Mutu 4
Kodi “Chipangano Chakale” Nchokhulupirika Motani?
M’mitu yoŵerengeka yotsatirapo, tidzafotokoza zina za zitsutso zonenedwa motsutsana ndi Baibulo ndi otsutsa amakono. Ena amatsutsa kuti Baibulo limadzitsutsa ndipo liri “losakhala lausayansi,” ndipo zisulizo zimenezi zidzafotokozedwa m’mitu yamtsogolomu. Koma choyamba, lingalirani chitsutso chonenedwa kaŵirikaŵiri chakuti Baibulo sirili losiyana ndi nthanthi zosonkhanitsidwa pamodzi ndi nthano zongopeka. Kodi otsutsa Abaibulowo ali ndi maziko olimba kaamba ka chisulizo chimenecho? Poyamba, tiyeni tiyambe tayang’ana pa Malemba Achihebri, otchedwa chotero Chipangano Chakale.
1, 2. Kodi kuzingidwa kwa Yeriko kunali kotani, ndipo kodi ndimafunso otani amene amadzutsidwa mogwirizana nako?
MZINDA wamakedzana uli wozingidwa. Owuukira ake adza muunyinji wawo kuwoloka Mtsinje wa Yordano ndipo tsopano amanga misasa kunja kwa malinga ake aataliwo. Koma ha ndi maluso omenyera nkhondo achilendo chotani nanga! Tsiku lirilonse kwa masiku asanu ndi limodzi, gulu lankhondo loukiralo laguba mozungulira mzinda, mwakachetechete kusiyapo gulu la ansembe limene likuliza mphalasa. Tsopano, patsiku lachisanu ndi chiŵiri, gulu lankhondolo mwakachetechete likuguba kuzungulira mzindawo kasanu ndi kaŵiri. Mwadzidzidzi, ansembe akuomba mphalasa zawo ndi mphamvu zawo zonse. Gulu lankhondolo likuleka kukhala kwake cheteko mwa kufuula kwamphamvu kwa nkhondo, ndipo mzinda wokhala ndi malinga aataliwo ukugwa m’fumbi laphwititi ngati mtambo, kukumasiya mzindawo wopanda chitetezo.—Yoswa 6:1-21.
2 Umutu ndimo mmene bukhu la Yoswa, bukhu lachisanu ndi chimodzi la Malemba Achihebri, likufotokozera kugwa kwa Yeriko kumene kunachitika pafupifupi zaka 3 500 zapitazo. Koma kodi zinachitikadi? Ambiri a osuliza kwambiri akayankha mwachidaliro kuti ayi.a Iwo amanena kuti bukhu la Yoswa, limodzi ndi mabukhu oyambirira asanu a Baibulo, ngopangidwa ndi nthano zongopeka zolembedwa zaka mazana ambiri zapitazo pambuyo pa kuchitika kwa zochitika zonenedwazo. Ofukula za m’mabwinja ambiri nawonso akayankha kuti ayi. Malinga ndi kunena kwawo, pamene Aisrayeli analoŵa m’dziko la Kanani, Yeriko angakhale kunalibeko.
3. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kufotokoza kuti kaya Baibulo liri ndi mbiri yowona kapena ayi?
3 Zimenezi ziri zinenezo zowopsa. Pamene muŵerenga m’Baibulo lonse, mudzawona kuti ziphunzitso zake ziri zogwirizanitsidwa thithithi kwambiri ndi mbiri. Mulungu akuchita ndi amuna enieni, akazi, mabanja, ndi mitundu, ndipo malamulo ake akuperekedwa kwa anthu enieni a m’mbiri. Akatswiri amakono amene amakaikira kukhala kwa m’mbiri kwa Baibulo amakaikiranso kufunika ndi kudalirika kwa uthenga wake. Ngati Baibulo liridi Mawu a Mulungu, pamenepo mbiri yake iyenera kukhala yodalirika ndi kusakhala ndi miyambi chabe yongopeka ndi nthano. Kodi olemba ameneŵa ali ndi maziko okaikirira kukhala kwake lowona kwa m’mbiri?
Chisulizo Chapamwamba—Kodi Nchodalirika Motani?
4-6. Kodi ndiziti zimene ziri zina za nthanthi za Wellhausen za chisulizo chapamwamba?
4 Chisulizo chapamwamba cha Baibulo chidayambika mwaphamphu mkati mwa zaka za zana la 18 ndi 19. M’theka lotsirizira la zaka za zana la 19, wosuliza Baibulo Wachijeremani Julius Wellhausen anachititsa nthanthi yakuti mabukhu oyambirira asanu ndi limodzi a Baibulo, kuphatikizapo Yoswa, analembedwa m’zaka za zana lachisanu B.C.E. kukhala yofala—pafupifupi zaka chikwi pambuyo pa zochitika zofotokozedwazo. Komabe, iye anati, iwo ali ndi mfundo zimene zinalembedwa poyambirirapo.1 Nthanthi imeneyi inasindikizidwa m’kope la 11 la Encyclopædia Britannica, lofalitsidwa mu 1911, limene linafotokoza kuti: “Genesis liri bukhu lolembedwa pambuyo pa kuthaŵa la magwero aunsembe a pambuyo pa kuthaŵa (P) ndi magwero achikale osakhala aunsembe amene amasiyana mwapadera ndi P m’chinenero, kalembedwe ndi lingaliro la chipembedzo.”
5 Wellhausen ndi otsatira ake analingalira mbiri yonse yolembedwa m’mbali yoyambirira ya Malemba Achihebri kukhala “osati mbiri yeniyeni, koma miyambo yofala yakalekale.”2 Zolembedwa zoyambirira zinalingaliridwa kukhala chisonyezero chabe cha mbiri yamtsogolo ya Israyeli. Mwachitsanzo, udani pakati pa Yakobo ndi Esau suunachitike kwenikweni, koma unasonyeza udani pakati pa mitundu ya Israyeli ndi Edomu m’nthaŵi zamtsogolo.
6 Mogwirizana ndi zimenezi, osuliza ameneŵa analingalira kuti Mose sanalandire konse lamulo lirilonse la kupanga likasa lachipangano ndi kuti chihema, phata la kulambira kwa Israyeli m’chipululu, sizinakhaleko. Iwo amakhulupiriranso kuti udindo wa ansembe a Aroni unakhazikitsidwa mokwanira kokha pambuyo pa zaka zoŵerengeka chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Ababulo chisanachitike, chimene osulizawo amakhlupirira kuti chinachitika kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E.3
7, 8. Kodi ndi “maumboni” otani amene Wellhausen anali nawo kaamba ka nthanthi zake, ndipo kodi iwo anali olama?
7 Kodi ndi“umboni” wotani umene iwo anali nawo wokhalira ndi malingaliro ameneŵa? Zisulizo zapamwamba zimanena kuti zikhoza kugaŵanitsa cholembedwa cha mabukhu oyambirira a Baibulo kukhala zolembedwa zosiyanasiyana zingapo. Njira yaikulu yochitira zinthu imene iwo amagwiritsira ntchito ndiyo kulingalira kuti, kungonena mwachisawawa, vesi lirilonse la Baibulo lomagwiritsira ntchito liwu Lachihebri la Mulungu (’Elo·himʹ) mwa ilo lokha linalembedwe ndi wolemba mmodzi, pamene vesi lirilonse lomatchula Mulungu ndi dzina lake, Yehova, lingakhale litalembedwa ndi winawake—monga ngati kuti wolemba mmodzi sakanatha kugwiritsira ntchito maina aŵiri onsewo.4
8 Mofananamo, nthaŵi iriyonse imene chochitika chikulembedwa koposa kamodzi m’bukhu, chimalingaliridwa kukhala umboni wa wolemba woposa mmodzi wabukhulo, ngakhale kuli kwakuti m’zolembedwa zachikale Zachisemu ziri ndi zitsanzo zina zofanana za kubwereza. Ndiponso, kumalingaliridwa kuti kusintha kulikonse kwa kalembedwe kumatanthauza kusintha kwa wolemba. Komabe, ngakhale olemba a zinenero zamakono kaŵirikaŵiri amalemba m’njira yosiyana panthaŵi zosiyansiyana m’ntchito yawo, kapena pamene iwo akusamalira nkhani yokambitsiridwa yosiyana.b
9-11. Kodi ndiziti zimene ziri zina za zofooka za osuliza apamwamba amakono?
9 Kodi pali umboni uliwonse weniweni wanthanthi zimenezi? Kutalitali. Wothirira ndemanga wina anati: “Kusuliza, ngakhale kwabwino kopambana, nkongoyerekezera ndi kongoyesa, kanthu kena kamene nthaŵi zonse kooti nkusinthidwa kapena kutsimikiziridwa kukhala kolakwa ndi kofunikira kuloŵedwa mmalo ndi kanthu kenanso. Ndiko kachitidwe ka anthu anzeru, kooti nkukhala ndi zikaikiro ndi zoyerekezera zonse zimene ziri zosalekanitsika ndi kachitidwe koteroko.”5 Kusulizidwa kwapamwamba kopambana kwa Baibulo, makamaka, “nkongoyerekezera ndi kongoyesa” kwakukulukulu.
10 Gleason L. Archer, Jr., akusonyeza cholakwa chachikulu m’kulingalira kwa achisulizo chapamwamba. Iye akunena kuti, vuto nlakuti, “sukulu ya Wellhausen inayamba ndi kuyerekezera chabe (kumene iwo sanavutike nako konse kuti akusonyeze) kuti chipembedzo cha Israyeli chinali ndi chiyambi chaumunthu chabe mofanana ndi china chirichonse, ndi kuti chinafunikira kufotokozedwa monga chotulukapo cha chisinthiko.”6 M’kunena kwina, Wellhausen ndi otsatira ake anayamba ndi lingaliro lakuti Baibulo liri chabe mawu a anthu, ndiyeno iwo anayamba kumaganiza kuchokera pamenepo.
11 Kalero mu 1909, The Jewish Encyclopedia inasonyeza zolakwa ziŵiri munthanthi ya Wellhausen: “Zigomeko zimene Wellhausen pafupifupi kotheratu wagwira nazo gulu lonse la osuliza Baibulo anzake zazikidwa pamalingaliro aŵiri: loyamba, nlakuti dzoma limakhala lolemekezeka kwambiri m’kukula kwa chipembedzo; lachiŵiri, nlakuti magwero achikale kwambiri amachita ndi ziyambiyambi za kuyambika kwa dzoma. Lingaliro loyambiriralo liri losemphana ndi umboni wa makhalidwe achikale, ndipo lomaliziralo liribe chichirikizo muumboni wa malamulo a dzoma ofanana ndi aja a ku India.”
12. Kodi ndimotani mmene chisulizo chapamwamba chamakono chiriri mothandizidwa ndi kufukula za m’mabwinja?
12 Kodi pali njira iriyonse yopendera chisulizo chapamwamba chooti tiwone kaya ngati nthanthi zake ziri zolondola kapena ayi? The Jewish Encyclopedia inapitirizabe kunena kuti: “Malingaliro a Wellhausen ngozikidwa pafupifupi kotheratu pampangidwe chabe, ndipo adzafunikira kuchirikizidwa ndi kupenda mwa lingaliro la kufukula za m’mabwinja kokhazikitsidwa.” M’kupita kwa zaka, kodi kufukulidwa kwa za m’mabwinja kukuwonekera kukhala kukutsimikizira nthanthi za Wellhausen? The New Encyclopædia Britannica imayankha kuti: “Kusuliza kwa zofukulidwa za m’mabwinja kukuwonekera kukhala kukuchirikiza kudalirika kwa mfundo zatsatanetsatane zenizeni za m’mbiri ngakhale za nyengo zakale kopambana [za mbiri ya Baibulo] ndi kutsutsa nthanthi yakuti zolembedwa za Pentateuch [zolembapo za mumbiri m’mabukhu oyambirira a Baibulo] ziri chabe chisonyezero cha nyengo zamtsogolo mwake kwambiri.”
13, 14. Mosasamala kanthu za kukhala kwake ndi maziko ogwedezeka, kodi nchifukwa ninji kusuliza kwapamwamba kwa Wellhausen kukulandiridwabe mofala?
13 Polingalira kufooka kwake, kodi nchifukwa ninji chisulizo chapamwamba chiri chofala kwambiri pakati pa anthu anzeru kopambana a lerolino? Chifukwa chakuti chimawauza zinthu zimene iwo akufuna kumva. Katsiwiri wina wa m’zaka za zana la 19 anafotokoza kuti: “Ineyo, ndikulandira bukhu limeneli la Wellhausen koposa pafupifupi wina aliyense; pakuti vuto lalikulu la mbiri ya Chipangano Chakale likuwonekera kwa ine kukhala potsirizira pake litathetsedwa m’mkhalidwe wogwirizana ndi lamulo lochitira zinthu la chisinthiko cha munthu limene ndiri wokakamizika nalo kuligwiritsira ntchito kumbiri ya zipembedzo zonse.”7 Mwachiwonekere, chisulizo chapamwamba chikugwirizana ndi malingaliro ake okhotetsedwa monga wokhulupirira chisinthiko. Ndipo, ndithudi, nthanthi ziŵirizo zimatumikira chifuno chofanana. Monga momwedi chisinthiko chikachotsera kufunika kwa kukhulupirira mwa Mlengi, chotero chisulizo chapamwamba cha Wellhausen chikatanthauza kuti munthu sakafunikira kukhulupirira kuti Baibulo linali louziridwa ndi Mulungu.
14 M’zaka zino za zana la 20 lodalira pakulingalira, lingaliro lakuti Baibulo siliri mawu a Mulungu koma a anthu limawonekera kukhala lokondweretsa kwa anthu anzeru.c Kuli kosavuta kwambiri kwa iwo kukhulupirira kuti maulosi analembedwa pambuyo pa kukwaniritsidwa kwawo koposa kuwavomereza kukhala enieni. Iwo amasankha kutsutsa zolembedwa za Baibulo za zozizwitsa kukhala nthanthi, nthano zongopeka, kapena nthano zamakolo akale, koposa ndi kulingalira kuthekera kwakuti izo zinachitikadi. Koma lingaliro loterolo nlolakwika ndipo silimapereka chifukwa champhamvu chokanira Baibulo kukhala lowona. Chisulizo chapamwamba chiri cholakwa kwakukulu, ndipo kuukira kwake Baibulo kwalephera kusonyeza kuti Baibulo siliri Mawu a Mulungu.
Kodi Kufukula M’mabwinja Kumachirikiza Baibulo?
15, 16. Kodi ndikukhalapo kwa wolamulira wamakedzana uti kotchulidwa m’Baibulo kumene kunatsimikiziridwa ndi kufukula za m’mabwinja?
15 Kufukula m’mabwinja kuli mbali yozikidwa mwamphamvu kwambiri ya kupenda koposa ndi chisulizo chapamwamba. Mwa kukumba pakati pa mabwinja a kutsungula kwakale, ofukula za m’mabwinja awonjezera m’njira zambiri kumvetsetsa kwathu mmene zinthu zinaliri makedzana. Chotero, nkosadabwitsa kuti cholembedwa cha zofukulidwa za m’mabwinja mobwerezabwereza chimagwirizana ndi zimene timaŵerenga m’Baibulo. Nthaŵi zina, kufukula za m’mabwinja kwachirikiza Baibulo motsutsana ndi olisuliza ake.
16 Mwachitsanzo, malinga ndi kunena kwa bukhu la Danieli, wolamulira wotsirizira m’Babulo asanagwere kwa Aperisi anali kutchedwa Belisazara. (Danieli 5:1-30) Popeza kuti panawonekera kukhala pasakutchulidwa Belisazara kusiyapo Baibulo, chitsutso chinapangidwa kuti Baibulo linali lolakwa ndi kuti munthu ameneyu sanakhaleko nkomwe. Koma mkati mwa zaka za zana la 19, timipembe tingapo tolembedwa mumpangidwe wa zilemba zozokota tinatumbidwa m’mabwinja a kumwera kwa Iraq, ito tinapezedwa kukhala tikuphatikizapo pemphero lopempherera thanzi la mwana woyamba wa Nabonidusi, mfumu ya Babulo. Dzina la mwana ameneyu? Belisazara.
17. Kodi tingafotokoze motani chenicheni chakuti Baibulo limatcha Belisazara mfumu, pamene kuli kwakuti zolembedwa zozokota zakale zochuluka zinamutcha kalonga?
17 Chotero Belisazara anakhalako! Komabe, kodi iye anali mfumu, pamene Babulo anagwa? Zolembedwa zochuluka zopezedwa pambuyo pake zimam’tchula kukhala mwana wa mfumu, kalonga mfumu. Koma cholembedwa chochita kuzokota chotchedwa monga “Cholembedwa cha Zochitika za Nabonidusi” chinasonyeza bwino kwambiri malo audindo enieni a Belisazara. Icho chinasimba kuti: “Iye [Nabonidusi] anapatsa ‘Msasa’ kwa mwana wake wamkulu (wamwamuna), wachisamba, iye analamulira magulu ankhondo kulikonse m’dzikolo pansi pa (ulamuliro) wake. Iye analola (chirichonse) kuchitika, iye anapatsa ufumu kwa iye.”8 Chotero Belisazara anapatsidwa ufumu. Ndithudi, mulimonse zimenezo zinampanga kukhala mfumu!d Unansi umenewu pakati pa Belisazara ndi atate wake, Nabonidusi, umafotokoza chifukwa chake Belisazara, mkati mwa phwando lotsirizira lija m’Babulo, analonjeza kupanga Danieli kukhala wolamulira wachitatu muufumuwo. (Danieli 5:16) Popeza kuti Nabonidusi anali wolamulira woyambirira, Belisazara iye mwiniyo anali wachiŵiri yekha wolamulira wa Babulo.
Umboni Wina Wochirikiza
18. Kodi ndichidziŵitso chotani chimene kufukula za m’mabwinja kumatipatsa kutsimikizira mtendere ndi kulemerera za ulamuliro wa Davide?
18 Ndithudi, zotumbidwa zambiri zofukulidwa m’mabwinja zasonyeza kulondola kwa m’mbiri kwa Baibulo. Mwachitsanzo, Baibulo limasimba kuti Mfumu Solomo atalandira ufumu kuchokera kwa atate wake, Davide, Israyeli anasangalala ndi kulemerera kwakukulu. Timaŵerenga kuti: “Ayuda ndi Israyeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.” (1 Mafumu 4:20) Mochirikiza mawu ameneŵa, timaŵerenga kuti: “Umboni wa zofukulidwa m’mabwinja umavumbula kuti panali kuchuluka kwa chiŵerengo cha anthu mu Yuda mkati ndi pambuyo pa zaka za zana lakhumi B.C. pamene mtendere ndi kulemerera zimene Davide anazidzetsa zinakupangitsa kukhala kothekera kumanga matauni ambiri atsopano.”10
19. Kodi ndiumboni wina wowonjezereka wotani umene kufukula za m’mabwinja kumatipatsa ponena za nkhondo pakati pa Israyeli ndi Moabu?
19 Pambuyo pake, Israyeli ndi Yuda anakhala mitundu iŵiri, ndipo Israyeli anagonjetsa dziko lapafupilo la Moabu. Panthaŵi ina Moabu, pansi pa Mfumu Mesa, anapandukira, ndipo Israyeli anagwirizana ndi Yuda ndi ufumu woyandikana nawo wa Edomu kumka kukamenyana nkhondo ndi Moabu. (2 Mafumu 3:4-27) Mwapadera, mu 1868 mu Yordano, stela (sileti la mwala wozokotedwa) linatumbidwa limene linalembedwa m’chinenero Chachimoabu linali ndi cholembedwa cha Mesa iye mwiniyo cha nkhondo imeneyi.
20. Kodi kufukula za m’mabwinja kumatiuzanji ponena za kuwonongedwa kwa Israyeli ndi Asuri?
20 Ndiyeno, m’chaka cha 740 B.C.E., Mulungu analola ufumu wakumpoto wopanduka wa Israyeli kuwonongedwa ndi Asuri. (2 Mafumu 17:6-18) Ponena za cholembedwa cha Baibulo cha chochitika chimenechi, wofukula za m’mabwinja Kathleen Kenyon akunena kuti: “Wina angakhale ndi chikaikiro chakuti zina za zimenezi nzongosinjirira.” Koma kodi ziri choncho? Iye akuwonjeza kuti: “Umboni wa zofukulidwa za m’mabwinja wonena za kugwa kwa ufumu wa Israyeli uli pafupifupi wamoyo kwambiri koposa wa cholembedwa cha Baibulo. . . . Kufafanizidwiratu kwa matauni a Israyeli a Samariya ndi Hazori ndi kuwonongedwa kotsagana nako kwa Megido ndiumboni weniweni wa zofukulidwa za m’mabwinja umene wolemba [Baibulo] sanauwonjezerere mawu.”11
21. Kodi ndimfundo zatsatanetsatane zotani zonena za kugonjetsedwa kwa Yuda ndi Ababulo zimene zikuperekedwa ndi zofukulidwa m’mabwinja?
21 Pambuyo pakenso, Baibulo limatiuza kuti Yerusalemu pansi pa Mfumu Yehoyakini anazingidwa ndi Ababulo ndipo anagonjetsedwa. Chochitika chimenechi chinalembedwa m’Mbiri ya Ababulo, mwala wozokotedwa umene unatumbidwa ndi ofukula za m’mabwinja. Pauwo, timaŵerengapo kuti: “Mfumu ya Akadi [Babulo] . . . inazinga mzinda wa Yuda (iahudu) ndipo mfumuyo inalanda mzindawo patsiku lachiŵiri la mwezi wa Addaru.”12 Yehoyakini anatengedwera ku Babulo ndi kuikidwa m’ndende. Koma pambuyo pake, malinga ndi kunena kwa Baibulo, iye anamasulidwa muukaidi ndi kupatsidwa gawo la chakudya. (2 Mafumu 24:8-15; 25:27-30) Zimenezi zikuchirikizidwa ndi zolembedwa za olamulira a Babulo, zimene zimandandalika magawo a chakudya opatsidwa kwa “Yaukîn, mfumu ya Yuda.”13
22, 23. Mwachisawawa, kodi nchiyani chimene chiri mgwirizano pakati pa kufukula za m’mabwinja ndi zolembedwa za m’mbiri za Baibulo?
22 Ponena za mgwirizano wa pakati pa zofukulidwa m’mabwinja ndi cholembedwa cha m’mbiri cha Baibulo, Profesala David Noel Freedman akunena kuti: “Komabe, mwachisawawa, zofukulidwa m’mabwinja zayedzamira kukuchirikiza kukhalapo kwenikweni kwa m’mbiri kwa kufotokoza kwa Baibulo. Ndandanda ya zochitika za m’mbiri ya nthaŵi yaitali kuyambira kwa makolo oyambirira kukafika kunthaŵi ya C[hipangano] C[hatsopano] zimagwirizana ndi zenizeni za zofukulidwa m’mabwinja. . . . Zotumbidwa zamtsogolo mosakaikira zidzachirikiza kaimidwe kamakono kachikatikati kakuti mwambo wa Baibulo ngwozikidwa m’mbiri, ndi wonenedwa mokhulupirika, ngakhale kuli kwakuti suuli mbiri m’lingaliro lake lenileni kapena lasayansi.”
23 Ndiyeno, ponena za zoyesayesa za osuliza apamwamba kutsutsa Baibulo, iye akunena kuti: “Zoyesayesa za kusintha mbiri ya Baibulo ndi akatswiri amakono—mwachitsanzo, lingaliro la Wellhausen lakuti nyengo ya makolo akale inali chisonyezero cha ufumu wogaŵanika; kapena kukanidwa kwa Mose kukhala munthu wa m’mbiri ndi kutuluka ndi kukonzanso mbiri ya Israyeli kotulukapo kochitidwa ndi Noth ndi otsatira ake—kwalephera chiyeso kutayerekezeredwa ndi tsatanetsatane wa zofukulidwa m’mabwinja kudzanso kufotokoza kwabaibulo.”14
Kugwa kwa Yeriko
24. Kodi nchidziŵitso chotani chimene Baibulo limatipatsa ponena za kugwa kwa Yeriko?
24 Kodi zimenezi zimatanthauza kuti zofukulidwa pansi zimagwirizana ndi Baibulo m’chirichonse? Ayi, pali kusagwirizana kungapo. Kumodzi ndiko kugonjetsedwa kochititsa nthumanzi kwa Yeriko kofotokozedwa kuchiyambiyambi kwa mutu uno. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, Yeriko unali mzinda woyambirira kugonjetsedwa ndi Yoswa pamene iye anatsogolera Aisrayeli kuloŵa m’dziko la Kanani. Kaŵerengedwe ka nthaŵi ka Baibulo kamasonyeza kuti mzindawo unagwa m’theka loyambirira la zaka za zana lachi 15 B.C.E. Pambuyo pa kugonjetsedwako, Yeriko anawotchedweratu ndi moto ndiyeno anasiyidwa wosakhalidwa kwazaka mazana ambiri.—Yoswa 6:1-26; 1 Mafumu 16:34.
25, 26. Kodi ndimalingaliro aŵiri osiyana otani amene ofukula za m’mabwinja awafikira ponena za chotulukapo cha kukumba pa Yeriko?
25 Nkhondo yachiŵiri ya dziko isanachitike, malo okhulupiriridwa kukhala Yeriko anakumbidwa ndi Profesala John Garstang. Iye anapeza kuti mzindawo unali wakale kwambiri ndipo unali utawonongedwa ndi kumangidwanso nthaŵi zambiri. Mkati mwa chimodzi cha ziwonongekozo, Garstang anapeza kuti malingawo anagwa monga ngati ndi chivomezi, ndipo mzindawo unawotchedweratu psiti ndi moto. Garstang anakhulupirira kuti zimenezi zinachitika pafupifupi mu 1400 B.C.E., osati patali kwambiri ndi deti losonyezedwa ndi Baibulo la chiwonongeko cha Yeriko chochitidwa ndi Yoswa.15
26 Pambuyo pa nkhondoyo, wokufula za m’mabwinja wina, Kathleen Kenyon, anachitanso kukumba kwina pa Yeriko. Iye anafika palingaliro lakuti malinga akugwawo amene Garstang anawasonyeza anali a m’zaka mazana ambiri kalero koposa mmene iye anaganizirira. Iye anasonyeza chiwonongeko chachikulu cha Yeriko m’zaka za zana la 16 B.C.E. koma anati panalibe mzinda pamalo a Yerikowo mkati mwa zaka za zana la 15—pamene Baibulo limanena kuti Yoswa anali kuukira dzikolo. Iye akupitiriza kusimba za zisonyezero zothekera za chiwonongeko china chimene chingakhale chitachitika pamalowo mu 1325 B.C.E. ndipo akupereka lingaliro lakuti: “Ngati chiwonogeko cha Yeriko chiti chigwirizanitsidwe ndi chiukiro chotsogozedwa ndi Yoswa, deti [lotsirizirali] ndilo limene ofukula za m’mabwinja akulingalira kukhala liri.”16
27. Kodi nchifukwa ninji zosiyana pakati pa kufukula za m’mabwinja ndi Baibulo siziyenera kutivutitsa maganizo mosayenera?
27 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Baibulo nlolakwa? Kutalitali. Tiyenera kukumbukira kuti pamene kuli kwakuti kufukulidwa kwa m’mabwinja kukutipatsa zenera lowonera zakale, nthaŵi zonse siliri zenera lowonekera bwino. Nthaŵi zina limakhala lachizimezime. Monga momwe wothirira ndemanga wina anenera kuti: “Mwatsoka umboni wa zofukulidwa pansi uli, wazidutswazidutswa, ndipo chifukwa cha chimenecho suli wokwanira.”17 Izi ziri makamaka choncho ponena za nyengo zakale kwambiri za mbiri ya Israyeli, pamene umboni wa zofukulidwa m’mabwinja uli wosawoneka bwino. Ndithudi, umboniwo uli wosawonekera bwino koposerapo pa Yeriko, popeza kuti malowo akumbika moipa kwambiri.
Kupereŵera kwa Kufukula Zapansi
28, 29. Kodi ndizopereŵera zotani za kufukula za m’mabwinja zimene ophunzira azivomereza?
28 Ofukula za m’mabwinja iwo eniwo amavomereza zopereŵera za sayansi yawo. Mwachitsanzo, Yohanan Aharoni, akufotokoza kuti: “Ponena za kutanthauzira kwa m’mbiri kapena mbiri ndi malo, wofukula za m’mabwinja amatayika pasayansi yeniyeni, ndipo iye ayenera kudalira pakulingalira makhalidwe ndi nthathi zosatsimikiziridwa kuti afike pa chitunzithunzi chomvekera bwino cha m’mbiri.”18 Ponena za madeti operekedwa ku zotumbidwa zosiyanasiyana, iye akuwonjeza kuti: “Chifukwa cha chimenecho, tiyenera kukumbukira nthaŵi zonse, kuti simadeti onse amene ali otsimikizirika ndipo ali okaikitsa m’milingo yosiyanasiyana,” ngakhale kuli kwakuti iye amalingalira kuti ofukula za m’mabwinja a lerolino angathe kukhala achidaliro kwambiri ponena za kuika kwawo madeti koposa mmene zinaliri makedzana.19
29 The World of the Old Testament imafunsa kuti: “Kodi njotsimikizirika kapena njasayansi kwenikweni motani mmene iriri njira yofukulira za m’mabwinja?” Imayankha kuti: “Ofukula za m’mabwinja ali otsimikizira pamene akufukula zenizeni koposa pamene akuzitanthauzira. Koma zowatanganitsa zawo zaumunthu zidzayambukiranso njira zawo zimene amagwiritsira ntchito ‘pokumba.’ Iwo sangathandizire kuwononga umboni wawo pamene iwo akuwukumba kumka pansi kupyola miyalo yadothi, kotero kuti iwo alephera ‘kupenda’ zimene iwo akufufuza mwa kuzibwereza. Zimenezi zimapangitsa kufukula za m’mabwinja kukhala kwapadera pakati pa masayansi ambiri. Ndiponso, kumapangitsa kusimba kwa ofukula za m’mabwinja kukhala kofuna zochuluka kopambana ndi ntchito yokhala ndi zolephera zambiri.”20
30. Kodi ophunzira Baibulo amalingalira motani kufukula za m’mabwinja?
30 Chotero kufukula za m’mabwinja kungathe kukhala kothandiza kwambiri, koma mofanana ndi kuyesayesa kulikonse kwa anthu, kuli nzolakwa. Pamene kuli kwakuti timalingalira nthanthi za zofukulidwa m’mabwinja ndi chikondwerero, sitiyenera kuzilingalira kukhala chowonadi chosakhoza kutsutsidwa. Ngati ofukula za m’mabwinja atanthauzira zofukula zawo m’njira imene imatsutsana ndi Baibulo, sikuyenera mwa iko kokha kulingaliridwa kuti Baibulo nlolakwa ndipo ofukula za m’mabwinja ali olondola. Mamasulidwe awo adziŵidwa kukhala akusintha.
31. Kodi ndilingaliro latsopano lotani limene laperekedwa posachedwapa ponena za kugwa kwa Yeriko?
31 Nkokondeweretsa kudziŵa kuti mu 1981 Profesala John J. Bimson anapendanso pa chiwonongeko cha Yeriko. Iye anapenda mosamalitsa chiwonongeko chamoto cha Yeriko chimene chinachitika—malinga ndi kunena kwa Kathleen Kenyon—pakatikati pa zaka za zana la 16 B.C.E. Malinga ndi kunena kwa iye, sikokha kuti chiwonongeko chimenecho chikugwirizana ndi cholembedwa cha Baibulo chonena za kuwononga mzinda kochitidwa ndi Yoswa koma chithunzithunzi cha ofukula za m’mabwinja chonena za Kanani yense wathunthu chikugwirizana ndendende ndi kufotokoza kwa Baibulo kwa Kanani pamene Aisrayeli anaukira. Chotero, iye akupereka lingaliro lakuti kuika madeti kwa ofukula za m’mabwinja nkolakwa ndipo akupereka lingaliro lakuti chiwonongeko chimenechi kwenikweni chinachitika pakatikati pa zaka za zana la 15 B.C.E., mkati mwa nthaŵi ya moyo wa Yoswa.21
Baibulo Liri Mbiri Yeniyeni
32. Kodi ndichikhoterero chotani chimene chasungidwa pakati pa akatswiri ena?
32 Zimenezi zikusonyeza chenicheni chakuti ofukula za m’mabwinja kaŵirikaŵiri amasiyana pakati pawo. Pamenepo, nkosadabwitsa kuti ena amasemphana ndi Baibulo pamene ena amagwirizana nalo. Komabe, akatswiri ena akufikira pakulemekeza Baibulo lonse lathunthu, kukhala kwake la m’mbiri, ngati kusali m’tsatanetsatane aliyense. William Foxwell Albright anaimira sukulu ina ya anzeru pamene analemba kuti: “Kwakhalapo kubwerera kwa anthu onse kukuzindikira kulondola, ponse paŵiri m’chirichonse ndi m’tsatanetsatane wa zenieni, wonena za mbiri ya chipembedzo cha Israyeli. . . . Kunena mwachidule, ife kachiŵirinso tsopano tingathe kuwona Baibulo kuyambira kuchiyambi kwake mpaka kumapeto monga cholembedwa chodalirika cha mbiri yachipembedzo.”22
33, 34. Kodi ndimotani mmene Malemba Achihebri iwo eniwo amaperekera umboni wa kukhala olondola mogwirizana ndi mbiri?
33 Kunena zowona, Baibulo lenilenilo liri ndi chidindo cha mbiri yolondola. Zochitika zikugwirizanitsidwa ndi nthaŵi zenizeni ndi madeti, mosemphana ndi nthanthi zambiri zakale ndi nthano zongopeka. Zochitika zambiri zolembedwa m’Baibulo zikuchirikizidwa ndi zozokotedwa zolembedwa m’madeti amenewo. Kumene tipeza kusiyana pakati pa Baibulo ndi zozokotedwa zina zamakedzana, kusiyanako kaŵirikaŵiri kungagwirizanitsidwe ndi kuipidwa kwa olamulira akale kwa kulemba kugonjetsedwa kwawo ndi chikhumbo chawo cha kukuza zipambano zawo.
34 Ndithudi, zochuluka za zozokotedwa zamakedzana zimenezo siziri zochitika izo kwakukulukulu ndizo mawu onyengerera aukumu. Mosemphana ndi zimenezo, olemba Baibulo amasonyeza kunena zowona kosawonekawoneka. Anthu amene anali makolo akale aakulu onga ngati Mose ndi Aroni akuvumbulidwa ndi zofooka zawo zonse ndi nyonga zawo. Ngakhale zophophonya za mfumu yaikulu Davide zikuvumbulidwa mowona mtima. Zolephera zamtundu wonse wathunthu zikuvumbulidwa mobwerezabwereza. Kunena zowona kumeneku kumasonyeza Malemba Achihebri kukhala a chowonadi ndi odalirika ndipo amachititsa mawu a Yesu kukhala amphamvu, amene, popemphera kwa Mulungu, anati: “Mawu anu ndichowonadi.”—Yohane 17:17.
35. Kodi anzeru odalira pamalingaliro analephera kuchitanji, ndipo kodi nkuti kumene ophunzira Baibulo amayang’anako mmalo mwakuti atsimikizire kuti Baibulo liri louziridwa?
35 Albright anapitirizabe kunena kuti: “Mulimonse zamkati mwa Baibulo ziposa mabukhu onse akale achipembedzo; ndipo liposanso kwambirimbiri mabukhu ena onse otsatirapo m’kusavuta kwachindunji kwauthenga wake ndi m’kukhala kwaponseponse [kufalikira kwakukulu] kwa kuyambukira kwake amuna a m’maiko onse ndi nthaŵi.”23 Ndiwo ‘uthenga wapamwamba,’ umenewu koposa ndi umboni wa ophunzira, umene umatsimikizira kuuziridwa kwa Baibulo, monga momwe tidzawonera m’mitu yotsatirapo. Koma tiyeni tiwone pano kuti anzeru amakono odalira pamalingaliro alephera kutsimikizira kuti Malemba Achihebri saali mbiri yeniyeni, pamene kuli kwakuti zolembedwa zimenezi mwa izo zokha zikupereka umboni uliwonse wa kukhala zolondola. Kodi zofananazo zingathe kunenedwa ponena za Malemba Achikristu Achigriki, “Chipangano Chatsopano”? Tidzalingalira zimenezi m’mutu wotsatirapo.
[Mawu a M’munsi]
a “Chisulizo chapamwamba” (kapena “njira yosuliza ya m’mbiri”) ali mawu ogwiritsiridwa ntchito kufotokoza kuphunziridwa kwa Baibulo ncholinga cha kupeza tsatanetsatane wonga ngati woliyambitsa, magwero a mawu ake, ndi nthaŵi ya kulembedwa kwa bukhu lirilonse.
b Mwachitsanzo, wolemba ndakatulo Wachingelezi John Milton analemba ndakatulo yake yotchukayo “Paradise Lost” (Paradaiso Wotaika) m’njira yakalembedwe yosiyana kwambiri ndi ndakatulo yake yakutiyo “L’Allegro.” Ndipo matrakiti ake a ndale zadziko analembedwanso m’kalembedwe kena kosiyana.
c Anzeru ochuluka lerolino amayedzamira kukhala okhulupirira pamalingaliro. Malinga ndi kunena kwa bukhu lofotokoza mawu, kukhulupirira pamalingaliro kumatanthauza “kudalira pa lingaliro monga maziko otsimikizirira chowonadi cha chipembedzo.” Odalira pamalingaliro amayesa kufotokoza kanthu kalikonse m’mawu a anthu koposa ndi kulingalira kuthekera kwa kachitidwe ka Mulungu.
d Mokondweretsa, chifanizo cha wolamulira wakale chopezeka kumpoto kwa Siriya mu 1970 chinasonyeza kuti sikunali kwachilendo kwa wolamulira kutchedwa mfumu pamene, kwenikweni, iye anali ndi ulamuliro wocheperapo. Chifanizocho chinali cha wolamulira wa Gozan ndipo chinalembedwa mawu m’Chisuri ndi Chiaramu. Mawu olembedwa m’Chisuriwo anatcha munthuyo bwanamkubwa wa Gozan, koma mawu olembedwa m’Chiaramu ofanana nawo anamutcha mfumu.9 Chotero sikukakhala kosiyana ndi kwina kulikonse kuti Belisazara atchedwe kalonga mfumu m’zolembedwa zaukumu Zababulo pamene kuli kwakuti m’cholembedwa Chachiaramu chonena za Danieli iye akutchedwa mfumu.
[Mawu Otsindika patsamba 53]
Mosafanana ndi mbiri za makedzana za kudziko, Baibulo mosabisa limasimba zolephera za anthu olemekezeka onga ngati Mose ndi Davide
[Bokosi patsamba 44]
Phindu la Kufukula za m’Mabwinja
“Kufukula za m’mabwinja kumapereka chitsanzo cha zipangizo ndi ziwiya zamakedzana, malinga ndi nyumba, zida zankhondo ndi zodzikometsera nazo. Zochuluka za zimenezi zingathe kulinganizidwa mogwirizana ndi ndandanda ya nthaŵi ndi kudziŵidwa bwino lomwe ndi mawu enieni ndi malemba opezeka m’Baibulo. M’lingaliro limeneli Baibulo lasunga molondola mumpangidwe wolembedwa kakhalidwe kake kamkhalidwe wamakedzana. Tsatanetsatane wa nkhani za m’Baibulo saali chotulukapo choyerekezera choperekedwa ndi wolemba koma mmalo mwake ndizo zisonyezero zodalirika zonena za dziko m’limene zochitika zolembedwazo, mwaudziko ndi mwa zozizwitsa, zinachitika.”—The Archaeological Encyclopedia of the Holy Land.
[Bokosi patsamba 50]
Zimene Zofukula za m’Mabwinja Zingachite ndi Kusachita
“Kufukula za m’mabwinja sikumatsimikizira kapena kusatsimikizira Baibulo m’njira zotsimikizirika, koma kuli ndi ntchito zinanso, zokhala ndi kufunika kwakukulu. Kumavumbula kumlingo wakutiwakuti dziko la zinthu zowoneka limene linasonyezedwa ndi Baibulo. Kudziŵa, tinene kuti, zipangizo zimene nyumba inamangidwa nazo, kapena mmene ‘malo okwezeka’ anawonekerera, kumawonjezera kwambiri kumvetsetsa kwathu cholembedwacho. Chachiŵiri, kumadzadzitsa cholembedwa cha m’mbiri. Mwachitsanzo, Mwala Wachimoabu, umapereka mbali ina ya nkhaniyo yotchulidwa mu 2 Mafumu 3:4 ndi mavesi otsatiraŵa. . . . Chachitatu, kumavumbula moyo ndi lingaliro la oyandikana nawo a Israyeli wakale—kumene kuli kosangalatsa mwa iko kokha, ndi kumene kumasonyeza ziganizo zambiri zosiyanasiyana mu zimene lingaliro la Israyeli wakale linapangikira.”—Ebla—A Revelation in Archaeology.
[Chithunzi patsamba 41]
Milton analemba m’kalembedwe kosiyanasiyana, osati kamodzi chabe. Kodi osuliza apamwambawo amakhulupirira cholembedwa chakecho kukhala chotulukapo cha chiŵerengero cha olemba osiyanasiyana?
[Chithunzi patsamba 45]
“Cholembedwa cha Zochitika za Nabonidusi” chimasimba kuti Nabonidusi anaikizira ufumu kwa mwana wake wachisamba
[Chithunzi patsamba 46]
Mwala wa Moabu umapereka kufotokoza kwa Mfumu Mesa kwa nkhondo pakati pa Moabu ndi Israyeli
[Chithunzi patsamba 47]
Zolembedwa zaukumu za Ababulo zimachirikiza cholembedwa cha Baibulo chonena za kugwa kwa Yerusalemu