Kupatsa—Magwero a Chimwemwe
Ndi mtola nkhani wa Galamukani! ku Jeremani
KODI ndani amene samakonda kulandira mphatso yabwino? Nkosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti munthu wina amasamala! Komabe, chokondweretsa mofananamo ndicho chimwemwe cha kupatsa. Kwenikweni, malinga ndi kunena kwa Yesu, woyambitsa Chikristu, “muli chimwemwe chachikulu m’kupatsa koposa chimene chiri m’kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
Baibulo limasimba nkhani zambiri za kupatsa, nthaŵi zina kupatsadi zochuluka. Pamene mfumukazi ya ku Seba inadziwonera yokha nzeru ya Mfumu Solomo, ‘inaninkha mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi aŵiri, ndi zonunkhira zaunyinji, ndi timiyala ta mtengo wapatali.’ (1 Mafumu 10:10) Golidi yekha angakhale wa ndalama zoposa madola mamiliyoni 46 pamtengo wamakono! Ndipo nthaŵi ina Farao wa Igupto anapatsa mmodzi wa ana ake aakazi mphatso ya mzinda wonse!—1 Mafumu 9:16.
Koma mphatso siziyenera kukhala zopambanitsa kuti zikhale magwero a chimwemwe. Mungakumbukire Msamariya wachifundo m’fanizo la Yesu, amene mwachibadwa anathandiza munthu mnzake wofuna thandizo. (Luka 10:30-37) Kapena mpingo Wachikristu m’Korinto umene unatumizira abale awo osoŵa ku Yerusalemu ‘mphatso yachifundo.’—1 Akorinto 16:3.
Komabe, mwinamwake chitsanzo chodziŵika bwino koposa cha kupatsa chotchulidwa m’Baibulo ndicho cha openda nyenyezi—odziŵika kwambiri monga anzeru—amene anapereka mphatso kwa Yesu mwanayo. Anthu ambiri amazika mwambo wawo wa kupereka mphatso panthaŵi ya Krisimasi pachochitikachi.—Mateyu 2:2-11.
Bwanji za Kupatsa kwa pa Krisimasi?
Kunena zowona, ambiri mowona mtima amakonda kuloŵetsedwa m’chimene amatcha mzimu wa Krisimasi—mzimu wa kupatsa. Ena a iwo amalinganiza zinthu pasadakhale, akumakondwera ndi kufunafuna mphatso zazikulu ndi makadi amauthenga oyenerera. Komabe, omalizirawa anayamba kukhalako m’ma 1840 ku Mangalande, ngakhale kuti pali mkangano ponena za amene kwenikweni anawayambitsa. Kaya ikhale mphatso kapena khadi, ambiri amapeza chimwemwe chenicheni kutulukira kanthu kapadera ka munthu wina wapadera.
Kumbali ina, sitingakane kuti opatsa ambiri a pa Krisimasi saali m’gulu limeneli. Mwini sitolo Wachijeremani anati ponena za ogula zinthu pa Krisimasi: “Pamene tiyandikira kwambiri Tsiku Lotsatiridwa ndi Krisimasi, anthu amapanikizikanso kwambiri. Pomalizira, amangogula kalikonse kamene angapeze.”
Kukankhana m’masitolo aakulu odzala ndi anthu pokafunafuna mphatso zoyenerera kodya nthaŵi kumachititsa ogula zinthu ena kudandaula ndi chipsinjo, piringupiringuyo, ndi chitsenderezo. Malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ina ya ku Austria, kasitomala wachitatu aliyense amadandaula ndi “namtindi wa anthu,” akumanena kuti adzapeza mpumulo “ngati piringupiringuyo watha.” Ndipo achichepere Achijeremani, atafunsidwa zimene amaganiza ponena za Krisimasi, anayankha motere, “Imandikwiitsa,” “Sumadziŵa zimene ungapereke,” ndipo, “Iri youma mtengo kwambiri.”
Mwachiwonekere sialiyense amene akupeza “chimwemwe chachikulu m’kupatsa” kumene Yesu ananena. Mosakaikira zimenezi ziri kwakukulukulu chifukwa chakuti Krisimasi yaloŵetsedwa m’malonda kotheratu, yakhala yokwiitsa kwambiri kwa anthu ochuluka. Malinga ndi The World Book Encyclopedia, “okwanira chigawo chimodzi mwa zinayi a malonda apachaka amakhalako panthaŵi ya Krisimasi.” Mwachiwonekere nyimbo ya “Jingle Bells” imene amalonda amakonda kumvetsera kwambiri imaimbidwa ndi mabelu olira ngwinjingwinji a makina ogulitsira.
Mwachiwonekere, kupatsa kwa pa Krisimasi kaŵirikaŵiri kumalephera kupereka chimwemwe chimene kupatsa kuyenera kudzetsa. “Ndimaiwopa Krisimasi,” anavomereza motero mkazi Wachikatolika.
Nchifukwa chake kuyenerera kwa kupatsa kwa pa Krisimasi kukukaikiridwa. Kodi kulidi kwanzeru?