-
Analimba Mtima Kuteteza Anthu a MulunguNsanja ya Olonda—2011 | October 1
-
-
Esitere ayenera kuti anachita mantha kwambiri atamva uthengawo. Pamenepa chikhulupiriro chake chinayesedwa. Zimene Esitere anayankha Moredekai zinasonyeza kuti anali ndi mantha kwambiri. Iye anakumbutsa Moredekai za lamulo loletsa kukaonekera kwa mfumu usanaitanidwe lija, chifukwa zimenezi zingachititse kuti uphedwe. Munthu ankapulumuka pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide. Ndipo akaganizira zimene zinachitikira Vasiti atakana kukaonekera kwa mfumu, Esitere ankaona kuti ngakhale kuti ndi mkazi wa mfumu, n’kutheka kuti mfumuyi singamuchitire chifundo. Esitere anauza Moredekai kuti panali patatha masiku 30 asanaitanidwe kuti akaonekere kwa mfumu. Zimenezi ziyenera kuti zinachititsa Esitere kuyamba kukayikira ngati mfumuyi, yomwe sinkachedwa kupsa mtima, inkamukondabe.d—Esitere 4:9-11.
-
-
Analimba Mtima Kuteteza Anthu a MulunguNsanja ya Olonda—2011 | October 1
-
-
d Sasita Woyamba ankadziwika kuti anali munthu wosachedwa kupsa mtima. Mwachitsanzo, katswiri wina wa ku Greece wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodotus, analemba zinthu zina zimene Sasita anachita pamene ankamenyana ndi Agiriki. Mfumuyi inalamula kuti panyanja ya Hellespont pamangidwe mlatho pogundaniza mabwato. Mphepo yamkuntho itaphwasula mlathowo, Sasita analamula kuti anthu amene anamanga mlathowo adulidwe mitu. Iye analamulanso asilikali ake kuti alange nyanjayo mwa kukwapula madzi kwinaku akuwerenga mokweza mawu olalata. Pa nkhondo yomweyi, munthu wina wolemera atapempha kuti mwana wake asalowe usilikali, Sasita analamula kuti mwanayo adulidwe pakati ndipo mtembo wake uikidwe poonekera kuti anthu ena atengerepo phunziro.
-