Igupto Wakale—Woyambirira wa Mphamvu Zazikulu za Dziko
IGUPTO—dziko lakale la a Farao ndi Nile—linali limodzi la malo achitukuko chachikulu a dziko. Luso lake limakometsera malo osungirako zinthu zakale aakulu. Mbiri yake inalembedwa m’mabukhu ophunzirira a kusukulu. Zikumbutso zake zazikulu zimasangalatsa anthu apaulendo. Kuwonjezerapo, zochitika za m’Baibulo zambiri zinawoneka kapena kukhudza dziko limeneli. Igupto ndi anthu ake amalozeredwako nthaŵi zoposa 700 mu Baibulo.
Komabe, nchiyani chimene kwenikweni mumadziŵa ponena za Igupto wakale? Kuphunzira zambiri ponena za iye kudzakuthandizani kumvetsetsa zinthu zambiri zotchulidwa m’Baibulo.
Mu Igupto, akatswiri odziŵa za zinthu zofotseredwa pansi apeza zambiri zomwe zimatsimikizira mbiri ya Baibulo. Mwachitsanzo, lingalirani mbiri yonena za Yosefe. Maina, maina aulemu, thayo la Yosefe monga wosunga nyumba, thayo loperekedwa kwa iye monga wolamulira wachiŵiri m’dzikolo ndipo monga wogaŵira chakudya, machitachita a kuika maliro Aigupto, ndipo ngakhale kachitidwe ka ophika mkate kunyamula mitanga ya mkate pa mitu yawo—zonsezi zapezeka kutsimikizira miyambo ya Aigupto a m’nthaŵi imeneyo.—Genesis, mitu 39–47; 50:1-3.
Dziko ndi Anthu Ake
Igupto amadalira pa Nile. Chigwa cholemera cha mtsinje umenewo, chikumafika pa avereji ya kokha makilomita 19 mulifupi kuchokera ku Aswân kufikira ku Cairo, mofutukuka kulinga kumpoto monga nduwira yowonda yobiriŵira kudutsa chipululu cha Africa. Kalelo, kusefukira kwake kwa pachaka kunkabweretsa zinyalala zomwe zinapatsa nthaka chonde chomwe chinapangitsa Igupto kukhala wotumiza wa chakudya ndi malo a chisungiko m’nthawi ya njala. (Genesis 12:10) Bango la gunda, lopezeka m’mphepete mwa gombe lake, linapangidwa kukhala mapepala oyambirira.
Malo aakulu, kumene madzi a Nile amafutukuka asanalowe mu Mediterranean wobiriŵira, amatchedwa Kunsi kwa Igupto. Pano, mwachiwonekere, pali “dziko la Goseni,” kumene Aisrayeli anakhala mkati mwa ulendo wawo wautali mu Igupto.—Genesis 47:27.
Chipembedzo cha Aigupto
Aigupto akale anakhulupirira kuti Farao wawo anali mulungu. Nsongayi imawonjezera tanthauzo ku funso lonyoza la Farao kwa Mose: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake?” (Eksodo 5:2) Aigupto analinso ndi milungu ina yambiri. Maina 740 a ina ya iyi anapezeka mu ndandanda yopezedwa mu manda a Thutmose III. Aigupto analambira milungu itatu, kapena utatu, ndipo mmodzi wa yotchuka ya iyi unali utatu wa Osiris, Isis, ndi Horus.
Yambiri ya milungu yotchuka ya Igupto inasonyezedwa ndi matupi a anthu ndi mitu ya zinyama. Aigupto anaimira Horus ndi mutu wa mphamba ndipo Thoth ndi mutu wa ibis kapena nchima. Amphaka, nkhandwe, ng’ona, anyani, ndi mbalame zosiyanasiyana zinali kulingaliridwa kukhala zopatulika chifukwa cha kugwirizana kwawo ndi milungu yakutiyakuti. Nkhunzi ya Apis, yolingaliridwa kukhala thupi launyama la mulungu Osiris, inaikidwa mu kachisi pa Memphis, kenaka kupatsidwa mwambo wa maliro wolemekezeka ndipo ngakhale kukonzedwa bwino pambuyo pa imfa. Zokometsera zotchuka za ku Igupto, zovalidwa monga mkanda wa zithumwa zotetezera, zinali zoimira za m’kunkhuniza—zolingaliridwa kukhala kudziwonetsera kwa mulungu wolenga.
Mosasamala kanthu za kukhala kwa nthaŵi yaitali mu Igupto ndi kugwirizana kwachindunji ndi anthu a dziko limenelo, Aisrayeli anali kokha ndi Mulungu mmodzi, Yehova, ndipo anayenera kumtumikira iye yekha. Iwo anachenjezedwa kusapanga fano lirilonse la chipembedzo—kaya la Mulungu iyemwini kapena mbalame, nyama, nsomba, kapena china chirichonse. Kulambira kwawo kwa mwana wang’ombe wa golidi mwamsanga pambuyo pa kutuluka kwawo mu Igupto kungakhale kunatulukapo kuchokera ku chisonkhezero cha Chiigupto.—Eksodo 32:1-28; Deuteronomo 4:15-20.
Chikhulupiriro mu Kusafa kwa Moyo
Aigupto anali akhulupiriri amphamvu a kusafa kwa moyo. Chotero, atsogoleri Aigupto anakonzekeretsedwa manda okometseredwa bwino, odzaza ndi zofunika za moyo ndi zosangulutsa, kuyembekezera kupeza chimwemwe chosatha m’moyo wa pambuyo pa imfa. Nyumba zakale zosungiramo mitembo ziri chitsanzo chowonekera kwambiri cha mchitidwewu.
Zokometsera za golidi, zovala, mipando, vinyo, zakudya, miphika yowumba, mabokosi aminyanga, ndipo ngakhale zidutswa za miyala zoperera utoto woika m’maso zinaikidwa mosamalitsa mu manda a Aigupto. Chinakhulupiriridwa kuti zinthu zimenezi zinagwiritsiridwa ntchito m’moyo kuseri kwa manda. M’nthaŵi zoyambirira, akapolo anali kuphedwa ndi kuikidwa limodzi ndi ambuye awo, kukawatumikira iwo pambuyo pa imfa. Kusonkhanitsidwa kwa malaulo odziŵika monga “Bukhu la Akufa” kunapezeka mkati mwa zikwi za mabokosi a maliro Aigupto. Zinayembekezeredwa kuti malaulo amenewa akathandiza munthu wakufa kulaka mavuto osiyanasiyana a pambuyo pa moyo.
Kanali kosiyana chotani nanga kawonedwe ka Aisrayeli! Iwo anadziŵa, monga mmene Baibulo pambuyo pake linadzanenera, kuti “akufa sadziŵa kanthu bi.” Ndipo pamene munthu afa, “tsiku lomwelo zotsimikiza mtima wake zitaika.”a Chiyembekezo chawo kaamba ka moyo wa mtsogolo chinali m’chiwukiriro.—Mlaliki 9:5, 10; Masalmo 146:4; Yobu 14:13-15.
Ndani Anakhalako pa Nyengo Iti?
Akatswiri odziŵa za miyambo ya Igupto amazindikira “maufumu” 31 a mafumu a Igupto ndi kulankhula za Ufumu Wakale kukhala (Maufumu 3-6), Ufumu wa Pakati (Maufumu 11, 12), ndi Ufumu Watsopano (Maufumu 18-20). Koma njira iyi yokumbukira siiri yolongosoka kwenikweni. Imaphatikizapo zolembedwa zokaikirika ndi zoduka ndipo zingaphatikizepo mafumu ambiri akulamulira m’magawo osiyana pa nthaŵi imodzimodzi, m’malo mwa kulamulira kosiirana mmodzi pambuyo pa wina.b
Pamene Mose anayamba kulemba mabukhu oyambirira a Baibulo, iye anatsatira chomwe mwachiwonekere chinali mwambo weniweni wa Igupto wa kulozera kwa mfumu yawo monga “Farao” popanda kugwiritsira ntchito dzina laumwini. Chotero, sitikudziŵa dzina la Afarao amene Abrahamu ndi Yosefe anadziŵa kapena ndi uti amene analamulira pa nthaŵi ya kutuluka kwa Israyeli kuchokera mu Igupto. Komabe, dzina laulemu lakuti “Farao” pambuyo pake linayamba kugwiritsidwa ntchito limodzi ndi dzina lenileni la mfumuyo, kuchipanga icho kukhala chothekera kugwirizanitsa zochitika za Baibulo ndi ndandanda ya mfumu ya Igupto. Pano pali ena a Afarao omwe ali osangalatsa mwapadera kwa ophunzira Baibulo:
Akhenaton (wa Ufumu wotchedwa wa 18) anali mlambiri wowona mtima wa zizindikiro za mulungu wa dzuwa. Mu 1887 kusonkhanitsidwa kwa magome adothi 377 kunapezedwa pa Tel el-Amarna, chifupifupi makilomita 320 kummwera kwa Cairo. Magome osangalatsa amenewa anali makalata aukazembe olandiridwa ndi Akhenaton ndi atate ake Amenhotep III. Ophatikizidwa anali makalata ochokera kwa olamulira a Yerusalemu, Megido, Hazori, Sekemu, Lakisi, Hebroni, Gaza, ndi mizinda ina ya boma mu Palestina. Mwinamwake olembedwa mwamsanga Israyeli asanaloŵe mu Kanani, makalata amenewa anavumbula ndalama zolipira nkhondo ndi makonzedwe. Iwo anasonyezanso kuti mzinda uliwonse unali ndi mfumu yakeyake, monga mmene bukhu la Baibulo la Yoswa limasonyezera.
Tutankhamen, mkamwini wa Akhenaton, ali “Mfumu Tut” wotchuka amene zokongoletsa manda zake za golidi zinafukulidwa ndi akatswiri odziŵa kufukula zinthu zofotseredwa kale ndipo zinasonyezedwa m’malo osungira zinthu zakale zosiyanasiyana. Zokongoletsa zimenezi ziri chisonyezero chowonekera cha chuma cha Afarao. Chinali chuma choterechi chimene Mose poyambirirapo anachikana pamene iye “anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao, nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi.”—Ahebri 11:24, 25.
Merneptah anali wa “Ufumu wa 19.” Pa chikumbutso chachipambano chopezeka mu kachisi pa Thebes, Farao ameneyu analemba kuti “Israyeli wakhalitsidwa bwinja, mbewu yake yachotsedwa.” Uku ndi kutchula kokha kwachindunji kwa Israyeli monga mtundu kopezekabe mu mbiri ya Igupto wakale. Ngakhale kuti mwachiwonekere kunali kudzitukumula kopanda pake, kudzinenera kumeneku kukuwoneka kusonyeza kuti chipambano cha Israyeli pa Kanani chinali chitawoneka kale. Chotero, chipambano chimenecho cha 1473 B.C.E. chiyenera kukhala chinawoneka pakati pa nthaŵi imene Akhenaton analandira makalata a ku Tel el-Amarna ndi masiku a Merneptah.
Sisaki (Sheshonk I, “Ufumu wa 22”) ali Farao woyamba kutchulidwa ndi dzina m’Baibulo. Ndi gulu lamphamvu la magareta a nkhondo ndi anthu a pa kavalo, iye analoŵerera Yuda, kuwopsyeza Yerusalemu, ndipo “anachotsa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu. Anazichotsa zonse.” (2 Mbiri 12:9) Chochitikachi chinatsimikiziridwa ndi chithunzi cha khoma la kum’mwera la kachisi wa Amoni pa Karnak (Thebes wakale). Chimasonyeza andende omangidwa manja 156, aliyense akuimira mzinda wolandidwa kapena mudzi, kuphatikizapo Megido, Sunemu, ndi Gibiyoni. Pakati pa malo olandidwa, Sisaki amandandalitsa ngakhale “Munda wa Abram”—kulozera koyambirira kwambiri kwa Abrahamu m’mbiri ya Aigupto.
Mphamvu Zina za Dziko Zibuka
Kenaka, Igupto analowedwa m’malo ndi Asuri monga mphamvu yolamulira ya dziko. Koma iye anakhalabe mphamvu yokangalika ya ndale. Hoseya, mfumu yomalizira ya ufumu wa kumpoto wa mafuko khumi wa Israyeli, anachita chiwembu ndi Mfumu So ya ku Igupto m’kuyesera kopanda chipambano kwa kugwetsa goli la Asuri. (2 Mafumu 17:3, 4) Zaka zambiri pambuyo pake, mkati mwa ulamuliro wa Mfumu Hezekiya ya Yuda, Mfumu Tirihaqa ya ku Ethiopia (mwinamwake wolamulira wa chiEthiopia wa ku Igupto, Farao Taharqa) anayenda kupita ku Kanani ndipo kwakanthaŵi anapatutsa kuukira kwa mfumu ya Asuri Sanakeribu. (2 Mafumu 19:8-10) Mbiri zenizeni za Sanakeribu, zopezeka mu Asuri, mwachiwonekere zimalozera ku ichi pamene zimanena kuti: “Ine mwaumwini ndinagwira wamoyo . . . okwera pa magareta ankhondo a mfumu ya Ethiopia.”—Oriental Institute Prism of Sennacherib, University of Chicago.
M’neneri wa Yehova Yesaya ananeneratu kuti Igupto adzaperekedwa “m’dzanja la ambuye wa nkhalwe” ndipo kuti mfumu “yaukali” idzalamulira Aigupto. (Yesaya 19:4) Kuwona kwa ulosi umenewu kukutsimikiziridwa ndi cholembedwa cha Asuri m’chimene mwana wa Sanakeribu Esari-hadoni akudzitukumula ponena za chipambano chake cha Igupto, akumanena kuti: “Mfumu yake, Tirihaka, ndinavulaza nthaŵi zisanu ndi mivi ndipo ndinalamulira pa dziko lake lonse.”
Farao Neko anayenda kulinga cha kumpoto chifupifupi 629 B.C.E. kukatsekereza magulu ankhondo a mphamvu ya dziko yomadza yachitatu, Babulo. Baibulo linanena kuti Yosiya wa ku Yerusalemu mopanda nzeru anayesera kuletsa magulu ankhondo a Igupto pa Megido ndipo anagonjetsedwa ndi kuphedwa.c (2 Mbiri 35:20-24) Chifupifupi zaka zinayi pambuyo pake, mu 625 B.C.E., Farao Neko iyemwini anagonjetsedwa ndi Ababulo pa Karikemisi. Ponse paŵiri mbiri za Baibulo ndi Babulo zimalozera ku chochitikachi, chomwe chimapereka umbuye wa Babulo kumadzulo kwa Asia.
Mu 525 B.C.E. Igupto anabwera pansi pa ulamuliro wa mphamvu yachinayi ya dziko, Medo-Persia. Chifupifupi zaka mazana aŵiri pambuyo pake, mu 332 B.C.E., Alexander Wamkulu anabwera pa chiwonetsero ndipo anabweretsa Igupto pansi pa mphamvu ya dziko yachisanu, Grisi. Alexander anapeza mzinda wa Alexandria m’dera la kothilira kwa Nile wa ku Igupto, kumene, chifupifupi 280 B.C.E., kutembenuzidwa koyamba kwa Baibulo kuchokera ku Chihebri kupita ku Chigriki kunayambika. Kutembenuza kumeneku, komwe kunadzadziŵika monga Septuagint, kunali Baibulo logwiritsiridwa ntchito ndi atsatiri a Yesu mu dziko lolankhula Chigriki.
M’nthaŵi ya Roma, mphamvu ya dziko yachisanu ndi chimodzi, Yesu anabweretsedwa ku Igupto monga mwana wachichepere kumpulumutsa iye kuchokera kwa Herodi wa nsanje. (Mateyu 2:13-15) Aigupto analipo mu Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. kudzamva ziphunzitso zozizwitsa za mbiri yabwino ya Chikristu. Ndipo Mkristu wolongosoka wa m’zana loyamba Apollo anabwera kuchokera kumeneko.—Machitidwe 2:10; 18:24.
Inde, Igupto ndi Aigupto awonekera kwambiri m’mbiri ya Baibulo, ndipo zopeza zambiri za ofufuza zofotseredwa pansi zimatsimikizira zimene Malemba amanena ponena za dziko lakale limeneli. Ndithudi, Igupto anali wowonekera kotero kuti mu ndime zina za ulosi, amaimira dziko lonse lomwe liri pansi pa ulamuliro wa Satana. (Ezekieli 31:2; Chivumbulutso 11:8) Koma Igupto wakale, mosasamala kanthu za mphamvu yake monga mphamvu ya dziko, sanali wokhoza kuthetsa kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova. Ndipo ichi chinalinso chowona ndi mphamvu ya dziko yachiŵiri ya mbiri ya Baibulo, Asuri, monga mmene tidzawonera m’kope lotsatira la magazini ya Nsanja ya Olonda.
[Mawu a M’munsi]
a The Jewish Encyclopedia imanena kuti: “Chikhulupiriro chakuti moyo umapitirizabe kukhalapo pambuyo pa kufa kwa thupi . . . sichinaphunzitsidwe molongosoka kulikonse m’Malemba Oyera.”
b Kaamba ka kukambitsirana kosangalatsa kwa mavuto ogwirizana ndi ndandanda zimenezi, onani bukhu la Aid to Bible Understanding, masamba 324-325, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c Iyi inali imodzi ya nkhondo zosankha zomenyedwa pa Megido, yomwe inatsogolera ku kukhala kwake chizindikiro cha nkhondo yosankha yomalizira ya Mulungu motsutsana ndi mitundu ya anthu yowukira pa Harmagedo, kapena pa Armagedo.—Chivumbulutso 16:16.
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mediterranean Sea
Carchemish
Euphrates
Megiddo
Jerusalem
Alexandria
GOSHEN
Memphis
Nile
LOWER EGYPT
Thebes
[Mawu a Chithunzi]
Based on a map copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi patsamba 24]
Mulungu wa Igupto wosonyezedwa ndi thupi la munthu ndi mutu wa mphamba
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the British Museum, London
[Zithunzi patsamba 25]
Mbali ya “Bukhu la Akufa” lopezedwa mkati mwa bokosi la maliro la mu Igupto
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Superintendence of the Museo Egizio, Turin
Bokosi la maliro la mu Igupto ndi chophimba cha mtembo wokonzedwa bwino
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Superintendence of the Museo Egizio, Turin
[Chithunzi patsamba 26]
Mfumu Tutankhamen pambali pa mulungu wokhala pansi Amon
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Superintendence of the Museo Egizio, Turin