Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi mkazi wachichepere Wachiyuda wotchedwa Estere anachita chisembwere ndi mfumu ya ku Perisiya kuti amkonde ndikupeza mwaŵi?
Ena aganizira motero kuchokera m’malipoti akudziko, koma cholembedwa chodalirika cha Baibulo chimatsutsa kalingaliridweko.
Katswiri Wachiyuda wa mbiri yakale wotchedwa Flavius Josephus akupereka lipoti lakudziko losimba kuti Vasiti mfumukazi ya ku Perisiya anakana kukawonekera pamaso pa mwamuna wake, Ahaswero. Zitatero, mfumuyo, mwachiwonekere Xerxes I wa m’zaka za zana lachisanu B.C.E., mwaukali anamkana Vasiti ndipo anavomereza kuti pakhale kufunafuna muufumuwo kuti apeze mfumukazi yatsopano. Anamwali achichepere okongola anasonkhanitsidwa ndikukongoletsedwa kwanthaŵi yaitali.
“Chotero, pamene [mdindo wa mfumu] analingalira kuti anamwaliwo asamaliridwa mokwanira . . . ndipo tsopano anali oyenerera kukaloŵa ku kama wa mfumu, iye anatumiza mmodzi tsiku lirilonse kuti akagone ndi mfumu, amene, pambuyo pa kugonana naye, anam’bwezanso kwa mdindoyo. Koma, pamene Estere anafika kwa iye, anasangalatsidwa naye ndipo choncho, pokhala anamkonda iye, anamtenga kukhala mkazi wake walamulo nachita phwando laukwati.”—Jewish Antiquities, Bukhu XI, 184-202, lotembenuzidwa ndi Ralph Marcus, (Bukhu 11, mutu 6, ndime 1, 2, monga momwe latembenuzidwira ndi William Whiston).
Mbiri yakudzikoyi ingatsogolere munthu kulingalira kuti anamwaliwo anakhalamo ndi phande m’chisembwere chakugonana ndi mfumuyo ndikuti kusiyana kokha kwa Estere kunali kwakuti chisembwere chake chinatsogolera kuukwati ndikukhala kwake mfumukazi. Komabe, Baibulo limatipatsa chidziŵitso cholondola ndi chokhutiritsa.
Pambuyo pofotokoza machitidwe okongoletsa, Baibulo limati: ‘Ndipo namwali aliyense analoŵa kwa mfumu motero, . . . Madzulo ake analowamo, nabwera m’mawa mwake kumka ku nyumba yachiŵiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang’ono a mfumu; iyeyu sanalowanso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko.’—Estere 2:13, 14.
Malemba akunena kuti Estere “anatengedwa” kumka “kunyumba ya akazi” kwanthaŵi yaitali, nakongoletsedwa: ‘Momwemo anatengedwa Estere kumka kwa mfumu Ahaswero . . . Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti.’—Estere 2:8, 9, 16, 17.
Kodi mwawona m’zolembera za Baibulo kumene akazi anaperekedwa pambuyo pa kuthera usiku ndi mfumu? ‘Kunyumba yachiŵiri ya akazi, nasungidwa ndi wosunga akazi aang’ono.’ Chotero iwo anakhala akazi aang’ono. Moredekai, yemwe analemba bukhu la Baibulo la Estere, anali Mhebri, ndipo m’fuko lake kumbuyoko, mkazi wamng’ono adali ndiudindo wa kukhala mkazi wachiŵiri. Chilamulo chaumulungu chinavomereza kuti mwamuna Wachiisrayeli angatenge msungwana wachilendo amene anagwidwa m’nkhondo, ndipo akakhala mkazi wake wamng’ono, kapena mkazi wachiŵiri, wokhala ndikuyenerera ndi kutetezeredwa kwalamulo. (Deuteronomo 21:10-17; yerekezerani ndi Eksodo 21:7-11.) Ana obadwa kwa mkazi wamng’ono walamuloyu anali olandiridwa mwalamulo ndipo akakhoza kutenga choloŵa. Ana aamuna 12 a Yakobo, makolo a mafuko 12 a Israyeli, anali mbadwa ya akazi ake ndi akazi ake aang’ono.—Genesis 30:3-13.
Njira yotsatiridwa inali yakuti pambuyo pakuti anamwaliwo akhala ndi mfumu ya ku Perisiya, iwo anaperekedwa kunyumba ya wosunga akazi. Ichi chikusonyeza kuti iwo anakhala akazi ake achiŵiri.
Bwanji nanga ponena za Estere? Baibulo silimati anagona ndi mfumu napeza chiyanjo. Ilo silimasimbanso kuti anaperekedwa kunyumba ya osunga akazi, koma limangoti: ‘Momwemo anatengedwa Estere kumka kwa mfumu Ahaswero, kunyumba yake yachifumu . . . Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse.’ Kumbukirani kuti pachiyambi, popanda kupotoza maubwino ake aunamwali mwakugonana, iye anatha ‘kukomeredwa’ ndi “Hege wosunga akazi.” Kuwonjezera apa: “Ndipo Estere anayamikiridwa pamaso pa onse ompenya.” (Estere 2:8, 9, 15-17) Chotero Estere mwachiwonekere anasangalatsa mfumu nalemekezedwa naye, monga mmene analemekezedwera ndi ena.
Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kukhala ndi mfundo zenizeni ndi chidziŵitso chimene Baibulo likutipatsa! Ngakhale kuti papita zaka zikwi zambiri chiyambire kuchitika kwa zochitikazo, tiri nachodi chifukwa chokhalira ndi chidaliro chakuti Estere anachita molongosoka ndipo mogwirizana ndi miyezo yaumulungu.