-
Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha ChikhulupiriroNsanja ya Olonda—2014 | February 15
-
-
Mfumu Ahabu ya Isiraeli inali yoipa kwambiri ndipo Yehova anasankha zoti abweretse chilala m’dziko lake kwa zaka zingapo. Eliya atangonena za chilalacho, Mulungu anamubisa kuti Ahabu asamupeze ndipo anagwiritsa ntchito akhwangwala kuti azimubweretsera mkate ndi nyama. Kenako Yehova anauza Eliya kuti: “Nyamuka, upite ku Zarefati m’dziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wina wa kumeneko, mkazi wamasiye, kuti azikakupatsa chakudya.”—1 Maf. 17:1-9.
-
-
Mkazi Wamasiye wa ku Zarefati Anadalitsidwa Chifukwa cha ChikhulupiriroNsanja ya Olonda—2014 | February 15
-
-
Mkazi wamasiyeyu ankadziwa kuti Eliya anali Mwisiraeli woopa Mulungu. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha mawu ake akuti “pali Yehova Mulungu wanu wamoyo.” Zikuoneka kuti ankadziwa ndithu za Mulungu wa Aisiraeli koma anali asanafike pomuona kuti ndi Mulungu wake. Mayiyu ankakhala kutauni ya Zarefati yomwe inali pafupi ndi mzinda wa Sidoni m’chigawo cha Foinike ndipo zikuoneka kuti zinthu zambiri kutauniyi zinkachokera ku Sidoniko. N’zosakayikitsa kuti ku Zarefati kunkakhala anthu olambira Baala. Koma Yehova ayenera kuti anaona mayiyu kukhala wosiyana kwambiri ndi athu a m’deralo.
Ngakhale kuti mayi wamasiyeyu ankakhala ndi anthu olambira mafano, iye anasonyeza chikhulupiriro. Yehova anauza Eliya kuti apite kwa mayiyu n’cholinga choti onse awiriwo athandizike. Apansotu tikhoza kuphunzirapo mfundo ina yofunika.
Sikuti anthu onse a m’tauni ya Zarefati anali oipa. Potumiza Eliya kwa mkazi wamasiyeyu, Yehova anasonyeza kuti amathandiza anthu oona mtima amene sanayambe kumutumikira. Choncho m’pomveka kunena kuti “[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Mac. 10:35.
-