko ambiri mwa mayikoŵa chawonjezeka kwambiri. Pachifukwa chimenecho, mabaibulo ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo zambiri zikufunika zedi.
Momwemonso Nyumba za Ufumu. Nyumba za Ufumu 9,000 zinanso zikufunika panopo kuzungulira dziko lonse lapansi. Titati tizimanga Nyumba ya Ufumu imodzi tsiku lililonse, zingatenge zaka zoposa 24 kuti kusoŵaku kukhutiritsidwe! Izi zili choncho, mipingo yatsopano ngati isanu ndi iŵiri imapangidwa tsiku lililonse, yambiri ya iyo m’madera a dziko kumene ndalama n’zosoŵa kwambiri. Komabe, ambiri mwa malo ameneŵa safunikira nyumba zamtengo wapatali. M’malo ena, Nyumba ya Ufumu yokhutiritsa kusoŵaku ndi kuperekanso umboni wabwino kwa anthu a kumaloko ingamangidwe ndi ndalama zokwana $6,000 zokha.
M’zaka za zana loyamba, Akristu ena anali ndi chuma kuposa ena, chotero mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusoŵa kwawo nthaŵi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwawo kukwanire kusoŵa kwanu.” (2 Akorinto 8:14) Lerolino, ‘kulinganiza’ koteroko ndiko kupereka ndalama zofunika kupangira mabaibulo, zofalitsa zofotokoza Baibulo, Nyumba za Ufumu, chithandizo kwa ogwidwa n’tsoka, ndi zinthu zina m’mbali zambiri za dziko. Kupatsa kumeneku ndi dalitso lalikulu zedi kwa woperekayo ndi wolandira yemwe!—Machitidwe 20:35.
Monga momwe makalata amene Sosaite imalandira kuchokera kwa anthu a mtima wopatsa asonyezera, ambiri oŵerenga magaziniyi amafuna kuthandiza koma sakudziŵa njira zosiyanasiyana zimene angachitire zopereka zawo. Ndithudi bokosi lomwe lili m’nkhani ino lidzathandiza kuyankha mafunso awo.
Mu ulamuliro waulemerero wa Solomo, “mafumu onse a padziko lapansi” amene anamva za iye anadzam’chezera. Komabe, Baibulo limangotchulapo wolamulira mmodzi yekha—mfumu yaikazi ya ku Seba. (2 Mbiri 9:23) Anapangatu kuyesetsa kwakukulu kwabasi! Koma analandira mphotho yaikulu—yaikulu zedi moti pamapeto pa kucheza kwake, ‘analibe mawu ndipo anali wodabwa.’—2 Mbiri 9:4, Today’s English Version.
M’tsogolomu, Yehova, Mfumu ndi Wopatsa wamkulu koposa, adzachita zambiri kwa awo amene amapereka nsembe kwa iye kuposa zimene Solomo anachita. Motero iwonso adzangoimirira ‘opanda mawu ndi odabwa,’ chifukwa Yehova sadzawasunga amoyo chabe patsiku lake loopsa lachiweruzolo komanso pambuyo pake ‘adzaoloŵetsanso dzanja lake ndi kukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 145:16.
[Bokosi patsamba 22]
Njira Zimene Ena Amasankha Popereka
ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE
AMBIRI amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku likulu la dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yakwawo.
Ndalama zoperekedwa modzifunira zingatumizidwenso mwachindunji ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso yeniyeni iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
CHOPEREKA CHAMAKONZEDWE APADERA
Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society pamakonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso chifukwa cha kusoŵa kwinakwake, zoperekazo zidzabwezeredwa kwa iye. Kuti mudziŵe zambiri, chonde lemberani ku Accounting Office paadiresi yosonyezedwa m’munsimu.
KUPATSA KOLINGANIZA
Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi ndalama zoperekedwa pamakonzedwe apadera, palinso zopereka zina zopindulitsa utumiki wa Ufumu wapadziko lonse. Zimenezi zikuphatikizapo:
Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni.
Maakaunti a ku Banki: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikizidwe kapena mwiniwake atamwalira angalipiridwe ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanuko.
Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’malonda ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena pamakonzedwe akuti woperekayo azipitirizabe kulandira malipiro.
Malo: Malo okhoza kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo mwiniwake, amene angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Munthuyo ayenera kulankhula ndi Sosaite asanailoŵetse m’pangano la malo alionse.
Chuma cha Masiye ndi Choikizira: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwalamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzalandira mapindu a pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma chopindulitsa gulu lachipembedzo lingakhale ndi mapindu ena a kuchepetsa msonkho.
Monga mwa tanthauzo la mawuwo “kupatsa kolinganiza,” zopereka zoterezi zimafunadi kuti woperekayo alinganize bwino. Accounting Office iyenera kudziŵitsidwa ndi kulandira makope a zikalata zilizonse zofunika za makonzedwe alionse ameneŵa. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri ponena za alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza kumeneku, lankhulani ndi Accounting Office, kaya mwa kuwalembera kalata kapena pafoni, paadiresi yosonyezedwa pansipa kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu.
ACCOUNTING OFFICE
Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
P.O. Box 30749, Lilongwe 3
Telefoni: 782392
[Zithunzi patsamba 23]
Ntchito za Mboni za Yehova zimachirikizidwa ndi zopereka zodzifunira