Mulungu Anapereka Chiyembekezo cha Moyo Wosatha Padziko Lapansi
“Chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake . . . pamaziko a chiyembekezo.”—AROMA 8:20.
1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi n’chofunika kwambiri kwa ife? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakayikira zodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi?
MWINA mukukumbukira mmene munasangalalira pamene munamva koyamba kuti posachedwapa anthu sadzakalambanso kapena kufa, koma adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. (Yoh. 17:3; Chiv. 21:3, 4) Mosakayikira panopa mumasangalala kuuza ena za chiyembekezo cha m’Malemba chimenechi. Ndipotu, chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi, ndi mbali yofunika kwambiri ya uthenga wabwino umene timalalikira. Chiyembekezo chimenechi, chimakhudza kwambiri moyo wathu wonse.
2 Koma Matchalitchi Achikhristu ndi amene makamaka amanyalanyaza chiyembekezo chimenechi cha moyo wosatha padziko lapansi. Ngakhale kuti Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akafa palibe mbali yake ina imene imapitiriza kukhala ndi moyo, matchalitchi ambiri amaphunzitsa zinthu zotsutsana ndi Malemba. Iwo amati munthu ali ndi mzimu womwe sufa ndipo munthuyo akafa mzimu umenewo umakakhala kudziko lamizimu. (Mlal. 9:5) N’chifukwa chake, anthu ambiri amakayikira zodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Motero tingafunse kuti: Kodi Baibulo limaphunzitsadi za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi? Ngati limatero, kodi Mulungu anayamba kunena zimenezi liti?
‘Kuperekedwa ku Mkhalidwe Wopanda Pake . . . Pamaziko a Chiyembekezo’
3. Kodi cholinga cha Mulungu kwa anthu chinadziwika bwanji, kumayambiriro kwa mbiri ya anthu?
3 Yehova anafotokoza cholinga chake kwa anthu kalekale atangolenga kumene anthu oyambirira. Mulungu anasonyeza bwino kuti Adamu akanakhala ndi moyo wosatha akanamvera. (Gen. 2:9, 17; 3:22) Mbadwa zoyambirira za Adamu zinkadziwa kuti anthu anachimwa, ndipo zinkaona umboni wa zimenezi. Zinkaona kuti njira ya kumunda wa Edene inali yotseka ndipo anthu ankakalamba ndi kufa. (Gen. 3:23, 24) Pamene nthawi inkapita, zaka zimene anthu ankakhala ndi moyo zinayamba kuchepa. Mwachitsanzo, Adamu anakhala ndi moyo zaka 930, Semu, amene anapulumuka chigumula, anakhala ndi moyo zaka 600 ndipo mwana wake Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka 438 zokha. Tera, yemwe anali bambo ake a Abulahamu, anakhala moyo zaka 205. Abulahamu anakhala ndi moyo zaka 175, mwana wake Isake zaka 180, pomwe Yakobo zaka 147. (Gen. 5:5; 11:10-13, 32; 25:7; 35:28; 47:28) Anthu ambiri ayenera kuti anadziwa kuti moyo unayamba kukhala waufupi chonchi chifukwa chakuti moyo wosatha unatayika. Kodi panali chifukwa chilichonse choyembekezera kuti angapezenso moyo wosatha?
4. N’chifukwa chiyani anthu akale okhulupirika anali ndi chiyembekezo chakuti Mulungu adzabwezeretsa madalitso amene Adamu anataya?
4 Mawu a Mulungu amati: “Chilengedwe [kutanthauza anthu] chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake . . . pamaziko a chiyembekezo.” (Aroma 8:20) Kodi chiyembekezo chake n’chotani? Ulosi wa m’Baibulo woyambirira weniweni unanena za “mbewu” imene ‘idzalalire mutu wa njoka.’ (Werengani Genesis 3:1-5, 15.) Lonjezo la Mbewu limeneli, linawapatsa anthu okhulupirika chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo chakuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu sichidzalephereka. Linapatsa anthu monga Abele ndi Nowa chifukwa chokhulupirira kuti Mulungu adzabwezeretsa madalitso amene Adamu anataya. Anthu amenewa ayenera kuti anazindikira kuti ‘kulalira chitende cha mbewu’ kunatanthauza kukhetsa magazi.—Gen. 4:4; 8:20; Aheb. 11:4.
5. N’chiyani chikusonyeza kuti Abulahamu anali ndi chikhulupiriro chakuti akufa adzauka?
5 Taganizirani za Abulahamu. Poyesedwa, iye anali wokonzeka kupereka ‘nsembe mwana wake wobadwa yekha Isake.’ (Aheb. 11:17) N’chifukwa chiyani iye anali wofunitsitsa kuchita zimenezi? (Werengani Aheberi 11:19.) Chifukwa chakuti ankakhulupirira kuti akufa adzauka. Abulahamu anali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira zimenezi. Pajatu Yehova anabwezeretsa mphamvu ya kubereka ya Abulahamu, ndipo anachititsa kuti iye ndi mkazi wake Sara abereke mwana, ngakhale kuti iwo anali okalamba. (Gen. 18:10-14; 21:1-3; Aroma 4:19-21) Panalinso lonjezo limene Yehova anauza Abulahamu. Mulungu anali atamuuza kuti: “Mwa Isake zidzaitanidwa mbewu zako.” (Gen. 21:12) Motero Abulahamu anali ndi zifukwa zomveka zokhalira ndi chiyembekezo chakuti Mulungu adzaukitsa Isake.
6, 7. (a) Kodi Yehova anachita pangano lotani ndi Abulahamu? (b) Kodi lonjezo la Yehova kwa Abulahamu linapereka bwanji chiyembekezo kwa anthu?
6 Chifukwa cha chikhulupiriro cholimba chimene Abulahamu anali nacho, Yehova anachita naye pangano lokhudza mbadwa kapena kuti “mbewu” yake. (Werengani Genesis 22:18.) Yesu Khristu ndi amene anadzakhala mbali yoyamba ya “mbewu” imeneyi. (Agal. 3:16) Yehova anali atauza Abulahamu kuti “mbewu” yake idzachuluka ngati “nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” Zimenezi zinatanthauza kuti chiwerengero chake chinali chosadziwika kwa Abulahamu. (Gen. 22:17) Koma kenako chiwerengerocho chinadzadziwika. Yesu Khristu ndiponso anthu 144,000 amene adzalamulira naye mu Ufumu wake, ndiwo “mbewu” imeneyi. (Agal. 3:29; Chiv. 7:4; 14:1) Kudzera mu Ufumu wa Mesiya “mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.”
7 Abulahamu sakanatha kumvetsa tanthauzo lonse la pangano lake ndi Yehova. Ngakhale zinali choncho, Baibulo limanena kuti iye “anali kuyembekeza mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:10) Mzinda umenewu ndi Ufumu wa Mulungu. Koma popeza Abulahamu anamwalira, kuti adzalandire madalitso mu Ufumu umenewu, afunika adzakhalenso ndi moyo. Iye adzatha kupeza moyo wosatha padziko lapansi mwa kuukitsidwa. Ndiponso anthu amene adzapulumuke Armagedo kapena amene adzaukitsidwe akhoza kudzakhala ndi moyo wosatha.—Chiv. 7:9, 14; 20:12-14.
‘Mzimu Undifulumiza’
8, 9. Tikudziwa bwanji kuti buku la Yobu silimangofotokoza nkhani ya mayesero amene munthu mmodzi anakumana nawo?
8 Yobu anakhala ndi moyo mdzukulutuvi wa Abulahamu, Yosefe, atakhalako kale koma Mose asanakhale mneneri. Buku la m’Baibulo la Yobu, lomwe liyenera kuti linalembedwa ndi Mose, limafotokoza chifukwa chake Yehova analola kuti Yobu avutike ndiponso mmene zinthu zinakhalira pambuyo pake. Komatu buku la Yobu silimangofotokoza nkhani ya mayesero amene Yobu anakumana nawo. Nkhani yake yaikulu imakhudza anthu onse ndiponso zolengedwa zauzimu. Bukuli limasonyeza kuti Yehova amalamulira mwachilungamo. Limasonyezanso kuti nkhani imene inabuka mu Edene imakhudza umphumphu wa atumiki onse a Mulungu padziko lapansi ndi chiyembekezo chawo cha moyo wosatha. Ngakhale kuti Yobu sankadziwa nkhani imeneyi, iye sanalole kuti anzake atatu aja amupangitse kuganiza kuti walephera kusunga umphumphu. (Yobu 27:5) Zimenezi ziyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutithandiza kudziwa kuti ifenso tikhoza kusungabe umphumphu ndiponso kuchirikiza ulamuliro wa Yehova.
9 Mabwenzi atatu a Yobu, amene kwenikweni sanamutonthoze, atamaliza kulankhula, “Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha.” Kodi n’chiyani chinamuchititsa kulankhula? Iye anati: “Ndadzazidwa ndi mawu, ndi mzimu wa mkati mwanga undifulumiza.” (Yobu 32:5, 6, 18) Ngakhale kuti mawu ouziridwa amene Elihu analankhula anakwaniritsidwa pamene zinthu zinayambanso kumuyendera bwino Yobu, mawu akewo alinso ndi tanthauzo kwa anthu ena. Amapereka chiyembekezo kwa anthu onse osunga umphumphu.
10. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti nthawi zina uthenga umene Yehova amapereka kwa munthu mmodzi umagwiranso ntchito kwa anthu onse?
10 Nthawi zina Yehova amapereka uthenga kwa munthu mmodzi umene umagwiranso ntchito kwa anthu onse. Chitsanzo cha zimenezi ndi ulosi wa Danieli wokhudza maloto a mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara. Malotowo anali onena za mtengo waukulu umene unalikhidwa. (Dan. 4:10-27) Ngakhale kuti malotowa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara, analoseranso za zinthu zina zazikulu zodzachitika m’tsogolo. Anasonyeza kuti ulamuliro wa Mulungu umene unaimiridwa padziko lapansi ndi ufumu wa m’banja la Mfumu Davide, udzayambiranso patadutsa zaka 2,520 kuchokera mu 607 B.C.E.a Ulamuliro wa Mulungu umene umakhudza dziko lapansi unayamba kugwira ntchito m’njira yatsopano pamene Yesu Khristu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba mu 1914. Posachedwapa Ufumuwo udzakwaniritsa m’njira yodabwitsa kwambiri zinthu zimene anthu omvera akuyembekezera.
“Mlanditse, Angatsikire Kumanda”
11. Kodi mawu a Elihu anasonyeza chiyani za Mulungu?
11 Poyankha mawu a Yobu, Elihu ananena za ‘mthenga, womasulira mawu mmodzi mwa chikwi, woonetsa munthu chomuyenera.’ Ndiyeno kodi chikuchitika n’chiyani mthengayo ‘atapembedza Mulungu, kuti akomere mtima munthuyo’? Elihu anati: “Pamenepo Mulungu am’chitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, ndam’pezera dipo. Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.” (Yobu 33:23-26) Mawu amenewa anasonyeza kuti Mulungu anali wokonzeka kulandira “dipo,” kapena kuti chophimba machimo, a anthu olapa.—Yobu 33:24.
12. Kodi mawu a Elihu amapereka chiyembekezo chotani kwa anthu onse?
12 Mofanana ndi aneneri, amene sanamvetse zinthu zina zimene analemba, Elihu ayenera kuti sanadziwe tanthauzo lonse ndi kufunika kwa dipo. (Dan. 12:8; 1 Pet. 1:10-12) Ngakhale zili choncho, mawu a Elihu anasonyeza kuti pali chiyembekezo chakuti tsiku lina Mulungu adzalandira dipo ndipo adzamasula anthu ku ukalamba ndi imfa. Mawu akewo anapereka kwa anthu chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha. Buku la Yobu limasonyezanso kuti akufa adzauka.—Yobu 14:14, 15.
13. Kodi mawu a Elihu ali ndi tanthauzo lotani kwa Akhristu?
13 Masiku ano, mawu a Elihu adakali ndi tanthauzo kwambiri kwa Akhristu mamiliyoni ambiri amene akuyembekeza kudzapulumuka chiwonongeko cha dongosolo la zinthu lilipoli. Pakati pa anthu opulumuka amenewa, padzakhala okalamba amene adzabwerera ku masiku a ubwana wawo. (Chiv. 7:9, 10, 14-17) Ndiponso anthu okhulupirika amasangalala ndi chiyembekezo choti adzaonanso anthu oukitsidwa atabwerera ku unyamata wawo. Kuti Akhristu odzozedwa adzalandire moyo wosakhoza kufa kumwamba, ndiponso kuti “nkhosa zina” za Yesu zidzalandire moyo wosatha padziko lapansi, m’pofunika kukhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu.—Yoh. 10:16; Aroma 6:23.
Imfa Idzamezedwa Padziko Lapansi
14. N’chiyani chikusonyeza kuti Chilamulo cha Mose pachokha sichikanatha kupatsa Aisiraeli chiyembekezo cha moyo wosatha?
14 Mbadwa za Abulahamu zitalowa m’pangano ndi Mulungu, zinakhala mtundu woima paokha. Powapatsa Chilamulo, Yehova anati: “Muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nawo ndi moyo.” (Lev. 18:5) Koma popeza kuti Aisiraeli analephera kutsatira mfundo zangwiro za Chilamulo, iwo anayenera kufa malinga ndi Chilamulocho, choncho anafunika kumasulidwa.—Agal. 3:13.
15. Kodi Davide anauziridwa kulemba za madalitso a m’tsogolo ati?
15 Kuwonjezera pa Mose, Yehova anauziranso anthu ena olemba Baibulo kuti atchule za chiyembekezo cha moyo wosatha. (Sal. 21:4; 37:29) Mwachitsanzo, wamasalmo Davide anamaliza salmo lake lonena za mgwirizano umene olambira oona ku Ziyoni anali nawo, ponena kuti: “Pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.”—Sal. 133:3.
16. Pofotokoza za zimene zidzachitike m’tsogolo “padziko lonse lapansi,” kodi Yehova analonjeza chiyani kudzera mwa Yesaya?
16 Yehova anauziranso Yesaya kulosera za moyo wosatha padziko lapansi. (Werengani Yesaya 25:7, 8.) Mofanana ndi “chophimba” cholepheretsa munthu kupuma, uchimo ndi imfa zakhala zikusautsa anthu kwambiri. Yehova akutsimikizira anthu ake kuti uchimo ndi imfa zidzamezedwa, kapena kuti kuchotsedwa, “padziko lonse lapansi.”
17. Malinga ndi ulosi, kodi ndi udindo uti wa Mesiya umene unatsegula njira ya ku moyo wosatha?
17 Taganiziraninso za mwambo wa m’Chilamulo cha Mose wokhudza mbuzi ya Azazeli. Kamodzi pa chaka, pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe ‘ankaika manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zawo zonse, monga mwa zochimwa zawo zonse; n’kuika izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu.’ (Lev. 16:7-10, 21, 22) Yesaya analosera za kubwera kwa Mesiya, amene anali kudzakhala ndi udindo ngati umenewu wonyamula “zowawa,” “zisoni” ndi “machimo a ambiri,” n’kutsegula njira ya ku moyo wosatha.—Werengani Yesaya 53:4-6, 12.
18, 19. Kodi lemba la Yesaya 26:19 ndi la Danieli 12:13 limafotokoza za chiyembekezo chotani?
18 Kudzera mwa Yesaya, Yehova anauza anthu ake, Aisiraeli, kuti: “Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yawo idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m’fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba.” (Yes. 26:19) N’zoonekeratu kuti Malemba Achiheberi amapereka chiyembekezo cha kuuka kwa akufa ndiponso chakuti anthu adzakhala ndi moyo padziko lapansi. Mwachitsanzo, Danieli ali ndi zaka pafupifupi 100, Yehova anamutsimikizira kuti: “Udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.”—Dan. 12:13.
19 Chifukwa choti anali ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka, Marita anatha kuuza Yesu za mlongo wake amene anamwalira kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” (Yoh. 11:24) Kodi zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso zimene ophunzira ake analemba mouziridwa, zinasintha chiyembekezo chimenechi? Kodi Yehova amaperekabe kwa anthu chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi? Tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi chilengedwe, kapena kuti anthu, “chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake” pamaziko a chiyembekezo chotani?
• Kodi tikudziwa bwanji kuti Abulahamu anali ndi chikhulupiriro chakuti akufa adzauka?
• Kodi mawu a Elihu kwa Yobu amapereka chiyembekezo chotani kwa anthu?
• Kodi Malemba Achiheberi amatsindika bwanji za chiyembekezo chakuti akufa adzauka ndiponso chakuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi?
[Chithunzi patsamba 5]
Mawu a Elihu kwa Yobu amapereka chiyembekezo chakuti anthu adzamasulidwa ku ukalamba ndi imfa
[Chithunzi patsamba 6]
Danieli anatsimikiziridwa kuti ‘adzaima m’gawo lake masiku otsiriza’