Mwetulirani—N’zothandiza kwa Inu!
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU JAPAN
KUKAKHALA koona kumafafaniza kukayikirana. Kumachotsa malingaliro olakwika ambiri okundikidwa kwazaka zambiri. Kumafeŵetsa mitima youma chifukwa chosakhulupirira ndiponso kusakhulupirirana. Kumadzetsa mpumulo ndiponso chimwemwe kwa anthu ambiri. Kumafotokoza kuti, “Ndikudziŵa. Osada nkhaŵa.” Kumapereka mawu olimbikitsa akuti, “Ndikukhulupirira kuti tingakhale paubwenzi.” Koma kodi chida champhamvu kwambiri chimenechi n’chiyani? Ndicho kumwetulira. Ndipo kukhoza kukhala kumwetulira KWANU.
Kodi kumwetulira n’chiyani? Kaŵirikaŵiri madikishonale amamasulira kumwetulira kuti ndiko ‘kaonekedwe ka nkhope kamene pakamwa pamapindikira m’mwamba pang’ono, kusonyeza chisangalalo, chiyanjano, kapena chimwemwe.’ Pamenepo m’pamene pagona chinsinsi cha kumwetulira kwaubwenzi. Kumwetulira ndi njira yofotokozera malingaliro a munthu kapena yogwirizanitsira maganizo a munthu ndi maganizo a ena popanda kutulutsa mawu. N’zoona kuti, kumwetulira kungasonyezenso kunyodola kapena kunyoza, komatu imeneyo ndi nkhani ina.
Kodi kumwetulira kumasinthadi zinthu? Chabwino, kodi mukukumbukira nthaŵi yomwe kumwetulira kwa munthu winawake kunakupatsani mpumulo kapena kunakukhalitsani womasuka? Kapena pamene munachita mantha kapena kudzimva kukhala wokanidwa chifukwa chakuti winawake sanakumwetulireni? Inde, kumwetulira kumasinthadi zinthu. Kumakhudza onse aŵiri, womwetulirayo komanso womwetuliridwa. Ponena za adani ake, munthu wa m’Baibulo Yobu anati: “Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.” (Yobu 29:24) “Kusangalala” kwa nkhope ya Yobu kuyenera kuti kunasonyeza chimwemwe chake kapena kukondwera kwake.
Kumwetulira kudakali ndi zotsatira zabwino mpaka lerolino. Kumwetulira kwaubwenzi kungathandize kuthetsa nkhaŵa. Kungakhale kofanana ndi kaboo kotulukira mpweya pa mphika wa maungu. Pamene tavutika maganizo kapena kukhumudwa, kumwetulira kungatithandize kuthetsa kuvutika maganizo kwathuko ndiponso kugonjetsa mkwiyo wathuwo. Mwachitsanzo, nthaŵi zambiri Tomoko ankati akaona ena akumuyang’ana ankalingalira kuti iwo akumunyodola, iwo akamayang’ana kwina maso awo ndi ake akangokumana. Tomoko anali wosungulumwa komanso wosasangalala. Tsiku lina mnzake anamuuza kuti iye azimwetulira maso a anthuwo akangokumana ndi ake. Tomoko anayesa kuchita zimenezo kwa milungu iŵiri ndipo anadabwa kuona kuti aliyense ankam’mwetuliranso. Kuvutika maganizo konse kunatha. “Moyo tsopano wakhala wosangalatsa kwambiri,” iye anatero. Inde, kumwetulira kumatikhalitsa omasuka kwambiri ndi anthu ena ndipo kumatithandiza kukhala aubwenzi kwambiri.
Zotsatira Zabwino kwa Inu Komanso kwa Ena
Kumwetulira kungakhudze mtima wa munthu. Kumathandiza munthu kukhalabe ndi maganizo abwino. Komanso n’kwabwino kaamba ka thanzi lakuthupi. Pali mwambi umene umati, “Kuseka ndiko mankhwala abwino.” Ndithudi, odziŵa zamankhwala amati zolingalira za munthu zimakhudza kwambiri thanzi la munthuyo. Kufufuza kosiyanasiyana kumasonyeza kuti kuvutika maganizo kwakukulu, malingaliro oipa, ndi zina zotero zimafooketsa mphamvu ya m’thupi mwathu yoteteza ku matenda. Pamene kumwetulira kumatipangitsa kumva bwino, kuseka kumalimbikitsa mphamvu ya m’thupi mwathu yoteteza ku matenda.
Kumwetulira kumakhudza anthu ena kwambiri. Talingalirani kuti mukupatsidwa uphungu kapena kuti mukulangizidwa. Kodi n’kaonekedwe kotani ka nkhope kamene mungakonde kukaona pankhope ya munthu amene akukulangizaniyo? Kaonekedwe kopanda ubwenzi kapena kaukali kangasonyeze mkwiyo, kuŵaŵidwa mtima, kukana, kapenanso udani. Komano, kodi kumwetulira kwaubwenzi kooneka pankhope ya amene akukulangizaniyo sikungakukhalitseni womasuka kwambiri ndiponso kulabadira uphunguwo? Ndithudi, panthaŵi ya mavuto kumwetulira kumathandiza kuchepetsa kusamvana.
Malingaliro Abwino Amapangitsa Kumwetulira Kukhala Kosavuta
Kunena zoona, ambirife sitiri ngati akatswiri a maseŵero a zisudzo amene angamwetulire mwamsangamsanga nthaŵi iliyonse; komanso sitifuna kukhala anthu otero. Timafuna kuti kumwetulira kwathu kukhale kwachibadwa komanso kwenikweni. Mlangizi wina wa pasukulu yophunzitsa kuyankhulana anachitira ndemanga kuti: ‘Kumasuka ndiponso kumwetulira ndi mtima wonse n’kofunika. Kupanda kutero kumwetulira kwanu kungaoneke kwachiphamaso.’ Kodi tingamwetulire motani kuchokera pansi pa mtima? Baibulo lingatithandize pankhani imeneyi. Ponenapo za kayankhulidwe kathu ilo limatiuza pa Mateyu 12:34, 35 kuti: “Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima. Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m’chuma chake choipa.”
Kumbukirani kuti kumwetulira ndi njira yofotokozera malingaliro athu popanda kutulutsa mawu. Kukumbukira kuti timayankhula “mwa kusefuka kwake kwa mtima” ndi kuti “zabwino” zimatuluka ‘m’chuma chabwino,’ m’poonekeratu kuti chinsinsi cha kumwetulira koona chagona m’malingaliro ndi m’maganizo mwathu. Inde, mosakayika zinthu zimene zili mumtima mwathu zidzaonekera ndithu panthaŵi inayake, osati kokha mwa mawu ndi zochita zathu komanso mwa kaonekedwe ka nkhope yathu. Choncho, tifunikira kuyesetsabe kukhala ndi malingaliro abwino. Kaonekedwe ka nkhope yathu kamakhudzidwa kwambiri ndi maganizo athu ponena za anthu ena. Pachifukwa chimenechi, tiyeni tisumike maganizo athu pantchito zabwino za a m’banja mwathu, anthu amene tikukhala nawo, ndi mabwenzi athu apamtima. Tikatero kudzakhala kosavuta kuti tiwamwetulire. Kudzakhala kumwetulira koona, chifukwa chakuti kukuchokera mumtima wodzala ndi zinthu zabwino, chifundo, komanso chisomo. Maso athu adzakhala oŵala, ndipo anthu ena adzadziŵa kuti zimenezo n’zenizenidi.
Komabe, m’pofunikanso kudziŵa kuti anthu ena amavutika kwambiri kuti amwetulire kusiyana ndi ena chifukwa cha malo omwe anakulirako kapena chikhalidwe chawo. Iwo alibe chizoloŵezi chomwetulira anansi awo, ngakhale atakhala okoma mtima chotani kwa anansiwo. Mwachitsanzo, malinga ndi mwambo wawo, amuna a ku Japan amayembekezeka kukhala odekha ndiponso kukhala chete nthaŵi zonse. Choncho, ambiri mwa iwo alibe chizoloŵezi chomwetulira anthu amene akuoneka achilendo. Zingakhalenso choncho pachikhalidwe cha anthu ena. Mwinanso anthu ena angakhale amanyazi mwachibadwa ndipo kungakhale kowavuta kuti amwetulire ena. Motero, sitiyenera kuweruza ena mwa kuona mmene akumwetulirira kapena kuti amamwetulira kaŵirikaŵiri kapena ayi. Anthu ndi osiyanasiyana, chimodzimodzinso mikhalidwe yawo ndiponso njira zawo zoyankhulirana ndi ena.
Komabe, ngati kumwetulira anthu ena kumakuvutani, bwanji osayesetsa kutero? Baibulo limalangiza kuti: “Tisaleme pakuchita zabwino . . . Tichitire onse chokoma.” (Agalatiya 6:9, 10) Njira imodzi yochitira “chokoma” anthu ena ndiyo kuwamwetulira, ndipo inuyo mukhoza kuchita zimenezi! Choncho yambani ndinu kulonjera anthu ena ndi kuwalimbikitsa uku mukumwetulira. Adzakuyamikirani kwambiri. Komanso, mudzaona kuti kumwetulira n’kosavuta pamene mukukulitsa mkhalidwewu.
[Bokosi patsamba 30]
Chenjezo
N’zomvetsa chisoni kuti si kumwetulira konse kumene timaona komwe kumakhala koona. Anthu achinyengo, akuba, amalonda opanda khalidwe, ndi ena angamwetulire mochititsa chidwi kwambiri. Amadziŵa kuti kumwetulira kungafooketse anthu ndi kuwaphimba m’maso. Nawonso anthu a makhalidwe okayikitsa kapena anthu a zikhumbo zoipa angamwetulire mokopa kwambiri. Komano, kumwetulira kwawoko n’kwachabechabe; n’kwachinyengo. (Mlaliki 7:6) Choncho pamene tikukhala mosakayikira anthu ena monkitsa, tiyenera kudziŵa kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza,’ omwe ndi ovuta kuchita nawo. Tifunikira kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda,” monga momwe Yesu mwiniyo analangizira.—2 Timoteo 3:1; Mateyu 10:16.
[Chithunzi patsamba 31]
Yambani ndinu kulonjera anthu ena uku mukumwetulira