Kodi Muli ndi Dzina Lotani?
M’Baibulo, liwulo “dzina” nthaŵi zina limatanthauza mbiri ya munthu. Mwachitsanzo, Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mbiri [“dzina,” NW] yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.” (Mlaliki 7:1; yerekezerani ndi Miyambo 22:1.) Malinga ndi kunena kwa Solomo, munthu sabadwa ndi dzina labwino. M’malo mwake, pa moyo wake wonse amapeza mbiri yokhala ndi tanthauzo lenileni. Dzina lake limamdziŵikitsa monga mwa mikhalidwe yake, kaya ndi wopatsa kapena wodzikonda, wachifundo kapena wankhanza, wodzichepetsa kapena wodzikweza, ndiponso wolungama kapena woipa.
Lingalirani za Davide. Panthaŵi ya ufumu wake, anali wolimba ndi wosagwedera. Komanso, Davide modzichepetsa anazindikira zolakwa zake ndipo analapa machimo ake aakulu. Pazifukwa zokwanira, mneneri wa Yehova anasonyeza kuti Davide anali “munthu wa pamtima [pa Mulungu].” (1 Samueli 13:14) Davide wachinyamatayo anali kale ndi dzina labwino ndi Mulungu.
Komabe, Mfumu ya Yuda Yehoramu inadzipangira dzina loipa. Inachotsa nzika zake pa kulambira Yehova ndiponso inapha abale ake asanu ndi mmodzi ndiponso akalonga ena a Yuda. Potsiriza, Yehova anakantha Yehoramu ndi matenda oŵaŵa amene anafa nawo. Baibulo limati Yehoramu ‘anamuka wopanda wina womlakalaka,’ kapena malinga ndi Today’s English Version, “atafa palibe anadandaula.”—2 Mbiri 21:20.
Moyo wa Davide ndi Yehoramu umasonyeza choonadi cha mwambi wa Baibulo wonena kuti: “Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.” (Miyambo 10:7) Motero aliyense wa ife ayenera kulingalira bwino funso ili, ‘Kodi ndikupanga dzina lotani ndi Mulungu komanso ndi anzanga?